Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 4/8 tsamba 6-8
  • Zamoyo Zakuthambo—Kodi Ziri Kuti?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zamoyo Zakuthambo—Kodi Ziri Kuti?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zikaikiro Ziyamba
  • Maziko Ogwedera
  • Chipembedzo Cholakwa
  • Zamoyo Zakuthambo—Loto Lakalekale
    Galamukani!—1990
  • Kodi Dzuwa ndi Mapulaneti Olizungulira Zinakhalako Bwanji?
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Zamoyo Zakuthambo—Kupeza Yankho
    Galamukani!—1990
  • Zimene Zinthu Zakuthambo Zimatiuza
    Galamukani!—2021
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 4/8 tsamba 6-8

Zamoyo Zakuthambo—Kodi Ziri Kuti?

MOGWIRIZANA ndi wolemba sayansi Isaac Asimov, limeneli ndi “funso limene, mwanjira ina yake, limawononga zonse” kwa awo amene amakhulupirira moyo wa pa mapulaneti ena. Poyambirirapo lofunsidwa ndi katswiri wa physics ya nyukliya mu 1950 Enrico Fermi, funsolo linadzutsa mkangano womwe unali wotere: Ngati moyo waluntha wabuka pa mapulaneti ena m’khamu lathu la nyenyezi, payenera kukhala anthu amene akhalako zaka mamiliyoni ambirimbiri kuposa ife. Iwo anakayenera kukhala anayambitsa kuyenda pakati pa nyenyezi kale kwambiri ndi kufalikira m’khamu la nyenyezi, akumalamulira ndi kufufuza mwakufuna kwawo. Chotero kodi ali kuti?

Pamene kuli kwakuti asayansi ena a SETI adzidzimutsidwa ndi “nthanthi ya Fermi” imeneyi, kaŵirikaŵiri amayankha mwakusonya mmene chingakhalire chovuta kuyenda pakati pa nyenyezi. Ngakhale atamayenda pa liŵiro la kuwala, mosasamala kanthu za kukula kwake, kungatengere chombo cha mlengalenga zaka zikwi zana limodzi kudutsa khamu lathu la nyenyezi. Kupyola liŵiro limenelo kukulingaliridwa kukhala kosatheka.

Nthanthi za sayansi zimene zimasonyeza zombo zikulumpha kuchokera ku nyenyezi imodzi kupita ku inzake m’masiku kapena maola owerengeka m’zachinyengo, osati sayansi. Mitunda ya pakati pa nyenyezi njaikulu kwambiri kuposa mmene tingalingalirire. Kwenikwenidi, ngati tikanapanga chithunzi cha khamu lathu la nyenyezi chaching’ono kwambiri kotero kuti dzuŵa lathu (limene nlalikulu kotero kuti lingameze maiko miliyoni imodzi) linachepetsedwa ku ukulu wa lalanje, mtunda wapakati pa nyenyezi m’chithunzichi ukanakhalabe makilomita 1,600!

Chimenecho ndicho chifukwa chake asayansi a SETI amayedzamira mokulira pa maradio telescope; iwo amaganiza kuti popeza kuti anthu otsungula sangayende pakati pa nyenyezi, iwo angafunefunebe mitundu ina ya moyo kupyolera mwa njira zotchipa ndi zosavuta za mafunde a wailesi. Koma nthanthi ya Fermi ikuwavutitsabe.

Katswiri wa physics wa ku America, Freeman J. Dyson wamaliza kuti ngati anthu otsungula alipo m’khamu lathu la nyenyezi, kupeza umboni wawo kuyenera kukhala kosavuta mofanana ndi kupeza zizindikiro za luso la zopangapanga lotsungula pa Chisumbu cha Manhattan mu Mzinda wa New York. Khamu la nyenyezi liyenera kumalira ndi zizindikiro zachilendo ndi makonzedwe awo a uinjiniya wapamwamba. Koma palibe zimene zapezedwa. Kwenikwenidi, nkhani ina pa mutuwo inadziŵitsa kuti “kufufuza, osapeza chirichonse” kwakhala ngati nyimbo yachipembedzo ya akatswiri a zakuthambo a SETI.

Zikaikiro Ziyamba

Asayansi angapo ayamba kuzindikira kuti mabwenzi awo anapanga zolingalira zapatali zotsimikiza polingalira za funsoli. Asayansi oterowo amabwera ndi chiŵerengero chotsika kwambiri cha anthu otsungula m’khamu lathu la nyenyezi. Ena anena kuti pali amodzi okha—ife. Ena anena kuti mwamasamu, payenera kukhala ochepera pa mmodzi—nafenso sitiyenera kukhala pano!

Maziko a kusuliza kwawo ngosavuta kuwawona. Kungafupikitsidwe ndi mafunso aŵiri: Ngati zamoyo zakuthambo zoterozo ziripo, kodi zingakhale kuti? Ndipo kodi zinafikako motani?

‘Ndithudi, zingakhale pa mapulaneti ena,’ ena angayankhe motero funso loyambalo. Koma pali kokha pulaneti imodzi m’dongosolo lathu la dzuŵa limene silingakhale lankhalwe kwa moyo, pamene tiripa. Koma bwanji ponena za mapulaneti ozungulira zikwi za mamiliyoni a nyenyezi m’khamu lathu la nyenyezi? Kodi ena a amenewo angakhale ndi zamoyo? Nsonga njakuti kufikira tsopano asayansi sanatsimikizirebe mokhutiritsa kukhalapo kwa pulaneti ndi imodzi yomwe kunja kwa dongosolo lathu la dzuŵa. Kodi nchifukwa ninji sanatero?

Chifukwa chakuti kuzindikira imodzi n’kovuta kwambiri. Popeza kuti nyenyezi ziri kutali kwambiri ndipo mapulaneti samatulutsa kuwala mwa iwo okha, kupeza pulaneti yaikulu, monga ngati Jupiter, kuli kofanana ndi kuyesera kupeza kadontho ka fumbi kowuluka mozungulira golobo lamphamvu la pamtunda wa mamailosi ambiri.

Ngakhale ngati mapulaneti oterowo aliko—ndipo umboni wina wosakhala wachindunji wasonkhanitsidwa kusonyeza kuti alikodi—zimenezi sizitanthauzabe kuti iwo amazungulira mwachindunji nyenyezi yolondola m’khamu la nyenyezi lapafupi, pa mtunda wabwino wachindunji kuchokera ku nyenyeziyo, ndikuti iwo eni ali ndi ukulu wolondola mwachindunji ndi mkhalidwe kuti nkuchilikiza zamoyo.

Maziko Ogwedera

Komabe, ngati mapulaneti ambiri alipo amene amakwaniritsa zofunika zoyenerera zochilikiza moyo monga mmene timaudziŵira, funso lidakalipo, Kodi ndimotani mmene moyo ungayambire pa maiko amenewo? Zimenezi zimatibwezera ku maziko enieni a chikhulupiriro cha zamoyo pa maiko ena—chisinthiko.

Kwa asayansi ambiri, chimawoneka chanzeru kukhulupirira kuti ngati moyo ungachokere ku zinthu zopanda moyo pa pulaneti ino, zimenezo zingakhalenso zowona pa maiko ena. Monga mmene mlembi wina akunenera kuti: “Lingaliro lachisawawa pakati pa akatswiri a zamoyo ndilakuti moyo ungayambe ngati pali mikhalidwe imene ungayambike.” Koma pamenepo ndi pamene chisinthiko chimakumana ndi chitsutso chachikulu. Akatswiri a chisinthiko sangathe kulongosola nkomwe mmene moyo unayambira pa pulaneti lino.

Asayansi Fred Hoyle ndi Chandra Wickramasinghe akuyerekeza kuti ziyembekezo zolimbana ndi kupangika mwangozi kwa maenzyme ofunika koposa amoyo ziri chimodzi mwa 1040,000 (1 ndipo ma 0 otsatira kumbuyo kwake nkukhala 40,000). Asayansi Feinberg ndi Shapiro akupitirira apo. M’bukhu lawo lakuti Life Beyond Earth, akuika ziyerekezo zolimbana ndi kupangika kwa nsuzi wa zamoyo kukhala chamoyo pa chimodzi mwa 101,000,000. Tikanati tilembe nambala imeneyi, magazine amene muli nawowa akanakhala ochindikila masamba oposa 300!

Kodi mukupeza manambala ovutawa kukhala ovuta kuwamvetsetsa? Liwu lakuti “chosatheka” nlapafupi kulikumbukira, ndipo nlolongosoka.a

Komabe, akatswiri a zakuthambo a SETI mosangalala amalingalira kuti moyo uyenera kukhala unayambika mwangozi pa chilengedwe chonse. Gene Bylinsky, m’bukhu lake lakuti Life in Darwin’s Universe, akulingalira pa njira zosiyanasiyana zimene chisinthiko chingakhale chinachitika pa maiko achilendo. Iye akupereka lingaliro lakuti maoctopus aluntha, nyama zotchedwa marsupial zokhala ndi zikwama pamimba pawo, ndi anthu okhala ngati mleme amene amapanga zoimbira sali konse ongopeka. Asayansi otchuka atamanda bukhu lake. Komabe, asayansi ena, monga ngati Feinberg ndi Shapiro, amawona chophophonya chodzetsa mpata m’kulingalira koteroko. Iwo amachitira chisoni “kufooka m’maziko enieni a kuyesa” kwa nthanthi za asayansi zonena za mmene moyo unayambira pa dziko lapansi. Komabe, iwo amadziŵitsa kuti asayansi “agwiritsirabe ntchito maziko ameneŵa kuimika nsanja zimene zafikira kumalekezero a Chilengedwe chonse.”

Chipembedzo Cholakwa

‘Kodi nchifukwa ninji,’ inu mungazizwe, ‘asayansi ambiri chotero amawona zosatheka mosasamala?’ Yankho nlapafupi ndipo lomvetsa chisoni. Anthu amakhulupirira zimene amafuna kukhulupirira. Asayansi, mosasamala kanthu za kudzinenera kwawo kwa kukhala ndi chonulirapo, sali opatulidwa ku kulephera kwa anthu kumeneku.

Hoyle ndi Wickramasinghe analongosola kuti “nthanthi yakuti moyo unapangidwa ndi waluntha” iri “kwakukulukulu” yothekera kwambiri kuposa ndi kukhalako kwamwadzidzidzi. “Ndithudi,” iwo akuwonjezera kuti, “nthanthi yoteroyo njodziŵikiratu kotero kuti ena amadabwa kuti nchifukwa ninji siri yolandiridwa mofala kukhala yowonekeratu. Zifukwa zake nzamaganizo osati za sayansi.” Inde, asayansi ambiri amanyalanyaza lingaliro la Mlengi, ngakhale kuti umboni umasonya kumeneko. M’chochitikacho, iwo apanga chipembedzo chawochawo. Monga mmene akonzi apamwambawo akuwonera izo, chiphunzitso cha Darwin chimangoloŵa m’malo liwu lakuti “Mulungu” ndi liwu lakuti “Chilengedwe.”

Chotero poyankha funso lakuti, “Kodi kuli aliyense kunja kumeneko?” mowonekeratu sayansi sikupereka maziko akukhulupirira za moyo pa mapulaneti ena. Kwenikwenidi, pamene zaka zikupita ndipo bata lochokera ku nyenyezi likupitirizabe, SETI ndiyo chochititsa manyazi kwa asayansi amene amakhulupirira chisinthiko. Ngati mitundu yosiyanasiyana ya moyo inasinthika kuchokera ku zopanda moyo, pamenepo kodi nchifukwa ninji sitimamva za izo m’chilengedwe chonse chachikuluchi? Kodi iwo ali kuti?

Kumbali ina, ngati funsolo liri ku mbali ya chipembedzo, kodi tingapeze motani yankho? Kodi Mulungu analenga moyo pa maiko ena?

[Mawu a M’munsi]

a Nthanthi yonse ya chisinthiko njodzazidwa ndi mavuto. Chonde wonani bukhu lakuti Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Bokosi patsamba 8]

Kodi Ndi Alendo Ochokera Kutali?

Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akuchezeredwa, kapena anachezeredwa kalelo, ndi zamoyo zakuthambo. Asayansi mwachisawawa amakana malingaliro ameneŵa; iwo amasonya ku kusoŵeka kwa umboni wotsimikizirika m’zochitika zonse ndi kusungabe kuti zowoneka zambiri za UFO (unidentified flying object; chinthu chouluka chosazindikiridwa) zingalongosoledwe ndi nthanthi ya chilengedwe. Iwo amaleka kudzinenera kwa malo osafufuzidwa a maganizo ovutitsidwa a anthu kapena zosoŵa zamaganizo ndi chipembedzo.

Wolemba nkhani zopeka za sayansi wina anadziŵitsa kuti: “Chisonkhezero cha kufufuza ndi kukhulupirira zinthuzi nchachipembedzo. Tidali ndi milungu. Tsopano tikufuna kudzimva kuti sitiri tokha, oyang’aniridwa ndi mphamvu zochinjiriza.” Kuwonjezerapo, zokumana nazo zina za UFO zimasonyeza kuwombeza osati sayansi.

Koma asayansi ambiri amakhulupirira “alendo” m’njira yawoyawo. Iwo amawona kusatheka kwa kuyambika kwa moyo mwangozi pano pa dziko lapansi, chotero amanena kuti uyenera kukhala unafika pano kuchokera ku thambo. Ena amati alendo anaika mbewu ya moyo pa pulaneti lathu mwakutumiza maroketi odzaza ndi bacteria. Wina wafikira polingalira kuti alendo anachezera pulaneti lathu zaka zingapo zapitazo ndipo kuti moyo unachokera mwangozi ku zinyalala zimene anazisiya! Asayansi ena amamaliza kuchokera ku umboni wakuti mamolecule amoyo ngambiri m’thambo. Koma kodi umenewo ulidi umboni wa kupangika kwamoyo kwamwangozi? Kodi sitolo logulitsamo zitsulo liri umboni wakuti galimoto iyenera kudzipanga yokha mwangozi mmenemo?

[Chithunzi patsamba 7]

Ngakhale ngati kutakhala mapulaneti ena okhalika ndi anthu, kodi pali umboni uliwonse wakuti moyo ungachokere pa iwo mwangozi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena