Lingaliro la Baibulo
Chimene Muyenera Kudziŵa Ponena za Angelo
“Akatswiri achipembedzo chifupifupi 3,000 anakumana kwa masiku anayi mu New York mlungu wathawu kudzamvetsera maripoti oposa 500 pankhani zoyambira pa mbali ya kuseketsa m’maulaliki kufikira pa kufunika kwa dzoma kwa Apentekoste. Palibe ndi mmodzi amene anatchula angelo.”—Daily News, December 26, 1982.
LEROLINO, zaka zisanu ndi zitatu pambuyo pake, atsogoleri achipembedzo adakanenabe zochepera ponena za angelo. Nchifukwa ninji? Kodi kungakhale kwakuti chifukwa chakuti amithenga akumwamba amenewa amangowonedwa kukhala nthano zakale? Kapena kodi iwo alikodi? Ngati ziri choncho, kodi muyenera kudziŵanji ponena za iwo?
Kodi Iwo Aliko?
Angelo sali kokha “zimphamvu” kapena “zoyendayenda za kuthambo,” monga momwe anthanthi ena amanenera. Iwo ali enieni mokwanira kuti atchulidwe nthaŵi mazana ambiri m’Mawu a Mulungu, Baibulo. M’zinenero zoyambirira za Babibulo, mawu otembenuzidwa kukhala “angelo” (Chihebri, mal·’akh΄; Chigriki, agʹge·los) kwenikweni amatanthauza “wobweretsa uthenga” kapena mwachidule “mthenga.” Mawu amenewa amawonekera chifupifupi nthaŵi 400 m’Baibulo lonse, nthaŵi zina amalozera kwa anthu, koma kaŵirikaŵiri kwa amithenga auzimu.
Mngelo amene anawonekera kwa mkazi wosabala wa Manowa ndi kulengeza za kukhala ndi pakati pa mwana wake wamwamuna, Samson, anali weniweni kwa iye. Choteronso angelo atatu amene anawonekera kwa Abrahamu ndi mkazi wake Sara, ndi aŵiri amene anafunafuna Loti, ndi mmodzi amene anakhala patsinde pamtengo waukulu ndi kulankhula kwa Gedioni. (Genesis 18:1-15; 19:1-5; Oweruza 6:11-22; 13:3-21) Pakubadwa kwa Yesu, mngelo anawonekera mwadzidzidzi ku kagulu ka abusa m’kuunika kowala, konyezimira.—Luka 2:8, 9.
Angelo amenewo anali enieni. Sanali maloto ongoyerekezera kapena chinthu chopanda thupi. Iwo anakwaniritsa chifuno cholinganizidwa monga amithenga ochokera kwa Mulungu, ndipo zochitikazi zalembedwa bwino lomwe m’Baibulo kuti zitipindulitse lerolino. (2 Timoteo 3:16) Chotero Baibulo limavumbula mfundo zofunika zonena za angelo zimene mufunikira kudziŵa, zina za zimenezo zimawombana ndi malingaliro ozoloŵereka.
Kodi Kawonekedwe Kawo Nkotani?
Mwinamwake inu mumalingalira angelo kukhala ziphadzuŵa za akazi kapena zolengedwa zojintcha, zonga makanda zokhala ndi mapiko, zomwetulira mwaubwenzi zovala minjiro yoyera, zikumaliza azeze aang’ono, ndi kuyandama m’mlengalenga. Ngati ziri choncho, muyenera kudziŵa kuti amenewa ndiwo malingaliro opeka otengedwa ku malingaliro achikunja, monga ngati nthanthi ya Agriki. Kapena malingalirowo anatengedwa pambuyo pakumalizidwa kwa kulembedwa kwa Baibulo. M’masomphenya aulosi a Baibulo, zolengedwa zauzimu zonga ngati aserafi ndi akerubi ziri ndi mapiko.—Yesaya 6:2; Ezekieli 10:5; Chivumbulutso 14:6.
Mawu a Mulungu amalongosola angelo kukhala mizimu yamphamvu kwambiri, ndipo mzimu ngwosawoneka ndi maso. (1 Mafumu 22:21; Salmo 34:7; 91:11) Anali “mngero wa Yehova” amene anakantha Asuri 185,000 mumsasa wa adani a Israeli muusiku umodzi wokha! (Yesaya 37:36) Pamene angelo anadziwonetsera kwa anthu, nthaŵi zonse iwo anawonekera monga amuna ovala mokwanira, osati monga akazi kapena ana ndipo sanawonekerepo mumpangidwe wochepera pa munthu.
