Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 6/8 tsamba 14-16
  • Kodi Ndiyenera Kuphatikana ndi Gulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ndiyenera Kuphatikana ndi Gulu?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chichirikizo ndi Ubwenzi
  • ‘Osatsata Unyinji wa Anthu’
  • Kukhala ndi Moyo ndi Lupanga
  • Kupeza Lingaliro Lenileni Lokhala Mbali ya Chinachake
  • Zimene Tifunikira Kudziŵa Ponena za Magulu Aupandu
    Galamukani!—1998
  • Kodi Ndingadzichinjirize Motani ku Kuukiridwa ndi Gulu?
    Galamukani!—1991
  • Kutetezera Ana Athu ku Magulu Aupandu
    Galamukani!—1998
  • Mliriwo Ufalikira
    Galamukani!—1998
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 6/8 tsamba 14-16

Achinyamata Akufunsa Kuti . . .

Kodi Ndiyenera Kuphatikana ndi Gulu?

“Pamene ndinakhala m’chipinda chosungira zinthu kusukulu, anyamata ameneŵa anadza kwa ine nayamba kundivutitsa. Mmodzi wa iwo anandimenya nkhonya pachifuwa. Panthaŵiyo mmodzi wa anyamatawo yemwe ndinamdziŵira m’mudzi wakwathu anadza nandichinjiriza. Ndinalingalira kuti, ‘Ngati ndiphatikana ndi gulu, mwinamwake ndingakhale ndi chitetezo chofananacho.’”—Greg.

MAGULU akuchuluka m’sukulu zambiri ndi m’midzi. Mu 1989 apolisi anayerekezera kuti mu Los Angeles County, U.S.A., mokha, munali magulu 600, okhala ndi ziŵalo 70,000. Komabe, magulu sali olekezera ku United States. Mwachitsanzo, magazini a Maclean’s anasimba kuti m’mzinda wa Vancouver, Canada, muli magulu 13, okhala ndi ziŵalo zoposa 600.

Mofanana ndi Greg, anthu ambiri amaphatikana ndi magulu kuti apeze chitetezo ku chiwawa chakusukulu, ndipo m’nthaŵi zino zachiwawa, sikovuta kumvetsetsa chifukwa chake achichepere ena angalingalire chimenecho kukhala chofunika. Tikuchitira umboni ‘kuchuluka kwa kusayeruzika’ kwapadziko lonse. (Mateyu 24:12) Komabe, pali zifukwa zina zimene magulu a m’makwalala aliri okhumbirika mwamphamvu chotero kwa achichepere ena.

Chichirikizo ndi Ubwenzi

“Ndinafunadi kukhala ndi mabwenzi, lingaliro lokhala mbali ya winawake kapena gulu, winawake yemwe ungamsamalire,” akufotokoza motero Bernard, chiŵalo chakale cha gulu. Marianne, yemwe anaphatikana ndi gulu la asungwana, akuvomereza kuti anatero “chifukwa cha kufuna [kwake] mphamvu yolamulira chinthu chinachake,” kuphatikizaponso “mkhalidwe wabanja” umene linapereka.

Pamene kuli kwakuti nzowona kuti achichepere ena amaphatikana ndi magulu kuti aŵathandize kulaka kusungulumwa kapena kaamba ka chikondwerero chimene angapereke, kukuwoneka kuti ambiri a iwo amadziphatikako kuti akhale ndi lingaliro lokhala mbali ya chinachake, kuti alandire chichirikizo chamalingaliro, kupeza mabwenzi omwe ali ndi zikondwerero zofanana. Kaŵirikaŵiri izi zimachitidwa kuti apeze choloŵa m’malo mkhalidwe wosakhumbirika wabanja.

Bernard akunena za iyemwini ndi ziŵalo zinzake za gulu motere: “Ambirife tinachokera ku mabanja osweka. Ambiri anali kuleredwa ndi kholo limodzi, kaŵirikaŵiri amayi, m’mabanja aakulu. Chotero panalibe aliyense woombola nthaŵi yolankhula nawo. Ambiri anachokera ku mabanja kumene anachitiridwa nkhanza mwakuthupi ndi kunyozedwa ndipo panalibe aliyense amene anadera nkhaŵa mmene zinaŵakhudzira iwo. Chotero iwo anadzimva bwino, monga mmene ndinachitira, ponena za kukhala okhoza kulankhula kwa winawake ndi kumvedwa.”

Mfundo imeneyi yaperekedwanso ndi Lew Golding, phungu wa achichepere wa ku Canada. Iye anati: “Ana okhala ndi mavuto kunyumba amanonomera kugulu kaamba ka chisamaliro cha malingaliro.”

Mu United States, magulu ambiri amapangidwa pazifukwa zamakhalidwe ndi zamwambo. Chotero, magulu m’dzikolo amapereka chiitano chowonjezereka cha kuyanjana ndi awo omwe ali ndi malingaliro amodzimodzi ponena za zakudya, nyimbo, chinenero, ndi zinthu zina zambiri. Kwa achichepere ndi achikulire omwe, chikhumbo chakudzimva wofunika ndi wolandirika nchachibadwa. Koma kodi malingaliro ameneŵa ndi zosoŵa zingakhutiritsidwedi mwakuphatikana ndi gulu?

Miyambo 17:17 imati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse.” Kodi ziŵalo za magulu zimasangalaladi ndi kukhulupirika kotero ndi ubwenzi weniweni? Mosiyana, kukangana ndipo ngakhale ndewu pakati pa ziŵalo zina za gulu nzofala kwambiri. Ndithudi, m’malo okhala otsendereza kwambiri mmene magulu amagwirira ntchito, maudani amabuka mosavuta. Kusiyana kwa malingaliro kumatengedwa kukhala kusakhulupirika. Bernard akusimba kuti: “Ngati tinali ndi mkangano, ndinayenera kukhala watcheru chifukwa mwadzidzidzi, mpeni kapena mfuti ikatulutsidwa. Ndipo ameneŵa anayenera kukhala mabwenzi anga! Moyo wa m’gulu unandisiya wogwiritsidwa mwala chifukwa ndinalibe mabwenzi enieni.”

Chiŵalo china chagulu cha zaka zakubadwa 18 chikuwonjezera kuti: ‘Sumakhala ndi mabwenzi alionse, osati ngakhale m’gulu lakolako. Umakhala wekha.’

‘Osatsata Unyinji wa Anthu’

‘Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.’ (Eksodo 23:2) Izi zinanenedwa kwa anthu a Mulungu m’nthaŵi zamakedzana, ndipo m’lingaliro lenileni zimagwira ntchito bwino kwa wachichepere aliyense wolingalira kuphatikana ndi gulu. Inu mungalingalire gulu kukhala njira yodzitetezera kapena magwero a ubwenzi. Komabe, m’chenicheni, chiŵalo cha gulu chimakakamizidwa mosapeŵeka kulondola zolinga ‘zoipa.’

Magazini a The Globe and Mail akunena za ichi kuti: ‘Gulu limakhala banja. Chimenecho chimatanthauzanso kuti gulu limakhazikitsa chimene chiri mkhalidwe wolandirika. M’dziko la achichepere osalamulirika, kuba, kumenya anthu, ndi kugwirira chigololo kungakhale “zinthu” zochita.’

Mu 1989 mokha, magulu ku Los Angeles County anachita mbanda 570. Ndipo pafupifupi kulikonse kumene magulu ali, kumakhala chiwawa. Kuyesa kukana kuloŵamo kumalingaliridwa kukhala kusachirikiza gulu kapena, choipa kwenikweni, kukhala wamantha. M’chirichonse cha zochitika ziŵirizi, mukhoza kuukiridwa mosavuta. Monga momwe chiŵalo china cha gulu chinanenera kuti: “Sungakanire [gulu] lako.” Kodi lingaliro lokhala mbali yake kapena chitetezero nloyenerera mtundu umenewu wa chitsenderezo?

Wolemba Miyambo 1:10-15 akuyankha kuti: ‘Mwananga, akakukopa ochimwa usalole. Akanena, Idza nafe, tibisalire mwazi, tilalire osachimwa opanda chifukwa. . . . Udzachita nafe maere. . . . Mwananga, usayende nawo m’njira.’

Kukhala ndi Moyo ndi Lupanga

Talingaliraninso, ponena za zotulukapo zothekera za thanzi lanu ndi ubwino. Chiŵalo china cha gulu chinanena kuti ‘muyenera kukhala wofunitsitsa kufera ziŵalo zinzanu za gulu.’ Ndipo kaŵirikaŵiri zimakhaladi motero.

Mosiyana, talingalirani phunziro limene Yesu anaphunzitsa ophunzira ake pausiku wa kugwidwa kwake. Yesu analibe chida ndipo anayang’anizana ndi gulu lachiwawa. Kodi Yesu anafuna kuti ophunzira ake asonkhane pamodzi ndipo mwachiwawa amchinjirize? Petro analingalira motero. Iye anasolola lupanga lake nakantha mmodzi wa amuna m’gululo, kudula khutu lake. Komabe, yankho la Yesu liyenera kuti linamdabwitsa Petro. Yesu mozizwitsa anachiritsa khutu la munthuyo nanena kwa Petro: ‘Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.’—Mateyu 26:52.

Kodi phunziro nlotani? Kudzikonzekeretsa ndi chida chodzichinjirizira sikongotsutsidwa ndi malemba komanso nkupusa, kosathandiza. Mwambi umakufotokoza motere: “Koma zoipa zidzamfikira wozilondola.”—Miyambo 11:27.

Kupeza Lingaliro Lenileni Lokhala Mbali ya Chinachake

Zaka 50 zapitazo, kupenda kunapangidwa kumene kunandandalitsa zinthu zochititsa magulu kupangidwa. Pakati pa mavuto ondandalitsidwa panali moyo wabanja wosakhutiritsa, umphaŵi, maunansi omanyonyotsoka, ndi kusoŵa maphunziro abwino. Zochita za gulu sizinathandize konse mkhalidwewu, ndipo sizinathandizedi achichepere osungulumwa kupeza mabwenzi enieni. Komabe, mpingo Wachikristu umakupangitsani kuyanjana ndi anthu amene amakukondani kwambiri. Bwanji osapanga mabwenzi kumeneko?

Komabe, ndimotani mmene mungadzitetezere ngati mukhala m’dera kumene magulu ngofala? Nkhani yamtsogolo idzafotokoza zimenezi.

[Bokosi patsamba 16]

‘Ndinaphatikana ndi Gulu Lamkhwalala’

“Ndinali ndi zaka zakubadwa 17. Mabwenzi anga ndi ine tinavutitsidwa kuwona anthu akuwomberedwa mfuti, kufwambidwa, ndi kugwiriridwa chigololo m’dera lathu. Tinalingalira kuti ngati tikayamba gulu lathulathu, mwinamwake tingazithetse. Panthaŵi imodzimodziyo, ndinafuna kukhala ndi lingaliro lokhala mbali ya gulu. Chotero tinapanga gulu.

“Tinayamba kuyendera m’dera lathu, ndipo posachedwa magulu ena anatiyesa. Mamembala athu aŵiri anaukiridwa ndi gulu lina lolimbana nafe. Mmodzi anapandidwa kumaso ndi chomenyerako baseball; winayo anagwazidwa mpeni. Tinabwezera chisalungamocho ndipo posapita nthaŵi tinakhala gulu lowopedwa koposa kumalowo.

“Komabe, ndinapeza kuti ziŵalo za gulu siziri mabwenzi enieni. Sutha kukhulupirira aliyense. Ena sakakuchirikiza ngati unagwera m’vuto. Ndipo ena sanafune malingaliro anga—iwo anayamba kuukira ndipo ngakhale kupha anthu popanda chifukwa. Chotero ndinayamba kuda moyo wanga. Ndinalingalira kuti Mulungu aliko koma ndinazizwa chifukwa chake iye analola chisalungamo chachikulu chotero. Ndinaphunziranso kusukulu kuti tchalitchi ndicho chinali ndi thayo la Zilango Zankhanza ndi kuwononga kutsungula konse m’dzina la Mulungu. Ndinakhulupirira kuti chipembedzo chinali chinyengo chopangira ndalama.

“Tsiku lina, ndinapemphera kwa Mulungu kundithandiza kupeza gulu limene amagwiritsira ntchito. Ndinayang’ana m’Baibulo limene amalume anandipatsa ndipo ndinaŵerenga Machitidwe 20:20. Ilo limanena za kunka kunyumba ndi nyumba. Amene ndinadziŵa kuti amachita zimenezo anali Mboni za Yehova zokha. Chotero ndinafufuza kumene Nyumba ya Ufumu yakumaloko inali ndikupita m’maŵa wotsatirapo. Ndi misozi m’maso anga, ndinafikira Mboni ina ndi kunong’oneza kuti, ‘Ndifuna kuphunzira.’ Ndinapeza anthu a Mulungu. Masiku anga monga chiŵalo cha gulu anatha.”—Wolemba nkhaniyi, yemwe wasankha kusatchulidwa, tsopano akutumikira monga woyang’anira wotsogoza wa mpingo wa Mboni za Yehova.

[Chithunzi patsamba 15]

Nanga bwanji osapanga mabwenzi ndi anthu amene amakukondani kwambiri?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena