Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingachikanize Motani Chitsenderezo cha Kusuta?
“Kumandipatsa mpumulo, kumandisangalatsa ndi kundipatsa mtendere.”
“Ndikotaira nthaŵi.”
“Kumakupangitsa kudzimva wosungika koposa.”
‘Ndichinthu chomwe ndiyenera kuchita ndi manja anga.’
IZI zinali zifukwa zimene achichepere ena anapereka pamene anafunsidwa chifukwa chake iwo amasuta. (Teens Speak Out) Inde, mosasamala kanthu za machenjezo onena za kansa yamapapo, emphysema, ndi nthenda ya mtima, kusuta kudakali ndi chisonkhezero chosapeŵeka kwa achichepere ambiri. Mwinamwake mungakhale munayesedwapo kuyesa kusuta inu mwini.
Osatsa malonda amakubweretserani zithunzithunzi za amuna ndi akazi omwe amasuta nthaŵi zonse, okongola ndi ovala bwino. Palibe ndimmodzi yemwe wa iwo amawoneka kukhala wodwala kansa. Kapena mungakhale pansi pachitsenderezo cha mabwenzi chakuyesa kusuta. Mungavutitsidwe ndi zisonkhezero zoipa kusukulu zonga izi: ‘Kodi ndiwe wogona?’ ‘Munthu aliyense wochangamuka amasuta.’ Ndipo ngati muli pakati pa achichepere omwe amasuta, mungadzimve kusalinga m’gululo ngati mulibe ndudu m’dzanja lanu.
Chitsenderezo cha kusuta chikhozanso kuchokera kunyumba. Mungasokonezeke kwambiri ngati kholo lanu limodzi limapewa kusuta koma linalo limasuta. Ndipo ngati makolo onse aŵiri amasuta, chitsenderezo chikhoza kukhala chachikulu kwambiri. ‘Makolo anga amasuta pafupifupi mapaketi aŵiri patsiku, chotero nthaŵi zonse ndudu zimakhala pafupi,’ anatero Rebecca, wazaka 14 zakubadwa. Kuuzidwa ndi makolo otero kuti simuyenera kusuta kungawoneke kukhala chinyengo chenicheni! Allison wachichepere akudandaula kuti: “Pamene tiuza makolo kuti timadera nkhaŵa thanzi lawo, iwo samamvetsera. Chotero kodi ndimotani mmene iwo angatiyembekezere kuwamvetsera?”—The Private Life of the American Teenager.
Zirizonse zimene zingakhale zifukwa zawo, achichepere ambiri amasankha kuyesa kusuta ndipo nthaŵi zambiri amakhala omwerekera m’moyo wawo wonse.a Ndithudi, inu mukufuna kanthu kena kabwinopo kaamba ka inu mwini. Mumadziŵa zotulukapo zoipa za kusuta ndi kuwona kuti palibe chifukwa chimene muyenera kukhalira woyamba kuyang’anizana nazo. Chikhalirechobe, mungafune kudziŵa mmene mungalimbanire ndi zitsenderezo za kusuta.
Kusayenerana ndi Chitaganya
Choyamba tiyeni tipende zifukwa zina za kusuta zimene achichepere amapereka. Mofanana ndi achichepere ogwidwa mawu poyamba, ambiri amanenetsa kuti kugwira ndudu kumaŵapangitsa kuwoneka ofikapo ndi “achikulire.” Oren wachichepere anazikhulupirira zimenezi kukhala zowona kwa iye. Pokhala wosayenerana kwambiri ndi chitaganya, iye amakumbukira kuti: “Ndinali wosakhazikika kwenikweni, makamaka pamapwando. Sindinadziŵe konse zimene ndinayenera kuchita kapena kunena. Kusuta kunawonekera kukhala yankho lothetsera vuto langa.”
Komabe, kusuta utsi waululu kumangochititsa munthuwe kuwoneka wopusa, wopanda chisungiko, ndi wosalingalira ena. Chiŵerengero chomawonjezereka cha achichepere ayamba kuiwona motero nkhaniyi. M’kufufuza kochitidwa ndi Jane Rinzler, 63 peresenti ya asungwana ndi 73 peresenti ya anyamata omwe anafunsidwa anatsutsa kusuta! Msungwana wina wazaka 16 zakubadwa anati: “Anthu amalingalira kuti [kusuta] kumaŵapangitsa kuwoneka apamwamba, koma kukuwoneka kuti iwo akungoyesera mopambanitsa.” Ngakhale ngati kusuta kunapangitsadi wina “kuwoneka wapamwamba,” kodi kukalungamitsa kuchita chizoloŵezi chakupha ndi chomwerekeretsa?
Komabe, chokondweretsa ndichimene Maurice Falk, profesa wa nthenda zamaganizo za ana, akunena kuti: “Achichepere omwe amadziŵa chochita m’zochitika za chitaganya samadzimva kwenikweni kukhala osayenerera. . . . [Iwo] sali othekera kwenikweni kusuta.” Zimenezi zatsimikizira kukhala zowona kwa achichepere ambiri pakati pa Mboni za Yehova. Iwo amakulitsa kukhazikika ndi chidaliro mwakulankhula ndi anthu a misinkhu yonse m’ntchito yapoyera yolalikira. Mwakugwiritsira ntchito mokwanira programu yophunzitsa yoperekedwa pamisonkhano Yachikristu pa Nyumba Yaufumu, amaphunziranso kulankhula mwaluso ndi modzichepetsa pamaso pa omvera. Zimenezi zimakhozetsa munthu kusadalira pa chinachake kuti akhale wosatekeseka poyanjana ndi anthu.
Ngati mumadzimva wosakondwa kapena wamanyazi kapena wosakhazikika pakati pa anthu, pamenepo yesani kugwirizana mwathithithi ndi mpingo wa Akristu owona. Kuli kovuta kukhalabe wamanyazi kwanthaŵi yaitali pamene muyanjana ndi ena mokangalika. Mukhozanso kukambitsirana ndi makolo anu ponena za nkhaŵa zanu. Komabe, kumbukirani kuti mumadzipezera ulemu kwa ena, osati mwakugwedeza ndudu ku milomo yanu, koma mwakukhala monga momwe Baibulo limafulumizira: ‘Chitsanzo . . . m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.’—1 Timoteo 4:12.
“Kumandipatsa Mpumulo”
Bwanji ponena za zimene ena amanena kuti kusuta ndikachitidwe kosangalatsa? Alvin Rosenbaum, wolemba nkhani akutero kuti: “Osuta ena amanena kuti sangapeze mpumulo popanda ndudu, kuti kusuta kumathetsa kukwinjika, nkhaŵa, ndi mkwiyo.” Komabe, mmalo mokhala chodzetsa mpumulo, “chikonga ndichotsitsimula,” akutero Rosenbaum.
Nangano nchiyani chimene chimachititsa mpumulo umene wosutayo amamva? Kwenikwenidi, chimene wosutayo amamva ndicho mpumulo wodzetsedwa ndikukhutiritsidwa kwa kumwerekera! Inde, anthu amakhala omwerekera ndi chikonga chopezeka m’fodya. Kumwerekera kumeneku kulidi kofanana kwenikweni ndi kumwerekera ndi heroin kapena cocaine, ndipo ena amanena kuti kuli kovutirapo kukulaka.
Pamene thupi la wosuta lisoŵa chikonga, limayamba kuchilakalaka. Iye amakhala wosakhazikika, wokwinjika, ndi wokwiitsidwa kufikira “atakhutanso” chikonga. Iye amadzimva kukhala ndi mpumulo mwakanthaŵi—kufikira pamene thupi lake lidzalakalakanso chikonga. Chotero kusuta kuli njira yopusa yopezera mpumulo. Kumvetsera kunyimbo zosangulutsa, kuŵerenga, ndi kupita kokayenda ziri njira zachisungiko koposa.
Kulimbana ndi Chitsenderezo cha Ausinkhu Wanu
George, wazaka 14 zakubadwa, akusimba kuti: “Achichepere ambiri amandipatsa ndudu ndipo ndimangowanyalanyaza.” Chitsenderezo cha ausinkhu wanu chikuwonekera kukhala chifukwa chachikulu chimene achichepere ambiri amayambira kusuta. Kufufuza kwina kwa achichepere kunavumbula kuti ‘ochepera pa 1 peresenti anasuta ngati panalibe mmodzi wa mabwenzi awo anasuta, pamene kuli kwakuti 73 peresenti anasuta pamene mabwenzi awo onse anasuta.’ Ngati mukutsenderezedwa ndi ausinkhu wanu, mungafunse kuti: ‘Kodi cholakwika nchiyani ndi kusuta kamodzi kotero kuti ena asamandivute?’
Achichepere ena oleredwa m’mabanja Achikristu alingalira kuti sikukakhala kolakwika kwambiri ndipo alolera molakwa chikhulupiriro chawo.b Angapo avomera kuti anagwira ndudu m’dzanja lawo kapena ngakhale kuiika kukamwa kwawo—kotero kuti ‘akhale ofanana ndi ena.’ Komabe, Baibulo limati: ‘Mwananga, akakukopa ochimwa usalole.’ (Miyambo 1:10) Ndipo unyinji wa achichepere oleredwa m’mabanja Achikristu akulabadira mawu ameneŵa kuubwino wawo. Mwachitsanzo, Maribel wazaka 14 zakubadwa, anapatsidwa ndudu ndi anansi ake, ndipo anaikana. Iye akukumbukira kuti: “Iwo anayamba kundipeŵa ndi kundinyodola.” Komabe, iye anakumbukira kuti, ‘kuli bwino kukhala ndi chivomerezo cha Mulungu kuposa cha dziko’ ndipo sanagonje ku chitsenderezocho!
Kwenikwenidi, kodi ndimabwenzi otani amene akakufulumizani kusuta chinthu chakupha? ‘Mnzawo wa opusa adzapwetekedwa,’ imachenjeza motero Miyambo 13:20. Ngati kuli kofunika, funani mabwenzi ena atsopano. Eya, kungokhala pafupi ndi osuta nkwaupandu ku thanzi! Brenda wazaka 15 zakubadwa akuti: “Palibe ndimmodzi wa mabwenzi anga yemwe amasuta. Chotero ndiribe vuto lirilonse la chitsenderezo cha mabwenzi.”
Komabe, kungakhale kosatheka kwa inu kupeŵa kotheratu achichepere osakhala Akristu. Mukafunikira kutetezera zikhulupiriro zanu ndi kukana kusuta kwa mtu wagalu! Izi sizitanthauza kwenikweni kuti muyenera kuwapatsa ulaliki wa maupandu a fodya. Sharon Scott, wolemba nkhani, akulongosola kuti kaŵirikaŵiri kungonena kuti “ayi, sindifuna” kumagwira ntchito. Iye akulimbikitsa kuti pamene zimenezi zalephera, kanani ndi mawu amphamvu kuti, “Ndati SINDIFUNA!”
Njira zina ndizo kuchoka pamalowo, kunyalanyaza choperekedwacho, kapena kungosintha nkhani. Mungayesezedi pasadakhale mmene mudzachikanira chitsenderezo cha kusuta. Ndipo ngati malongosoledwe atsatanetsatane angafunidwe, muyenera kukhala wokonzekera kuwapereka. Mongadi mmene Baibulo limanenera kuti: ‘Konzekerani nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wakukufunsani chifukwa.’—1 Petro 3:15.c
Maphunziro Abaibulo operekedwa pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova athandiza ambiri kuleka kusuta. Oren akukumbukira kuti: “Chikhumbo cha kulankhula kwa ena za kukhala ndi moyo kosatha ndi thanzi langwiro padziko lapansi laparadaiso loyeretsedwa kunandipatsa chisonkhezero cha kuleka.” Njira yanzeru ndiyo kusayamba konse kusuta!—Akolose 4:5.
[Mawu a M’munsi]
a Zigawo zitatu mwa zinayi za osuta ku United States anayamba kusuta asanakwanitse zaka 21. M’kufufuza kwina theka la gulu la osuta achichepere anasuta ndudu yoyamba asanamalize sukulu yapulaimale.
b Ngati munayesapo kusuta fodya mseri, chonde funani chithandizo mwakuwadziŵitsa makolo anu vutolo. (Miyambo 28:13) Iwo angakwiye atadziŵa vuto lanu. Koma ngati iwo ndi Akristu, adzasumika malingaliro pa kukuthandizani kupeŵa kubwereza cholakwacho kukwiya kwawo koyamba kutatha. Oyang’anira mumpingo wakumaloko wa Mboni za Yehova angakhalenso othandiza kwambiri ndi achilimbikitso kwa inu ponena za nkhaniyi.—Yakobo 5:14, 15.
c Onani kope la Galamukani! la August 8, 1991, kaamba ka chidziŵitso chonena za maupandu a kusuta.
[Chithunzi patsamba 12]
Mmalo mopangitsa wina kuwoneka wachikulire, kusuta kungasonyeze kupanda chisungiko