Kodi zolengedwa zauzimu zamphamvuzi zinachokera kuti? Baibulo limanena kuti “pakuti mwa iye [Yesu], zinalengedwa zonse za m’mwamba, ndi zapadziko, zowoneka ndi zosawoneka.” (Akolose 1:16) Yehova Mulungu, kupyolera mwa Mwana wachisamba ameneyu, sanalenge kokha angelo kalekale munthu asanalengedwe komanso anawapanga iwo kukhala apamwamba kuposa anthu.—Yobu 38:4, 7; 2 Petro 2:11.
Kodi Iwo Ali Ndi Maumunthu?
Angelo, mofanana ndi anthu, ali ndi malingaliro. Pambuyo powona kulengedwa kwadziko lapansi, timauzidwa kuti angelo “anaimba limodzi,” ngakhaledi “kufuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:7) Baibulo imavumbulanso kuti “kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.” (Luka 15:10) Ndithudi, palibe “mphamvu” yopanda thupi imene ikadakhala ndi chimwemwe chosefukira chofotokozedwa m’ndime zimenezo.
Angelo alinso ndi polekezera. Mfundo zina zonena za Kristu ndi mtsogolo zinavumbulutsidwira aneneri aumunthu koma osati kwa angelo. Mawu a Mulungu amatiuza kuti “zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.” (1 Petro 1:10-12) Ponena za deti lenileni losankhidwa ndi Mulungu la kudza kwa Ambuye, Yesu anati: “Koma za tsiku ilo ndi nthaŵi yake sadziŵa munthu aliyense, angakhale angelo a kumwamba, kapena Mwana, koma Atate yekha.”—Mateyu 24:36.
Ndiponso, maina aangelo aŵiri, Mikaeli ndi Gabrieli, amawonekera m’Baibulo. (Danieli 12:1; Luka 1:26) Kodi zimenezi sizikuwonjezera kuumboni wa kukhala kwawo anthu? Monga anthu, iwo sanalinganizidwiretu, mofanana ndi kompyuta kapena roboti, kuchita mwanjira yoikika. Mmalo mwake, angelo anapatsidwa mphatso ya mphamvu za kuzindikira ndipo ali ndi ufulu wa kupanga zosankha zawo zamakhalidwe abwino. Chotero, pokhala zolengedwa zokhala ndi ufulu wakudzisankhira, angelo ena anasankha kupandukira Mulungu ndipo anakhala Satana ndi ziwanda zake.—Genesis 6:1-4; Yuda 6; Chivumbulutso 12:7-9.
Kodi Ayenera Kulambiridwa?
Ngakhale kuti tingavomereze kukhalako kwa angelo kukhala nsonga yeniyeni, osati yopeka, tiyenera kupeŵa kupambanitsa. Magulu ena a chipembedzo apereka ulemu wopambanitsa kwa angelo, ngakhale kuti kulambira angelo nkotsutsidwa m’Baibulo. (Akolose 2:18; Chivumbulutso 22:8, 9) Tchalitchi cha Katolika chakweza Mikaeli ndi Gabrieli kukhala oyenera kulambiridwa. Ndipo m’matchalitchi a Orthodox Akummawa, angelo alidi ndi malo ofunika m’mapemphero. Nzosiyana chotani nanga ndi chenjezo loperekedwa ndi mngero wa Yehova pamene mtumwi Yohane anagwada pamapazi ake: “Tapenya, usatero; ine ndine kapolo mnzako.”—Chivumbulutso 19:10.
Kodi nchifukwa ninji pali chisokonezo chotero ponena za angelo? Satana, amene amadzisanduliza kukhala “mngelo wakuunika,” “wachititsa khungu maganizo a osakhulupirira.” (2 Akorinto 4:4; 11:14) Chotero, kodi sikungakhale kwanzeru kuyembekezera kuti ambiri lerolino akamamatira ku malingaliro awo ponena za kukhalako ndi mpangidwe wa angelo mmalo mwa kuvomereza chimene Mawu a Mulungu amanena? Inde, ngakhale kuti atsogoleri achipembedzo lerolino anganene zochepera ponena za angelo, ife tiri ndi chitsimikiziro cha Mulungu kupyolera mwa cholembedwa cha Baibulo chakuti iwo alikodi ndipo amachita utumiki wolemekezeka monga amithenga a Yehova.—Ahebri 1:7, 14; 6:18.
[Chithunzi patsamba 28]
Angelo oimiridwa monga zolengedwa zonga makanda zokhala ndi mapiko atengedwa kuchokera ku malingaliro achikunja
[Mawu a Chithunzi]
Cupid a Captive by François Boucher, c. 1754