Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 6/8 tsamba 24-25
  • Ilamulireni Wailesi Yakanema Isanakulamulireni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ilamulireni Wailesi Yakanema Isanakulamulireni
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kulamulira
  • Kodi Mphunzitsi Wanu Ndani?
  • Kodi Wailesi Yakanema Yakusinthani?
    Galamukani!—1991
  • Njira Zothandiza Kuti Musamaonere TV Kwambiri
    Galamukani!—2006
  • Kugwiritsa Ntchito Wailesi ya Kanema Mosamala Kwambiri
    Galamukani!—2000
  • Kodi TV Imakuberani Nthawi?
    Galamukani!—2006
Galamukani!—1991
g91 6/8 tsamba 24-25

Ilamulireni Wailesi Yakanema Isanakulamulireni

WAILESI YAKANEMA iri ndi mphamvu yodabwitsa. Pamene indasitale ya TV ya ku Amereka inkaumiriza maiko otukuka kumene kukhala ndi TV, inasonyeza zithuzithunzi za Malo Angwiro opeka. Maiko athunthu akasinthidwa kukhala zipinda za makalasi, ndi malo akumidzi kwambiri akumvetsera ku maprogramu a nkhani za maluso amalimidwe, kusungitsa nthaka, ndi kaleredwe ka ana. Ana ankaphunzira physics ndi chemistry napindula ndi kusinthana miyambo koulutsidwa.

Ndithudi, zisonyezero zoterozo kwakukulukulu zinazimiririka m’kuulutsa kwenikweni kwa zamalonda—koma osati kotheratu. Ngakhale Newton Minow, tcheyamani wa Federal Communications Commission yemwe anatcha wailesi yakanema kukhala “dzala lalikulu,” anavomereza m’nkhani imodzimodzi mu 1961 kuti TV inali ndi zipambano zazikulu ndi zosangalatsa zabwino.

Mosakaikira zimenezo nzowona lerolino. Nkhani zoulutsidwa pa TV zimatidziŵitsa zochitika zapadziko. Maprogramu achilengedwe a pa TV amatipatsa zitsanzo za zinthu zimene mwinamwake sitidzaziwonapo: kukongola kwa mbalame yotchedwa hummingbird yosonyezedwa ikuuluka pang’onopang’ono, ikuwoneka ngati ikusambira m’mphepo; kapena kuphukira kodabwitsa kwa maluŵa kojambulidwa, akumera m’thaka amitundumitundu yokongola. Kenaka pali zochitika zamwambo, zonga ngati mavinidwe otchedwa ballet, maimbidwe otchedwa symphony, ndi maopera. Ndipo pali maseŵero, makanema, ndi maprogramu ena—ena abwino ndi opatsa chidziŵitso, ena ongosangulutsa.

Palinso maprogramu amaphunziro kaamba ka ana. National Institute of Mental Health ikusimba kuti monga momwe ana angaphunzirire nkhalwe kuchokera ku chiwawa cha pa TV, angaphunzirenso kukhala osadzikonda, aubwenzi, ndi odziletsa kuchokera ku zitsanzo zabwino za pa wailesi yakanema. Maprogramu osonyeza mmene mungachitire m’zinthu zamwadzidzidzi apulumutsadi miyoyo ya ana. Chotero, Vance Packard akulemba mu Our Endangered Children kuti: “Makolo okwiitsidwa kapena ovutitsidwa amene amakhomera TV yawo moisungiramo mwake mwinamwake amachita mopambanitsa, pokhapo ngati pakhala mkhalidwe wosalamulirika wa ana awo.”

Kulamulira

Mwachiwonekere, kaya tikulankhula za akulu kapena ana, mfungulo ndiyokhayo—kulamulira. Kodi timailamulira TV, kapena kodi TV imatilamulira? Monga momwe Bambo Packard akulingalirira, kwa ena njira yokha yolamulira TV ndiyo kuichotsapo. Koma ena ambiri apeza njira zolamulirira TV pamene akugwiritsirabe ntchito mapindu ake. Nawa malingaliro ena.

✔ Kwa mlungu umodzi kapena iŵiri, sungani cholembedwa chosamalitsa cha kupenyerera TV kwa banja lanu. Onkhetsani maola pakutha kwa nyengoyi ndipo dzifunseni ngati TV njoyenerera nthaŵi imene imadya.

✔ Wonererani maprogramu a TV—osati TV yokha. Fufuzani ndandanda ya TV kuwona ngati pali chirichonse choyenera kuwonerera.

✔ Sungani ndi kutetezera nthaŵi inayake kaamba ka kukambitsirana kwa banja ndi kukhala pamodzi.

✔ Akatswiri ena amachenjeza kusalola ana kapena achichepere kukhala ndi TV m’chipinda chawo. Makolo angakupeze kukhala kovuta kulamulira zimene mwana amawonerera.

✔ VCR (videocassette recorder), ngati mungathe kugula imodzi, ingakhale yothandiza. Mwa kubwereka mavideotape abwino kapena mwakujambula maprogramu amtengo wapatali ndi kuwawonerera pamene kuli koyenerera, mungagwiritsire ntchito VCR kulamulira zimene ziri pa TV yanu—ndi pamene TV yanu iri yoyatsidwa. Komabe chenjezo. Kuilekerera VCR ingangowonjezera nthaŵi yowonongedwera pakuwonerera TV kapena kutsegula njira ya ku mavideotape oipa.

Kodi Mphunzitsi Wanu Ndani?

Munthu ndimakina okhoza kuphunzira. Nzeru zathu nthaŵi zonse zimaloŵetsa chidziŵitso, kutumizira ubongo wathu unyinji wa tizidutswa ta chidziŵitso toposa pa 100,000,000 kamphindi kalikonse. Kumlingo winawake tingasonkhezere zamkati mwa unyinji umenewo mwakusankha zimene tidzadyetsa nzeru zathu. Monga momwe nkhani ya TV imafotokozera mwafanizo mowonekera bwino, maganizo aumunthu ndi mzimu zingaipitsidwe mosavuta ndi zimene timawonerera mofanana ndimmene thupi lingaipitsidwire ndi zimene timadya ndi kumwa.

Kodi ndimotani mmene tidzaphunzirira za dziko lotizinga? Kodi ndi magwero achidziŵitso otani amene tidzasankha? Kodi ndani kapena nchiyani chimene chidzakhala mphunzitsi wathu? Mawu a Yesu Kristu amapereka lingaliro lotonthoza ponena za chimenechi kuti: “Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense amene aphunzitsidwa mokwanira adzafanana ndi mphunzitsi wake.” (Luka 6:40, New International Version) Ngati tithera nthaŵi yochuluka mopambanitsa ndi wailesi yakanema monga mphunzitsi wathu, tingayambe kuitsanzira—kutengera makhalidwe ndi miyezo imene imapereka. Monga momwe Miyambo 13:20 imanenera kuti: ‘Ukayenda ndi wanzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.’

Ngakhale pamene TV sikubweretsa anthu opusa kapena amakhalidwe oipa m’nyumba mwathu, iyo ikuphonyabe chinachake chofunika kwambiri. Zimene zimawoneka pa TV sizimapereka chosoŵa chachikulu cha munthu aliyense: chosoŵa chauzimu. TV ingakhale yabwino koposa m’kusonyeza kuipa kochititsa chisoni kumene dziko lino lagweramo, koma kodi imachitanji kutiuza chifukwa chake anthu akuwoneka kukhala osakhoza kudzilamulira okha? Iyo ingakhoze koposa kutisonyeza kukongola kwa chilengedwe, koma kodi iyo imachitanji kutikokera kwa Mlengi wathu? Iyo ingatitengere ku ngondya zinayi za dziko lapansi, koma kodi ikhoza kutiuza kaya anthu adzakhalapo pamtendere kumeneko?

Palibe “njira yopezera chidziŵitso” imene ingakhale yeniyeni popanda kuyankha mafunso auzimu ofunika oterowo. Chimenecho nchimene moyenerera chimalipangitsa Baibulo kukhala lamtengo wapatali chotero. Ilo limapereka “njira yopezera chidziŵitso” m’lingaliro la Mlengi wathu. Linalinganizidwira kutithandiza kumvetsetsa chifuno chathu m’moyo ndi kutipatsa chiyembekezo champhamvu kaamba ka mtsogolo. Mayankho okhutiritsa ku mafunso a moyo ovutitsa koposa amapezekamo mosavuta. Iwo angoyembekezera kuŵerengedwa m’masamba ochititsa chidwi mosalekeza a Baibulo.

Koma ngati sitilamulira TV, kodi nthaŵiyo tidzaipeza kuti?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena