Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 9/8 tsamba 17-18
  • Malo Omwe Maseŵera Ali Nawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Malo Omwe Maseŵera Ali Nawo
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugogomezeredwa Kwakale kwa Maseŵera
  • Maseŵera mu “Chipangano Chatsopano”
  • Malo Oyenera a Maseŵera Olimbitsa Thupi
  • Kodi Mpikisano m’Maseŵero Ngwoipa?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Ndiyenera Kuchita Maseŵero Apakompyuta Kapena Apavidiyo?
    Galamukani!—1996
  • Kodi Ndiyenera Kuganizira Mfundo Ziti pa Nkhani ya Masewera?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kuika Maseŵera m’Malo Ake Oyenera
    Galamukani!—1991
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 9/8 tsamba 17-18

Malo Omwe Maseŵera Ali Nawo

MLENGI Wamkulu amafotokozedwa m’Baibulo kukhala “Mulungu wachimwemwe,” ndipo amafuna kuti zolengedwa zake zikhale zachimwemwe. (1 Timoteo 1:11, NW) Chotero sikuyenera kutidabwitsa kuti analenga anthu okhala ndi kuthekera kwa kusangalala ndi maseŵera. Chotero, The New Encyclopædia Britannica imasimba kuti: “Mbiri ya maseŵera ndi zisudzo iri mbali ya mbiri ya anthu.”

Kukhalapo kwa mpira kukunenedwa kukhala mbali yaikulu m’mbiri ya maseŵera. “Mfundo yakuti nyama zimasangalala ndi kujidimuka ndi zoseŵerera kumapereka lingaliro lakuti pangakhale panalibe nthaŵi . . . pamene choloŵa mmalo mpira sichinali kuseŵeredwa mochithamangitsa kapena kuponyedwa,” likutero bukhu lanazonse logwidwa mawu pamwambapa.

Mosangalatsa, zipangizo zina zakhala zikugwiritsiridwanso ntchito kwanthaŵi yaitali kumenyera mpira. “Ndithudi panali maseŵera omenya mpira ndi ndodo omwe anaseŵeredwa ndi Aperesi, Agiriki, ndi Amwenye a ku Amereka,” ikutero Britannica. Mwachiwonekere “liwu lakuti Polo, lochokera ku Tibeti linali lotchuka mumpangidwe wakutiwakuti kwa Aperesi m’nthaŵi ya Dariyo I (yemwe analamulira mu 522-486 BC). Ngakhale kuti Scotland imanena kuti inayambitsa maseŵera a golf mumpangidwe wake wamakono, maseŵerawo adali ndi mbiri yolemekezeka m’nthaŵi ya Roma ndi m’maiko ambiri a ku Ulaya.”

Kugogomezeredwa Kwakale kwa Maseŵera

Zaka mazana ambiri kulembedwa kwa Malemba Achihebri (“Chipangano Chakale”) kusanathe, maseŵera olinganizidwa anali otchuka. Mwachitsanzo, maseŵera anali kuchitidwa pambuyo pazaka zinayi zirizonse ku Olympia wamakedzana, m’Grisi. Britannica ikusimba kuti: “Pali zolembedwa za ngwazi za ku Olympia kuyambira 776 BC mpaka AD 217,” kapena kwa pafupifupi zaka chikwi chimodzi! Maseŵera a Olympic anali ofunika koposa m’moyo Wachigiriki kwakuti anagwiritsiridwa ntchito kuŵerengera nthaŵi, nyengo iriyonse ya zaka zinayi yokhala pakati pa maseŵerawo inatchedwa Olympiad. Chotero, mogwirizana ndi njira yoŵerengera nthaŵi yakaleyo, Yesu Kristu anabadwa mkati mwa Olympiad ya 194.

Malemba Achihebri samanena kalikonse ponena za maseŵera olinganizidwa, ngakhale kuti mmodzi wa aneneri amalankhula za ‘misewu ya [Yerusalemu yokhala ndi] ana aamuna ndi aakazi akuseŵera.’ (Zekariya 8:5) Kwa zaka zoposa zana limodzi Yesu asanabadwe, mipikisano Yachigiriki ya maseŵera olira nyonga inayambitsidwa m’Israyeli. Sukulu yophunzitsa maseŵera olimbitsa thupi inakhazikitsidwa m’Yerusalemu, ndipo ngakhale ansembe ena ananyalanyaza maudindo awo kuti akaseŵere.—2 Maccabees 4:12-15.

Kaisara Augusto, wolamulira Wachiroma pamene Yesu anabadwa, ankakonda maseŵera olira nyonga, ndipo maseŵera anakhala otchuka m’Roma. Komabe, zochitika zomwe zinakondweretsa kwenikweni nzika za Roma zinali zija zoloŵetsamo kumenyana, monga ngati maseŵera a nkhonya ndi opingana ndale. Kaŵirikaŵiri “maseŵera” ameneŵa anatulukira m’kulimbana kwachiwawa ndi kokhetsa mwazi mmene anthu anayang’anizana okhaokha kapena ndi zirombo kumenyana kufikira imfa.

Maseŵera mu “Chipangano Chatsopano”

Komabe, kuchita maseŵera mwanjira zolakwika zoterozo sikunatanthauze kuti kuwaseŵera kunali koipa. Sitimaŵerenga konse m’Malemba za Yesu kapena otsatira ake akutsutsa maseŵera kapena kuwaseŵera. Mmalomwake, kaŵirikaŵiri atumwi anagwiritsira ntchito mbali za maseŵera kufotokoza mwafanizo mfundo zophunzitsira.

Mwachitsanzo, mwachiwonekere mtumwi Paulo anali kulingalira za maseŵera othamanga m’Maseŵera a Olympic pamene analimbikitsa Akristu kuti: ‘Kodi simudziŵa kuti iwo akuchita makani a liŵiro, athamangadi onse, koma mmodzi alandira mfupo? Motero thamangani, kuti mukalandire.’ Anawonjezera kuti: ‘Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.’—1 Akorinto 9:24, 25.

Pachochitika china, Paulo ananena kuti Mkristu ayenera kuthamanga motsimikiza mtima kuti apate mphotho ya moyo. Analemba kuti: “Ndilondetsa polekezerapo, kutsatira mfupo wa maitanidwe akumwamba a Mulungu.” (Afilipi 3:14) Ndiponso, pofotokoza mwafanizo kufunika kwa kumamatira ku malamulo a moyo wa makhalidwe abwino, Paulo anakumbutsa Timoteo kuti: ‘Koma ngatinso wina ayesana nawo m’makani a maseŵero, samveka korona ngati sanayesana [mogwirizana ndi malamulo, NW].’ (2 Timoteo 2:5) Ndipo mtumwi Petro analemba kuti abusa Achikristu amene amakwaniritsa mathayo awo ‘adzalandira korona wa ulemerero, wosafota.’—1 Petro 5:4.

Mosakaikira, Timoteo wachichepereyo anali kuweta Akristu achichepere amene anasangalala ndi maseŵera. Chotero, Paulo anamlembera kuti ‘chizoloŵezi cha thupi [monga wochita maseŵera olimbitsa thupi] chipindula pang’ono,’ mwakutero kuvomereza kuti maseŵera olimbitsa thupi ochitidwa mwamphamvu ndi Agiriki analiko ndi phindu. Mwamsanga Paulo anawonjezera kuti: ‘Koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.’—1 Timoteo 4:8; onani The Kingdom Interlinear Translation of the Greek Scriptures.

Malo Oyenera a Maseŵera Olimbitsa Thupi

Chotero Malemba amasonyeza kuti maseŵera olimbitsa thupi angakhale ndi malo oyenera m’moyo. Komabe, pamafunikira kukhala wachikatikati, ndi wolingalira. “[Kulingalira, NW] kwanu kuzindikirike ndi anthu onse,” analemba motero Paulo. (Afilipi 4:5) Komabe, kuli kovuta chotani nanga kukhala wachikatikati!

Agiriki akale anagogomezera maseŵera mopambanitsa, ndipo Aroma anachita mitundu ina imene inavulaza otengamo mbali limodzinso ndi okondweretsedwa ndi maseŵera achiwawa. Kumbali ina, anthu ena atsutsa ndi kuletsadi maseŵera m’dzina la chipembedzo. The New Encyclopædia Britannica inanena kuti: “Malingaliro onkitsa otsutsa kusanguluka a m’zaka za zana la 17 anachepetsa zosangulutsa ku Ulaya ndi Amereka.”

Posachedwapa maseŵera abukanso mwinamwake mosafanana konse m’mbiri. “Ngachiŵiri ku nyengo,” ikutero The World Book Encyclopedia, “mwinamwake anthu amalankhula zambiri ponena za maseŵera koposa nkhani ina iriyonse.” Maseŵera anenedwadi kukhala “omwereketsa mofanana ndi mankhwala ogodomalitsa.”

Kodi ndimavuto ati amene changu chotero cha maseŵera chapanga? Kodi inuyo kapena banja lanu mukuvutika ndi ziyambukiro zirizonse zoipa zotuluka m’changu cha maseŵera? Kodi ndimotani mmene mungaikire maseŵera m’malo ake oyenera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena