Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchiyani Chikuchitika ku Thupi Langa?
MASINTHIDWE ozizwitsa ayamba kuchitika m’thupi lanu.
Ngakhale kuli tero, pakalipano iwo angawoneke kukhala ozizwitsa. Mungadzimve kukhala wosokonezeka, wonyazitsidwa, kapena wochititsidwadi mantha ndi zimene zikuchitika kwa inu. “Sindinali wokonzekera,” anatero mtsikana wina. “Ndinalingalira kuti, O, ayi, sindikufunatu kuti zoterezi ziyambe kuchitika kwa ine.” Adatero mnyamata wina: “Sindikudziŵa kaya ndapunduka kapena ndiri bwino. Ndine wazaka 13 ndipo masinthidwe akuchitika m’thupi langa . . . Ndikudzimvadi wosiyana ndikuti ndiri ndekha nthaŵi zina ndipo zindichititsadi mantha kuti wina akandiseka nazo.”
Nzomveka kuti nanunso mungadzimve chimodzimodzi. Inu mukupyola mu imene wazaka zapakati pa 13 ndi 19 anailongosola kukhala nthaŵi imene thupi lake “linayamba kupenga.” Koma zimene zingawoneke kukhala “kupenga” panthaŵiyo ziridi kachitidwe kadongosolo kamene kakukusinthani kuchoka ku mwana kukhala wamkulu. Iko kumatchedwa unamwali. Ndipo mosasamala kanthu za dzina lake losamveka bwino, unamwali suli mtundu winawake wa matenda, ndipo sindinu woyamba kupyolamo. Amayi anu ndi atate anu anakumana nazo. Anzanu apasukulu ndi mabwenzi ena amsinkhu wanu mothekera akupyolamo. Ndipo motsimikizirika, mudzatulukamo.
Koma kodi nchiyanidi chimene chiri kusintha kwachilendo kumeneku komachitika ku thupi lanu?
Choloŵanecholoŵane wa Unamwali
Baibulo limanena kuti nthaŵi inayake pambuyo pokwanitsa zaka 12 zakubadwa, “Yesu anakulabe . . . mumsinkhu.” (Luka 2:52) Inde, ngakhale Yesu Kristu anapyola mu unamwali. Mkati mwa nthaŵi yaunamwali, mudzakumana ndi nyengo ya kukula ndi kusintha kwathupi. Komabe, chimene chimachititsadi kukula kumeneku chiri chinsinsi chenicheni, chozizwitsa! Zikutikumbutsa za fanizo la Yesu m’limene ananena za mwamuna amene anabzala mbewu. Yesu adati: “Mbewu zikamera, ndi kukula, iye sadziŵa umo zichitira.” (Marko 4:27) Mofananamo, adokotala angatipatse kalongosoledwe kapatalipatali ka zimene zimachitika m’nthaŵi ya unamwali.
Nthaŵi inayake pakati pa misinkhu ya chifupifupi 9 ndi 16, mumaloŵa mu unamwali. (Msinkhu umasiyana malinga ndi munthu, ndipo atsikana kaŵirikaŵiri amafulumira kwa chaka chimodzi kapena ziŵiri.) Ubongo wanu umayamba zochitika zotsatizanatsatizana mwakuyambitsa kachiŵalo kakang’ono kokhala kumwamba kwa kamwa yanu kotchedwa pituitary gland. Pituitary imeneyi imayankha mwakutulutsa mauthenga a mphamvu ya m’maselo otchedwa mahormone. Ameneŵa amayenda m’mwazi wanu ndi kuwuza ziŵalo zanu zakubala kupanga mahormone enanso. Machende amnyamata amatulutsa mahormone achimuna, monga ngati testosterone; maovary a mtsikana, amatulutsa mahormone achikazi, onga ngati estrogen.
Mahormone ameneŵa, nawonso, amauza magland ndi ziŵalo zina kuyamba kusintha mawonekedwe anu.
Masinthidwe Amene Atsikana Amakumana Nawo
Ngati ndinu mtsikana, chinthu choyamba chimene mungawone ndicho kukula kwapang’onopang’ono kwa maŵere anu. Mahormone anu achititsa mamammary gland anu kuyamba kukula. (Magland otulutsa mkaka ameneŵa amakhozetsa azimayi kudyetsa makanda awo.) Mahormone anu amayambitsanso kupangika kwa mafuta, amene amawumba maŵere anu. Mafuta adzaikidwanso m’chiuno mwanu, ntchafu, ndi m’matako. Mudzawonjezera kulemera kwa thupi ndipo mungakhale ndi kukula thupi kofulumira.
Pamene kuli kwakuti unyinji wa atsikana amalandira masinthidwe athupi ameneŵa, si atsikana onse amene amawalandira onse. Mwachitsanzo, ubweya pa mikono yanu, miyendo, ndi m’khwapa ungachindikale ndi kuderako. Pamenepa, m’maiko ena, ubweya wathupi woterowo ungalingaliridwe kusakhala ukazi kapena kusawoneka bwino. Mosasamala kanthu za mawonekedwe, iko kuli chizindikiro chabwino chakuti mukukula kufika ku ukazi.
Kusintha kwina kosalandiridwa kungakhale kugwira ntchito kowonjezereka kwa magland athukuta—mudzayamba kutulutsa thukuta mowonjezereka. Fungo lotsagana nalo lingakuchititseni mwanyazi. Koma ngati musamba kaŵirikaŵiri ndi kuvala zovala zaudongo, nthaŵi zambiri sipamakhala mavuto a fungo. Achichepere ena amasankha kugwiritsira ntchito mafuta akupha fungo monga chinjirizo lina ku fungo.
Kusintha kwina kwaumwini kwambiri kumaloŵetsamo kukula kwa ubweya mozungulira malo anu akumpheto. Uwo umatchedwa ubweya wakumpheto. Ngati simunauzidwe pasadakhale ponena za zimenezi, mungachipeze kukhala chochititsa mantha. Koma iko kuli kwachibadwa ndipo sichochita nacho manyazi.
Unamwali ungayambitsenso chimene The New Teenage Body Book linachitcha “nkhaŵa yoyamba [mawonekedwe] ya achichepere”—mavuto a khungu. Masinthidwe a m’choloŵanecholoŵane wa thupi lanu kaŵirikaŵiri amapangitsa khungu kukhala lamafuta. Zipupu ndi zisungu zakumaso zimayamba. (Mogwirizana ndi kufufuza kwina, mavuto a khungu anakantha chifupifupi 90 peresenti ya amsinkhu wapakati pa 13 ndi 19 ofunsidwa!) Mwamwaŵi, vutolo kaŵirikaŵiri lingachepetsedwe ndi kusamalira khungu kwabwino.—Wonani nkhani yakuti “Can’t I Do Something About My Acne?” yopezeka mu Awake! ya February 22, 1987.
Masinthidwe Amene Anyamata Amakumana Nawo
Ngati ndinu mnyamata, zotulukapo zoyambirira za unamwali sizidzakhala zowonekera monga za mtsikana. Pamene dongosolo lanu lakubala liyamba kugwira ntchito, ziŵalo zanu zakumpheto zimakula pang’onopang’ono. Ubweya umayamba kumera mozungulira mpheto yanu. Kachiŵirinso, zimenezi nzachibadwa.
Panthaŵi imodzimodziyo, mungakhale ndi kukula kofulumira. Mafuta ndi minofu imayamba kuwonjezeka ku thupi lanu. Mumakhala wamkulu thupi, wamphamvu, mapewa anu amakula. Pang’onopang’ono thupi lanu limaleka kuwoneka laubwana nkumawoneka monga mwamuna wamkulu.
Kusintha kwina kokondweretsa kumaloŵetsamo kukula kwa ubweya m’miyendo yanu, pachifuwa, pa nkhope, ndi m’khwapa. Izinso zimachititsidwa ndi hormone yotchedwa testosterone. Bukhu lakuti Changing Bodies, Changing Lives, lolembedwa ndi Ruth Bell, linagwira mawu wachichepere wina yemwe anati: “Pamene ndinali wazaka khumi ndi zinayi ndinkayendayenda ndi dontho la litsiro pa mlomo wanga wapamwamba kwa chifupifupi milungu iŵiri. Ndinkayeserabe kulichotsa koma silinkachoka. Kenaka ndinaliyang’anitsitsa nkupeza kuti linali ndevu.”
Ndiiko nkomwe, kuchuluka kwa ubweya umene mungakhale nawo kulibe chochita ndi mtundu wamwamuna amene muli; iko kuli chabe nkhani ya choloŵa. M’mawu ena, ngati atate anu ali ndi chifuwa chaubweya, mothekera nanunso mudzatero. Chimodzimodzinso ndi nkhope yaubweya. Komabe, kaŵirikaŵiri zimatenga nthaŵi kufikira kumapeto auchichepere wanu kapena kuchiyambi kwa zaka zanu zam’ma 20, kuti muyambe kumeta mokhazikika.
Ndithudi, mudzakhala ndi nthaŵi zochititsidwa manyazi. Anyamatanso amapeza kuti magland awo athukuta amagwira ntchito mowonjezereka. Mudzafunikira kukhala wodera nkhaŵa kwenikweni ponena za ukhondo waumwini kotero kuti mupewe mavuto a fungo. Nanunso mungatuluke zakumaso chifukwa cha khungu lotulutsa mafuta.
M’nthaŵi ya pakati pa uchichepere wanu, m’mero wanu udzakula; zotulutsa mawu zanu zidzachindikala ndi kutalika. Monga chotulukapo, liwu lanu lidzakula. Anyamata ena amakhala ndi kusintha kofulumira kuchoka ku liwu laling’ono kukhala ndi lalikulu. Koma kwa ena, liwu limasintha pang’onopang’ono kutenga nthaŵi yaitali yovutitsa kwa milungu kapena miyezi. Mawu aakulu, ndi ochindikala amamveka ndi phokoso lochititsa manyazi. Ngakhale kulitero, khazikani mtima. Liwu lanu lidzasalala m’kupita kwanthaŵi. Pakalipano, ngati mungadziseke nokha, zimathandiza kuchepetsa kuchititsidwa manyaziko.
Kukula Kofunika Koposa
Kukula kuli kozizwitsa ndi kosangalatsa! Kungakhalenso kochititsa manyazi ndi mantha. Koma chinthu chimodzi nchotsimikizirika: Inu simungafulumize kapena kuchedwetsa kukula. Chotero m’malo molandira masinthidwe ochititsidwa ndi unamwali moipidwa ndi mwamantha, kondwerani nawo, alandireni mwachisomo—ndi lingaliro lachisangalalo. Zindikirani kuti unamwali suli chotulukapo chomalizira koma chochitika chomangopita. Pamene namondwe wa unamwali wapita, inu tsopano mudzawoneka mwamuna kapena mkazi wofikapo msinkhu!
Komabe, musaiŵale konse kuti kukula kwanu kofunika koposa kumaloŵetsamo, si kutalika kwanu, kaumbidwe, kapena mawonekedwe a nkhope, koma kukula kwanu monga munthu—maganizo, malingaliro, ndi uzimu. Mtumwi Paulo adati: “Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinaŵerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana.” (1 Akorinto 13:11) Kuwoneka ngati mkulu sikokwanira. Mwapang’onopang’ono muyenera kuphunzira kuchita, kulankhula, ndi kuganiza ngati mkulu. Musade nkhaŵa kwenikweni ndi zomwe zikuchitika ku thupi lanu kotero kuti muchite kuiŵala kusamalira “munthu wamkati.”—2 Akorinto 4:16, The Jerusalem Bible.
Chikhalirechobe, zochitika zina zaunamwali zingakhale zokwinjitsa kwenikweni. Mmene mungachitire nazo ndiwo udzakhale mutu wa nkhani zamtsogolo.
[Zithunzi patsamba 19]
Masinthidwe akukula samakubwezani kumbuyo