Njira Khumi Zolekera Kusuta
1. Khalani wosonkhezeredwa mowona. Khalani ndi zifukwa zabwino zolimba zofunira kuleka—ulemu waumwini; nkhaŵa kaamba ka umoyo wanu, watsopano ndi wamtsogolo; nkhaŵa kaamba ka okondedwa oyambukiridwa ndi chizoloŵezi chanu changozi; chikhumbo cha kukhala waudongo, mwakuthupi ndi mwamakhalidwe, pamaso pa inumwini ndi Mulungu.
2. Khazikitsani deti la kuleka, ndipo litsatireni. Lekani popanda chothandizira chirichonse; chimapweteka mwamsanga, koma chimachira mwamsanga.
3. Tengani kachitidwe kophulapo kanthu kuti muswe chizoloŵezicho. Duladulani ndudu zirizonse zomwe ziri m’nyumbamo, ndipo thirani madzi pa izo. Chapani zovala zanu zonse zonunkha fodya. Yambaninso chatsopano, dzimveni watsopano!
4. Peŵani malo oipitsidwa ndi fodya ndi mabwenzi osuta pamene mukumaliza kusiya kwanu kotheratu kuchoka ku chikonga. Chezerani malo kumene kusuta kuli koletsedwa, onga ngati malo osungirako zinthu zakale ndi malaibulale.
5. Sungani ndalama zomwe mukanathera pa fodya ndipo ziŵerengeni izo pambuyo pa mwezi umodzi! Gulani chinachake chomwe muchifuna kwenikweni. Kapena gulani mphatso kaamba ka wokondedwa yemwe angasangalalenso m’chilakiko chanu.
6. Dzisungeni inumwini ndi manja anu kukhala otanganitsidwa m’nthaŵi zimenezo zomwe inu mwa nthaŵi zonse mukanatenga ndudu. Tafunani chungamu (osati chungamu chokhala ndi chikonga) kapena idyani zipatso zonunkhira pamene chikhumbo cha kusuta chikuvutani. M’malo mosuta, tsukani mano pambuyo pa chakudya. Tengani kaulendo, lembani makalata, sokani, limani m’dimba, konzani zinthu, tsukani galimoto, ndi zina zotero.
7. Pamene mukudzimva wovutitsidwa kapena pansi pa chipsyinjo, pumani mwakuya ndipo mwa pang’onopang’ono. M’malo motenga ndudu, imwani madzi ambiri ndi madzi a zipatso. Zamadzi zimatsuka.
8. Seŵerani mosapambana pa malire anu a kuthupi. Fufuzani ndi dokotala wanu choyamba ponena za chimene chiri choyenera. Mkhalidwe wanu wakuthupi womawongokera udzakulimbikitsani.
9. Chepetsani kumwa zakumwa zoledzeretsa. Zakumwa zoledzeretsa ndi ndudu kaŵirikaŵiri “zimayenderana,” popeza kuti chakumwa choledzeretsa chingayambitse chikhumbo cha kusuta. Lekani kugwirizana kwa mayanjano pamene chimenechi chingachitike. Onani zosatsa malonda za fodya monyansidwa—pendani zakunja ndi mkati mwake. Musatengedwe kachiŵirinso.
10. Ngati inu mukukonzekera kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, pempherani mwakhama kwa Mulungu kaamba ka thandizo ndipo kenaka chitani mogwirizana ndi mapemphero anu. Musayembekezere chozizwitsa; tangochipangani icho kuchitika.