Chiwawa—Chifukwa Chimene Pali Kudera Nkhaŵa Komakulakula
Ndi mlembi wa Galamukani! mu Britain
KODI inu mukukhala m’dera la “osadutsa”? Iyi iri mbali ya mzinda imene ogwira ntchito yapoyera—adokotala, anamwino, ndipo ngakhale apolisi—ali a mantha a kuloŵamo okha. Mwalamulo, palibe iriyonse mu Britain, koma ‘dera lovuta’ liri dzina losakhudza kwambiri kaamba ka chinthu chofananacho. Ndipo aulamuliro ena amanena kuti pali oposa 70 a amenewa mu London mokha, ndi ambiri ochulukira m’mizinda ina ya dzikolo.
Mlembi wa boma la Dziko la Britain analongosola kudera nkhaŵa kwake, akumanena kuti: “Mtendere wa chitaganya chathu ukudidikizidwa tsopano osati ndi chiwopsyezo chakunja, koma ndi chilakolako kaamba ka chiwawa chochitidwa ndi nzika zinzathu zochulukira.”
Osati kuti Britain (yokhala ndi kukula kwake kwa 17 peresenti mu upandu wachiwawa mkati mwa nyengo ya miyezi 12 ya posachedwapa) iri pamwamba pa ndandandayo. Kutalitali ndi chimenecho. Malo ena ochulukira ali ndi mlingo wokulira wa upandu. Mu miyezi isanu ndi inayi yoyambirira ya chaka chatha, maupandu achiwawa 10,607—kupha, kugwirira chigololo, kuba, ndi kusakaza—anachitidwa kokha m’njira za Mzinda wa New York! Ngakhale kuli tero, wofufuza Dr. Michael Pratt akunena kuti pali umboni wochirikiza kudzinenera kwakuti “makwalala a London akukhala monga New York.”
Komabe, New York suli mzinda woipitsitsa kaamba ka upandu. Atlanta, Miami, Detroit, ndi Chicago iri pakati pa isanu ndi itatu yokulira ya mizinda ya U.S. yomwe inasimba maupandu achiwawa ochulukira pa unyinji wa anthu khumi aliwonse mu 1987 kuposa mmene New York inachitira. Kulikonse, chikuwoneka kuti, chiwawa chiri chochititsa kudera nkhaŵa chomakulakula. Katswiri wa zamaganizo Thomas Radecki anawona kuti ‘maiko ambiri a Kumadzulo awona kuwonjezereka m’chiŵerengero cha chiwawa kuchokera pa 200 kufika ku 500 peresenti mkati mwa zaka 20 zapitazo.’
Maupandu achiwawa awonjezerekanso kwina. Mu Kenya, East Africa, mwachitsanzo, sikale kwambiri pamene osakaza achiwawa 400 anapha mosasankha amuna 190, akazi, ndi ana, akumasiya matupi awo mosasamala kuti adyedwe ndi miimba ndi afisi.
Mu Soviet Union, chiwawa cha maseŵera a mpira chinasimbidwa ‘kukhala chikusakaza mtunduwo.’ Mofananamo, Komiti Yaikulu ya ku China kaamba ka Kuchirikiza Mayanjano a Mafuko inalankhula motsutsana ndi ‘kukangana, kumenyana kwa nkhonya, ndipo ngakhale kuvulaza ndi imfa mkati mwa maseŵera a mpirawo.’ Komitiyo inachitira chisoni kuti: ‘Olakalaka maseŵera, makamaka achichepere, ayenera kuphunzitsidwa kukhala otsungula.’
Mowonekera, maupandu achiwawa ali chochititsa kudera nkhaŵa chomakulakula. Koma kodi nchiyani chomwe chikuchitidwa kupambana chitokoso chomwe iwo akubweretsa?