Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g90 9/8 tsamba 28-31
  • “Iwo Anandiuza Kuti Sindidzayendanso!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Iwo Anandiuza Kuti Sindidzayendanso!”
  • Galamukani!—1990
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chiyambukiro Choyamba
  • Kufunika kwa Kuyang’anizana ndi Chitokosocho
  • Kuchita ndi Zovuta
  • Kodi Nchiyani Chingachitidwe?
  • Zothandiza Ziripo
  • Chiritso Lenileni
  • Kulimbana ndi Mavuto mwa Kukhala N’zolinga
    Galamukani!—2001
  • Kodi Ndingalake Motani Kupunduka Kwanga?
    Galamukani!—1993
  • Kodi Ndinalakwa Chiyani Kuti Ndidwale Chonchi?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Olumala Komabe Obala Zipatso
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1990
g90 9/8 tsamba 28-31

“Iwo Anandiuza Kuti Sindidzayendanso!”

PAMSINKHU wa zaka 20, Ed anali m’ngozi yapagalimoto yowopsya kwambiri. Pamene anatsitsimuka, analephera kudzuka. Iye anazindikira kuti anafa ziŵalo koma anaganiza kuti zikakhala za kanthaŵi kochepa. Ed anakumbukira zimene zinachitika m’chipatala pambuyo pake: “Iwo anandiuza kuti sindidzayendanso!” Iye anafa ziŵalo kuyambira m’chifuwa kutsika m’munsi.

“Ndinakwiyitsidwa pamene mwana wanga anavulala,” anakumbukira motero atate ake a Ed. “Iye anali mwamuna wachichepere wojintcha, koma tsopano sadzayendanso. Ichi chinalemazika moyo wake akali mwana.” Ed anali kulondola utumiki wa nthaŵi zonse, wotchedwa ndi Mboni za Yehova kukhala upainiya.

Mwamuna wina wachichepere wa m’zaka zake za m’ma 20, Bill, mwamaseŵera analumphira pa mathithithi ndi kumenyetsa mutu wake pa mchenga. Panthaŵi yomweyo, iye analephera kuyenda kapena kupuma. Tiyamikira mabwenzi amene anali pafupi, Bill sanamire. Komabe, iye anafa ziŵalo kuyambira pakhosi kutsika m’munsi. Adokotala anamuuza Bill kuti sadzayendanso.

Chiyambukiro Choyamba

Bill anaulula kuti: “Ndinafuna kudzipha, koma sindikanatero pa kama wa m’chipatala.” Bill anatumikirako mu Nkhondo ya Vietnam ndipo ankakonzekera kukhala woulutsa ndege. Pamene anavulala mu 1969, maloto ake onse anathetsedwa, ndipo sanawone chifukwa chokhalira ndi moyo.

Chiyambukiro choyamba cha Ed chinali chosiyana pamene anauzidwa kuti adzakhala ndi ziŵalo zakufa kwa moyo wonse. “Sindinakhumudwitsidwe, ndipo chinali chifukwa cha chikhulupiriro changa m’malonjezo a Mulungu opezeka m’Baibulo. Ndinazindikira kuti mkhalidwe wanga ungakhale wa moyo wonse tsopano koma sudzakhala wa moyo wonse kosatha.” Chifukwa cha chiyembekezo chimene anali nacho, Ed wakhala wokhoza kuchita mwachipambano ndi kupunduka kwake kwa zaka zoposa 25 tsopano.

Kufunika kwa Kuyang’anizana ndi Chitokosocho

Kumbali ina, Bill sanadziŵe za malonjezo a Mulungu. Komabe, tsiku lina kunachitika chinachake chimene chinamfulumiza kuchita chinachake ponena za iyemwini.

Pambuyo pokhala m’chipatala kwa miyezi isanu ndi itatu yokha, Bill anaikidwa pa mpando wa magudumu kupita ku bafa kukametedwa ndevu ndi namwino wamwamuna. “Pamene ndinayang’ana pa kalirole,” iye anati, “ndinawona munthu amene sanali ineyo!”

Bill adali mwamuna wamphamvu wolemera makilogalamu 90, wa msinkhu wa masentimita 185, koma tsopano anali mafupa okhaokha olemera makilogalamu 40 okha. Iye anakana kukhulupirira kuti chithunzi cha munthu amene anawona pa kalirole chinali chake. Chokumana nachocho chinamfulumiza kukhala ndi mzimu wolimbana ndi kuvomereza kupunduka kwake. Bill akuti: “Chaka choyamba cha kupunduka kwa munthuwe ndi nthaŵi yowawitsa popeza kuti ndiyo nthaŵi imene mukusankha njira imene mudzamukamo.”

Kuchita ndi Zovuta

Ed simunthu wa manjenje, koma akuvomereza kukhumudwitsidwa kwake. “Nthaŵi zina sinditha kuchita zinthu zopepuka monga kunyanyamphira chinachake,” akulongosola motero Ed, “ndipo ndingachite tondovi.”

Bill amapeza vuto lalikulu kwambiri kukhala ndi thupi limene liri ndi polekezera ndi ubongo wopanda ntchito. “Chiri chofanana ndi maganizo otsogozedwa ndi chinachake m’thupi longoveka,” iye akutero.

Palinso zovuta zakuthupi zimene zimagwirizana ndi kuvulala kwa mafupa a pansana, monga ngati kulephera kulamulira chikodzedzo ndi chimbudzi, zironda zopangitsidwa ndi kugonetsa, ndi mavuto popuma. Ed wakhala ndi matenda a imso chiyambire kuvulala kwake ndipo amakhala ndi nyengo za masiku asanu ndi limodzi mpaka asanu ndi aŵiri nthaŵi zina pamene kutentha kwa thupi lake kumakwera kufika pa 40° Celsius. Kukhala wosakhoza kulamulira chikodzedzo ndi chimbudzi m’kokwiyitsanso kwambiri kwa Bill. Monga mmene akunenera: “Sumatha konse kuzoloŵera kukhala ndi thupi la khanda.”

Ed akulimbikitsa anthu opunduka onse kukhala odzidalira koposa monga momwe angathere. Iye akuti: “Yesetsani kudzichitira zinthu, ndipo mudzafika patali.” Chimenecho ndicho chifukwa chake pamene ankachoka m’chipatala, chinthu choyamba chimene anachita chinali kuika m’galimoto lake zowongolera zamanja kotero kuti angathe kuyendetsa. Tsopano Ed amagwiritsira ntchito mwachipambano galimoto lalikulu lokhala ndi ziwiya zapadera m’ntchito yake yosesa m’maofesi.

“Yesani kuiwala kupunduka kwanu,” akulangiza motero Bill, “ndipo chitani zonse zimene mungathe ndi moyo wanu. Ngati simuchita monga munthu wopunduka, anthu sadzakuchitirani monga wopunduka.” Bill amachita zimene amanena. Iye mwachipambano wakhala ndi bizinesi ndi kugwiriramo ntchito, akumayendayenda ndi ngolo yake, pampando wamagudumu, ndi ndodo zoyendera.

Kodi Nchiyani Chingachitidwe?

Chotsekereza chimodzi kwa munthu wopunduka chinganenedwe kukhala m’maganizo mwa anthu osapunduka. Njira yabwino koposa yochotsera chotsekerezachi ndiyo kumvetsetsa. Anthu opunduka amafuna kulingaliridwa ndi kumvetsetsedwa kofanana ndi komwe kungasonyezedwe kwa munthu wosapunduka thupi.

Anthu ena amawoneka amantha ndi osamasuka pamene ayang’anizana ndi munthu wopunduka. Bill akuti: “Kunena zowona tonsefe ndife opunduka mwanjira ina. Ena amangokhala opunduka kwenikweni kuposa ena.” Awo amene ngopunduka ali kokha anthu amene zinangochitika mwachitsanzo, kuti satha kuyenda, kuwona, kapena kumva monga mmene amachitira anthu ena. Nkofunika kuti tidziwona kupunduka kulikonse kukhala kwa pamkhalidwe ndi kuwona munthuyo kuti ngwathunthu.

“Ndimayamikira pamene anthu andiwona monga momwe amawonera wina aliyense,” anatero Ed. “Mudzindiyang’ana ineyo. Osayang’ana mpando.” Kenaka anasimba chokumana nacho ichi chimene iye ndi mkazi wake anakumana nacho ku resitilanti: “Woperekera zakudya anatenga oda ya mkazi wanga choyamba ndipo kenaka anamfunsa iye, m’malo mwa ine, kuti amuuze chimene ndinafuna. Sindine wogontha! Sindingathe kuyenda basi.”

“Anthu ambiri amafuna kusonyeza chifundo kwa opunduka,” akulongosola motero Ed, “koma samadziŵa zimene angachite.” Uphungu wake ngwakuti: “Chinthu chabwino koposa ndicho kudikira kuti mupeze chimene mungachite musanayambe kuchita chinachake.”

Chotero tsimikizani kufunsa choyamba kuti, “Kodi ndingathandize?” Kapena, “Kodi pali chirichonse chimene ndingachite kuti ndithandize?” Musangolingalira kuti munthu wopunduka akufuna thandizo lanu; iye sangalifune.

“Chiyamikiro chachikulu kwenikweni kwa munthu wopunduka,” akulangiza motero Bill, “chiri kumchitira mwachibadwa, kulankhula naye monga mmene mungachitire ndi wina aliyense.” Zowona, ena angapeze ichi kukhala chovuta kuchichita. Pangakhale chotsekereza chaumwini chamaganizo kapena malingaliro pakati pa iwo ndi anthu opunduka. Komabe, pamene tizoloŵerana kwambiri ndi anthu ameneŵa monga munthu payekha, tidzalingalira zochepa ponena za kupunduka kwawo.

Ed, yemwe wakhala ndi mpingo umodzimodziwo wa Mboni za Yehova kwa zaka zambiri, akulongosola motere: “Mabwenzi ambiri samandilingalira kukhala wopunduka. Kunena zowona, m’ntchito yathu yolalikira poyera, iwo amanditumiza pa ulendo wobwereza ku nyumba yokhala ndi zipinda khumi zosanja! Ndiyeno ndimabwerera ndi kuwauza kuti atumize winawake.”

Kodi Ed amakwiya pamene mabwenzi ake aiwala za polekezera pake mwakuthupi? Kutalitali. Iye akusimba kuti: “Nchosangalatsa kuti iwo amaganiza kuti sindifunikira thandizo lirilonse. Ndimachiyamikira chimenechi, popeza kuti ndimadzimva kuti kwa iwo sindine wopunduka, koma munthu wina wabwinobwino.”

Zothandiza Ziripo

M’zaka zaposachedwapa kupita patsogolo kwakukulu kwapangidwa m’maiko ambiri m’kupereka thandizo kwa opunduka mwakuthupi. Magulu ambiri, zopangidwa, ndi mautumiki alipo owathandiza kusangalala ndi kakhalidwe kodziimira pawokha. M’malo ambiri, zonse zimene munthu amafunikira ndizo kuyang’ana m’bukhu la manambala a lamya kaamba ka chidziŵitso chonena za magulu ndi mautumiki ameneŵa.

Nyumba zambiri zaunyinji ndi zipinda tsopano zikukonzedwa ndi anthu opunduka m’maganizo. Makampani ena a ndege ndi magulu a aulendo amapereka maulendo apadera kwa anthu opunduka. Ndipo lerolino anthu opunduka miyendo yonse ndi mikono angasangalale ndi kudziyendera m’magalimoto ndi magalimoto aakulu okhala ndi ziwiya zapadera.

Luso lamakono la zopangapanga, limene m’zochitika zina lapangitsa kukhala kotheka kupitirira mitsempha yowonongeka, latheketsa anthu ena akufa ziŵalo kuyendanso. Komabe, Dr. J. Petrofsky, wofufuza wotsogolera m’munda, akuvomereza kuti anthu ena angakhale ndi ziyembekezo zonyenga ponena za luso la zopangapanga loterolo. Iwo angafikire pa kukhulupirira kuti lingatheketse aliyense wakufa ziŵalo kuyendanso. Dr. Petrofsky akuti: “Zonse zomwe mungachite ndizo kukhala wowona mtima, ndi kuyesera kuwauza zenizeni ponena za kufufuza koteroko. Mudziŵa, sitikuchiritsa chirichonse.”

Chiritso Lenileni

Komabe, chiritso lenileni ndi losatha la kupunduka konse kwakuthupi lidzakhalapo m’kupita kwa nthaŵi. Chiyembekezo chotsimikizirika chimenechi chokhala wokhozanso kuyenda chachilikiza Ed ndipo chamuthandiza kuchita ndi kupunduka kwake kwa zaka zonsezi. Lonjezo la Baibulo nlakuti: ‘Maso a akhungu adzatsegudwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba; pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.’—Yesaya 35:5, 6.

Kuchiritsa kwa zovuta zonse kudzazindikiridwa pompano pa dziko lapansi pamene Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo ulamuliro wonse wa maboma a anthu. (Danieli 2:44) Ndithudi, Ufumu wa Mulungu, umene Kristu anaphunzitsa atsatiri ake kuupempherera, udzabweretsa dziko latsopano m’limene lonjezo la Baibulo ili lidzakwaniritsidwa: “Wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24; Mateyu 6:9, 10.

Pa nthaŵi ya ngozi yake, Bill sankadziŵa tanthauzo la malonjezo a Baibulo ameneŵa, ngakhale kuti nthaŵi zonse ankalemekeza kwenikweni Baibulo. M’zaka zisanu zoyambirira za kupunduka kwake, iye anayamba kugwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa. “Ndinkagwiritsira ntchito mankhwala ogodomalitsa mu Vietnam kuti ndithawe zowopsya,” iye akutero, “ndipo pambuyo pake ndinawagwiritsira ntchito kuti ndipirire ndi moyo mu mpando wamagudumu.”

Komabe, mu 1974, ndi thandizo la Mboni za Yehova, Bill anafikira pa kukhulupirira kuti Baibulo liridi lowona ndikuti malonjezo ake ngodalirika kwenikweni. “Kuyambira pa nthaŵi imeneyo kumka mtsogolo,” iye anatero, “mamba, kunena kwake titero, anachoka m’maso mwanga!” Miyezi isanu ndi iŵiri pambuyo pake Bill anapereka moyo wake kwa Yehova Mulungu, ndipo posakhalitsa iye ndi mkazi wake anayambira pamodzi moyo muuminisitala wanthaŵi zonse monga apainiya.

Polingalira za zokumana nazo zake zapita, Bill akuvomereza kuti ngozi yake ndi kupunduka kotsatirapo zinali zopweteka. “Koma,” iye akugogomezera, “ndapindula zambiri ndi kuvulala kumeneko.” Kodi iye anganenerenji tero?

“Ndikukaikira ngati ndikanakhala Mkristu weniweni lerolino pakadapanda kupundukaku,” iye akufotokoza tero. “Kalelo, ndidali wonyada kwambiri, wodzitukumula, ndipo mwinamwake sindikanakhala pamalo amodzi kwa utali wokwanira kwakuti nkulandira uthenga Wachikristu.”

Chotero tsopano, mofanana ndi Ed, Bill ali ndi chikhulupiriro cholimba m’dziko latsopano la Mulungu, iye adzakhalanso wokhoza kugwiritsira ntchito mokwana thupi lake. Ndipo mosasamala kanthu za mkhalidwe wowoneka wopanda chiyembekezo, munthu aliyense wopunduka angakhale ndi chidaliro chimodzimodzicho m’mphamvu yochiritsa ya Mulungu. Mtima wa munthu woteroyo ungalimbitsidwe tsiku ndi tsiku ndi chitsimikizo ichi: “Ndidziŵa kuti ndidzayendanso!”—Yothandiziridwa.

[Chithunzi patsamba 30]

Mosasamala kanthu za kupunduka kwake, Ed amakhalamo ndi phande lokwanira muuminisitala Wachikristu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena