“Anthu Okhala Ngati Mfuko”
NYENGO zozizira zachisanu. Lukanelukane wa michera yopitamo sitima ya makilomita 1,100 yomwe mkati mwake m’mofunda kuposa kunja mumzinda. Chiŵerengero chomakula cha anthu opanda kokhala—okwanira 75,000, malinga ndi kuŵerengera kwina kongoyerekezera. Mu New York City, U.S.A., mfundo zitatuzo zagwirizana kupanga vuto lowopsa la m’madera akutauni: okhala m’mchera, kapena “anthu okhala ngati mfuko,” monga momwe ena amawatchera. Mumabande a m’mbali mwa ulalo ndi m’masitepe, m’zipinda zosungiramo zinthu zosiidwa, michera, ndi ngondya zina zonyalanyazidwa za mum’cheramo, iwo amanga tinyumba tokhalamo. Mu mchera wina wanjanji wosagwiritsiridwa ntchito kwanthaŵi yaitali wa ku Manhattan, unyinji wa anthu ameneŵa akukhala m’nyumba zosungira konkiri zosagwiritsidwa ntchito, mapanga apansi, ndi m’nsolomondo. Ena amanga ngakhale timiraga mumcheramo.
Komabe, moyo wamumchera ndiwovuta. Makoswe aakulu ngati amphaka amathamangathamanga mumdima. Chaka chirichonse anthu ambiri amaphedwa ndi sitima zothamanga m’micherayo ndiponso ndi njanji yachitatu yamagetsi. Apolisi amafunafuna m’njanjimo mokhazikika kuti apitikitse anthu opanda kokhala. Antchito oyendayenda amatsatira, akumapasula timisasato. Amachotsamo makama ndi nsanza, mawailesi ndi mawailesi akanema, ngakhale kuchotsa mapepala omamatizidwa ku zipupa za michera yobisalako.
Apolisi atapita, opanda kokhalawo amabwerera. Monga momwe ofisala wina wapolisi anafotokozerera The New York Times, zoyesayesa zawo zonse zochotsa opanda kokhala zingangowasamutsira kwina mwakanthaŵi mkati mwa micherayo. “Iri liri kokha yankho lapakanthaŵi,” iye akunena motero. Koma kupanda kokhala siliri vuto lapakanthaŵi. Mogwirizana ndi kuŵerengera kwina, anthu mamiliyoni aŵiri mu United States mokha alibe kokhala. M’chaka chimodzi chokha, magulu awo anawonjezereka mowopsa ndi 18 peresenti. Mwachiwonekere, yankho lanthaŵi zonse ndilo limene timafunikira. Zimenezo ndizo zimene Mlengi wa anthu amalonjeza m’Baibulo—nthaŵi imene munthu aliyense padziko lapansi adzakhoza kumanga nyumba yakeyake ndi kukhalamo, kusangalala ndi moyo wopanda chisoni cha aumphaŵi ndi kupanda kokhala.—Yesaya 65:21-23.