Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 4/8 tsamba 19-20
  • “Uzilemekeza Atate Wako ndi Amako”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Uzilemekeza Atate Wako ndi Amako”
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • Chitirani Ulemu Anthu Onse
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Chitirani Ena Ulemu
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Lemekezani Yehova—Chifukwa Ninji Ndipo Motani?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Tizipereka Ulemu kwa Oyenera Kulemekezedwa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 4/8 tsamba 19-20

“Uzilemekeza Atate Wako ndi Amako”

MAWU amenewo akutifikira kuchokera m’nthaŵi ya makedzana, zaka mazana ambiri nthaŵi ya Kristu isanadze. Iwo anabweretsedwa kuchokera pamwamba pa phiri, olembedwa pamagome amiyala ndi chala cha Mulungu. Mose anagwiritsiridwa ntchito kutsogolera Aisrayeli kutuluka muukapolo wa Igupto, kuwoloka Nyanja Yofiira, ndikudzamanga misasa mphepete mwa Phiri lamakolokoto la Sinai. Atatha masiku 40 usana ndi usiku ndi Yehova pa Phiri la Sinai, Mose anatsika ndi magome aŵiri a miyala olembedwapo Malamulo Khumi.—Eksodo 34:1, 27, 28.

Limodzi la magomewo linalembedwapo lamulo lachisanu, lomwe tsopano liri m’Baibulo pa Eksodo mutu 20, vesi 12. Ilo limati: ‘Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti achuluke masiku ako m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.’ Mogwirizana ndi mtumwi Paulo, ndilo “lamulo loyamba lokhala nalo lonjezano,” lakuti: ‘Ukhale wa nthaŵi yaikulu padziko.’—Aefeso 6:1-3.

Zochitika zochititsa mantha za moto ndi utsi ndi kugwedezeka kwa Phiri la Sinai pamene Malamulo Khumi ankaperekedwa zinalengeza mowoneka kufunika kwake, kuphatikizapo lachisanulo, kulemekeza atate ndi amayi. Kodi kusonyeza ulemu kumeneku kumaphatikizapo chiyani? Siulemu ndi kumvera kokha komanso kuwasamalira ndi kuwachilikiza m’zinthu zakuthupi atazisoŵa.

Ichi chinamveketsedwa bwino zaka mazana ambiri pambuyo pake pamene Yesu anatsutsana ndi alembi ndi Afarisi ponena za miyambo yawo yapakamwa. Yesu anasonyeza kuti pamene iwo ankawamana chilikizo lakuthupi makolo awo osoŵa, iwo ankalephera kulemekeza atate kapena amayi awo. Iye anati kwa iwo, monga momwe zalembedwera pa Mateyu 15:3-6: ‘Mulungu anati, Lemekeza atate wako ndi amako; ndipo, wakunenera atate wake ndi amake zoipa, afe ndithu. Koma inu munena, Amene aliyense anena kwa atate wake kapena kwa amake, Icho ukanathandizidwa nacho, nchoperekedwa kwa Mulungu; iyeyo sadzalemekeza atate wake. Ndipo inu mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu.’

Ponena za Yesu iyemwini, iye anasonyeza chimvero kwa makolo ake, mwakukhala wogonjera kwa iwo. (Luka 2:51) Zaka zambiri pambuyo pake, pamene ankamwalira pamtengo wozunzirapo, iye anachitira ulemu amayi ŵake mwakupanga makonzedwe achikondi oŵasamalira ndi kuŵachilikiza.—Yohane 19:25-27.

Mtumwi Paulo anadziŵa bwino lomwe kuti chinali chiyeneretso cha Mulungu kwa ana, ndipo ngakhale adzukulu, kusamalira makolo osoŵa. Ndipo mosangalatsa, iye anagwirizanitsa chithandizo chakuthupi choterocho ndi kuchitira ulemu motere: ‘Chitira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu. Koma ngati wamasiye wina ali nawo ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kuchitira ulemu a m’banja lawo, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ichi ncholandirika pamaso pa Mulungu.’ (1 Timoteo 5:3, 4) Makolo anu anakusamalirani pamene munali khanda ndi mwana wosatha kudzisamalira; muukalamba wawo, ndinthaŵi yanu yakuwathandiza m’kusoŵa kwawo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena