Kugulitsa Mwazi Kuli Bizinesi Yaikulu
GOLIDE WOFIIRA! Monga momwe dzinalo likusonyezera, ichi nchinthu chimodzi chowonedwa kukhala chamtengo wapatali. Ali madzi amtengo wake, chuma chachilengedwe chofunika koposa chimene chayerekezedwa osati ku golide yokha komanso ku mafuta ndi malasha. Komabe, golide wofiirayu samakumbidwa m’mitsempha yokhala m’matanthwe ndi zokumbira ndi zophwanyira miyala. Amakumbidwa m’mitsempha ya anthu koma mwamachenjera kwambiri.
“Chonde, msungwana wanga wachichepere akufunikira mwazi,” chimachonderera motero chikwangwani chomwe chiri pamwamba m’msewu woyendamo anthu ambiri mu Mzinda wa New York. Zikwangwani zina zosatsira malonda zimasonkhezera motere: “Ngati ndinu wosonkha mwazi, ndinu munthu amene dzikoli silingathe kukhalapo popanda inu.” “Mwazi wanu ngwamtengo wake. Perekani thandizo.”
Mwachiwonekere anthu amene amafuna kuthandiza ena amaumva uthengawo. Iwo amandandama m’magulu aakulu, padziko lonse. Mosakaikira ambiri a iwo, limodzinso ndi anthu osonkhanitsa mwaziwo ndi outhirawo, mowona mtima amafuna kuthandiza anthu okanthidwa ndipo amakhulupirira kuti akuterodi.
Koma mwaziwo utasonkhedwa ndipo usanathiridwe, umadutsa mwa anthu ambiri ndi madongosolo ambiri kuposa mmene timazindikira ambirife. Mofanana ndi golide, mwazi umayambitsa umbombo. Ungagulitsidwe ndikupeza phindu ndipo kenaka nkugulitsidwanso ndikupeza phindu lalikulu. Anthu ena amamenyera kuyenera kwalamulo kwakusonkhanitsa mwazi, iwo amaugulitsa pamtengo waukulu, amapanga nawo mapindu aakulu, ndipo amafikira pakuuzembetsa kuchoka kudziko lina kunka ku linanso. Padziko lonse, kugulitsa mwazi kuli bizinesi yaikulu.
Mu United States, osonkha mwazi ankalipiridwa pomwepo kaamba ka mwazi wawo. Koma mu 1971 mkonzi wa ku Briteni wotchedwa Richard Titmuss anatsutsa naati mwakuwakopa osauka ndi odwala kusonkha mwazi wawo chifukwa cha madola oŵerengeka, dongosolo la ku Amerekalo linali lopanda chisungiko. Iye anatsutsanso kuti sanali makhalidwe abwino kuti anthu adzipeza phindu chifukwa chopereka mwazi wawo kuti athandize ena. Kuukira kwake kunapangitsa kuthetsedwa kwa kulipiridwa kwa osonkha mwazi wathunthu mu United States (ngakhale kuti dongosololo lidakatchukabe m’maiko ena). Komabe, chimenecho sichinachepetse phindu la msika wa mwazi. Chifukwa ninji?
Mmene Mwazi Unakhalirabe Wodzetsa Phindu
M’ma 1940, asayansi anayamba kupatula mwazi m’zigawo zake. Dongosolo limeneli, tsopano lodziŵika kukhala fractionation, limapangitsa mwazi kukhala bizinesi yotchuka zedi. Motani? Eya, talingalirani izi: Itapasulidwa ndipo mbali zake nkugulitsidwa, galimoto yakale ingakhale ndimtengo wowirikiza kasanu kuposa uja wa pamene ili yathunthu. Mofananamo, mwazi umakhala ndimtengo waukulu ngati wagawidwagawidwa ndipo mbali zakezo zigulitsidwa paderapadera.
Plasma, imene imapanga pafupifupi theka la unyinji wonse wa mwazi, ndimbali yamwazi yopatsa phindu lalikulu. Popeza kuti plasma iribe mbali iriyonse yamaselo ya mbali za mwazi—maselo ofiira, maselo oyera, ndi magwero oumitsa mwazi utakha (maplatelet)—ingaumikidwe ndi kusungidwa. Kuwonjezerapo, wosonkhayo amaloledwa kupereka mwazi nthaŵi zisanu zokha pachaka, koma iye angapereke plasma kaŵiri pamlungu mwakuchotsa plasma yokhayokha. M’dongosolo limeneli, mwazi wathunthu umachotsedwa, kupatulamo plasma, ndiyeno mbali zokhala ndi maselo zimabwezeretsedwanso mwa wosonkhayo.
United States imavomerezabe osonkha mwazi kulipiridwa kaamba ka plasma yawo. Kuwonjezera apa, dziko limenelo limalolabe osonkha mwazi kupereka pafupifupi plasma yochuluka kuwirikiza nthaŵi zinayi pachaka kuposa imene World Health Organization imavomereza! Pamenepo, nzosadabwitsa kuti United States imasonkhanitsa plasma yoposa 60 peresenti ya dziko lonse. Plasma yonseyo payokha njokwanira pafupifupi mamiliyoni $450, koma imatulutsa ndalama zambiri pamsika chifukwa chakuti plasma nayonso ingatulutsidwemo misanganizo yake yosiyanasiyana. Padziko lonse, plasma ndiyo maziko a indasitale yopeza $2,000,000,000 pachaka!
Mogwirizana ndi nyuzipepala ya Mainichi Shimbun, Japan imagwiritsira ntchito pafupifupi mbali imodzi mwa zitatu ya plasma yapadziko lonse. Dziko limenelo limaitanitsa 96 peresenti ya mbali ya mwazi imeneyi, yambiri yochokera ku United States. Osuliza okhala m’Japan alitcha dzikolo kukhala “mfiti ya dziko lonse,” ndipo Undana wa Zaumoyo ndi Kakhalidwe ka Anthu m’Japan wayesayesa kuthetsa malondawo, umati nchinthu chosalingalirika kupeza phindu m’mwazi. Kwenikweni, Undunawu ukunena kuti ziungwe zamankhwala m’Japan zimapanga mapindu a $200,000,000 chaka chirichonse kuchokera ku mbali imodzi yokha ya plasma, yotchedwa albumin.
Fedulo Ripabliki ya Jeremani imagwiritsira ntchito mwazi wochuluka kuposa Yuropu yonse, wochulukanso pa munthu mmodzi kuposa dziko lina lirilonse padziko lonse. Bukhu lakuti Zum Beispiel Blut (Mwachitsanzo, Mwazi) likunena motere ponena za zinthu zochokera m’mwazi: “Zoposa theka zimaitanitsidwa, makamaka kuchokera ku U.S.A., komanso kuchokera ku Maiko Otukuka Kumene. Mulimonse mmene ziriri n’kuchokera kwa osauka, amene amafuna kuwongolera malipiro awo mwakusonkha plasma.” Anthu ena osauka ameneŵa amagulitsa mwazi wawo wambiri kwakuti amamwalira chifukwa cha kupereŵera kwa mwazi.
Malo amalonda ambiri a plasma aikidwira mwadala m’madera okhala anthu olandira malipiro ochepa kapena m’mphepete mwa malire a maiko osauka. Iwo amakopa amphaŵi ndi malova, amene amakhala ofunitsitsa kusinthanitsa plasma ndi ndalama ndipo ali ndi chifukwa chokwanira choperekera yochuluka koposa kapena kubisa matenda amene angakhale nawo. Kugulitsa plasma koteroko kwawonjezereka m’maiko 25 kuzungulira dziko lonse. Mwamsanga kutaletsedwa m’dziko lina, kumabuka m’linanso. Kupatsa chiphuphu nduna limodzi ndi kuzembetsa siziri zachilendo.
Phindu M’malo Osayenera Phindu
Koma nkhokwe zosungira mwazi zosapanga phindu zasulizidwanso moipa posachedwapa. Mu 1986 mtola nkhani wotchedwa Andrea Rock ananena m’magazini ya Money kuti yuniti imodzi ya mwazi imatengera nkhokwe zosungira mwazi $57.50 kuti asonkhanitse kuchokera kwa opereka mwazi, chimatengera zipatala $88.00 kuti ziugule kuchokera ku nkhokwe zosungira mwazi, ndikuti zimatengera odwala kuchokera pa $375 mpaka $600 kuti aulandire mwakuthiridwa mwazi.
Kodi mkhalidwewo wasintha chiyambire nthaŵiyo? Mu September 1989 mtola nkhani wotchedwa Gilbert M. Gaul wa pepala la The Philadelphia Inquirer analemba nkhani zingapo m’nyuzipepala zokhudza dongosolo losungira mwazi la U.S.a Pambuyo pa kufufuza kwa chaka chathunthu, iye anasimba kuti nkhokwe zina zosungira mwazi zinkapempha anthu kupereka mwazi ndiyeno pambuyo pake ankagulitsa mwaziwo ku zigawo zina zosungira mwazi, pa phindu lalikulu kwabasi. Gaul anayerekezera kuti nkhokwe zosungira mwazi zimagulitsa pafupifupi malita theka la miliyoni a mwazi chaka chirichonse mwanjirayi, pamsika wachinsinsi wa $50,000,000 pachaka umene umagwira ntchito mofanana ndi msika wogulitsirapo chuma.
Komabe, kusiyana kwakukulu ndi uku: Kusinthanitsana mwazi kumeneku sikumayang’aniridwa ndi boma. Palibe munthu angathe kudziŵa mlingo weniweni wa iko, osatchula za kutsogoza mitengo yake. Ndipo osonkha mwazi ambiri sadziŵa kanthu za ichi. “Anthu akunyengezedwa,” yemwe kale adali wamnkhokwe yosungira mwazi anauza motero The Philadelphia Inquirer. “Palibe amene akuwauza kuti mwazi wawo ukubwera kwa ife. Iwo angakwiye akanadziŵa zimenezo.” Nduna ya Red Cross inanena mosabisa mawu motere: “Osunga mwazi anyengeza anthu a ku Amereka kwa zaka zambiri.”
Mu United States mokha, nkhokwe zosungira mwazi zimasonkhanitsa malita 6.5 miliyoni a mwazi chaka chirichonse, ndipo amagulitsa mayuniti oposa 30 miliyoni a zinthu zopangidwa ndi mwazi kwa pafupifupi madola mamiliyoni chikwi chimodzi. Uwu ndiunyinji waukulu wa ndalama. Nkhokwe zosungira mwazi sizigwiritsira ntchito liwu lakuti “phindu.” Iwo amakonda mawu akuti “ndalama zotsala pa zomwe zinawonongedwa.” Mwachitsanzo, Red Cross inapanga “ndalama zotsala pa zomwe zinawonongedwa” zokwanira $300 miliyoni kuchokera mu 1980 mpaka 1987.
Amnkhokwe zosungira mwazi amatsutsa naati iwo ali magulu osapanga phindu. Iwo amati mosiyana ndi magulu aakulu olembetsedwa Pamsika Wachuma, ndalama zawo sizimapita kwa oikizamo chuma chawo m’malondawo. Koma ngati Red Cross idali ndi oikizamo chuma chawo, ikanakhala gulu laphindu koposa mu United States, monga ngati General Motors. Ndipo nduna za nkhokwe zosungira mwazi zimalandira malipiro abwino. Polongosola za nduna 62 zokhala mnkhokwe zosungira mwazi zimene zinafufuzidwa ndi The Philadelphia Inquirer, 25 peresenti zinkapanga ndalama zoposa $100,000 pachaka. Ena ankapanga ndalama zoŵirikiza kaŵiri kuposa pamenepo.
Osunga mwazi amanenanso kuti iwo “samagulitsa” mwazi umene amasonkhanitsa—amangolipiritsa mtengo wosamalira. Wosunga mwazi wina akunyanyuka ndi kunena kumeneko motere: “Zimandizunguza mutu pamene Red Cross imanena kuti sigulitsa mwazi. Nzofanana ndi masitolo aakulu amene anganene kuti iwo akukulipiritsani chifukwa cha katoni, koma osati mkaka umene ulimowo.”
Msika wa Padziko Lonse
Mofanana ndi malonda a plasma, malonda a mwazi wathunthu amakuta dziko lonse. Momwemonso kuliri kusulizidwa kwake. Mwachitsanzo, Red Cross ya ku Japan inadzutsa mkwiyo mu October 1989 pamene inayesera kuloŵerera m’msika wa Japan mwakuchotserako mtengo ku zinthu zonse zotengedwa ku mwazi wosonkhedwa. Zipatala zinatuta mapindu aakulu mwakusonyeza pamafomu awo a inshuwaransi kuti anagula mwazi pamtengo wa nthaŵi zonse.
Mogwirizana ndi nyuzipepala ya ku Thailand yotchedwa The Nation, maiko ena a ku Asia anafunikira kuthetsa msika wa golide wofiira mwakuthetsa kulipira osonkha mwazi. Mu India anthu ambiri okwanira 500,000 amagulitsa mwazi wawo weniweni kuti akhale ndi ndalama zodyera. Anthu ena, amene amatopa ndi kusowa tulo ndi amphaŵi, amadzibisa kotero kuti apereke mwazi wambiri kuposa umene amaloledwa. Ena amakhetsedwa mwazi mwadala ndi nkhokwe zosungira mwazi.
M’bukhu lake lakuti Blood: Gift or Merchandise, Piet J. Hagen akunena kuti zochita zobisa za nkhokwe zosungira mwazi zafika poipitsitsa m’Brazil. Nkhokwe zosungira mwazi zamalonda mazana ambiri za ku Brazil zimayendetsa msika wa $70 miliyoni umene umakopa osachenjera. Mogwirizana ndi Bluternte (Kututa Mwazi), osauka ndi malova amathamangira ku nkhokwe zosungira mwazi zosaŵerengeka za ku Bogotá, Colombia. Iwo amagulitsa lita yatheka ya mwazi wawo pamtengo wa mapeso ochepa okha okwanira 300 mpaka 500. Odwala amalipira kuyambira mapeso 4,000 mpaka 6,000 kaamba ka lita yatheka yamwazi imodzimodziyo!
Mwachiwonekere, pafupifupi chinthu chodziŵikiratu chimodzi chawonekera padziko lonse ku zomwe zakambidwazi: Kugulitsa mwazi ndi bizinesi yaikulu. ‘Choncho cholakwika nchiyani? Nchifukwa ninji mwazi suyenera kukhala bizinesi yaikulu?’ ena angafunse motero.
Eya, kodi nchiyani chimene chimapangitsa anthu ambiri kutekeseka ndi bizinesi yaikulu mwachisawawa? Ndiumbombo. Mwachitsanzo, umbombo umawonekera pamene bizinesi yaikulu ikakamiza anthu kugula zinthu zimene sazifunikira kwenikweni; kapena choipirapo, pamene ipitiriza kukakamiza anthu zinthu zina zodziŵika kukhala zangozi, kapena pamene ikana kuthera ndalama kupanga zinthu zake kukhala zachisungiko.
Ngati bizinesi ya mwazi yaipitsidwa ndi mtundu umenewo waumbombo, miyoyo ya anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse ili pangozi yaikulu. Kodi umbombo waipitsa bizinesi ya mwazi?
[Mawu a M’munsi]
a Mu April 1990, kuvumbula kwa Gaul kunapata Mphotho ya Pulitzer kaamba ka Utumiki Wokomera Aunyinji. Kunayambitsanso kufufuza kwakukulu kochitidwa ndi boma m’indasitale ya mwazi kumapeto kwa 1989.
[Bokosi patsamba 6]
Kugulitsa Nsapo
Mwinamwake akazi oŵerengeka okha omwe angobala kumene amazizwa ndi zimene zimachitika ku nsapo, mulu wa minyewa imene imadyetsa khanda lidakali m’chibaliro. Mogwirizana ndi The Philadelphia Inquirer, zipatala zambiri zimaisunga, kuiziziritsa, naigulitsa. Mu 1987 mokha, United States inatumiza makilogramu 0.8 a nsapo kumaiko akunja. Kampani yomwe iri pafupi ndi Paris, Falansa, imagula matani 15 a nsapo tsiku lirilonse! Nsapo ziri magwero opezamo mwazi wa plasma wa nakubala mosavuta, imene kampaniyo imakonza kukhala mankhwala osiyanasiyana ndikuwagulitsa ku maiko ena zana limodzi.
[Chithunzi patsamba 4]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Mbali Zazikulu za Mwazi
Plasma: pafupifupi 55 peresenti ya mwazi. Iyo njopangidwa ndi madzi 92 peresenti; zotsalazo ndi choloŵanecholoŵane wa maproteni, monga ngati maglobulin, mafibrinogen, ndi albumin
Maplatelet: pafupifupi 0.17 peresenti ya mwazi
Maselo Oyera: pafupifupi 0.1 peresenti
Maselo Ofiira: pafupifupi 45 peresenti