“Mfungulo ku Ngozi”
NDAGWIRA mfuti chiyambire pamene ndinali mnyamata, koma sindidzakhalanso konse ndi ina. Tiri ndi farmu yaing’ono, ndipo ndinadzimva kuti ndinafunikira mfuti kaamba ka kuchinjiriza makoswe. Tsiku lina mkazi wanga ndi ine tinali kugwira ntchito m’munda, kukonzekera kaamba ka kubyzala. Kunali kotentha mwapadera tsikulo, chotero tinasiya ana athu amuna aŵiri m’nyumba momwe munali mozizirako. Tinali kokha mapazi mazana oŵerengeka patali ndipo tinadzimva kuti iwo akakhala bwino akuseŵera pamodzi. Ine ndinali pa talakita pamene mnyamata wokulirako anabwera akuthamanga kulinga kwa ine ndi kulira akumati: “Atate, ndiganiza kuti khanda lawomberedwa mfuti!” Ndinathamangira kunyumba ndi kupeza mkazi wanga ali pa masitepi akumbuyo akupatsa mwanayo CPR (cardiopulmonary resuscitation). Pamene ndinali kutuma lamya 911, ndinapempha Yehova kuthandiza mwana wanga wamwamuna kukhala ndi moyo, koma ngati sitero chonde kumukumbukira iye m’chiwukiriro. Iye anamwalira pomwepo m’mikono ya amayi wake.
Iye anali wa zaka zakubadwa ziŵiri ndi theka. Iye anali wofewa chotero ndi wopanda liwongo. Ripoti la lamulo likundandalitsa kuwomberako kukhala kwangozi. Mnyamata wokulirapoyo anatenga mfutiyo kuchokera ku chipinda chathu chogona, kuikamo chipolopolo, ndipo anali kuseŵera nayo. Kutayikiridwa kwa mwana wathu wa mwamuna, makamaka mu mkhalidwe umenewu, kuli nkhonya yomwe tidzaimvabe kufikira tsiku limene Yehova am’bwezeretsa iye kwa ife.
Kusiya anyamatawo okha kunali kuphophonya, koma kukhala ndi mfuti m’nyumba kunali mfungulo ku ngozi. Mfuti siiri yoposa chiŵiya cha chiwonongeko. Sindidzakhoza konse kulungamitsa kukhala ndinali nayo.—Kalata yolandiridwa December watha kuchokera kwa Mboni mu Arizona.