Mtsogolo mwa Chipembedzo Poyerekezera ndi Nthaŵi Yake Yapita
Gawo 24: Tsopano ndi kwamuyaya—Kukongola Kwamuyaya kwa Chipembedzo Chowona
“Chipembedzo, ngati chiri chovekedwa m’zowonadi zakumwamba, chimangofunikira kuwonedwa chokhumbirika.”—William Cowper, wolemba ndakatulo Wachingelezi wa m’zaka za zana la 18
PALIBE chirichonse choyenera kukhumbiridwa ponena za chipembedzo chonyenga. Icho chabweretsera mtundu wa anthu zaka mazana 60 za chisoni ndi kuvutika. Njira zake zonama, zachinyengo, zamachenjera, ndi zaudani zachiipitsa icho ponse paŵiri m’maso mwa Mulungu ndi munthu. Kutalitali ndi kukhala chovekedwa m’zowonadi zakumwamba, chipembedzo chonyenga chiri mdani wa chowonadi ndi kukongola.
Posachedwapa makamu a Mulungu akupha adzaponya chipembedzo chonyenga m’phompho la kuchotsedwapo kwamuyaya mopanda chifundo. Mwamsanga pambuyo pake, dongosolo lonse la Satana lidzatsatira. Koma chipembedzo chowona, limodzi ndi aja ochichita icho, adzakhalabe. Chotero nchisangalalo chotani nanga kuwona kukongola kwake kwamuyaya kukusonyezedwa ku mlingo umene ife lerolino sitingaulingalire mokwanira!
Kodi Nkukongola Kotani?
Kukongola kwa chipembedzo chowona nkochuluka. Panopa pali koŵerengeka kokha. Bwanji osatenga nthaŵi kuyang’ana malemba a Baibulo omatsimikizira kukongola kwamuyaya kumeneko kukhala kozikidwa m’Baibulo?
Pakati pa kukongola kwamuyaya kwambirimbiri kwa chipembedzo chowona pali:
▪ Icho nchozikidwa pa chowonadi cha Mulungu wosalakwa, amene dzina lake ndilo Yehova, amene tingadalire kotheratu.—Salmo 83:18; Yesaya 55:10, 11.
▪ Icho chipezedwa ndi aliyense wa mtima wodzichepetsa, sichosungidwira aluntha lapamwamba okha.—Mateyu 11:25; 1 Akorinto 1:26-28.
▪ Icho sichimapenda fuko, kutchuka, ndi malo m’zachuma.—Machitidwe 10:34, 35; 17:24-27.
▪ Icho chimapereka chiyembekezo cha maziko olimba cha moyo m’dziko la mtendere ndi chisungiko lopanda chisoni, matenda, masoka, ndi imfa.—Yesaya 32:18; Chibvumbulutso 21:3, 4.
▪ Icho chimapereka kalinganizidwe m’kamene ziŵalo zake zingakhalire limodzi monga ubale wokhulupirika wa dziko lonse, ogwirizana m’chiphunzitso, mkhalidwe, ndi mzimu.—Salmo 133:1; Yohane 13:35.
▪ Icho chimapereka kwa aliyense—mwamuna, mkazi, ndi mwana—mwaŵi wa kugaŵanamo mokangalika m’ntchito ya Mulungu, kudzaza moyo ndi chifuno.—1 Akorinto 15:58; Ahebri 13:15, 16.
▪ Icho chimatichenjeza za ngozi zobisika, kutilangiza mmene tingadzisamalirire kotero kuti tipindule.—Miyambo 4:10-13; Yesaya 48:17, 18.
Ndipo kodi nchifukwa ninji chinganenedwe kuti kukongola kumeneku kuli kwamuyaya? Chifukwa chakuti kudzakhaladi ku utali umene chipembedzo chowona chidzakhala—kosatha.
Kudzaza m’Mipata
Chinganenedwe kuti imfa ili mmodzi wa adani aakulu koposa a chowonadi, popeza kuti anthu kaŵirikaŵiri amapita kumanda awo ndi chidziŵitso chimene palibe munthu winawake achidziŵa. Tsatanetsatane weniweni wa zochitika zofananako za posachedwapa—mwachitsanzo, kuphedwa kwa mu 1963 kwa prezidenti wa U.S., J. F. Kennedy—kudakali nkhani ya mtsutsano. Kodi zenizeni nzotani? Kodi ndani yemwe adziŵadi? Ambiri amene angadziŵe salinso amoyo. Ndipo ngati izi ziri zowona ponena za chochitika cha zaka 26 zokha zapitazo, bwanji ponena za zimene zinachitika zaka mazanamazana ngakhale zikwizikwi zapitazo?
Kuwonjezerapo, akatswiri a mbiri yakale ali kokha anthu, okhala ndi chidziŵitso chopeleŵera ndipo ogwira ntchito pansi pa chosoŵa cha kupanda ungwiro kwaumunthu ndi kunyada kothekera. Ndicho chifukwa chake munthu wofuna zenizeni achita bwino kusakhala woumirira pa zinthu zimene alibe nazo cholembedwa chaumulungu chowuziridwa, chodalirika.
Kulemba za mbiri yachipembedzo kumabweretsa mavuto ofananawo, popeza kuti akatswiri kaŵirikaŵiri amakangana pa zoyenera kukhala zenizeni. M’mpambo wa “Mtsogolo mwa Chipembedzo Poyerekezera ndi Nthaŵi Yake Yapita,” Galamukani! yayesera kupereka nsonga zolembedwa bwino lomwe, koma chiyenera kuvomerezedwa kuti pakali pano pali zinthu zinazake zimene sitikudziŵa kwenikweni. Mwachitsanzo, ndi ku ukulu wotani kumene magulu odzinenera kukhala Achikristu okhalapo pakati ndi pambuyo pa Nyengo za Mdima anamamatira kwenikweni ku Chikristu chowona?
Ponena za magulu amenewa, profesa wa mbiri ya tchalitchi A. M. Renwick akudziŵitsa kuti: “Unyinji wa zofufuza za m’mbiri ukufunikirabe kuti tipange nkhani yowona ndi malo a zaumulungu ponena za mabungwe ambirimbiri amenewo.” Mogwirizana ndi Renwick, “nthaŵi zakale akatswiri a mbiri yakale anadalira mopambanitsa pa ndemanga za adani a magulu otsutsa kuti apange kupenda kwawo chiphunzitso ndi makhalidwe.” Ndithudi, kudalira mopambanitsa pa ndemanga za mabwenzi awo nakonso kungakhale kukanatulukapo malingaliro opotozedwa. Chotero ngakhale pambuyo pa kufufuza kwa m’mbiri kokulira, mafunso ambiri mothekera akadakhalabe osayankhidwa.
Bwanji ponena za Baibulo? Monga bukhu lowuziridwa mwaumulungu lokuta mbiri ya chipembedzo, n’lodalirika m’chirichonse chimene limanena. Koma ilo limanena zocheperadi ponena za mitundu yonse yosiyanasiyana ya chipembedzo chonyenga imene yakhalapo chiyambire. Chotero ndi zomveka, popeza kuti ilo linaperekedwa kutumikira monga bukhu lophunziramo la chipembedzo chowona, osati chonyenga.
Ngakhale ponena za chipembedzo chowona, Baibulo silimatiuza zonse. Ilo limatipatsa chidziŵitso chokwanira chozindikirira chipembedzo chowona mwachipambano, koma nthaŵi zina limasiya tsatanetsatane. Pamene kuli kwakuti tsatanetsatane ameneyu angakhale wochititsa chidwi ndi wokondweretsa kudziŵa, pali pano sali wofunikira kwenikweni.
Ndiponso, Baibulo liri ndi mipata ya nthaŵi. Mwachitsanzo, ilo silimanena chirichonse pa zimene zinachita mkati mwa zaka zoposa 400 zimene zinapita pakati pa kumalizidwa kwa Malemba Achihebri, otchedwa mofala kukhala Chipangano Chakale, ndi kubwera kwa Yesu. Ndipo chiyambire pamene Baibulo linamalizidwa, papita chifupifupi zaka 1,900.
Chotero kwa mbali yaikulu ya zaka za zana la 18, sitinakhale ndi cholembedwa chowuziridwa ponena za Chikristu. Chimenechi ndicho chimene chimapangitsa zikaikiro ponena za ena odzinenera kukhala Akristu, monga momwe zinatchulidwa ndi mlembi Renwick. Ngakhale kuli tero, nkowonekeratu kuti anthu ena kubwerera kumbuyo m’zaka mazanamazana anali kumamatira ku Chikristu choyambirira. Komabe, pali mafunso osayankhidwa amene amachita ndi zolinga ndi kuwona mtima kothekera kwa anthu ena a m’zaka zapita. Bwanji ponena za atsogoleri ena a Kukonzanso? Pa nkhaniyo, bwanji ponena za amuna onga ngati Confucius ndi Muhammad? Ngakhale kuti dongosolo lamakono la chipembedzo lingaweruzidwe molongosoka pa maziko a zipatso zawo, anthu—makamaka ngati anafa kale—sangaterodi.
Komabe, m’dziko latsopano la Mulungu, ngati chidzakhala chifuno cha Mlengi kulembanso mabukhu a mbiri yakale—kuphatikizapo aja a mbiri ya chipembedzo—chidzakhala chotheka. Izi ziri choncho chifukwa cha kukongola kwina kwa chipembedzo chowona—chitsimikizo chakuti akufa adzawukitsidwa.—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Tangolingalirani chisangalalo cha kupeza mayankho olondola ku mafunso athu mwa kulankhula kwa anthu owukitsidwa amene anachitadi zinthu zimene tadziŵerenga m’mabukhu a mbiri. Talingalirani kukhala okhoza kudzaza tsatanetsatane wosoweka, wonga ngati dzina la Farao amene anafa pa Nyanja Yofiira ndi amene anakumana ndi miriri ya Igupto.
Ngati cholembedwa choterocho tsiku lina chingalembedwe, icho chidzalembedwa kulemekeza ndi kutamanda kwamuyaya muyambitsi wa chipembedzo chowona, Yehova Mulungu. Sipangakhale chikaikiro chirichonse ponena za chimenechi. Komabe, funso limene likukhalabe ndi iri: Kodi inu mudzakhalako kudzachiŵerenga icho?
Kukhumbira Sikokwanira
Kukongola kwamuyaya kwa chipembedzo chowona nthaŵi zonse sikumawonedwa mosavuta monga mmene mawu a Cowper, ogwidwa pachiyambi pa nkhani ino angasonyezere. Chotero, kope loyambirira la Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence linapanga ndemanga yotsatirayi zaka 110 zapitazo: “Chowonadi, monga duŵa laling’ono labwino m’chipululu cha moyo, chiri chozingidwa ndipo chifupifupi cholatsidwa ndi namsongole wokongola womakula wa cholakwa. Ngati inu mungachipeze icho muyenera nthaŵi zonse kukhala amaso. Kuti muwone kukongola kwake muyenera kuchotsapo namsongole wa cholakwa ndi minga za kunyada. Ngati mudzati mukhale nacho muyenera kudzichepetsa kuti muchipeze.”
Tikhulupirira kuti mpambo wa “Mtsogolo mwa Chipembedzo Poyerekezera ndi Nthaŵi Yake Yapita” wathandiza aŵerengi athu “kutaya namsongole wa cholakwa ndi minga ya kunyada” kotero kuti ayamikire mokwanira kukongola kwamuyaya kwa chipembedzo chowona.
Koma kuyamikira sikuli kokwanira. Wofika pa nsonga ndiwo mwambi wa ku China womwe umati: “Kuphunzitsa kumene kumaloŵa m’makutu koma osati m’mtima kuli ngati chakudya chodyeredwa m’maloto.” Ngati titi tipindule mwaumwini ndi kukongola kwamuyaya kwa chipembedzo chowona—osati kungolota ponena za iko—chiri chofunika kwambiri kuti zimene tiphunzira zifike pa mtima wathu, osati m’makutu athu mokha.
Ŵerengani mosamalitsa bokosilo lokhala ndi mutu wakuti “Kuzindikira Chipembedzo Chanu Kukhala Chowona kapena Chonyenga.” Kenaka dzifunseni inumwini kuti: ‘Kodi tsopano ndikuvomereza kuti pa mfundo ya ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, Voltaire anali wolondola pamene anatcha chipembedzo “mdani wa mtundu wa anthu”? Kodi kuyang’ana kumeneku mu mbiri yachipembedzo kwandithandiza kuzindikira chipembedzo chowona, ndipo kodi ndikudziŵa mu nthaŵi ino yothera ya zochitika za anthu kumene icho chingapezedwe? Ngati nditero, kodi ndimafuna kukhala ngati munthu wofotokozedwa ndi wolemba nkhani wa ku France wa m’zaka za zana la 18 Joseph Joubert, amene “amapeza mwa icho chisangalalo ndi ntchito yake”?’
Lolani kuti onse oyankha kuti inde ku mafunso amenewa apitirizebe kupindula mwa kuŵerenga Galamukani! ndi magazine inzake. Tikupemphani kutsatira chilangizo chanzeru choperekedwa ndi Zion’s Watch Tower yotchulidwa pamwambapo chakuti: “Musakhale wokhutiritsidwa ndi duŵa limodzi la chowonadi. Ngati chimodzi chinali chokwanira sipakanakhalanso china. Sonkhanitsani mosalekeza, funafunani zowonjezereka.”
Inde, pitirizani kusonkhanitsa, pitirizanibe kufunafuna—funafunani kukongola kwamuyaya kowonjezereka kwa chipembedzo chowona!
[Bokosi patsamba 26]
Kuzindikira Chipembedzo Chanu Kukhala Chowona kapena Chonyenga
▪ Chipembedzo chowona chimaika mwa alambiri ake chomangira chachikondi chosasweka ndi chigwirizano chosayambukiridwa ndi malire a maiko. (Yohane 13:35) Chipembedzo chonyenga sichimapereka chikondi choterocho. M’malomwake, mwa kutsanzira Kaini, ziŵalo zake zimapita ku nkhondo za mitundu yonse ndi kuphana wina ndi mnzake.—1 Yohane 3:10-12.
▪ Chipembedzo chowona chimadzilekanitsa ndi ndale zadziko za anthu ndipo chimayang’ana kwa Mlengi kuthetsa mavuto a dziko kupyolera m’boma lake Laufumu. Chipembedzo chonyenga chimatsatira chitsanzo cha Nimrode pa Nsanja ya Babele. Icho chimagwirizana ndi ndale zadziko, kukhulupirira m’milungu ya ndale zadziko ndi kudziloŵetsa m’machitachita ake, ndipo mwakutero kuyala maziko a chiwonongeko chake.—Danieli 2:44; Yohane 18:36; Yakobo 1:27.
▪ Chipembedzo chowona chimazindikira Yehova kukhala Mulungu wowona, ndi yekhayo wokhoza kupulumutsa kuchoka m’kuponderezedwa. Chipembedzo chonyenga, chonga chochitidwa mu Igupto ndi Grisi wakale, chimapereka unyinji wa milungu yanthanthi yopanda thandizo ndipo yonse yopanda phindu.—Yesaya 42:5; 1 Akorinto 8:5, 6.
▪ Chipembedzo chowona chimalonjeza moyo wamuyaya pa dziko lapansi m’chimwemwe. Chipembedzo chonyenga—mwachitsanzo, Chibuda—chimawona moyo pa dziko lapansi kukhala wosakhumbika ndi monga chinachake chofunika kumasulidwako m’moyo wa pambuyo pa imfa wosatsimikizirika.—Salmo 37:29; Chibvumbulutso 21:3, 4.
▪ Chipembedzo chowona, mwa bukhu lake lopatulika, Baibulo, chimakhomereza mwa anthu chikhulupiriro chosagwedezeka; chimawapatsa iwo chiyembekezo chotsimikizirika ndi kuwasonkhezera iwo ku machitidwe a chikondi chenicheni kulinga kwa Mulungu ndi mnansi. (2 Timoteo 3:16, 17) Chipembedzo chonyenga, mosasamala kanthu za mabuku ake opatulika, chiri kwakukulukulu chosakhutiritsa m’kuchita zinthu zimenezi.—1 Yohane 5:3, 4.
▪ Chipembedzo chowona chimazindikirika ndi oyang’anira ake odzichepetsa. Chipembedzo chonyenga chimadziŵika kaamba ka atsogoleri ake a zikhumbo zodzigangila, a maganizo odzitukumula, omafuna kukhotetsa chowonadi ndi ofunafuna phindu la ndale zadziko ndi la kutchuka m’dziko.—Machitidwe 20:28, 29; 1 Petro 5:2, 3.
▪ Chipembedzo chowona, njira ya kugonjera koyenera kwa Mulungu, chimagwiritsira ntchito lupanga lauzimu, osati lenileni. Chipembedzo chonyenga, kumbali ina, chimapotoza chiphunzitso chowona, kuswa uchete Wachikristu, ndi kulondola nkhaŵa za munthu kuposa zikondwerero zaumulungu.—2 Akorinto 10:3-5.
▪ Chipembedzo chowona chimakopa mitima ya osakhulupirira ku kulambiridwa kwa Mulungu wowona. Chipembedzo chonyenga chimathandizira ku mkhalidwe wachikaikiro, kuganiza kwaufulu, kupeza nzeru wekha, ndi udziko.—Luka 1:17; 1 Akorinto 14:24, 25.
▪ Chipembedzo chowona, monga chikuchitidwa ndi Mboni za Yehova, chikukula mwauzimu kuposa ndi kale lonse. Chipembedzo chonyenga, zovala zake zokhathamira ndi mwazi, chikuvutika ndi nthenda yauzimu ya kusadya mokwanira ndi chirikizo lomafokerafokera.—Yesaya 65:13, 14.
Kodi mtsogolo mwachipembedzo ndimotani poyerekezera ndi nthaŵi yake yapita? Chipembedzo chonyenga chiribe mtsogolo. Turukani mwa icho! (Chibvumbulutso 18:4, 5) Tembenukirani ku chipembedzo chowona. Icho chidzakhala kosatha.