Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g91 11/8 tsamba 22-23
  • Kodi Mulungu Amatsutsa Kumwa Zakumwa Zoledzeretsa?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Amatsutsa Kumwa Zakumwa Zoledzeretsa?
  • Galamukani!—1991
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kugwiritsiridwa Ntchito kwa Vinyo m’Baibulo
  • Kodi Umasangalatsa ndi Kupereka Mapindu Athanzi?
  • Chikatikati ndi Kudziletsa Nzfunika
  • Zakumwa Zoledzeretsa Nchiyani Chomwe Chiri Kawonedwe Kachikristu ka Izo?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Kumwa Mowa N’kulakwa?
    Galamukani!—2006
  • Kodi Kumwa Mowa Mwauchidakwa N’koipadi?
    Galamukani!—2004
  • Mowa
    Galamukani!—2013
Onani Zambiri
Galamukani!—1991
g91 11/8 tsamba 22-23

Lingaliro la Baibulo

Kodi Mulungu Amatsutsa Kumwa Zakumwa Zoledzeretsa?

‘USAVUTIKE maganizo ndi chamba, heroini, LSD, ndi marijuana—zakumwa zoledzeretsa ndizo zimene ziri vuto lalikulu kwambiri losakondweretsa limene chitaganya chiyenera kulimbana nalo. Zakumwa zoledzeretsa zimachititsa imfa zochuluka kwambiri ndi kuwononga makhalidwe koposa mankhwala onse oledzeretsa atagwirizanitsidwa pamodzi.’ Ameneŵa ndimawu onenedwa pamsonkhano wochitidwa kamodzi m’zaka zitatu zirizonse wa 31 wa World’s Woman’s Christian Temperance Union ku Canada zaka ziŵiri zapitazo.

Nthumwi zoterozo zimawona kuwonongedwa kwa moyo ndi thanzi laumunthu kochititsa kakasi m’kumwedwa kwa zakumwa zoledzeretsa komakulakulabe, limodzinso ndi mamiliyoni ochuluka a madola amene adzawonongedwa chaka ndi chaka ndi maboma amaikowo polimbana ndi mkhalidwe wakumwa zakumwa zoledzeretsa. Pokhutiritsidwa maganizo kuti Mulungu amatsutsa kuzigwiritsira ntchito, anthu ochuluka otsimikiza amapereka zigomeko za kuletsedwa kwa zakumwa zonse zoledzeretsa. Koma kodi Baibulo limachirikiza lingaliro limenelo?

Kugwiritsiridwa Ntchito kwa Vinyo m’Baibulo

Kalelo Mulungu analonjeza anthu ake omvera kuti: “Motero nkhokwe zako zidzangoti the, mbiya zako zidzasefuka vinyo.” (Miyambo 3:10) Inde, Iye ndiye amene anatipatsa mpesa wobala zipatsowo, ngakhale kupereka tamoyo tating’ono totupitsa timene timakuta mpesawo pamene uli pafupi ndi nthaŵi yakupanga vinyo.

Njira yotulutsira vinyo wokuntha bwino inafotokozedwa mwapang’ono ndi mneneri wa Mulungu Yesaya. Powoneratu madalitso adziko latsopano lolungama lirinkudza, Yesaya analemba kuti: “Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse . . . phwando la vinyo wa pamitsokwe . . . la vinyo wansenga wokuntha bwino.” (Yesaya 25:6) Opanga vinyo achidziŵitso amadziŵa kuti vinyo “wansenga,” wosadodometsedwa kwanyengo yanthaŵi yaitali mkati mwa kuŵira, mwapang’onopang’ono amadzikonza, akumakometsera ponse paŵiri fungo ndi kukoma.

Kodi Umasangalatsa ndi Kupereka Mapindu Athanzi?

Mulungu analongosola zonse ziŵiri chisangalalo ndi mapindu athanzi opezedwa m’vinyo. Mneneri wake Yotamu anatchula “vinyo . . . wakusekeretsa Mulungu ndi anthu.” (Oweruza 9:13) Mfumu Solomo analemba za ‘kusangulutsa thupi lake ndi vinyo.’ (Mlaliki 2:3) Ndipo m’cholembedwa chotchuka cha phwando laukwati ku Kana, Yesu, pachozizwitsa chake choyamba, anasandutsa madzi ochuluka kukhala “vinyo wabwino koposa,” amene anasangalatsa oitanidwa kuphwando laukwatiwo.—Yohane 2:6, 7, 10, The New English Bible.

Kuzindikira kwa Yesu kugwiritsiridwa ntchito kwa vinyo m’zamankhwala kukuwonekera m’fanizo lake la Msamariya wachifundo. Pomanga zilondazo za mwamuna wovulazidwa, Msamariya wachifundoyo anathira “mafuta ndi vinyo” pa zilondazo. (Luka 10:30-34) Langizo la mtumwi Paulo kwa Timoteo wachichepere la ‘kuchita naye vinyo pang’ono chifukwa cha m’mimba mwake ndi zofoka zake zobwera kaŵirikaŵiri’ limagwirizana bwino lomwe ndi kuzindikiridwa kwamakono kwa phindu lakadyedwe ndi lazamankhwala la vinyo.—1 Timoteo 5:23.

Dr. Salvatore P. Lucia, amene kale anali pulofesa pa University of California School of Medicine, anati m’bukhu lakelo Wine and Your Well-Being “vinyo [sali] chabe chakumwa choledzeretsa chopatsa thanzi chakale koma mbali yofunika koposa yazamankhwala yogwiritsiridwa ntchito mosalekeza m’mbiri yonse ya anthu.” Ndipo katswiri wopenda zakadyedwe Janet McDonald anati vinyo womwedwa mwachikatikati amawonekera kukhala wopindulitsa monga chotsitsimula chabwino, chodzutsa njala, ndi chithandizo chakupukusa ndi kunyembeteredwa kwa zinthu zopezeka m’zakudya zomwe timadya.

Chikatikati ndi Kudziletsa Nzfunika

Komabe, mosasamala kanthu za zisonyezero zabwino zoterozo zonena za vinyo ndi zakumwa zoledzeretsa ponse paŵiri m’Baibulo ndi m’zamankhwala, kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa zakumwa zoledzeretsa kwadzetsa tsoka lalikulu pa unyinji wa anthu. Kodi zimenezo zikupangitsa Mulungu kukhala ndi liwongo chifukwa cha masoka amene abuka mwa kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa zakumwa zoledzeretsa? Mosiyana, m’Mawu ake, Baibulolo, iye wapereka zitsogozo zochuluka zolamulira kugwiritsiridwa ntchito kwabwino ndi koipa kwa vinyo.

Mwachitsanzo, talingalirani chenjezo lotsatira lamphamvu lotsutsa kugwiritsiridwa ntchito molakwa kwa mphatsoyi: “Usakhale mwa akumwaimwa vinyo, ndi ankhuli osusuka.” Ndithudi zimenezo sizikutanthauza kuti odya therere amene samamwa zakumwa zoledzeretsa ndiwo okha amene amakondweretsa Mulungu, ndipo lembalo silikutsutsa amene amagwiritsira ntchito vinyo pang’ono kapena kudya nyama mwachikatikati. Mmalo mwake, chenjezo la Baibulo limatsutsa kumwerekera ponse paŵiri m’kudya ndi kumwa. Zimenezi nzachiwonekere monga momwe mwambi winawo umafotokozera kuti: “Ndani ali ndi chisoni? Ndani asauka? Ndani ali ndi makangano? Ndani ang’ung’udza? Ndani alasidwa chabe? Ndani afiira maso? Ngamene achedwa pali vinyo.”—Miyambo 23:20, 29, 30.

Olemba Baibulowo Petro ndi Paulo anagogomezera chikatikati mwakupatsa Akristu oyambirira uphungu kuti apeŵe “mamwaimwa” ndi kuti ‘asaledzere naye vinyo.’ Chenjezo limeneli liyenera kutengedwa mwamphamvu, monga momwe mtumwiyo anachenjezera kuti: ‘Oledzera sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.’ Mwa mawu ŵena, ozoloŵera kugwiritsira ntchito molakwa zakumwa zoledzeretsa alibe chivomerezo cha Mulungu ndipo adzalephera kupeza moyo wosatha.—1 Petro 4:3; Aefeso 5:18; 1 Akorinto 6:9, 10.

Chotero, ngati anthu ali osadziletsa pogwiritsira ntchito zoledzeretsa, iwo ayenera kuzipeŵa kotheratu. (Yerekezerani ndi Mateyu 5:29, 30.) Kuwonjezera pakunyentchera kwa thanzi, kudalira pa zakumwa zoledzeretsa kowonjezereka kungachititse chivulazo chowopsa mwauzimu. Chifukwa chake, mwanzeru Mulungu amatichenjeza motsutsa kumwerekera m’zakumwa zoledzeretsa.

Mosiyana ndi lingaliro la oletsa vinyo, Baibulo lenilenilo silimafunikiritsa, kapena ngakhale kusonyeza, kusala kotheratu vinyo kapena zakumwa zoledzeretsa kwa anthu onse. (Deuteronomo 14:26) Wamasalmoyo akuti ponena za Yehova: “Ameretsa msipu ziudye ng’ombe, ndi zitsamba achite nazo munthu; natulutse chakudya chochokera m’nthaka; ndi vinyo wokondweretsa mtima wa munthu.” Ndithudi, Mulungu wapereka vinyo kaamba ka chifuno chabwino ndi cholemekezeka, pamene amwedwa mwachikatikati.—Salmo 104:14, 15.

[Mawu a Chithunzi patsamba 22]

L’ Absinthe by Edgar Degas, 1877—E.R.L./Sipa Icono

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena