Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g88 4/8 tsamba 15-18
  • Nzeru Zoposa Zaka Zake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nzeru Zoposa Zaka Zake
  • Galamukani!—1988
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nkhani ya Kupatsidwa Mankhwala
  • Mlanduwo
  • Chigamulo
  • Waumphumphu Kufikira ku Mapeto
  • Phunziro kaamba ka Zipatala ndi Adokotala
  • Achichepere Amene Ali ndi “Ukulu Woposa Wamphamvu”
    Galamukani!—1994
  • Kodi Muli Wokhululukira?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Ndimayesetsa Kukhala ndi Zochita Zambiri M’gulu la Yehova
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Yendani Monga Momwe Mwalangizidwa ndi Yehova
    Nsanja ya Olonda—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1988
g88 4/8 tsamba 15-18

Nzeru Zoposa Zaka Zake

PANALI pakati pa usiku. Lisa wa zaka zakubadwa khumi ndi ziŵiri, wodwala kwambiri ndi wolefuka, anadabwitsidwa pamene namwino analowa m’chipinda chake cha m’chipatala kukamuthira mwazi.

Lisa anadandaula: “Kodi mungakakamize chimenechi motani pa ine? Atate anga ndi amayi anga sali ngakhale pano!” Ngakhale kuli tero namwino anamuthirabe.

Nkhani ya Kupatsidwa Mankhwala

Lisa, wanzeru, wachangu, wophunzira wa gawo la “A”, anasangalala ndi moyo ndi makolo ake ndi mbale wa zaka zakubadwa zisanu mu Winnipeg, Canada. M’ngululu ya 1985 iye anapatsidwa mankhwala akupha tizirombo kaamba ka matenda a zironda za pam’mero ndipo anavutika ndi zotulukapo zoŵaŵa. Umoyo wake unalefuka, ndipo mwamsanga pambuyo pake iye anauzidwa kukhala atakhala ndi matenda akutha kwamwazi oipa kwambiri, mkhalidwe umene kaŵirikaŵiri umapha.

Madokotala a ku Winnipeg analingalira za kupatsa dongosolo la kuchepetsako mphamvu ya matenda ndi kuthiridwa mwazi kwa kaŵirikaŵiri. Dongosolo la kuchepetsako mphamvu ya matenda kuli kuchiritsa kwa mankhwala a ululu. Nthanthi iri yakuti ululu umenewu umapha tizirombo. Komabe, Lisa ndi makolo ake anafuna kuchiritsa kosiyanako. Iwo anakana kuthiridwa mwazi kaamba ka zifukwa za m’Malemba. (Machitidwe 15:28, 29) Iwo anapezanso kukhala kodzetsa kupweteka kosaleka ndi zotulukapo zofooketsa za dongosolo la kuchepetsako mphamvu ya matendayo.

Potsirizira pake, makolo a Lisa anamtenga kupita naye ku chipatala cha ku Toronto cha Ana Odwala, akumayembekezera kupeza adokotala ogwirizana. Koma m’malo mogwirizana, kuthiridwa mwazi kwa usiku kunachitidwa. M’mawa motsatira, October 25, lamulo la khoti linatengedwa la kupatsa mlandu chipatala kaamba ka kukakamiza kupatsa mankhwala kumeneko. Woweruza David R. Main analongosola kuyenera kwa lamuloko. Iye anasankha Sarah Mott-Trille kukhala loya wa Lisa. Mlanduwo unasinthidwira ku Monday, October 28, 1985.

Mlanduwo

Mlanduwo unazengedwa masiku asanu ndipo unachitidwira m’chipinda cha m’chipatala. Tsiku lirilonse, pa kufunsira kwake, Lisa anatengedwa pa mpando woyendetsa kupita m’chipinda pa kama lake la m’chipatala. Ngakhale kuti anali wodwala kwambiri, iye anali wotsimikiza kukhala wolowetsedwamo mwaumwini m’chosankha chimene chinaphatikizapo chikhulupiriro chake.

Kukambitsiranako kunayamba ndi kuyenera kwa adokotala kaamba ka kupatsa mankhwala. M’kuweruza kwake kolembedwa, Woweruza Main analongosola kuti: “Kupatsidwa mankhwala monga momwe kwanenedwera ndi adokotala omwe achitira umboni pamaso pa bwalo la milanduli kuli ponse paŵiri koŵaŵa ndi kwankhalwe ndipo kukapita ku utali wolingaliridwa wa nyengo ya nthaŵi. Chikuyembekezeredwa kuti kuthiridwa mwazi kobwerezabwereza kudzafunikira kusungilira wodwalayo.” Chinadziŵidwanso kuti zotulukapo za pambali za dongosolo la kuchepetsako mphamvu ya matenda ziri zambiri ndi zoŵaŵa.

Chochitikacho chinapitirizabe moŵaŵa pa tsiku lachinayi. Lisa anachirikizidwa kotero kuti anakhoza kulongosola mwachindunji kwa woweruza. Aliyense m’chipinda cha milandu, kuphatikizapo Lisa, anadziŵa kuti iye anali kuyang’anizana ndi imfa mosasamala kanthu zakuti kaya analandira kuthiridwa mwazi kapena ayi. Palibe kuchiritsa ku matenda akutha kwa mwazi amene iye anali kuvutika nawo.

Loya wa Lisa anamfunsa iye mosamala ndi mwanzeru. Panali ochepa omwe sanalire pamene Lisa molimba mtima analongosola imfa yake yoyandikira, chikhulupiriro chake mwa Yehova, ndi kutsimikizira kwake kwa kukhala womvera ku lamulo lake pa kuyera kwa mwazi. Iye ananena kuti akakhoza molimbika ndi mwa kuthupi kulimbana ndi kuyesayesa kulikonse kwa kupereka kuthira mwazi kwa iye. Ndemanga yake yopepuka ndi yolimba mtima inagwira mtima wa aliyense.

“Tsopano watiuza kuti umakhulupirira mwa Mulungu,” loya wake anatero. “Kodi ungatiuze ife ngati iye ali weniweni kwa iwe?”

“Chabwino, iye ali monga bwenzi,” Lisa anayankha tero. “Nthaŵi zina pamene ndiri ndekha, ndingakhoze kulankhula kwa iye . . . monga bwenzi; nditawopsyezedwa ndipo nditakhala panyumba ndekha, ndimamfunsa iye kaamba ka chithandizo ndipo ndimangolankhula kwa iye monga ngati ali m’chipinda kumbali kwanga.”

“Lisa, ngati winawake akanena kwa iwe, kodi ndi ziti zimene ziri zinthu zofunika m’moyo wako, kodi nchiyani chimene iwe ukanena?”

“Chimvero changa kwa Yehova Mulungu ndi banja langa,” Lisa anayankha tero.

Loya wake anafunsa kuti: “Lisa, kodi chingapange kusiyana kulikonse kwa iwe kudziŵa kuti bwalo la milandu lakulamulira iwe kuti uthiridwe mwazi?”

“Ayi, chifukwa chakuti ndidzapitirizabe kukhala wokhulupirika kwa Mulungu wanga ndi kumvetsera ku malamulo ake chifukwa chakuti Mulungu ali wokulira kwambiri kuposa bwalo la milandu lirilonse kapena munthu aliyense.”

Lisa analongosola kudzimva kwake ponena za kuthiridwa mwazi kumodzi komwe kunakakamizidwa kale pa iye, akumanena kuti: “Chinandipangitsa ine kudzimva monga galu yemwe akugwiritsiridwa ntchito kaamba ka kufufuza, chifukwa chakuti sindinakhoze kulamulira chirichonse. Kokha chifukwa chakuti ndiri wachichepere, anthu amadzimva kuti angachite chirichonse kwa ine, koma ndimadzimva kuti ndiri ndi kuyenera kwa kudziŵa chimene chidzachitika kwa ine ndi chifukwa chimene iwo akuperekera mankhwala oterowo ndi chifukwa chimene akuwachita iwo popanda chilolezo cha makolo anga.”

“Kodi unagona usiku umenewo?” loya wake anafunsa tero.

“Ayi, sindinakhoze.”

“Kodi nchiyani chimene chinali chodera nkhaŵa chako?”

“Chabwino, chodera nkhaŵa changa chinali chimene Yehova Mulungu akanalingalira ponena za ine chifukwa ndimadziŵa kuti ngati nditapita molimbana ndi zifuno zake, sindidzakhala ndi lonjezo lirilonse la moyo wosatha, ndipo chinandidwalitsa kwambiri kuti ndinali kutenga mwazi wa munthu winawake mwa ine, chifukwa chakuti nthaŵi zonse pamakhala kuthekera kwa kutenga AIDS kapena kutupa kwa chiŵindi kapena kuyambukiridwa kwina, ndipo chonse chimene ndinachita usiku umenewo chinali kokha kungokwiya pa mwazi umenewo ndi kuyang’ana pa iwo.”

“Lisa, kodi ungalingalire za kusiyanitsa kuti ulongosole kwa woweruza chimene kuthiridwa mwazi kuliri molimbana ndi chifuno chako?”

“Chabwino, chimodzi chomwe ndingakhoze kulingalira chiri chigololo chogwirira chifukwa chakuti . . . kugwirira chigololo kuli kupangitsa chinthu chinachake kuchitika popanda kufuna kwako, ndipo ziri kokha mmenemo.”

Chigamulo

Tsiku la chisanu linali lovuta. Kuyambira pa chiyambi Woweruza Main anakhala wolingalira ndi wokhazikika. Kodi chikondi chake chikasonyezedwa mu chigamulo chake? Iye anatsiriza kuti: “Mwanayu Lisa Dorothy K. adzabwezedwa kunyumba, ku chisamaliro ndi kulamuliridwa kwa makolo ake.”

Woweruza Main analongosola chifukwa cha chiweruzo chake m’tsatanetsatane wokulira. Pakati pa zinthu zina, iye anati: “Mkhalidwe wa Lisa uli tsopano ndipo wakhala kuchokera pa tsiku limene anawona zolembedwa pa matendawa, kuti sanafune mbali iriyonse ya dongosolo la kuchepetsa mphamvu ya matenda ndi kuthiridwa mwazi. Iye amatenga kaimidweka osati kokha chifukwa chakuti kamalakwira zikhulupiriro za chipembedzo chake, ndipo ndiri wokhutiritsidwa kuti kamatero, komanso chifukwa chakuti iye sakufuna kukumana ndi kuŵaŵa ndi kuvutika kogwirizana ndi tsatanetsatane wa kupatsidwa mankhwala. . . . Ndikukana kupanga lamulo lirilonse lomwe lingaike mwanayu mumkhalidwe umenewo. Ndikupeza kukakamiza kwakuti iye apite m’kupatsidwa mankhwala kumeneku kukhala kosalandirika kotheratu.”

Ponena za kuthiridwa mwazi kwa chinyengo kwa pakati ka usiku uja kokakamizidwa pa Lisa, Woweruza Main ananena kuti: “Ndiyenera kupatsa mlandu wakuti [Lisa] walakwiridwa pa maziko a chipembedzo chake ndi msinkhu wake mogwirizana ndi gawo laling’ono la 15(1) la [Lamulo la ku Canada la Kuyenera ndi Ufulu]. M’mikhalidwe imeneyi, pa kupatsidwa kuthiridwa mwazi, kuyenera kwake ku chisungiko kwa umunthu wake mogwirizana ndi Gawo 7 kunaswedwa. Monga chotulukapo, ngakhale kuti iye angakhoze kunenedwa kukhala mwana yemwe anali wofunika chitetezero, kufunsirako kuyenera kuchotsedwa mogwirizana ndi gawo laling’ono la 24(1) la Lamulolo.”

Potsirizira pake, Woweruza Main anagogomezera kukhumbira kwake kwaumwini kulinga kwa Lisa, akumalongosola kuti: “Lisa ali wokongola, wanzeru koposa, wogwirizana, waulemu, wolingalira ndipo chofunika koposa, munthu wolimbika mtima. Iye ali ndi nzeru ndi ukulu msinkhu woposa bwino lomwe pa zaka zake ndipo ndikulingalira kuti chikakhala chabwino kunena kuti iye ali ndi mikhalidwe yonse yoyenera imene kholo lirilonse likaifuna mwa mwana wake. Iye ali ndi chikhulupiriro cha chipembedzo cholingaliridwa bwino, cholimba ndi chowonekera bwino. M’kawonedwe kanga, palibe unyinji uliwonse wa kulangiza kuchokera ku magwero alionse kapena kudidikiza kuchokera kwa makolo ake kapena wina aliyense, kuphatikizapo lamulo la bwalo la milanduli, komwe kudzagwedeza kapena kusintha chikhulupiriro chake cha chipembedzo.

“Ndikhulupirira kuti Lisa K. afunikira kupatsidwa mwaŵi wa kulimbana ndi matenda amenewa mwaulemu ndi mwamtendere wa maganizo. Chimenecho chingafikiridwe kokha mwa kulandira makonzedwe oikidwa ndi iye ndi makolo ake.”

Waumphumphu Kufikira ku Mapeto

Lisa ndi banja lake anachoka m’chipatala tsiku lomwelo. Lisa anatha, ndithudi, kulimbana ndi matenda ake ndi ulemu ndi mtendere wa maganizo. Pa November 17, 1985 iye anafa mwamtendere panyumba, m’manja okondedwa a amayi ake ndi atate.

Mkati mwa mlanduwo, Lisa analongosola kukambitsirana ndi amayi ake panthaŵi imene matenda a kutha mwazi ake anadziŵika choyamba, akumalongosola kuti: “Ndinakambitsirana ndi Amayi anga kuthekera kulikonse kumene ndinali nako ndipo tinaŵerenga Baibulo pamodzi ndipo tinaŵerenga mabukhu ena kuchokera ku chipembedzo chathu pamodzi, ndipo ndinauza iwo, . . . ‘Ngati ndidzafa, ndidzakuwonaninso m’dziko latsopano, ndipo ndidzakhala ndi chiyembekezo chotsimikizirika cha kukuwonani inu ndi kukhala pamodzi kosatha m’paradaiso wa padziko lapansi.’”

Phunziro kaamba ka Zipatala ndi Adokotala

Olemba za mankhwala a lamulo a ku Canada L. E. ndi F. A. Rozovsky anadziŵitsa mu Canadian Health Facilities Law Guide: “Zipatala ndi adokotala mofananamo angapeze phunziro lina kuchokera pa chigamulo chimenechi. Molunjika, iwo afunikira kupitiriza mosamalitsa ndi kupatsa mankhwala mosamalira zokana za munthuyo kapena makolo ake. Kusamala kufunikira kutengedwa kuti apewe kupatsa mankhwala kokakamiza ku mkhalidwe woikidwa monga ‘tsankho’ Gawo 15(1) la Lamulolo, kuphatikizapo msinkhu, mwamuna kapena mkazi, chipembedzo kapena chiyambi cha chibadwa.”

Komabe, ndimotani mmene adokotala afunikira “kupitiriza mosamalitsa” ndi kupewa tsankho la chipembedzo loterolo? A Rozovsky akulozera ku yankho lokhazikika: “Chifunikira kukumbukiridwa, ngakhale kuli tero, kuti ntchito yeniyeni ya malo a za umoyo iri osati kukhala mdani wa wodwala. Ntchito yeniyeni iri kuchita chimene chiri chokondweretsa kwenikweni kwa wodwalayo. M’nkhaniyi bwalo la milandu linapeza kuti chikondwerero chabwino chinayanja mkhalidwe wosiyanasiyana wa chisamaliro.”

Ndithudi, kumene wodwala ali mmodzi wa Mboni za Yehova, zikondwerero zabwino za iye zidzakumanidwa pamene banja ndi adokotala agwirizana m’kupereka zosinthana ndi kuthiridwa mwazi. Adokotala omwe atsatira kachitidweka sanawononge chisamaliro chabwino cha mankhwala. Monga mmene katswiri wodziŵa za mankhwala a achichepere pa M. D. Anderson Hospital mu Texas anachitira ripoti:

“Kuchiritsa kwa kuthira mwazi sikuli moyenerera kofunika kaŵirikaŵiri monga mmene kukuchitidwira. Mu mpambowu wa odwala a kansa ndi matenda olinganako, chisamaliro chabwino cha mankhwala sichinaipe kaamba ka chotulukapo cha kukana kuthiridwa mwazi.”

Ziyambukiro za mlandu wa Lisa ziri zofika patali. Kale kale, mwakutsatira chitsogozo cha bwalo la milandu la ku Canada, woweruza wa ku California wakana kukakamiza kupatsa mankhwala pa mtsikana wa zaka 14 zakubadwa. Kuwonjezerapo, pa February 11, 1986, British Columbia Health Association inapereka chitsogozo ku nduna zonse za zipatala chozikidwa mwachindunji pa mlandu wa Lisa, chikumanena kuti: “Mlanduwu ukupanga kachitidwe katsopano.”

M’nyengo ya kusokonezeka kwa lamulo ndi zamankhwala, chigamulo chimenechi chatsegula njira. Chiri cholungama ndi chabwino. Mtsogolo mudzatiuza ife mmene adokotala ambiri, zipatala, ndi oweruza adzatsatirira kutsogoza kwa umunthu ndi kwanzeru kopatsidwa kwa ife ndi Woweruza David R. Main ndi Lisa.

[Mawu Otsindika patsamba 17]

Panali oŵerengeka omwe sanalire pamene Lisa anakambitsirana molimba mtima za imfa yake yomwe inkadza

[Mawu Otsindika patsamba 18]

“Mlanduwu ukupanga kachitidwe katsopano.”—British Columbia Health Association

[Chithunzi patsamba 16]

Lisa, wa zaka 12, anasungilira umphumphu wake pansi pa kuvutika kwakukulu ndi chitsutso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena