Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 2/8 tsamba 12-13
  • Kupyolera m’Maso Amwana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupyolera m’Maso Amwana
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Iwo Sali Akulu Aang’ono
  • Limbikitsani ndi Kutsogoza M’malo Molamula
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Kuthandiza Mwana Wanu Panthawi Yachisoni
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Muziyamikira Ana Anu
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 2/8 tsamba 12-13

Kupyolera m’Maso Amwana

MAKOLO ambiri adzavomereza nsonga imodzi yakuti: kulera mwana mwachipambano kuli chimodzi cha zitokoso zovuta zimene ayang’anizanapo nazo. Pakhala zolembedwa zosaŵerengeka pa mmene zimenezi zingachitidwire ndi chipambano. Komabe, pali njira imodzi imene ili yofikirika kwa achikulire onse, akhale makolo, agogo, azakhali, amalume, kapena mabwenzi chabe. Kunena za kumvetsetsa ndi kuphunzitsa ana, kodi mwayesera kupenyera m’maso amwana? Kodi nchiyani chimene chiridi m’malingaliro aang’ono amenewo?

Kumbukirani, ana ali anthu aang’ono. Kuwaona mwa njira imeneyi kudzatithandiza kumvetsetsa mmene iwo amatiwonera. Iwo amabadwa aang’onong’ono m’dziko la anthu aakulu matupi, ulamuliro, ndi mphamvu. Kwa kamwana, akulu angatathauze chitetezo, chitonthozo, ndi thandizo kapena angakhale chiwopsyezo chovutitsa.

Iwo Sali Akulu Aang’ono

Nsonga ina yofunika yachidziŵitso ndiyo kukhala wosamala kusapanga chophophonya chakuwachitira monga akulu aang’ono. Ubwana uyenera kukhala imodzi ya nthaŵi zachimwemwe koposa m’moyo. Palibe chifukwa chowafulumizira kuwupyola uwo kapena kuwapangitsa kuwuphonya. Aloleni asangalale nawo. Monga kholo, mungatenge mwaŵi kukulitsa mwa iwo malamulo a makhalidwe abwino ofunika kuti m’kupita kwa nthaŵi akakhale achikulire olangizidwa bwino.

Pamene muchita ndi ana, kuwona zinthu kupyolera m’maso amwana sikumataya phindu lake. Mwachitsanzo, kulira sikuyenera konse kukhala kupepha kumenyedwa ndi makolo okwiyitsidwa. Kulira kapena kusisima kuli njira yachibadwa ya khanda lobadwa chatsopano yosonyezera zofuna zake. Mwana atatuluka m’malo achisungiko a m’chibaliro cha amake, amakhoza kusonyeza malingaliro ake ndi liwu mwa kulira kolaswa mtima!

Limbikitsani ndi Kutsogoza M’malo Molamula

Nkwabwino kulimbikitsa zoyesayesa za ana kulongosola malingaliro awo. Kawonedwe kawo kangavumbule mavuto, ndipo vuto lomvetsetsedwa bwino n’lopepukirapo kulithetsa. Koma mmene timayankhira ku zokamba zawo nkofunika monga mmene kuliri kuwapangitsa kulongosola malingaliro awo. Wendy Schuman, mmodzi wa alembi a magazine a Parents, akupereka chilangizo pa mmene tiyenera kuyesa kulankhula kwa ana: “Kusonyeza kulingalira wina m’mawu . . . kuli lingaliro lalikulu la zoyesayesa zaposachedwapa za kukhozetsa kulankhulana kwa pakati pa kholo ndi mwana. Koma kulingalira wina mwa iko kokha sikokwanira ngati sikusonyezedwa m’mawu. Ndipo zimenezi sizimangobwera mwachibadwa ku milomo ya makolo ambiri.”

M’mawu ena, ngati mwana wasonyeza kupanda ulemu kapena wachita chinachake choipa, chofunika kuchiwongolera, tiyenera kuyesetsa kusalola mkhalidwe wathu ndi mphamvu ya liwu kufanana ndi kuipidwa kwathu kapena kukwiyitsidwa. Ndithudi, zimenezi nzopepuka kuzinena kuposa kuzichita. Koma kumbukirani kuti, kuyankha kozaza kapena kosuliza, konga ngati, “Wopusa iwe” kapena, “Kodi sungachiteko chabwino nchimodzi chomwe?” sikumawongolera konse mkhalidwe wovuta kale.

Makolo ambiri apeza kuti kusonyeza kulingalira wina mwakupereka chiyamikiro, makamaka asanapereke uphungu, kungakhale ndi zotulukapo zabwino. Apanso pali mwaŵi wa kuyang’ana kopyolera m’maso amwana. Ana ambiri amazindikira bwino lomwe pamene chiyamikiro choterocho chikuperekedwa ndi cholinga chachiphamaso kapena pamene sichichokera ku mtima. Chotero, pamene tikuyamikira ana athu, tiyenera kutsimikizira kuti chitamandocho nchenicheni ndipo chofunikira.

Katswiri wotchuka wa maganizo a ana Dr. Haim G. Ginott, akugogomezera m’bukhu lake lakuti Between Parent and Child kuti makolo ayenera kutamanda zokwaniritsidwa mmalo mwa umunthu. Mwachitsanzo, mwana wanu atapanga chola cha mabuku nakusonyezani, ndemanga yanu yakuti, ‘Cholachi sichokongola kokha komanso nchothandiza,’ idzakulitsa chidaliro chake. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mukutamanda chokwaniritsa chake. Motero, chitamando chanu chimakhala chenicheni kwa mwana wanu. Komabe, mawu akuti, ‘Ndiwe m’misiri wabwino,’ sangatero chifukwa chakuti mukusumika pa iye monga munthu.

Dr. Ginott akudziŵitsa kuti: “Anthu ambiri amakhulupirira kuti chitamando chimakulitsa chidaliro cha mwana ndi kumpangitsa kudzimva wachisungiko. M’chenicheni, chitamando chingatulukepo kukwinjika ndi kupulupudza . . . Pamene makolo awuza mwana kuti, ‘Ndiwe mnyamata wabwino,’ iye sangachilandire icho chifukwa chakuti kawonedwe kake ka iyemwini kali kosiyana kwenikweni . . . Chitamando chiyenera kuchita ndi zoyesayesa ndi zipambano za mwanayo, osati mikhalidwe yake ya umunthu . . . Chitamando chiri ndi mbali ziŵiri: mawu athu ndi zotengapo za mwana. Mawu athu ayenera kusonyeza poyera kuti tikuyamikira zoyesayesa, ntchito, chokwaniritsa, thandizo, ndi zolingalira za mwanayo.”

Lingaliro labwino limeneli kaamba ka chiyamikiro n’logwirizana ndi chilangizo chowuziridwa chosonyeza kuwolowa manja, chopezeka pa Miyambo 3:27 chakuti: “Usawamane chabwino awo ochiyenerera, pamene chiri m’mphamvu yako kuchitapo kanthu.”—New International Version.

Kunena chowonadi tinganene kuti mosasamala kanthu za chilangizo chabwino kapena uphungu wanzeru umene timaŵerenga, palibe njira yachidule ku imene ena aitcha programu ya zaka 20 ya kulera mwana wamwamuna kapena wamkazi. Iyo imafunikira kuleza mtima, chikondi, kumvetsetsa, ndi kulingalirana. Koma thandizo lalikulu kulinga ku chipambano ndilo kuphunzira kuwona ndi kumvetsetsa mkhalidwe wa wachichepere wanu “kupyolera m’maso amwana.”

“Mwana wanzeru akondweretsa atate,” idalemba tero Mfumu yanzeru Solomo. (Miyambo 10:1) Lolani kuti kumvetsetsa kwabwinopo kwa kalingaliridwe ndi kawonedwe ka zinthu ka mwana wanu zikuthandizeni kupambana m’chokumana nacho chosangalatsa chimenechi.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena