Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 6/8 tsamba 14-16
  • Kodi Makolo Anga Adzandilola Liti Kudzikometsera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Makolo Anga Adzandilola Liti Kudzikometsera?
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukometsera—Chifukwa Chake Kuli Kofunika kwa Asungwana
  • Chifukwa Chimene Angakanire
  • Kuchita Mothekera Koposa ndi Mkhalidwewo
  • Kodi Zopakapaka Ndingazigwiritsire Ntchito Bwino Motani?
    Galamukani!—1990
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kudziphoda Komanso Kuvala Zodzikongoletsera?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • N’chifukwa Chiyani Atsikana Samandifuna?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Loyamba
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 6/8 tsamba 14-16

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Makolo Anga Adzandilola Liti Kudzikometsera?

Galamukani!: Kodi msungwana ayenera kukhala wa zaka zingati asanaloledwe kudzikometsera?

Juliea: Ndinganene kuti zaka 13 zakubadwa.

Galamukani!: Nchifukwa ninji?

Julie: Sindikudziŵa.

Galamukani!: Kodi zaka khumi ndi ziŵiri zachepa kwambiri?

Julie: Eee.

Galamukani!: Koma 13 nzokwanira?

Julie: Eee.

Sallie: Ndikuganiza kuti ngati msungwana amadziŵa kuzipaka bwino ndipo sadzipanga kuwoneka ngati woimba m’gulu la oimba a roko kapena chinachake, ayenera kuloledwa kudzikometsera.

John: Ndikuganiza kuti ayenera kudzikometsera kokha ngati sawoneka bwino popanda izo.

Gloria: Inde, zokometsera zimawonjezera mawonekedwe anu achibadwa.

Larry: Koma kodi nchifukwa ninji aliyense angafune ‘kuwonjezera mawonekedwe ake’ pa msinkhu wa 13? Ndikutanthauza kuti, safunikira kutero pa msinkhuwo! Ndikuganiza kuti asungwana ayenera kukhala pafupifupi 18 asanayambe kudzikometsera.

MU UNITED STATES, azaka zapakati pa 13 ndi 19 amathera madola oposa mamiliyoni zikwi zisanu pachaka pa zinthu zokometsera ndi zokongoletsera. Pamenepo, nzomveka kuti mungalingalire kuti nanunso muli ndi kuyenera kwa kudzipaka lipstick, blush, kapena eyeshadow ngati mungafune. Komabe, makolo anu angawone zinthu mosiyana kwambiri.

“Ndinawafunsa amayi anga ngati ndingayambe kudzikometsera pamene ndinali 13,” akukumbukira motero Nina wa zaka 17 zakubadwa. “Iwo ananena kuti, ‘Nina, sufunikira izo tsopano.’” Shelly wachichepere anakumana ndi chiyambukiro chofananacho kuchokera kwa makolo ake. “Ndinapempha chilolezo pamene ndinali pafupifupi 13, ndipo iwo anandiwuza kuti sindikanagwiritsira ntchito kufikira pamene ndikafika zaka 15. Ndinanena kuti, ‘Chifukwa ninji ayi?’”

Kukometsera—Chifukwa Chake Kuli Kofunika kwa Asungwana

Monga mmene kukambitsirana kotsegulira kukusonyezera, pali malingaliro osiyanasiyana pa nkhaniyi ngakhale pakati pa azaka zapakati pa 13 ndi 19. Pamenepa, nzosadabwitsa kuti inu ndi makolo anu mungakhale ndi vuto kumvana! Chikhalirechobe, kukanizidwa ndi makolo anu kungawoneke kukhala kusamalitsa kosalingalirika. “Mumayang’ana kwa asungwana kusukulu,” akukumbukira mkazi wachichepere wotchedwa Monica, “ndipo iwo onse adzikometsera.” Mumadabwanso kuti zingakhale bwanji BWINO kwa amayi anu, koma osakhala BWINO kwa inu! Kuwonjezerapo, mukukula, ndipo mawonekedwe anu amakhala ofunika kwa inu kuposa ndi kale lonse.

Unamwali wapangitsa masinthidwe mu msinkhu, kulemera, ndi mpangidwe wanu. Monga mmene bukhu lakuti The Secret of a Good Life With Your Teenager likulongosolera, “masinthidwe ameneŵa amasiya [achichepere] akudera nkhaŵa ponena za kukongola kwawo kuposa ndi kale lonse . . . Amaderanso nkhaŵa ndi kukhala ndi chitsimikizo cha munthu amene ali kaya wamkazi kapena wamwamuna. Iwo amafuna kupezedwa kukhala akazikazi kapena amunamuna.” Kapena monga mmene mlembi wina akuziikira, mumafuna “kuyamba kuumba sitayelo imene idzakhala yanu . . . [imene] imalongosola inu amene mumamkonda koposa ndipo amene mumamzoloŵera.”—Changing Bodies, Changing Lives, lolembedwa ndi Ruth Bell.

Kwa asungwana ambiri, kudzikometsera kuli njira imodzi yokhazikitsira sitayelo yaumwini imeneyo ndi kudzimva kukhala mkazikazi kapena wokongola. “Pamene ndadzikometsera, ndimadzimva kukhala wachidaliro moposapo,” analongosola motero msungwana wina wa zaka zapakati pa 13 ndi 19. Nina, wogwidwa mawu poyambapo, akuwonjezera kuti: “Pali asungwana ambiri okongola, ndipo kudzikometsera kumandipanga kudzimva bwino.”

Kudzikometsera kuli ngati mwambo wopitira ku uchikulire. Monga mmene wa zaka zapakati pa 13 ndi 19 wina akulongosolera kuti: “Sumafunanso kulingaliridwa kukhala mwana.” Ena amalingalira kuti kawonekedwe kauchikulire kangawapezere ulemu wokulira—kapena ngakhale kukopa anyamata achikulireko. Kwa ena, kudzikometsera kuli kokha njira yofananira ndi mabwenzi awo. Diane akunena kuti: “Ngati uwoneka wokulirako, ana enawo amalingalira kuti ndiwe wofatsa.”

Koma achichepere ambiri amafuna kudzikometsera chifukwa cha zifukwa zothandiza: kulinganiza mtundu wa khungu wosiyana, kubisa kawonekedwe kakhungu koipa kapena chipsyera, kugogomezera mbali zokongola za nkhope, kapena kuchepetsa mbali zosawoneka bwino. Ngakhale kuli tero, pempho la chilolezo cha kudzikometsera lingadzutse mkangano wa m’banja. Kodi nchifukwa ninji makolo kaŵirikaŵiri amavomereza mu mkhalidwe woipa woterowo?

Chifukwa Chimene Angakanire

Nzowona kuti nthaŵi zina makolo amachipeza kukhala chovuta kumvetsetsa kuti ana awo akukula. Chotero ena angakhoterere pa kukhala okhwima pang’ono. Mosasamala kanthu za izo, makolo ambiri amangofunira ana awo zabwino koposa. Chimenecho ndicho chifukwa chake Baibulo limachenjeza kuti: “Ananu, mverani mwambo wa atate, nimutchere makutu mukadziwe luntha.” (Miyambo 4:1) Makolo anu sangakhale okhoza kuika malingaliro awo m’mawu. (“Makolo anga sanandilole kupaka mascara,” akukumbukira motero msungwana wina wa zaka zapakati pa 13 ndi 19, “koma sanandiuze chifukwa chake.”) Mwachidziŵikire iwo ali ndi zifukwa zabwino zosamverera bwino ponena za nkhaniyo.

Mungamalingalire kuti kudzikometsera kuli mtundu wina wa choyenera, chinachake chimene chingalekeredwe kwa inu pamene mwafika “msinkhu wamatsenga,” monga 13. Koma monga mmene wolemba nkhani m’danga la nyuzipepala Elizabeth Winship akusonyera: “Palibe lamulo lonena za msinkhu weniweni pa umene kudzikometsera kuli kololedwa. Zimadalira pa miyambo ya banja ndi mudzi.” Makolo anu angaganize kuti kudzikometsera pa msinkhu wanu kunganyazitsidwe m’mudzi kapena ndi Akristu anzanu. Makolo anu adzakhala odera nkhaŵa kwenikweni ndi zimenezi ngati iwo ali Mboni za Yehova, popeza sangafune kuti kawonekedwe kanu kacheutse uminisitala wanu Wachikristu.—2 Akorinto 6:3.

Makolo anu angaganize kuti kudzikometsera pa nthaŵi ino kungakhale kopanda pake ndiponso kosayenerera. Ndiiko komwe, uchichepere uli ndi kukongola kwake, ulemerero umene ulidi wosakhalitsa. (Salmo 90:10; Miyambo 20:29) Iwo angalingalire kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji ayenera kuchita chinachake chimene chingabise kapena kusintha mawonekedwe ake auchichepere?’

Makolo anu angadziwenso kuchokera ku chokumana nacho chaumwini mmene “zilakolako za unyamata” zingakhalire zosokeretsa. (2 Timoteo 2:22) Iwo angamaope kuti mungabwereze zina za zophophonya zimene anazichita pamene anali achichepere, ndipo iwo akufuna kukuchinjirizani. Msungwana wina wa zaka zapakati pa 13 ndi 19 akukumbukira kuti: “Amayi anayamba kudzikometsera pamene anali aang’ono kwambiri. Iwo adali oloŵerera ndipo ankavala masiketi aafupi ndi kudzikometsera mopambanitsa. Iwo sanafune kuti nanenso ndikhale tero.”

Sizikutanthauza kuti mudzakhala mkazi wachiŵereŵere ngati mwadzipaka lipstick. Komabe, iwo angawope moyenerera kuti kudzikometsera kungakuunikireni ku zididikizo zimene simunazikonzekere. Tate wa asungwana aŵiri azaka zapakati pa 13 ndi 19 akugwidwa mawu ndi mlembi Ruth Bell kukhala akunena kuti: “Nzosangalatsa kuwona ana akukula kukhala achikulire. . . . Koma pamene ndiyang’ana iwo ndi kuwona asungwana anga achichepere, pamene ndinena kwa inemwini kuti, ‘Awo ndi ana anga ndipo akukhala achikulire ndipo adzafunikira kuchita ndi dziko kunjako popanda ine kuti ndiwachinjirize,’ pamenepo m’pamene ndimavutika maganizo. . . . Dzikoli nlovuta ndipo angavulazike.”

Kuwoneka wachikulire kuli chinthu china. Koma kuchita monga wachikulire ndi kuchita ndi zididikizo za achikulire kungakhale chinthu chinanso. Kodi ndinudi wokonzekera kuchita ndi chisamaliro chochokera kwa anyamata achikulireko azaka zapakati pa 13 ndi 19—kapena ngakhale amuna achikulire—amene angakopeke ngati kudzikometsera kukupangitsani kuwoneka wamkulu kuposa mmene muliri?—Yerekezerani ndi Genesis 34:1, 2.

Kuchita Mothekera Koposa ndi Mkhalidwewo

Pokhala mutalingalira zinthu zonse, mungaganizebe kuti ndinu wokonzekera kudzikometsera, ndipo mwinamwake ndinudi. Kodi muyenera kuchita chiyani? Msungwana wina wa zaka zapakati pa 13 ndi 19 anaulula kuti: “Ndinangoyamba kudzikometsera. Ndidaika eyeshadow yochepa, ndipo Amayi anaganiza kuti inawoneka bwino.” Komabe, kuyamba kudzikometsera popanda chilolezo kuli kwangozi! Miyambo 13:10 ikuchenjeza kuti: “Kudzikuza kupikisanitsa.” Monga mmene msungwana wina anavomerezera kuti: “Ndinadziŵa kuti makolo anga akaipidwa ngati ndikanangotulukira mwadzidzidzi nditadzikometsera.” Chotero, kodi nchiyani chimene mungachite? Vesi la Baibulo limenelo likupitiriza kuti: “Koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.”

Inde, sankhani ‘nthawi yake’ yokambitsirana ndi makolo anu. (Miyambo 25:11) Modekha longosolani malingaliro anu m’zimenezi. Longosolani chifukwa chimene ichicho chiri chofunika kwa inu, ndipo ndandalitsani zimene muli nazo m’maganizo. Atsimikizireni kuti simukufuna kuwoneka wamakono kapena wosalingalira m’mawonekedwe anu ndipo kuti mumawona malingaliro awo ndi chiweruzo kukhala zofunika. Mwinamwake angasinthe maganizo awo kapena kuvomerako zochepa.

Kumbali ina, iwo moyenera angatsimikizire kuti simuli wokonzekera kaamba ka kudzikometsera. Koma kumeneku sindiko kutha kwa dziko. Chitani zimene mungathe kuchita ndi mawonekedwe anu pansi pa mikhalidweyo. Mwachitsanzo, kusamalira khungu kwabwino kungachepetse mavuto a kawonekedwe kakhungu. “Ngati khungu lanu lawonongeka,” akulangiza motero katswiri wa kukongola Jane Parks-McKay, “chotsani chisamaliro ku ilo . . . mwakuvala chinachake chimene chimakupangani kuwoneka wokongola—chirichonse chimene chingachotse chisamaliro ku mbali yoipayo.” Mkhalidwe wathupi wabwino, zikadabo zoyengedwa bwino, tsitsi laudongo, lobiriŵira—zinthu zonsezi zingakuthandizeni kuwoneka bwino mutadzola kapena musanadzole zokometsera!

Komabe, kodi bwanji ngati makolo anu akuvomerezani kudzola zokometsera? Nkhani ya mtsogolo idzalongosola kuzigwiritsira ntchito kwake koyenera.

[Mawu a M’munsi]

a Maina enawo asinthidwa.

[Chithunzi patsamba 16]

“Iye wadzikometsera. Kodi ine ndingayambe liti?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena