Kulera Mabanja Padziko Lonse Kusonyeza Ukholo Mwachikondi, Chilango, Chitsanzo, ndi Makhalidwe Auzimu
MAKOLO ochokera kumaiko angapo atumiza malipoti onena za chipambano chawo m’kulera ana kuyambira kuukhanda mpaka kupyola zaka za pakati pa 13 ndi 19. Onse ndi Mboni za Yehova, chotero malipoti awo akugogomezera kufunika kwa kupereka chisamaliro ku mbali zinayi zondandalikidwa m’mutu wapamwambapa. Mawu achidule olembedwanso munomu akungosonyeza mbali zochepa zosiyana za kuphunzitsa banja zimene anatsatira.
Kuchokera ku Hawaii
“Monga momwe Baibulo limatiuzira, chikondi ndicho mkhalidwe ‘waukulu koposa.’ Chikondi m’mbali zake zonse zamtengo wake chiyenera kusonyezedwa panyumba ndi m’banja. Carol ndi ine takhala ndi mkhalidwe waumulungu umenewu muukwati wathu. Ndife ogwirizana. Timakonda kukhalira pamodzi. Sindingagogomezere mopambanitsa chikhulupiriro changa chakuti mfungulo yeniyeni ya kulera mwana kwachipambano ndiyo okwatirana achimwemwe.
“Ndimakumbukira bwino lomwe ngakhale lerolino malingaliro amphamvu omwe anabuka mumtima mwanga mkati mwa masiku ndi milungu yotsatirapo pamene mwana wathu woyamba anabadwa. Tinazizwa ndi kuyambika kwa cholengedwa chamoyo chatsopanocho. Ndikukumbukira kuwona Carol ali wachimwemwe ndi wokhutira poyamwitsa khandalo Rachel. Ndinasangalala naye, koma ndinadzimva kukhala wokankhidwira pambali pang’ono, wansanje pang’ono. Carol anali kugwirizana ndi Rachel, koma kodi unansi wanga ndi khandalo unali wotani? Ndinamva ngati kuti ndakankhidwa—mwapang’onopang’ono komabe ndinakankhidwira—kunja kwa maziko a banja lathu. Ndi thandizo la Yehova ndinali wokhoza kufotokoza malingaliro anga ndi kudera nkhaŵa kwanga kwa Carol, ndipo anasonyeza chifundo chachikulu ndi chichirikizo.
“Pambuyo pake ndinali wokhoza kuyandikana ndi khanda lathu latsopano mwakuthandiza kuchita ntchito zonse za khandalo, kuphatikizapo zosakondedwa—kuchapa theŵera losomeredwa kulidi chokumana nacho chapadera! Tinakhala ndi ana ena asanu pambuyo pa Rachel. Rebecca ndiye womalizira, tsopano ali ndi zaka zisanu ndi zitatu. Tinachititsa maphunziro Abaibulo, aumwini ndi aliyense wa ana athu.
“Chinthu china ponena za kulera ana koyambirira nchakuti, Carol ndi ine tinasangalala kulankhula ndi ana athu kuyambira pamene anabadwa. Tinalankhula nawo ponena za zinthu zonse. Nthaŵi zina tinalankhula za Yehova ndi ntchito zake zokongola, zodabwitsa. Nthaŵi zina tinalankhula za zinthu zopusa, zamaseŵera, zoseketsa. Ndithudi, tinali kuyesayesa kuwaphunzitsa chinachake, koma koposa chimenecho tinali kungokhalira pamodzi mosangalala, mopumula. Ndikhulupira kuti kulankhula koteroko kunathandizira kwakukulu kugwirizana kwa pakati pa kholo ndi mwana. Mosakaikira zinathandiza kupangitsa kulankhulana kwabwino komwe tiri nako m’banja mwathu.
“Yehova watiphunzitsa phindu lalikulu la zinthu zauzimu, kudzipereka enife. Carol ndi ine sitinakhalepo ndi zinthu zakuthupi zochuluka, koma sitinazifunefune kwenikweni kapena kuzilakalaka. Ngati tikanathera nthaŵi yathu yochuluka kufunafuna chuma, sitikanakhala ndi nthaŵi yokwanira kuipereka kwa Yehova ndi banja lathu. Tinapanga chosankha cholondola.” (Ndemanga za Carol zikutsatira.)
“Ndiganiza kuti kulera makanda anu kumathandiza kwakuluku kugwirizanitsa makanda ndi anakubala awo. Mumathera nthaŵi yochuluka kwambiri kufukata ndi kunyamula khanda lanu kwakuti simungathe kuleka kuyandikana nalo. Nakubalayo samachoka kumbali kwa khandalo kwa maola oposa aŵiri kapena anayi. Ed ndi ine tinali osamalitsa kusalola kusiira ana athu alezi. Nthaŵi zonse ndinafuna kukhala wokhoza kuphunzitsa makanda anga ndikuwawona akukula. Chotero m’nthaŵi imene anali aang’ono, sindinayambe ntchito yakuthupi. Ndiganiza kuti izi zinawathandiza kuzindikira mmene analiri ofunika kwa ife. Njira yeniyeni yoyandikirana ndi ana anu ndiyo kukhala nawo kwanthaŵi yaitali. Palibe chimene chimatenga malo a kukhala kwanu panyumba. Zinthu zonse zakuthupi sizidzatenga malo anu.
“Zaka zapakati pa 13 ndi 19 zinali zovuta kokha chifukwa chakuti ndinayenera kusintha molingana ndi kukula kwa makandawo. Chinali chovuta kuchilaka, kuzindikira kuti sanandifune mokulira ndipo anali kukhala odzidalira. Ndinthaŵi yochititsa mantha, ndipo imaika pachiyeso ntchito yanu yonse yophunzitsa, kulanga, ndi kuwongolera yomwe munachita. Kulidi kuchedwa kwenikweni kuyamba pamene ali azaka zapakati pa 13 ndi 19. Nkuchedwa kwenikweni kuyesa kuwaphunzitsa makhalidwe, kukonda anthu, ndipo makamaka kukonda Yehova. Zinthuzi ziyenera kukhomerezedwa kuyambira pamene abadwa kumka mtsogolo.
“Muli ndi zaka 12 kuti mumalize ntchito yanu zaka zapakati pa 13 ndi 19 zisanafike. Koma ngati munagwira ntchito zolimba kugwiritsira ntchito malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo, iri nthaŵi yakututa chimwemwe ndi mtendere pamene asankha kutumikira Yehova kuchokera mumtima.”—Edward ndi Carol Owens.
Kuchokera ku Zimbabwe
“Ana ndiwo ‘cholandira cha kwa Yehova.’ Limatero Baibulo pa Salmo 127:3. Kukumbukira chimenechi kwatithandiza ife monga makolo kuchita zonse zomwe tingakhoze m’kusamalira cholandira chimenechi. Chimodzi cha zoyesayesa zoyambirira za banja lathu chinali kuchitira zinthu pamodzi—kupempherera pamodzi, kuphunzirira Baibulo pamodzi, kulambirira pamodzi, kugwirira ntchito pamodzi, kuchezera mabwenzi pamodzi, kuseŵerera pamodzi.
“Chilango chinafunikira nthaŵi zina. Nthaŵi ina mwana wathu wamwamuna, kuchiyambi kwa zaka zake zapakati pa 13 ndi 19, anachedwa kufika panyumba. Tinadera nkhaŵa. Anachita mantha. Tinadziŵa kuti chinachake chalakwika, koma tinasankha kusatchula nkhaniyo kufikira m’maŵa wotsatira. Chapakati pausiku tinamva kugogoda pakhomo la chipinda chathu chogona. Anali mwana wathuyo, misozi iri m’maso.
“‘Atate, Amayi, ndalephera kugona kwa maola anayi apitawa, zonsezi nchifukwa chakuti sindinakumvereni pamene munandipatsa uphungu wochokera m’Baibulo wonena za mayanjano oipa. Lero pambuyo pa sukulu anyamata ena anandikakamiza kupita kukasambira nawo, ndipo mmodzi wa anyamatawo anandikanikizira pansi pamadzi. Ngati mnyamata wina sakanandithandiza, ndikanamira. Anandiseka ndikunditcha wamantha. Ndinabwera kunyumba nthaŵi yomweyo, koma ndinali kunja kwa nyumba chifukwa ndinadzimva waliŵongo. Pepani kuti sindinakumvereni pamene munandichenjeza za mayanjano oipa, monga momwe kwasonyezedwera m’Baibulo.’—1 Akorinto 15:33.
“Analira ndipo nafenso tinalira. Tinakondwera kuti anaphunzira phunziro, koma tinamlanga kuti amvetsetse. Eksodo 34:6, 7 amasonyeza kuti Yehova ngwachifundo ndipo amakhululuka mphulupulu, komabe ‘samasula wopalamula.’”—David ndi Betty Mupfururirwa.
Kuchokera ku Brazil
“Ndine mkazi wamasiye ndipo ndiyenera kulera ndekha mnyamata wanga. Panthaŵi imodzimodziyo, ndimagwira ntchito yauphunzitsi. Sikuli kokhweka kulangiza ndi kulanga ana. Komwe kumafunikira ndiko kulangiza kogwirizanika, chilango cholinganizika, ndi chitsanzo chabwino cha makolo. Kunali kovuta kwa ine kukhala wolimba ndipo panthaŵi imodzimodziyo wachifundo. Ndinayenera kukulitsa luso lakumvetsera, makamaka kumvetsera ndi mtima wanga. Kulankhulana kuli kofunika, osati kungokamba, koma kumuloŵetsamo mwanayo, kumpangitsa kuvomereza ndi malingaliro. Ndinayesa kumpangitsa kudzimva kukhala mbali ya banja mwakumuloŵetsamo m’kupanga bajeti ya banja. Pamene ngongole ya magetsi kapena madzi inafika, kapena pamene mitengo ya zovala kapena nsapato inakwera, tinakambitsirana pamodzi nkhani zimenezi.
“Kulinso kofunika kuyamikira mowona mtima pamene zinthu zachitidwa bwino. Pamene mwaŵi ubuka, ndimamsonyeza phindu lakutsatira malamulo ndi malamulo amakhalidwe abwino a Mulungu. Panthaŵi ina, pambuyo pomlangiza nthaŵi zingapo, ndinafunikira kugwiritsira ntchito nthyole yeniyeni. Ha, kunali kovuta motani nanga kwa ine, komabe, panatuluka zotulukapo zodalitsika zotani nanga! M’zaka zaunamwali timakhala ndi nthaŵi zathu zabwino ndi zoipa, koma tingawone phindu lakulangiza ndi kupereka chilango. Iye amandiuza mavuto ake aumwini ndikufotokoza malingaliro ake.
“Ndifunikira kukhala wamaso kuti tikhalebe ndi kulankhulana kwabwino. Chotero ndimayesa kupeŵa kukhala wotanganitsidwa kotheratu ndi ntchito yanga yakuthupi kotero kuti nthaŵi zonse ndipeze nthaŵi yokhala ndi mwana wanga. Pamene tikhala ndi mavuto, ndimayesera kumvetsera mwatcheru, ndipo ndichithandizo cha Yehova, timawalaka. Ndimamulola kudziŵa kuti nanenso ndimapanga zophophonya. Panthaŵi ina ndinakwiya kwambiri, ndipo ndinamuuza kuti ‘atseke pakamwa pake.’ Iye anandiuza kuti kuuza munthu wina kuti ‘atseke pakamwa pake’ kumasonyeza kusoŵeka kwa chikondi. Ananena zowona. Masana amenewo tinakambitsirana kwa nthaŵi yaitalidi.”—Yolanda Moraes.
Kuchokera ku Ripabuliki la Korea
“Ndinagwiritsira ntchito mosamalitsa malamulo amakhalidwe abwino Abaibulo m’moyo wa banja langa. Makamaka mawu a pa Deuteronomo 6:6-9 ndiwo anazama mumtima mwanga. Chotero ndinayesera kukhala ndi ana anga mochulukira monga momwe ndinathera, kuyandikana nawo, kuzamitsa malamulo amakhalidwe abwino a Mawu a Mulungu m’maganizo ndi mitima yawo. Ndinaitananso amishonale anthaŵi zonse ndi ziŵalo za banja la Beteli kunyumba kwathu kuti ana anga akhale ndi mzimu wa utumiki wanthaŵi zonse.
“Chinthu choyamba chimene makolo ayenera kuchita pamene ana apangitsa mavuto ndicho kusonyeza chipatso cha mzimu. Kuli kwapafupi kukwiya nawo anawo ndikukalipa. Komabe, makolofe tiyenera kukhala oleza mtima ndikusonyeza khalidwe labwino. Kuli kofunika kulemekeza ana ndikuwapatsa mwaŵi wakufotokoza mkhalidwewo. Ngati palibe umboni wokwanira wa kuchita cholakwa, pamenepo akhulupirireni ndipo amangirireni nthaŵi zonse. Pamene mufunikira kulanga mwana, choyamba kambitsiranani naye, musonyezeni kuti chimene anachita chinali cholakwa, ndipo sonyezani mmene machitidwe ake analiri osakondweretsa kwa Yehova ndi kwa makolo ake. Pokhapo mpamene mungaperekeno chilango. Kaŵirikaŵiri ana anga aamuna pambuyo popatsidwa chilango amanena kuti: ‘Atate, sindikumvetsetsa kuti nchifukwa ninji ndinali wopanduka. Ndinali wopusa.’ Iwo amayamikira makolo amene amasamala mokwanira kufikira pakuwapatsa chilango.
“Makolo afunikira kukhala maso ku kuyambika kwa khalidwe loipa. Pamene mwana wanga wamwamuna wamkulu anali m’kalasi lachitatu la sukulu ya sekondale, ndinamva nyimbo zokwera za rock zikuchokera m’chipinda chake. Ndinapeza kuti anagwirizana ndi gulu la ophunzira opereka chilango (ophunzira achikulire, achitsanzo chabwino omwe anali kupereka uphungu kwa ophunzira anzawo), ndipo anavumbulutsidwa ku zisonkhezero zakudziko. Ndinadziŵanso kuti pansi pa chididikizo chosalekeza kuchokera kwa anzake a m’gululo ndi kufunitsitsa kudziŵa, anasuta. Tinakambitsirana pamodzi za maupandu a kusuta, ndipo mwana wangayo anagamula yekha kuti ayenera kuchoka m’gululo, ndipo anachokadi. Kuti tidzaze malo osiidwa ndi kuleka machitachita okaikiritsa akusukulu, tinakonza kukhala ndi zosangulutsa zabwino ndi ziŵalo za banja ndi mpingo.
“Pomalizira, ndikufuna kunena kuti chinthu chofunika koposa ndicho chakuti makolo akhazikitse chitsanzo chabwino. Nthaŵi zonse ndinauza anyamata anga kuti ndinafuna kutumikira Mulungu kwanthaŵi zonse monga minisitala wolalikira mbiri yabwino. Pamene mnyamata wanga wachiŵiri anamaliza sukulu, ndinakhoza kuleka ntchito pafakitale ya silika ndipo ndinakhala minisitala wanthaŵi zonse. Anyamata anga aŵiriwo anawona kutsimikiza mtima kwanga ndipo anatsanzira chitsanzo changa. Pambuyo potumikira m’ndende chifukwa cha nkhani ya uchete, onse aŵiri anayamba utumiki wanthaŵi zonse ndipo akupitirizabe mpaka pano.”—Shim Yoo Ki.
Kuchokera ku Sweden
“Talera ana asanu ndi aŵiri, anyamata asanu ndi asungwana aŵiri. Tsopano ngachikulire, onse ali okangalika kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu. Kuyambira pamsinkhu wachichepere, anawo anafika pamisonkhano yampingo ndipo anapita nafe muutumiki wakumunda. Pang’onopang’ono iwo anaphunzira kuchita ntchito yolalikira—kugogoda pakhomo, kupereka moni, kutchula dzina lawo, ndi kupereka handibilu, trakiti, kapena magazini. Pamene anali achichepere kwenikweni, anapereka nkhani m’Sukulu Yautumiki Wateokratiki.
“Nthaŵi zina mavuto aakulu anafunikira chisamaliro chapadera. Kusonyeza chikondi ndi kuleza mtima zinali zofunika panthaŵiyo—osati kufuula kapena kukangana. Mavuto anathetsedwa mwakukambitsirana zinthu ndi kugogomezera malingaliro a Yehova. Tinawaphunzitsa zinthu zokhudza ndalama. Pamene anakula, iwo anagwira ntchito yogaŵira manyuzipepala, kufutsa zokolola, kulima, ndi zina zotero. Kuchezera agogo awo okhala kutali kunawapangitsa kuzindikira mavuto a okalamba ndi kuwachitira chisoni.
“Patsiku lokumbukira kuti tatha zaka 30 paukwati wathu, tinalandira kalata yotsatirayi:
“‘Kwa Makolo Athu Okondedwa:
“‘TIKUTHOKOZANI KAAMBA KA ZONSE! Chikondi chabwino chimene munatisonyeza, chikhulupiriro chenicheni chimene munatipatsa, chiyembekezo chabwino koposa chimene mwatipatsa—izitu sizingapimidwe ndi mawu kapena ndalama. Komabe, tikukhulupirira kuti mwa chokumbukira chaching’ono ichi, mudzamvetsetsa mmene timamverera ponena za inu, atate ndi amayi athu okondedwa. [Inasainidwa] Ana anu.’
“Kuyang’ana m’mbuyo pa ‘maprojekiti ameneŵa a zaka 20,’ timakhala oyamikira kwa Yehova, Atate wathu wakumwamba, amene wakhala wachifundo kwa ife.”—Bertil ndi Britta Östberg.
Mfundo Zothandiza Zosiyanasiyana Zochokera kwa Makolo
“Kuyamwitsa ndiko njira ya Yehova yogwirizanitsira khanda ndi nakubala mwakuthupi, koma tate angawonjezereko ndi mpando wogwedeza. Ndinasangalala kwenikweni kunyamula ana athu m’manja mwanga ndikuwatonthoza kuti agone pafupifupi usiku uliwonse.”
“Monga tate wawo, sindinali wokonzekeretsedwa kuwayamwitsa ana athu, koma ndinakhala ndi kukhudzana kwakuthupi mwakuwasambitsa madzulo. Inali nthaŵi yosangalatsa kwa ine ndi iwo!”
“Kwanthaŵi ndi nthaŵi, ndinatenga aliyense wa ana athu, payekha, kukadya naye ndekha. Iwo amakonda nthaŵi imeneyi yokhala wekha ndi Atate.”
“Pamene nthaŵi inali kupita, mwapang’onopang’ono tinayamba kuwapatsa ufulu wokulirako ndi kuwaikiza mathayo. Waya wofwamphuka yemwe wakanikizidwa m’manja ayenera kutaidwa mwapang’onopang’ono kuwopera kuti angadumphe ndikuthaŵa.”
“Asonyezeni chikondi chochuluka. Palibe mwana amene anamwalira ndi kukupatiridwa ndi kumpsompsonedwa—koma malingaliro awo angafe popanda izo.”
“Khalani woleza mtima, musawakhwethemule. Musamawakalipire nthaŵi zonse. Aloleni akulitse ulemu waumwini. Ngati muwasuliza kamodzi ayamikireni nthaŵi zinayi!”
“Apatseni kuyesayesa kwanu kwabwino koposa, kuti akhale abwino koposa monga momwe angathere.”
[Chithunzi patsamba 26]
Ana achichepere monga Rebecca amafuna chikondi chenicheni
[Chithunzi patsamba 27]
Kupeza nthaŵi yochitira zinthu pamodzi kudzathandizira kupanga chomangira chabanja cholimba