Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 5/8 tsamba 31
  • Nanga Nkuchitiranji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nanga Nkuchitiranji?
  • Galamukani!—1991
  • Nkhani Yofanana
  • N’kusiyiranji Kusuta?
    Galamukani!—2000
  • Ochirikiza Fodya Aponya Zibaluni Zawo za Mpweya Wotentha wa Zinyengo
    Galamukani!—1995
  • Kusuta—Kawonedwe Kachikristu
    Galamukani!—1989
  • Kodi Mawu a Mulungu Amati Chiyani pa Nkhani ya Kusuta Fodya?
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 5/8 tsamba 31

Nanga Nkuchitiranji?

“Monga wosuta, sindingatsutse chenicheni chakuti kuloŵerera m’chizoloŵezicho nkupusa kwenikweni. Aliyense wokhala ndi nzeru pang’ono amadziŵa kuti kusuta kumapereka chiwopsezo ku thanzi la munthu. Nchizoloŵezi chauve, chonyansa, chodya ndalama zambiri. . . . Kwa osuta, moyo ngwodzala ndi timbale taphulusa, mwaye wa chikonga, zipsera ndi ndalama zambiri zokachapitsira—kaamba ka zovala zonunkha fodya.”—Diane Francis, magazini a Maclean’s, Canada.

“Osuta angayembekezere kukhala ndi moyo waufupi kuposa osasuta: mwachitsanzo, moyo wa munthu wa zaka 25 zakubadwa amene amasuta mapaketi aŵiri patsiku udzakhala waufupi kwa uja wa wosasuta ndi zaka 8.3. Osuta ngothekera kwambiri kufa ndi kansa moŵirikiza katatu kuposa osasuta.”—The Columbia University College of Physicians and Surgeons Complete Home Medical Guide.

“Chaka chirichonse ndudu zimapha anthu a ku Amereka ambiri kuposa onse pamodzi amene anaphedwa m’Nkhondo Yadziko ya I, Nkhondo ya ku Korea, ndi ya ku Vietnam, pafupifupi unyinji womwe unafa m’Nkhondo Yadziko ya II. Chaka chirichonse ndudu zimapha anthu a ku Amereka kuŵirikiza nthaŵi zisanu kuposa ophedwa m’ngozi zapamsewu. Kansa yamapapu yokha imapha anthu ochuluka kwambiri mofanana ndi ophedwa m’ngozi zapamsewu. Indasitale ya ndudu ikugulitsa chida chakupha.” (Senator Robert F. Kennedy, First World Conference on Smoking and Health, September 11, 1967)—The Cigarette Underworld, lokonzedwa ndi Alan Blum, M.D.

“Fodya amapha pafupifupi anthu mamiliyoni aŵiri ndi theka chaka chirichonse kuzungulira dziko lonse. Ndiye nakatande mmodzi wokulira koposa, wokhoza kuchinjirizidwa wa imfa m’dziko lerolino. . . . Kumsuta mwa mtundu uliwonse, nchizoloŵezi chaupandu, chodula ndi chomwerekeretsa.”—Dr. Judith Mackay, mtsogoleri wamkulu wa Bungwe la ku Hong Kong Loyang’anira za Kusuta ndi Thanzi, wogwidwa mawu m’magazini a World Health.

Ngati dzanja lomwe linandipezera chakudya panthaŵi ina ndi indasitale ya fodya, pamenepo dzanja lomwelo lapha anthu mamiliyoni ambiri ndipo lidzapitirizabe kupha mamiliyoni owonjezereka pokhapo ngati anthu agalamuka nkuwona maupandu a ndudu. . . . Ndifuna kuthandiza anthu kugalamuka nkuwona mmene ndudu ziliri zaululu.”—Patrick Reynolds, mdzukulu wa woyambitsa R. J. Reynolds Tobacco Company.

Nangano nchifukwa ninji mamiliyoni ambiri a amuna, akazi, ndi achichepere omwe amasuta fodya? Kwa ena yankho lingakhale chitsenderezo cha anzawo, chikhumbo chofuna kuwoneka wapamwamba. Koma kwa ambiri yankho ndi kokha kumwerekera komwe kumatsogolera kukukakamizidwa. Monga momwe bukhu lina lopereka uphungu m’zamankhwala likunenera kuti: “Chifukwa chenicheni chimene anthu amasutira fodya nchakuti iwo ngomwerekera ku mankhwala ogodomalitsa amphamvu opezeka m’fodya—chikonga.”

Ndiyeno ndimotani mmene wosuta fodyayo angalekere? Mwakupeza chisonkhezero champhamvu, champhamvudi kuposa chikhumbo cha thupi chofuna chikonga. Kwa munthu wofunitsitsa kufitsa miyezo Yachikristu, kudzatanthauza kukulitsa chikondi kaamba ka Mulungu ndi mnansi chomwe chimapambana chikhumbo chadyera cha thupi.—Mateyu 22:37-40; 1 Akorinto 13:5, 7, 8.

Monga momwe bukhu lazamankhwala logwidwa mawu papitalo likunenera kuti: “Osuta amene akufuna kuleka ayenera kukumbukira mpangidwe womwerekeretsa wa mankhwala ogodomalitsa a chikonga ndi kukhala okonzekera kuyang’anizana ndi ziyambukiro zopweteka monga zotsatirapo zachibadwa za kuleka. Iwo ayenera kukumbukira kuti, kuleka kopwetekako ndi mkhalidwe wapakanthaŵi womwe, chinkana kuti ngwosakondweretsa, sumavulaza. Aliyense wogwiritsira ntchito fodya, mosasamala kanthu kuti ngwomwerekera motani, angasiye kusuta.”—The Columbia University College of Physicians and Surgeons Complete Home Medical Guide.

Ngati mungakonde kuthandizidwa kupeza mtundu wa chisonkhezero chofunikacho kuti muleke kusuta, chonde khalani omasuka kufikira Mboni za Yehova ku Nyumba yawo Yaufumu yakumaloko kapena kudzera m’keyala ya ofalitsa magazini ano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena