Kodi Nchifukwa Ninji “Kunyengererako”?
Mu 1622, Pope Gregory XV anakhazikitsa mpingo, kapena komiti, ya makadinala 13, atsogoleri apamwamba achipembedzo 2 ndi mlembi kukayang’anira amishonale a Tchalitchi cha Roma Katolika. Iye anautcha kukhala Congregatio de Propaganda Fide—Mpingo Wofalitsa Chikhulupiriro—kapena mwachidule Propaganda (Kunyengerera). M’kupita kwanthaŵi liwu limeneli linafikira kutanthauza kuyesayesa kulikonse kwa kufalitsa malingaliro kapena zikhulupiriro kuchitira kutembenuza anthu.
Tsopano, liwulo “kunyengerera” kaŵirikaŵiri limagwirizanitsidwa ndi kuipitsa zenizeni, kusonkhezera monyenga malingaliro a anthu, mwachitsanzo monga m’nthaŵi za nkhondo. Koma olamulira ena amalingalira kuti kutsatsa malonda kwabwino kwambiri kungafotokozedwe bwino lomwe kukhala kunyengerera, makamaka ngati kukuphatikizapo kupseterera. The World Book Encyclopedia likuthirira ndemanga kuti: Aphunzitsi m’zitaganya zademokrase amaphunzitsa anthu mmene angalingalilire, koma onyengerera amaŵauza zoti alingalire.”