Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g89 7/8 tsamba 10-11
  • Kodi Dziko Lanu Liri Chandamale Choyambirira?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Dziko Lanu Liri Chandamale Choyambirira?
  • Galamukani!—1989
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Miyezo Yowirikiza Kaŵiri M’kufalitsa Matenda ndi Imfa
  • Ena Amabwezera
  • Kodi Fodya Ngwabwino?
    Galamukani!—1991
  • Miyoyo Mamiliyoni Ambiri Ikuthera mu Utsi
    Galamukani!—1995
  • Fodya ndi Kusanthula
    Galamukani!—1989
  • Ochirikiza Fodya Aponya Zibaluni Zawo za Mpweya Wotentha wa Zinyengo
    Galamukani!—1995
Onani Zambiri
Galamukani!—1989
g89 7/8 tsamba 10-11

Kodi Dziko Lanu Liri Chandamale Choyambirira?

CHIFUKWA chakuti imagula fodya yodula mu Brazil ndi Zimbabwe, United States iri ndi fodya yotsalako. Chotero kodi nkuti kumene nduna zotchuka za fodya zikagulitsa iyo? Ku maiko a mu Africa ndi Asia. Chotero, maganizi ya Asiaweek ikusimba kuti: “Maiko a ku Asia tsopano amatenga chifupifupi 50 peresenti ya fodya yogulitsidwa kunja ya America, ikumalowa m’malo Britain ndi West Germany monga misika yotsogolera.”

Ndipo ndi mtengo wolemera chotani nanga womwe umakhala mtsogolo mwa ogulitsa fodya! Msika womwe uli ndi kuthekera kwa chiŵerengero cha chifupifupi anthu mabiliyoni aŵiri mkati mwa zaka 20 zotsatira. Chiŵerengero cha anthu chomwe chiripo cha kokha China ndi India chiri chozizwitsa—chiwonkhetso choikidwa pamodzi cha chifupifupi 1.8 biliyoni! Ndipo monga mmene World Health inalongosolera kuti: “Pamene kuli kwakuti misika ya fodya ikutsika kumadzulo pa mlingo wa peresenti imodzi pa chaka, kusuta kukuwonjezereka m’maiko otukuka kumene pa avereji ya maperesenti aŵiri pa chaka.” Ndipo kumbukirani kuti msika womazimiririka uli ndi chiŵerengero chaching’ono kwenikweni kuposa msika wokhala ndi kuthekera womwe ukupambana Kum’mawa. Indastri ya fodya mu U.S. ikuyembekezera kuti zogulitsidwa mu Asia zidzawonjezeka ndi 18 peresenti podzafika chaka cha 2000. Koma mwapang’ono pali choletsa chimodzi. Malamulo osamalira zoloŵetsedwa ndi zotulutsidwa m’dziko.

Miyezo Yowirikiza Kaŵiri M’kufalitsa Matenda ndi Imfa

Ndimotani mmene makampani a fodya a ku America angapangitsire maiko ena kulandira ndudu zawo zotsala? Mosemphana, iwo ali ndi chigawo, chimene ngakhale kuti chimachenjeza nzika zawo molimbana ndi ngozi za kusuta, mwachangu chimapititsanso patsogolo zogulitsa za fodya yakupha m’maiko ena. Kodi ndani ameneyu? Boma la U.S.!

Asiaweek ikulongosola kuti: “Mtokoma wa fodya wogulitsidwa kunja kwa dziko wasamuka ndi kuchirikiza kwa boma la U.S. kumbuyo kwake. . . . Ofesi ya U.S. Trade Representative . . . yatulukira kukagwetsa zoletsa malonda ndi kupeza mpata wolowera m’zowulutsira mawu za ku Asia kaamba ka makampani a America—ngakhale kuti kusatsa malonda a ndudu kwaletsedwa kwa nthaŵi yaitali kuchokera ku zowulutsa za pawailesi mu U.S.” Magazini ya World Health ikusimba kuti: “Makampani a fodya a [U.S.] ali ndi chisonkhezero cholingalirika cha ndale zadziko. Zilango za kuchepetsa malonda kapena chiwopsyezo cha zilango zoterozo zapangidwa motsutsana ndi Hong Kong, Taiwan, Japan ndi Korea kufikira atatsegula misika yawo ku kugulitsa ndi kusatsa malonda a zopangidwa za fodya za ku America.”

Ngakhale choipirako, makampani a fodya samagulitsa kokha zopangidwa zawo mu Asia komanso amachulukitsa zogulitsa zawo ndi kudidikiza kopambanitsa kwa kusatsa malonda. Maiko ena, onga ngati Taiwan ndi South Korea, chifukwa cha chididikizo, anakhoza ngakhale kumasula chiletso chawo pa kusatsa malonda a fodya! Tsopano China irinso pamwamba pa ndandanda yapamwamba ya opanga ndudu a ku U.S. Nchosadabwitsa kuti nduna yaikulu imodzi ya kampani yopanga fodya ikugwidwa mawu kukhala ikunena kuti: “Kodi mukudziŵa chimene tikufuna? Timafuna Asia.” Koma ndimotani mmene ena amawonera machenjera amenewa a chididikizo chopambanitsa a ku America?

Mogwirizana ndi mtola nkhani wa The New York Times, mwamuna wina wamalonda wa ku Korea analankhula mokwiya “motsutsana ndi mkhalidwe wa America wa kukankhira ndudu za ku America pa anthu a ku Korea.” Ndipo ali ndi nsonga yotsimikizirika. Pamene kuli kwakuti America ikumenya nkhondo yolimbana ndi cocaine ndi heroin yogulitsidwa m’dzikomo kuchokera ku maiko ena zomwe ziri maziko ku zachuma zina, iyo imafuna kutula zinthu zake za ululu pa mitundu ina. Popeza kuti America imadzinenera kukhala ndi miyezo yapamwamba ya ufuko, kodi kuli kulingalirana kaamba ka iye kukakamiza pa maiko ena, ambiri omwe ali m’zowawa za zachuma, zotsalapo zake za fodya yodzetsa ngozi?

Ena Amabwezera

Maiko ena a ku Africa, onga ngati Gambia, Mozambique, ndi Senegal, aletsa kusatsa malonda kwa ndudu. Nduna yoyang’ana pa zaumoyo ya ku Nigeria inalongosola chaka chatha kuti boma la Nigeria linali pa ulendo “woletsa kusatsa malonda kwa pa nyuzipepala, wailesi, wailesi ya kanema ndi kwa bolodi konse. Tidzaletsa kusuta m’malo apoyera onse ndi moyendera.” Galamukani! inadziŵitsidwa (January 1989) ndi nduna ya chidziŵitso ya ku Nigeria kuti nkhaniyi ikali kukambidwabe.

China iri mtundu wokhala ndi osuta 240 miliyoni. Podzafika chaka cha 2025, maulamuliro a zamankhwala akuyembekezera kutaya anthu mamiliyoni aŵiri chaka chirichonse monga chotulukapo cha matenda odzetsedwa ndi kusuta. China iri ndi vuto lalikulu, monga mmene magazini ya China Reconstructs ikuvomerezera kuti: “Mosasamala kanthu za kuletsa kwa boma la China pa kusatsa malonda a ndudu, mwa nthaŵi zonse maripoti a m’nyuzipepala ndi magazini ochenjeza zotulukapo zovulaza za kusuta, ndi mtengo womawonjezerekawonjezerekabe wa ndudu, chiŵerengero cha osuta mu China chikupitirizabe kukula.” Ndipo kodi nchiyani chomwe chiri chimodzi cha zotulukapo zake? “Kansa, matenda a mtima ndi mitsempha yake ya mwazi ndi kupuma tsopano ziri zakupha zazikulu mu China.”

Mu mbali zina za China, chikulingaliridwa kukhala chizindikiro cha kuchereza kupatsa ndudu pamene mukulandira alendo. Koma kodi ndi mtengo wotani nanga umene anthu a ku China akulipira! China Reconstructs ikusimba kuti: “Akatswiri a zamankhwala achenjeza kuti zochitika za kansa ya m’mapapo zikuwonjezereka pa mlingo wokulira.” Monga mmene katswiri mmodzi wa ku China analongosolera kuti: “Tikulipira kale mtengo wokulira koposa.”

Ngakhale kuli tero, pali ngozi ina mu mphamvu za osatsa malonda a fodya—chisonkhezero chawo cha machenjera pa zowulutsira.

[Chithunzi patsamba 10]

Kusatsa malonda koletsa kusuta mu Hong Kong

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena