Kuchinjiriza Kubweranso kwa Zizoloŵezi Zoipa
“NDALAKIKA! Yatha nkhondoyo potsirizira pake!”
Mawuŵa amasonyeza malingaliro achilakiko cha munthu yemwe wakhala akulimbana ndi chizoloŵezi choipa koma tsopano wachigonjetsa.
Komabe, kubwevuka kungamkwiitse chotani nanga munthu woteroyo! Nkogwiritsa mwala chotani nanga kutumba kuti chizoloŵezi choipacho, chomwe munaganiza kuti chinatheratu, chabweranso modabwitsa ndipo mwamphamvu!
Mwinamwake inuyo munakhalapo ndi chokumana nacho cha kubwevukira m’chizoloŵezi choipa chomwe munafunitsitsa kwambiri kuchigonjetsa. Ngati ziri choncho, pamenepo mungayambe kukaikira ngati mungakhoze kukasiya kwanthaŵi zonse kachitidwe kosafunidwako. Ndipo machitidwe osafunidwa angakhale ambiri: kudya mopambanitsa, “kumwerekera” ndi masiwiti, kumwa mopambanitsa, kugula kwansontho, kuchedwa kwachizoloŵezi, kutchova njuga, kusuta, ndi zizoloŵezi zina zambirimbiri.
“Kodi Ndinabwevukiranji Pamene Vuto Loipitsitsa Linatha?”
Zingawoneke ngati kuti pamene mwapyola masitepe oyamba a kuleka chizoloŵezi choipa, kuchipeŵa kukakhala kopepukirapo. Komabe, mafufuzidwe osiyanasiyana amasonyeza kuti kaŵirikaŵiri sizimakhala choncho.
M’bukhu lakuti Selfwatching, mkonzi R. Hodgson ndi P. Miller akulongosola kuti: “Kubwevuka mwachiwonekere kwambiri kumachitika m’miyezi itatu yoyambirira pambuyo pochiritsidwa. Kwenikweni, kufufuza kwina kwasonyeza kuti pafupifupi 66 peresenti ya osuta fodya, zidakwa ndi omwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa amabwerera ku mkhalidwe wawo wakale mkati mwa masiku 90 pambuyo pakupanga chosankha chawo chakusintha. Komabe, awo okhoza kuleka kumwerekera kwawo mkati mwa miyezi itatu kufika ku isanu ndi umodzi yoyambirira ali ndi mpata wabwino kwambiri wa kusungabe kudziletsa kumeneko.”
Kodi nchifukwa ninji kubwereranso kwa zizoloŵezi zoipa kumakhalanso chiopsezo miyezi—kapena nthaŵi zina zaka—pambuyo pa nyengo yoyamba yakuleka? Chifukwa china nchakuti zipsinjo zina m’moyo zingabuke, ndipo zizoloŵezi zoipa zinali zokupatsani mpumulo wapakanthaŵi nthaŵi zakale. Chotero ngakhale pambuyo polingalira kuti mwagonjetsa chizoloŵezi chosafunidwa, ngati muli m’chipsinjo—chonga chochititsidwa ndi mavuto a zandalama, thanzi, kugwiritsidwa mwala kosiyanasiyana—chenjerani ndi kubwevuka! Ngati mwasungulumwa kapena kusukidwa, musadabwe nazo ngati chizoloŵezi chanu chakale chiyesa kubweranso.
Zochititsa zina za kubwevuka zingakhale zipsinjo zakakhalidwe, kukangana ndi anthu, malingaliro oipidwa, ndi kukhala m’mikhalidwe yoyesa kwambiri.
Kuchinjiriza Kubwevuka
Ngakhale pambuyo pa nyengo yoyambirira ya kulimbana mwachipambano ndi chizoloŵezi chosafunidwa, nkofunika kuti mupitirizebe kumagwiritsira ntchito maluso omwe anakuthandizani kuleka chizoloŵezicho nthaŵi yoyamba. Maluso ameneŵa angagwiritsiridwe ntchito mopitirizabe, kapena m’zochitika zina kungakhale kwabwino kumawabwerezanso kwanthaŵi ndi nthaŵi, monga m’nyengo za kupsinjika kapena chiyeso champhamvu.
Mwachitsanzo, mwina munasunga zolembedwa zokuthandizani kupita patsogolo, zonga ngati kuŵerenga kwa tsiku ndi tsiku kapena kwa mlungu ndi mlungu pamene mukuyesayesa kutaya kulemera kwanu kwathupi. Ichi nchothandiza m’kuletsa chizoloŵezi ndipo simuyenera kuleka ngakhale pamene mwakhulupirira kuti upanduwo watha.
Mwina munakhalapo ndi njira yodzifupira pamene munapambana kutsutsa chizoloŵezi chimene munkayesayesa kuchilaka. Dongosolo lofupa lokonzedwa lingakhale lothandiza kuchinjiriza kubwevuka. Kapena, poleka chizoloŵezi, kodi munaphatikiza pa ndandandayo chithandizo cha bwenzi? Mloleni ameneyo akuthandizeni kumasuka ku chizoloŵezi chanu choipa chakale.
Kodi ndi maluso ena ati omwe adzakuthandizani kutsutsa kubwerera m’mbuyo, makamaka mkati mwa nyengo zakupsinjika?
Kanizani Mwakuloŵetsa China m’Malo
Dr. R. Stuart, wotsogolera wa ukatswiri wa zamaganizo wa Weight Watchers International, Inc., akuvomereza zotsatirazi kaamba ka awo oyesayesa kutaya kulemera kwathupi: “Tanganitsani maganizo anu ndi zochita zotenga maganizo. Ntchito ya zopangapanga imathandiza, ndiponso zochita zapamtima. Ngati nkotheka, zogwirira ntchito zikhalepo ndiponso malo ogwirirapo ntchito akhale okonzekeretsedwa, kotero kuti mungapitirize ntchito yanu pamphindi iriyonse.” Mwinamwake luso loterolo lingakuthandizeni.
Inde, loŵetsani m’malo chizoloŵezi chanu chakale choipa ndi ntchito yabwino. Kumbukirani, chizoloŵezi chimenecho mwachiwonekere chinakupatsani mpumulo wakutiwakuti pamene munapsinjika, chotero sankhani zoloŵa m’malo zimene zidzatumikira chifuno chofananacho mwachipambano. Inu mungaŵerenge, kuchita maseŵera olimbitsa thupi, kuseŵera nyimbo pa chiŵiya choimbira, kupaka utoto, kapena kuchezetsa mabwenzi. Yambani tsopano mwakulemba ndandanda ya zochita zothekera zoloŵa m’malo. Zindikiritsani zimene mwasankha kuzilondola mwatsatanetsatane. Yeserani zochita zatsopano zimenezi mobwerezabwereza monga momwe munachitira ndi chizoloŵezi chakale. Ichi chidzakupangitsa kukhala kosavuta kuzichita pamene mukhala ndi malingaliro opsinja. Ndiiko komwe, zochita zoloŵa m’malo zimenezi zidzakhaladi zizoloŵezi—zizoloŵezi zabwino!
Kufunika kwa Kulimbana ndi Kulefulidwa
Popeza kuti chiyeso chakubwerera ku zizoloŵezi zakale zoipa chingakhale champhamvu makamaka pamene muli wopsinjika, kodi mungasinthe ina ya mikhalidwe yanu m’moyo wanu kuti muchepetseko chipsinjocho? Ngakhale nga-ti mavuto ena sangapeŵedwe, mungaphunzire kulamulira malingaliro anu kotero kuti musadzazidwe ndi malingaliro akulefulidwa.
Kaŵirikaŵiri mphamvu yakulefulidwa imachepsedwa. Baibulo limati: ‘Mtima wa munthu umlimbitsa alikudwala; koma ndani angatukule mtima wosweka?’ (Miyambo 18:14) Nzowona chotani nanga! Kaŵirikaŵiri sivutolo limene limatifooketsa koma kulefulidwa komwe kumatulukapo.
Mwambi wina wa m’Baibulo umanena mwanjirayi: ‘Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.’ (Miyambo 24:10) Malingaliro oipidwa osalamulirika adzakufooketsani. Adzakuikani paupandu wakubwevuka, mwinamwake kukupanikizani kuti mubwerere ku chizoloŵezi chakale choipa kaamba ka mpumulo. Pamenepo, nkofunika chotani nanga kulimbana ndi kulefulidwa!
