Kalata Yochokera kwa Wopereka Mafuno Abwino
POSACHEDWAPA kalata inalandiridwa kuchokera kwa wopereka mafuno abwino m’dziko la m’Afirika kumene ntchito ya Mboni za Yehova njoletsedwa. Mwamunayo analemba kuti:
“Bambo Wokondedwa,
“Ndidzayamba ndi mfundo; ndingofuna kukukumbutsani kuti m’dziko lino boma linaletsa ntchito za tchalitchi chanu. Zikundikwiitsa chotani nanga!
“Sindikulandiranso Galamukani! yanga mokhazikika. Koma kukuuzani zowona, mwachiwonekere Galamukani! ndimagazini abwino koposa amene ndinawadziŵa. Amapereka uphungu kwa oŵerenga mmene angadzisungire mwachipambano ndi molondola, mwalamulo ndi mwauzimu. Iridi chozizwitsa.
“Ndinena motsimikiza kuti kulibe mphunzitsi wa pa yunivesite amene adziŵa zambiri motero kapena kuphunzitsa mwatsatanetsatane chotero. ‘Apasitala’ athu iwo ndiye pepani. Komabe mpamene boma lathu likuti magazini ameneŵa ndi ena ofanana nawo, omwe amaphunzitsa kwambiri, aletsedwa. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti owafalitsa samapereka sawatcha ku mbendera. Chabwino.
“Koma funso limodzi ndi iri: Ngati munthu apereka sawatcha ndiyeno amapitirizabe kuba ndalama za dzikolo, amalandira ziphuphu, apeŵa msonkho, amachita mbanda, ndi zina zotero, kodi munthuyo anganenedwe kukhala wokhulupirika? Izo nzimene ‘Akristu’ athu akuchita. Iwo amapereka sawatcha ku mbendera pa bwalo la perete ndipo ngakhale kuzitenga kupita nazo kumalo awo olambirira kukapereka sawatcha kwa izo kumeneko. Akristu ena anthuni! Sindine wangwiro kapena wabwino m’maso mwa Mulungu, ndikudziŵatu chimenecho. Koma imeneyi sindiyo njira yake mwachibadwa.
“Inu Mboni mumakana kupereka sawatcha ku mbendera, kulandira kuthiridwa mwazi, kusunga Krisimasi ndi Isitala ndipo ndimawu amphamvu koposa mumakana kuchita upandu, kuba ndalama, chiphuphu, ndi mbanda. Ndipo mumakana kuchita chigololo ndi dama. Tatchulani zoipa zonse, ndipo Mboni nzotsimikizira kukana.
“Ndikukhulupirira ndi kupemphera kuti boma lidzawona machenjera osokeretsawo ndi kupatsa tchalitchi chanu ufulu wake wakuphunzitsa.”