Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kupeŵa Matsenga?
“NDINAWAKONDADI agogo anga,” anatero msungwana wina wachichepere, “ndipo pamene anamwalira, ndinavutika maganizo kwambiri. Ndinafuna kudziŵa ngati kunali kothekera kulankhulanso nawo.” Ndimo mmene msungwana wachichepereyo anayambira kuphatikizidwa m’matsenga.
Ripoti la posachedwapa linanena kuti “ana ndi achichepere okwanira 200,000 mu Federal Ripabliki ya Jeremani anachitapo mitundu yosiyanasiyana ya matsenga.” Japan iri ndi gulu wamba la ana okhulupirira mizimu m’sukulu, ena ndi akatwitsiri m’kudziŵa maganizo a munthu popanda mawu, ena ndi ogoneka tulo, pamene ena amaturutsa mizimu yoipa. Mu Nigeria sikwachilendo masiku ano kumva za ana opita ku sukulu ya pulaimale kukhala akuchita ufiti. Ndipo, nzomvetsa chisoni kunena kuti, ngakhale achichepere ena oleredwa ndi makolo Achikristu, mosadziŵa, alingalira za kukhala ndi mphamvu zamatsenga.
Kodi nchifukwa ninji matsenga akusangalaridwa chotero ndi achichepere? Ndipo kodi nchifukwa ninji kuphatikizidwamo kuli kwaupandu kwambiri?
Chifukwa Chimene Amaloŵetsedweramo
Matsenga amaphatikizapo mphamvu zosakhala zachibadwa, kutulukiridwa kwa dziko lamizimu mogwiritsira ntchito kupenda nyenyezi, kuwombeza ula, ufiti, kuchita matsenga, ndi zina zotero. Ndipo kodi nchifukwa ninji achichepere ambiri chotero ali ofunitsitsa kusuzumira mu zinthu zoterozo? Dirk anali ndi chikhumbo chachikulu cha kulankhula ndi atate ake akufawo. Atakhutiritsidwa kuti akakhoza kutero ngati anakulitsa mphamvu zake za kuganiza, iye anayamba chizolowezi cha kusinkhasinkha mmene anayesayesa kupangitsa zinthu kuyenda popanda kuzikhudza. Kusinkhasinkha kotero, anatero Dirk, kunamfikitsa pakhomo lamizimu!
Achichepere ena amawopa mtsogolo. Amafuna uphungu wonena za ziyembekezo zawo za magiredi kapena ukwati ndipo amaganiza kuti mizimu ingawathandize. Kovutitsadi maganizo ndiko kulambiridwa kwa Satana iyemwiniyo! Kodi chosangalatsa nchiyani m’chipembedzo chonyansachi? “Ndinaloŵeramo kufunafuna mphamvu,” analongosola tero wachichepere wina wa ku Canada yemwe amalambira Satana. “Kumandipatsa mphamvu ya kuvulaza anthu.”
Komabe, ofufuza ambiri amakhulupirira kuti chifukwa chokulira chimene achichepere amadziloŵetsera m’matsenga ndicho kokha kufuna kudziŵa. “Ndinali kufuna kudziŵa kwambiri,” anavomereza motero msungwana wina amene anaphatikizidwa m’matsenga. Msungwana wina analongosola mwanjira iyi: “Poyamba ndinali wokaikira, ndiyeno ndinaganiza kuti, ‘komatu udzadziŵa mmenedi zinthu zimakhalira.’” Chotero anavomereza chiitano chochokera kwa bwenzi kukakhalapo pa maphunziro a kuchita matsenga.
Atasonkhezeredwa ndi chikhumbo chofuna kudziŵa, achichepere ena amayesera kuika manja awo pa Thabwa Lowombezera kapena kutulukira kwina mwa kupenda mayendedwe a galasi lozondotsedwa. Limenelo limakhala kokha sitepi loyamba lonkira ku kuphatikizidwa mozama m’kukhulupirira mizimu mwa kugwiritsira ntchito mipira ya galasi, makhadi owombezera, maphenda, masamba a tii, ndi mabukhu opendera zakuthambo. Ena amayamba kufunsiradi kwa owombeza ula kapena asing’anga. Komabe, akatswiri ambiri amatsimikizira kukhala onyenga. Mwachitsanzo, kuti awongolere magiredi ake, Alexander anapita kwa sing’anga wina. Iye sanangolephera kokha kuwongolera magiredi ake komanso anataikiridwa ndi ndalama. Ndalama zake zinagaŵidwa pakati pa sing’anga wonyenga ndi wotchedwa kuti bwenzi amene anam’vomereza.
Komatu kwa achichepere ambiri, kuphatikizidwa m’kukhulupirira mizimu kumatulutsa chivulazo chachikulu kuposa kutaikiridwa ndi ndalama.
‘Chizunzo Chosaneneka’
“Ndikadadziŵa” ndiwo mawu amene anamvedwa kaŵirikaŵiri pakati pa awo amene anamva chisoni chifukwa choseŵera ndi kuchita matsenga. Inatero Personality, magazine ya ku South Africa. Lofananalo ndilo dandaulo lakuti: “Ngati kokha sindikananyengeka. . . . Ndakanthidwa ndi chizunzo chosaneneka, mawu, ziloto, ziwopsezo, ndipo ndazunzidwa ndi olambira Satana m’maganizo ndi kuthupi pamene ndinayesa kuonjokamo.”
Aphunzitsi okwanira 24 peresenti ofunsidwa mu Jeremani anawona chisonkhezero chovutitsa maganizo cha kuchita matsenga kwa ophunzira. Ophunzira ena anali achete, anali ndi mavuto akuphunzira, anali amantha, anali atondovi, ndipo anayamba chizolowezi cha kudzivulaza iwoeni kapena ena. Dirk sankagona usiku kaŵirikaŵiri. Iye akukumbukira kuti: “Pokhala ndi mantha a kukhala ndi ziwanda, sindinayese kutseka maso anga. Ndinali watcheru paphokoso lirilonse.” Mofananamo wachichepere wina wotchedwa Michael anavutika ndi “kusagona usiku chifukwa cha kuvutitsidwa ndi ziwanda” pambuyo pakumwa mankhwala amene anauzidwa. Maripoti ena akufotokoza kusintha kowopsa kwa maumunthu mwa anthu otenga mbali m’matsenga. Mtsikana wina anachenjeza amake mwakuwauza kuti mtsogolomo iye akavala zovala zakuda (mtundu umene iye anafunanso kupaka chipinda chake) ndi kugona m’bokosi lamaliro losatsekedwa!
Nzika Zenizeni za Dziko Lamizimu
Malemba amanena momvekera bwino kuti “akufa sadziŵa kanthu bi.” (Mlaliki 9:5) Chotero dziko lamizimu silimakhalidwa ndi miyoyo ya okondedwa akufa. Nangano, kodi chimachititsa zokumana nazo zowopsazo nchiyani? Ziwanda zoipa! Mogwirizana ndi Baibulo, amenewa ndi angelo opanduka, atsatiri a Satana Mdierekezi. (1 Petro 3:19, 20; Chivumbulutso 12:9) Iwo ali ndi mbiri yopititsa patsogolo kupulupudza ndi kuvulaza anthu.
Mwachitsanzo, Luka 9:42, imatiuza za mwamuna wogwidwa ndi ziwanda amene “chiwandacho chinamgwetsa ndi kumng’ambitsa.” Ha ndi nkhalwe yotani nanga! Mofananamo Machitidwe 19:16 amafotokoza mmene mwamuna wogwidwa ndi chiwanda anawukirira anthu asanu ndi aŵiri amene adati adzakhale alauli. Zokumana nazo zamakono zimatsimikizira bwino lomwe kuti ziwanda sizinasinthe njira zawo zoipa mpang’ono pomwe.
Chotero wachichepere amene wayamba kuseŵera ndi ESP, kupenda nyenyezi, ndi makhadi owombezera, kapena mpangidwe uliwonse wa matsenga angakhale akutsegulira njira ku zokumana nazo zowopsa! Magazine a Personality ananena kuti: “M’chitidwe wodziŵika pa zokumana nazo za onse amene tinalankhulapo nawo [amene anadziloŵetsa m’matsenga] unali wakuti anamizidwa mowonjezerekawonjezereka m’thope la ziwanda kupyolera m’ngalande ndi chovala chophimba cha kulemekezeka.” Inde, matsenga ndiwo cholumikizira pofuna kulankhulira ndi Satana ndi ziwanda!
‘Uchi Pampeni Wakuthwa’
Chotero Chilamulo cha Mulungu kwa Aisraeli chinaletsa mpangidwe uliwonse wa kukhulupirira mizimu, chikumati: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.”—Deuteronomo 18:10, 11.
Akristu m’zaka za zana loyamba anadziyeretsa kukugwirizana ndi kukhulupirira mizimu kulikonse, akumawononga katundu yense wogwirizana ndi ziwanda. (Machitidwe 19:19) Mofananamo achichepere lerolino amene amakhumba ubwenzi ndi Yehova adzachotsa chirichonse chogwirizanitsidwa ndi matsenga. Chimenecho chingaphatikizepo akanema onse, mabuku, mabuku a nthano, ndi zikwangwani zogwirizanitsidwa ndi mizimu. Ngakhale nyimbo zosankhidwa ndi munthuwe ziyenera kupendedwa. Mwachitsanzo, kaŵirikaŵiri nyimbo zophokosera kwambiri, zagwirizanitsidwa ndi Satana.
Nzika za ku Tibet ziri ndi mwambi wakuti: ‘Samalitsani polandira uchi woperekedwa pampeni wakuthwa.’ Poyesa kunyambita uchi pampeni, mungadulidwe lirime! Mofananamo, mosasamala kanthu za kusangalatsa kumene matsenga angakhalire ku chikhumbo chanu cha kufuna kudziŵa, iwo ngakupha. Chotero kanani chiitano chirichonse cha kukhala ndi phande m’zochitika kapena ngakhale kupenyerera za matsenga. Chinthu chowoneka kukhala chosavulaza chonga maseŵera oyendetsa galasi chingatsogolere kukuloŵetsedwamo kwaupandu m’zauchiwanda. Zowona, inu mungakhale ndi chikhumbo cha kufuna kudziŵa. Koma kodi mungadye nyama yovunda kokha chifukwa chakufuna kudziŵa mmene zimamvekera mkamwa mutadya zakudya zovunda?
Dirk (wotchulidwa poyambirirapo) anali wokhoza kudzionjola ku matsenga. Mwa kuphunzira Baibulo mothandizidwa ndi mabuku a Watch Tower Sosaite, iye anafikira pa kumvetsetsa chowonadi chonena za atate wake akufawo, ndipo anaphunzira za chiyembekezo cha chiukiriro. (Salmo 146:4; Yohane 5:28, 29) Chowonadi chimenechi chinammasula ku chikhumbo chirichonse cha kufuna kulankhula ndi mizimu. (Yerekezerani ndi Yohane 8:32.) Kodi Dirk alikuti tsopano? Iye wagwirizana ndi Mboni za Yehova ndipo akugwira ntchito pa imodzi ya nyumba zosindikizira za Watch Tower Sosaite monga mtumiki wa nthaŵi zonse.
Inde, Baibulo limakhutiritsa ‘zosoŵa zathu zauzimu.’ (Mateyu 5:3) Ndipo m’kupita kwanthaŵi, ichi chimakhala chopindulitsa kwambiri kuposa kukhutiritsa chikhumbo choipa cha munthu cha kufuna kudziŵa kupyolera mwa matsenga aupandu, ndi akupha.
[Chithunzi patsamba 18]
Kuphatikizidwa m’matsenga kungayambire pamaseŵera owonekera kukhala osavulaza, onga ngati Thabwa Lowombezera iri kapena kugwiritsira ntchito tambula yozondotsedwa