Koma, bwanji ngati mukupezabe kuti mukuyamba kubwerera m’mbuyo mosasamala kanthu za kuyesayesa kwanu?
Kubwerera Kwakanthaŵi Mosiyana ndi Kubwevukiratu
Nkopepuka chotani nanga kulingalira kuti: ‘Ndinalephera, chotero ndibwino kuti ndingolekeratu.’ Limbanani ndi ganizo limenelo. Kanani kulola kubwerera m’mbuyo kwakanthaŵi, kapena ngakhale kubwerera m’mbuyo kungapo, kukuuzani kuti mwalephera.
Talingalirani fanizo ili: Ngati munali kukwera pamasitepe ndiyeno nkuphunthwa ndikubwerera m’mbuyo sitepe limodzi kapena aŵiri, kodi mukalingalira kuti, ‘Ndidzangotsika pansi ndikuyambiranso?’ Ndithudi ayi! Pamenepo, bwanji mudzafuna kugwiritsira ntchito lingaliro lonyenga limeneli polimbana ndi zizoloŵezi zoipa?
Malingaliro aliŵongo kaŵirikaŵiri amatsatira kubwevuka. Inu mungapambanitse malingaliro ameneŵa mwakugamula kuti sindinu munthu wabwino, kuti ndinu munthu wofooka ndikuti simuyenerera chabwino chirichonse. Musadzilole kumwerekera m’liŵongo losinjirira loterolo. Limakulandani nyonga imene mukuifunikira kuti muyambirenso kulimbanako. Ndipo kumbukirani ichi: Munthu wamkulu koposa yemwe anakhalapo padziko lapansi, Yesu Kristu, anadza kudzawombola ochimwa, osati anthu angwiro. Chotero palibe ndi mmodzi wa ife yemwe adzachita zinthu mwangwiro panthaŵi ino.
Mfundo ina yofunikira kuilingalira njakuti liŵongo lingakhale pothaŵira pomwe padzatilola kuchitanso chinthu chimodzimodzicho. M’bukhu lawo lakuti You Can’t Afford the Luxury of a Negative Thought, P. McWilliams ndi J. Roger amafotokoza chotulukapo chothekera ichi: “Liŵongo . . . tiyeni tichitenso. Pamene ‘tapereka malipiro’ kaamba ka ‘upandu’ wathu, ndife omasuka kuuchitanso malinga ngati tiri okonzekera kulipira mtengowo. Mtengo wotani? Liŵongo lowonjezereka.”
Simuyenera kulola kubwerera m’mbuyo kwakanthaŵi kuti kukhale kubwevuka kotheratu. Kumbukirani kuti, pomalizira pake, kulaka chizoloŵezi ndiko kuli kanthu, osati nthaŵi zimene munayang’anizanapo ndi kubwerera m’mbuyo.
Ponena za chimenechi nkwanzeru kusankha pasadakhale luso limene mudzagwiritsira ntchito ngati mwapeza kuti mukubwerera ku chizoloŵezi chanu chakale. Kukonzekera kothandiza koteroko kudzakukonzekeretsani kulimbana ndi kubwerera m’mbuyo pamphindi yoyambirira.
Nkotheka—Ndi Koyenerera!
Pamenepa, kulimbana ndi chizoloŵezi choipa kumaposa pakupirira nyengo yoyambirira ya kuleka kovutako. Kumaloŵetsamo kuchita ndi kugwiritsidwa mwala popanda kusinthira kotheratu ku chizoloŵezi choipa.
Nkovuta eti? Inde, koma nkotheka kwenikweni. Luso limene linakuthandizani kuleka chizoloŵezi poyamba, ngati mulipitiriza, lidzakuthandizani kuchinjiriza kapena kulaka kubwevuka. Kodi phindu lalikulu koposa nlotani? Kudzilemekeza—mphotho yamtengo mwa iyo yokha. Ndipo mwachiwonekere mudzalemekezedwanso koposa ndi aja okudziŵani.
[Chithunzi patsamba 29]
Kubwerera kumbuyo masitepe angapo sikumafunikiritsa kuyambiranso kuchiyambi
[Chithunzi patsamba 30]
Chiopsezo cha kubwevuka chimachepetsedwa mwakukhala wotanganitsidwa ndi zochita zotenga maganizo