Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 6/8 tsamba 14-17
  • Gawo 10: 537 B.C.E. kupita mtsogolo—Kudikirirabe Mesiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Gawo 10: 537 B.C.E. kupita mtsogolo—Kudikirirabe Mesiya
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulondola Chiyembekezo Chaumesiya
  • Abusa Osasamala ndi Kusagwirizana kwa Chipembedzo
  • Chiyuda Chopanda Kachisi, Chopanda Unsembe
  • Ziyembekezo za Umesiya mu Diaspora
  • Kuunika Kuthetsa Nyengo ya Mdima
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Masada—Kodi Ili Umboni Wakuti Mesiya Anabwera?
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Chilamulo cha Pakamwa—Kodi N’chifukwa Chiyani Chinalembedwa?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Chilamulo Kristu Asanadze
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 6/8 tsamba 14-17

Mtsogolo mwa Chipembedzo M’chiyang’aniro cha Nthaŵi Yake ya Kumbuyo

Gawo 10: 537 B.C.E. kupita mtsogolo—Kudikirirabe Mesiya

“Chigamulo chaumwini chiri mawu ofala ngati mtsogolo mulibe chiyembekezo.”—John F. Kennedy, prezidenti wa 35 wa United States

ZAKA makumi asanu ndi aŵiri za ukapolo wa Chibabulo zinatha! Wogonjetsa Wachibabulo Koresi, mfumu ya ku Peresiya, anali kulola Ayuda kubwerera kumudzi. Koma pamene anabwerera ku Dziko Lolonjezedwa (537 B.C.E.), chiyembekezo chawo cha kusangalala ndi chigamulo chaumwini monga mtundu womasuka chinapita chosazindikiridwa. Iwo analibe mfumu, ndipo ulamuliro wa ndale zadziko wa abwanamkubwa awo unatsekerezedwa mwamsanga ndi ulamuliro wachipembedzo wa mkulu wansembe, yemwe anadzawonedwa monga mkulu wa mtunduwo.

Kulondola Chiyembekezo Chaumesiya

Mogwirizana ndi The Concise Jewish Encyclopedia, munali mkati mwa nyengo imeneyi pamene chiyembekezo cha Mesiya chinayamba, “wolamulira woyenerera wa masiku amtsogolo [yemwe] sakakhala kokha wolamulira ‘wodzozedwa’ koma wolamulira yemwe akawononga adani a Israyeli ndi kukhazikitsa nyengo yangwiro ya mtendere ndi ungwiro.”

M’zana lachinayi B.C.E., mwa kugonjetsa, Alexander Wamkulu anasonkhanitsa Ayuda m’kuyangata kwake. Koma iye mwachidziŵikire sanali Mesiya amene iwo anali kudikirira, ngakhale kuti ulamuliro wake unakhaladi ndi chiyambukiro chachikulu pa dziko lawo, mwambo wawo, ndi chipembedzo chawo.

Pambuyo pa imfa ya Alexander, Palestina inakhalabe m’manja mwa Chigriki, choyamba pansi pa Aptolemy a Chiigupto ndipo pambuyo pake pansi pa Aseleucid a ku Syria, maufumu onse aŵiriwo okhazikitsidwa ndi aloŵa m’malo a Alexander. Pamene chisonkhezero cha Chigriki chinakula, Ayuda otchuka ndipo okhala ndi ulamuliro anayamba kuwona miyambo ndi zizoloŵezi za Chiyuda kukhala zachikale. Lomwe linali kutsogolera linali banja la Tobiad, yemwe anasonkhezera Menelaus, mwachidziŵikire wachibale wawo, kukhala mkulu wansembe mkati mwa kulamulira kwa mfumu ya Seleucid Antiochus IV Epiphanes (175-164 B.C.E.). Anachita ichi, ngakhale kuti Menelaus sanali wa nyumba ya mwambo ya ansembe ya Zadoki, mkulu wansembe mu kachisi wa Solomo. Chisonkhezero cha Chigriki chinafikira kukhala champhamvu kotero kuti mapwando achipembedzo a Chiyuda analetsedwa ndipo kachisi inasinthidwa kukhala kakachisi ka Chigriki!

Mu 167 B.C.E., wansembe Wachiyuda Mattathias ndi ana ake aamuna asanu, mofala otchedwa Maccabees, kapena Hasmonaeans, anapanduka. Kuwukira kwa Maccabees, poyambapo kwa mtundu wa chipembedzo, mwamsanga kunakhala kulimbana kwa ndale zadziko kaamba ka chigamulo chaumwini kwa Chiyuda. Mu 165 B.C.E., kachisi inalandidwanso ndi kuperekedwanso, chochitika chimene Ayuda lerolino kuzungulira dziko amakondwerera chaka ndi chaka mkati mwa madyerero a masiku asanu ndi atatu a zowunikira odziŵika monga Hanukkah. Koma Mesiya sanawonekerebe.

Abusa Osasamala ndi Kusagwirizana kwa Chipembedzo

Pa nthaŵi imeneyi, “sikuti kokha utsogoleri wauzimu ndi wa mayanjano wa anthuwo unali m’manja mwa ansembe,” ikuchitira ndemanga Pictorial Biblical Encyclopedia Yachiyuda, “koma anapanga gulu lamphamvu koposa ndipo lachuma koposa m’Yerusalemu, mwa ndale zadziko ndi mwa zachuma.” Ngakhale kuli tero, ansembewo anakhala monga mafumu ndipo osasamala m’kukwaniritsa mathayo awo a kuŵeta, kotero kuti osakhala ansembe anayamba kuwaloŵa m’malo mwa kumasulira Chilamulo ndi kupereka chilungamo. Amuna amenewa, odziŵika monga alembi, anali ofunitsitsa kupeza zophophonya mwa anthu okhoterera pa kunyazitsa Chilamulo.

Mkati mwa nyengo imodzimodziyo ya nthaŵi, chipembedzo cha Chiyuda chinasweka kukhala magulu ampatuko osiyanasiyana. Afarisi anaphunzitsa kuti Mulungu anapatsa Israyeli lamulo la mbali ziŵiri, mbali ina yolembedwa ndipo mbali ina yapakamwa. Panali pa maziko a lamulo lapakamwa limeneli pamene anazindikira kukhala wa lamulo mzera wa mkulu wansembe ngakhale pambuyo pa kusweka kwa mzera wa mwambo. Asaduki, ku mbali ina, akumakana kukhalapo kwa lamulo lapakamwa, anadzinenera kuti kokha mbadwa yachindunji ya Zadoki ingatumikire monga mkulu wansembe.

Dzina lakuti “Mfarisi” linabwera kuchokera ku liwu lotanthauza “wopatulidwa” kapena “wolekanitsidwa.” Ena amanena kuti linagwiritsidwa ntchito ndi otsutsa awo kuwasonyeza iwo kukhala opatuka. Ena amadzinenera kuti limalozera ku mkhalidwe “wolekanitsidwa” umene iwo anatenga, kudzipatula iwo eni kuchoka kwa ‛am ha·’aʹrets (anthu a ku dziko), omwe anawalingalira kukhala odetsedwa. Afarisi anali odzilungamitsa mopambanitsa m’kusunga kwawo ponse paŵiri lamulo lolembedwa ndi lamulo lapakamwa. Mkhalidwe wofananawo wolimba wa Asaduki kulinga ku lamulo lolembedwa mothekera “unabuka osati kuchokera ku kudzimva kwapadera kwa chipembedzo,” akulemba tero mkonzi Wachiyuda Gaalyahu Cornfeld, “koma monga chida chandale zadziko m’kutsutsana kwawo ndi mphamvu zopereka malamulo za Afarisi.”

Aessene, gulu lina la chipembedzo, mwachidziŵikire linakula mkati mwa nthaŵi imodzimodziyo. Iwo anapatukana ndi gulu la ansembe lalamulo, kukana kutengamo mbali mu mautumiki achipembedzo ndi nsembe pa kachisi, koma mwanjira ina yake anamamatira mwathithithi ku Chilamulo. Mofanana ndi Afarisi, kwa amene anali m’njira zambiri olingana, anakhala minkhole ya chisonkhezero cha Chihelene, kutengera chikhulupiriro cha kusafa kwa moyo.

Gululo mwinamwake linalibe ziŵalo zoposa pa 4,000, onse amuna achikulire, ambiri a amene anali mbeta. Iwo anakhala m’nyumba za ambiri m’midzi yomwazikana mu Palestina monse. Encyclopædia Judaica ikulankhula za mtendere wawo wolingaliridwa, ikumanena kuti iwo “unali mwinamwake wofanana ndi uja wa Mboni za Yehova zamakono.” Koma chiri chachiwonekere kuti Aessene sanachite kwenikweni uchete wotheratu umene lerolino ukuchitidwa ndi Mboni za Yehova. Pictorial Biblical Encyclopedia Yachiyuda ikunena kuti Aessene “anamenya mwachipambano m’chipanduko molimbana ndi Roma, atsogoleri ena anafikira ngakhale pa kuchoka pa mathayo awo.” Katswiri wa mbiri yakale Wachiyuda Josephus akulozera kwa wolamulira wina woteroyo—“John Essene” winawake yemwe anatumikira monga kazembe Wachiyuda m’kuwukira kwa mu 66 C.E.

Mipukutu ya ku Dead Sea, yopezedwa mu 1947, imapereka chidziŵitso ponena za mpatuko wa chipembedzo wa Qumran, wolingaliridwa ndi ophunzira ena kukhala wofanana ndi Aessene. Koma ponena za malingaliro akuti Yohane Mbatizi ndi Yesu anali ku gulu limeneli, kapena kuti anasonkhezeredwa chifupifupi ndi ilo, The New Encyclopædia Britannica ikunena kuti: “Zitsutso zofunika koposa . . . zimalankhula motsutsana ndi chiyerekezo chimenechi.” Pali “kusiyana kwakukulu pakati pa mpatuko wa Qumrān ndi Yohane Mbatizi . . . [limodzinso ndi] kusiyana kotsutsana pakati pa kawonedwe ka mpatukowo ndi ukulu wa utumiki wa Yesu, uthenga wake wa chipulumutso, kumvetsetsa kwake kwa chifuniro cha Mulungu . . . ndipo, makamaka, mkhalidwe wozama wa lamulo lake la chikondi ndi kuyanjana kwake ndi ochimwa ndi okanidwa mwa mayanjano.”

M’chenicheni, mpatuko wachipembedzo Wachiyuda uliwonse unatsutsa Yohane Mbatizi ndi amene iye anamulengeza kukhala Mesiya. M’malo mopereka chikhulupiriro ku uthenga wa Yohane, ambiri a ansembewo, akutero Josephus, anatembenukira kwa Azealot, gulu la osinthanso Achiyuda okhoterera pa chigamulo chaumwini. Kwa zaka makumi angapo magulu onga awa, otsutsa ku ulamuliro Wachiroma womwe unaloŵa m’malo Grisi mu 63 B.C.E., anachita machitachita auchigawenga. Pomalizira pake mu 66 C.E., iwo anasweka mu kuwukira kwapoyera. Ichi chinatsogolera ku kuwonongedwa kwa kachisi Yachiyuda ndi unsembe wawo. Chiyembekezo cha Umesiya chinazimiririka.

Chiyuda Chopanda Kachisi, Chopanda Unsembe

Mazana angapo kumbuyoko, mkati, kapena mwinamwake mwamsanga pambuyo pa kupita kundende ya Chibabulo, chigogomezero chachikulu chinaikidwa pa kutenga chidziŵitso cha Chilamulo. Malo apakati a chilangizo, odziŵika monga masunagoge, anamangidwa, ndipo pambuyo pa chimenecho kachisi inayenderedwa kokha pa zochitika zapadera ndi kaamba ka cholinga cha kupereka nsembe. Chotero podzafika zana loyamba C.E., chinali chachibadwa kulambira m’masunagoge. Kenaka, pambuyo pa kuwonongedwa kwa kachisi mu 70 C.E., iwo mwachiwonekere anawonedwa kukhala anailoŵa m’malo iyo.

Chigogomezero tsopano chinasamuka kuchoka ku unsembe wosakhalako kupita kwa aphunzitsi odziŵika monga arabi. Asaduki analeka kukhalako monga bungwe lokhutiritsa, ndipo Aessene anangozimiririka, chotero Afarisi anatulukira monga atsogoleri osatsutsidwa. Ellis Rivkin wa Hebrew Union College akulongosola chisonkhezero chimene iwo anali nacho. “Lamulo lapakamwa la Afarisi linabala Mishnah, Matalmud a ku Palestina ndi ku Babulo, geonic, mbadwo wapakati, ndi responsa yamakono, ndi mitundu yosiyanasiyana ya ndandanda ya lamulo Lachiyuda.” The New Encyclopædia Britannica ikuwonjezera kuti: “Ngakhale lerolino magulu osiyanasiyana Achiyuda, kaya a Orthodox, Conservative, kapena Osinthanso, onse amadzinenera kukhala mbadwa zauzimu zachindunji kuchokera ku nzeru za Afarisi ndi arabi.”

Ziyembekezo za Umesiya mu Diaspora

Ngakhale isanafike 70 C.E., mamiliyoni a Ayuda anakhala kunja kwa Palestina, makamaka mu Syria, Asia Minor, Babylonia, ndi Igupto. Ngakhale kuli tero, pambuyo pa 70 C.E., Ayuda alionse opulumuka anazulidwa kotheratu, kubalalitsidwa kukatenga moyo mu diaspora, liwu la Chigriki kaamba ka “kubalalitsa.” Ngakhale kumeneko, ambiri anasungirira chiyembekezo chawo cha chigamulo chaumwini pansi pa Mesiya womadzayo. Mtsogoleri Wachiyuda Bar Kokhba anatsimikizira kukhala mesiya wonyenga, mopanda chipambano kutsogolera chiwukiro molimbana ndi Roma mu 132 C.E. Mogwirizana ndi The Jewish Encyclopedia, amesiya 28 onama oterowo anawoneka pakati pa nthaŵiyo ndi 1744 C.E.

Chotero, mwinamwake momvetsetseka, chiyembekezo cha Umesiya chinakhala chosokonezedwa. Encyclopædia Judaica ikulongosola kuti: “Luntha la kulingalira la Chiyuda mu Mbadwo Wapakati silinalandire kuchokera ku nyengo yakale lingaliro lomveka, logwirizanitsidwa la Mesiya, . . . ndipo mabukhu a talmud ndi Midrashim osiyanasiyana anaphatikizapo malingaliro ambiri osiyanasiyana.” Kuchiyambiyambi mu zana la 12, wanthanthi Wachiyuda Moses Maimonides anatsutsa kuti kulamulira kwa Mesiya kunali mwinamwake kokha chithunzi cha mtundu wapamwamba wa chitaganya. M’zana la 19, Ayuda Osinthanso “analoŵa m’malo chikhulupiriro cha mbadwo wa umesiya ndi chikhulupiriro mwa Mesiya waumwini. . . . Chiyembekezo cha umesiya chinachotsedwa ku zigwirizanitso zake zamwambo ndi kubwerera kwa andende ku Ziyoni.”

Mwamsanga chisanachitike ichi, gulu la Haskalah (Chiwunikiro) mu Europe mowonjezera linasokoneza nkhaniyo. Linapititsa patsogolo Chiyuda chomwe chinali chofunitsitsa kumamatira ku njira ya moyo ya Kumadzulo. Linathandiza kugawa Ayuda kukhala awo owona chigamulo chaumwini m’dziko lokhazikitsidwanso la Chiyuda pansi pa Mesiya kukhala lapamwamba loyambirira, ndi awo odzimva kuti kugwirizana m’moyo wa dziko lobadwira kunali kofunika koposa.

Zochitika zimenezi, kuphatikizapo kubuka kwa kutsutsa Chisemitic, kunapanga njira kaamba ka kubadwa kwamakono kwa Chiziyoni, chotsogozedwa ndi Theodor Herzl pa mapeto pa zana la 19. Lerolino, mu May 1989, zaka 41 kufika ku mwezi pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Boma la Israyeli, Ayuda akusangalala ndi chigamulo chaumwini monga mudzi Wachiyuda m’dziko la kwawo Lachiyuda limene analichitira masomphenya. Kodi chiyembekezo chawo cha Umesiya chazindikiridwa?

Ngati ndi tero, nchifukwa ninji Ayuda ena, mogwirizana ndi The Times ya ku London, amawona “mu Chiziyoni kutonza komwe kunakhala kwenikweni ndi kulengedwa kwa Israyeli”? Nchifukwa ninji katswiri wa mbiri yakale malemu Theodore H. White, iyemwini Myuda, mwachindunji anavomereza kuti: “Pali chifupifupi mipatuko yambiri yosiyanasiyana ya Ayuda, imene imakangana ndi wina ndi mnzake, . . . monga mmene iliri pakati pa Aprotesitanti”? Nchifukwa ninji magazini ya Time, ikumaitanira chisamaliro mu 1987 ku magulu ampatuko achipembedzo okangana mkati mwa bungwe la ndale zadziko la ziŵalo 120 la Israyeli, Knesset, inalemba kuti: “Yankho lina lotsimikizirika liyenera kupezeka ngati Israyeli . . . sayenera kukhala nyumba yogawanikana mwakupha pakati pake”?

Chigamulo chaumwini Chachiyuda chamakono chimapereka chiyembekezo chochepa kaamba ka mtsogolo. Mwa kukhulupirira mu ndale zadziko za umunthu kukazindikira chiyembekezo chake cha Umesiya, Chiyuda chanyalanyaza mawu a zolembedwa zake zenizeni zopatulika: “Chiri bwino kutenga pothaŵirapo mwa AMBUYE kuposa kudalira mwa munthu. . . . Musaike chikhulupiriro chanu mwa akalonga, osatinso mwa mwana wa munthu, mwa amene mulibe chithandizo.”—Salmo 118:8; 146:3, The Holy Scriptures, lofalitsidwa ndi Jewish Publication Society of America.

M’kusiyanitsa ndi vuto limene Ayuda ambiri lerolino ali nalo m’kuzindikira chiyembekezo chawo cha Umesiya, unyinji wa makolo awo kumbuyoko m’zana loyamba C.E. analibe vuto lirilonse. (Onani Yohane 1:41.) Iwo anakhala atsatiri a Mmodzi amene anamulandira kukhala Mesiya, kukhala achirikizi achangu a chipembedzo chimene moyenerera tingachitche “Njira ya Chikhulupiriro, Chiyembekezo, ndi Chikondi.” Nkhani yathu yotsatira idzalongosola.

[Chithunzi patsamba 16]

Chipupa cha Kumadzulo, mofala chotchedwa Wailing Wall, chiri chonse chimene Ayuda atsala nacho cha kachisi yawo yopatulika, yowonongedwa mu 70 C.E.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena