Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Bwanji Nanga za Zinthu Zapamtima?
ZINTHU zapamtima zimabweretsa chisangalalo. Izo zamasuliridwa kukhala “pafupifupi chirichonse chimene munthu amakonda kuchita panthaŵi yake yotsalako.” Achichepere ena amathera nthaŵi yawo yosatanganidwa akusambira, kuseŵera mpira, kapena kuthamanga. Achichepere amene samakonda kwambiri maseŵera angakonde kumvetsera nyimbo, kuyenda mtunda wautali, kapena kungokhala panyumba kumaŵerenga. Komabe ena amakonda kukulitsa maluso kapena kusonkhanitsa zinthu. Chinthu chapamtima cha Natalie ndicho kuliza chitoliro. Mchemwali wake wamng’ono, Nikki, amasonkhanitsa zidole.
Zinthu zapamtima zimapereka kulinganizika pakati pa ntchito ndi maseŵera, kuchinjiriza kusungulumwa m’nthaŵi yakusanguluka. Zingakuthandizeni kupumula. Ndipo kupumula kwabwino kumatulukapo thanzi labwinopo lamaganizo ndi lakuthupi. Dokotala wa ku Canada Bwana William Osler ananena kuti: “Palibe munthu amene amakhaladi wachimwemwe kapena wotetezereka popanda chinthu chapamtima,” nawonjezera kuti: “Chimapangitsa kusiyana kochepa kwambiri ndi zimene zingakhale kunja . . . Zirizonse zikhoza kuchitika malinga ngati ali ndi chinthu chapamtima ndipo achichita ndi chisamaliro chachikulu.” Koma monga momwedi katswiri wokwera kavalo amafunikira kulamulira kavalo wake, nanunso mufunikira kulamulira chinthu chapamtima panu m’malo molola chinthu chapamtimacho kukulamulirani. Motani?
Choyamba, muyenera kutsimikizira kuika zinthu zofunika koposa m’moyo pamalo oyamba, monga ngati kufika pamisonkhano Yachikristu, kusamalira ntchito zanu zapanyumba, ndi kuchita homuweki yanu. (Afilipi 1:10) Tsopano mukhoza kupeza kuchuluka kwa nthaŵi yanu yotsalako imene ingakhale ya zinthu zapamtima.
Zinthu Zapamtima Zopindulitsa
Zinthu zapamtima zina zimakuthandizani kukulitsa maluso aphindu, monga ngati kuluka, kusoka malaya, kapena kulondola maluso akaphikidwe. Zowonadi, zinthu zapamtima zimenezi zimasangalatsa makamaka asungwana. Komabe, palibe cholakwika ngati mwamuna aphika. (Yerekezerani ndi Yohane 21:9-12.) Mwina simungafikire miyezo yapamwamba yakaphikidwe, koma kuyesa kuphika kungakuthandizeni kukulitsa maluso amene adzakhala othandiza kwenikweni ngati mudzafunikira kukhala nokha. Kumbali ina, asungwana angapindule mwakuyesa kukonza magalimoto kapena kukonza zinthu zina zapanyumba.
Chinthu china chopindulitsa chochita panthaŵi yopuma ndicho kuphunzira chinenero. Mwachitsanzo, James wachichepere akuphunzira Chirussia pakali pano. Mwinamwake chinenero china chingadzakutheketseni tsiku lina kuphunzitsa chowonadi cha Baibulo kwa ena m’dziko lachilendo! Ndithudi, kaŵirikaŵiri zinthu zapamtima zingatumikire monga njira yothandizira anthu ena.
Mwachitsanzo, kodi kulima ndiko chinthu chanu chapamtima? Bwanji osagwiritsira ntchito maluso anu a kulima maluŵa padimba la agogo anu kapena okalamba ena amene amakupeza kukhala kovuta kulisamalira moyenerera? Kodi mumakonda ntchito yodzichitira nokha? Pamenepo bwanji osadzipereka kuthandiza munthu wokalamba kapena mkazi wamasiye kukonza zinthu panyumba? Ngati kuphika kuli chinthu chapamtima panu ndipo muli ndi chakudya chimene mumachikonda, bwanji osachiphika ndi kukapatsa munthu wina wosoŵa monga mphatso? Kumbukirani kuti, “muli chimwemwe chambiri,” anatero Yesu, “m’kupatsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35, NW.
Chinthu chapamtima chingakuthandizeni kupita patsogolo mwauzimu. Mwachitsanzo, ngati mumakonda kupanga zifanizo, kodi kumanga chingalaŵa chaching’ono sikungazamitse chiyamikiro chanu cha kulimba kwa chikhulupiriro cha Nowa? (Onani bokosi.) Kumanga chifanizo cha chihema kapena kachisi kungawongolerenso chidziŵitso chanu cha mmene atumiki a Mulungu anali kulambirira kalelo. M’nthaŵi za Baibulo mbusa wachinyamata Davide ankaseŵera zeze panthaŵi yake yotsalako. Pambuyo pake analemba nyimbo zokongola zotamanda Yehova. Kodi nanunso mungaphunzire kuliza chiŵiya choimbira? Ngati nditero, bwanji osagwiritsira ntchito luso lanu kutamanda Mulungu mwakuphunzira zina za nyimbo zopezeka m’bukhu lanyimbo la Sing Praises to Jehovah?a Pamene mukuimba nyimbozo, sinkhasinkhani pa malingaliro amene mawu a nyimboyo amapereka. Kodi ndinu wosonkhanitsa zinthu? Pamenepo sonkhanitsani zinthu zimene zimakhudza Baibulo. Kapena yesani kudzaza bukhu loikamo zinthu zakale ndi zithunzithunzi za maiko a Baibulo.
Ŵerengerani Mtengo Wake
Mosasamala kanthu kuti chinthu chapamtima chingakhale chopindulitsa motani, kaŵirikaŵiri kumakhala kwanzeru kudzifunsa kuti, Kodi chikanditengera ndalama zochuluka motani? (Luka 14:28) Kodi chinthu chapamtimacho chikhoza kukwanira ndi ndalama zomwe muli nazo? Ichi chingakhale chopereka chitokoso kwenikweni ngati kusonkhanitsa ndiko chinthu chanu chochita panthaŵi yopumula, kaya akhale masitampu amakalata, zithunzi, kapena ngakhale zidole!
Kumbukirani kuti kagwiritsidwe ka ndalama zanu kangayambukire ziyembekezo zanu za kupeza moyo wosatha. Yesu anati: “Pangani mabwenzi ndi chuma chosalungama [ndalama zanu], kotero kuti, pamene izo zikalephera, iwo [Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu] akalandire inu m’mahema osatha.” (Luka 16:9, NW) Kodi chinthu chapamtima chidzakutengerani ndalama zambiri kwakuti simukakhala ndi zotsala ‘zakulemekeza nazo Yehova ndi chuma chanu’? (Miyambo 3:9) Kodi kulipirira chinthu chapamtima kukafunikira kuti mutenge ntchito yaganyu, mwinamwake kuchititsa kutaikiridwa kwa zinthu zauzimu?
Khalani Olinganizika!
Nthaŵi zina anthu okonda zinthu zapamtima amalakalaka kukhala ndi awo amene amasangalala ndi zinthu zofananazo. Komabe, ichi chingadzetse ngozi. Dzifunseni kuti: Kodi mayanjano oterowo akakhala omangirira? Kodi miyezo yawo ya kavalidwe ndi kapesedwe, zosangulutsa zimene amasankha, kapena zokamba zawo zikakhala ndi chiyambukiro choipa pa inu? Kodi mungadzipeze kukhala wokokedwera kwambiri kwa iwo kuposa banja lanu kapena anzanu Achikristu? Mulimonse mmene zingakhalire, kodi mumalola zikondwerero zofananazo kukutsogolerani ku maunansi oipa? Kumbukirani kuti, “mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.”—1 Akorinto 15:33.
Mfundo ina yofunika ndi iyi: Kodi chinthu chanu chapamtima chimalimbikitsa mkhalidwe wotani? Kodi chimadzutsa mzimu woipa wakupikisana? Kodi chimaloŵetsamo kuika paupandu thanzi kopambanitsa? Ngati ndichoncho, mwinamwake kukakhala kwabwino kukumbukira mawu a mtumwi Paulo aŵa: ‘Pakuti chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono, koma [kudzipereka kwaumulungu, NW] kupindula zonse.’—1 Timoteo 4:8; Agalatiya 5:26.
Kumbali ina, Solomo anati: ‘Kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chirichonse cha pansi pa thambo chiri ndi mphindi yake.’ Ndipo zimenezo zimaphatikizapo “mphindi yakuseka.” Inde, zinthu zapamtima ndi zosangulutsa ziri ndi malo awo. Komabe, khalani otsimikiza kuti chinthu chanu chapamtima sichikutenga chidwi chanu kwakuti munyalanyaze mawu otsatira a Solomo akuti: ‘Opa Mulungu, nusunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.”—Mlaliki 3:1, 4; 12:13.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi patsamba 15]
Ndinamanga Chingalaŵa cha Nowa!
Ndimakonda kugwira ntchito ndi manja anga. Ndipo pamene tsiku lina ndinali ndi chisonkhezero chakuphunzira zambiri ponena za chingalaŵa cha Nowa, ndinagamulapo kupanga chifanizo chake.
Ndinayamba mwakuphunzira mosamalitsa mbiri ya Baibulo ya pa Genesis 6:14-16 ndi chithandizo cha zothandizira kufufuza zofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Posakhalitsa ndinazindikira kuti chingalaŵacho sichinali chofanana ndi masitima apamadzi amakono. Mmalo mwake, chinali chibokosi chachikulu: mikono 300 m’litali ndi mikono 50 m’bwambi ndi mikono 30 msinkhu wake. Ziŵerengero zimenezo zimasintha kukhala mamita 133.5 m’litali, mamita 22.3 m’bwambi, ndi mamita 13.4 msinkhu wake. Choncho chingalaŵacho chinali cha utali wa mamita 133.5—pafupifupi kuwirikiza kamodzi ndi theka kutalika kwa bwalo la mpira la ku United States. Ngakhale chinthu chachikulu choterocho sichikanatenga mitundu miliyoni imodzi ya zinyama zimene asayansi amanena kuti ziripo. Komabe, ndinaphunzira kuti ofufuza ena amakhulupirira kuti “mitundu” 43 yokha ya nyama zoyamwitsa, “mitundu” 74 ya mbalame, ndi “mitundu” 10 ya zokwaŵa ingakhale inabala mitundu yosiyanasiyana yomwe ilipo lerolino.
Kufufuza kwanga kunandithandizanso kumvetsetsa ukulu wa ntchito ya Nowa: kudula mitengo popanda macheka amagetsi, kukoka zipinjiri kunka nazo kuchimangoko popanda matalakitala, kunyamula mitanda yolemera ya tsindwi popanda makina onyamulira zinthu zolemera. Ntchito yanga inali yokhweka poyerekezera ndi ya Nowa! Kuti ndipeze “mitengo,” ndinangothyola mitolo ya timitengo touma. “Nyama” zanga zinapangidwa ndi dongo. Ponena za mayalidwe a mkatimo, ndinangolota. Ndinalingalira kuti Nowa ndi banja lake mwinamwake anasankha kukhala m’chipinda chapamwamba, kumene akakhala ndi kuunika kochuluka ndi mpweya. Ndinaika nyamazo m’zipinda zapansi za chingalaŵacho.
Pambuyo pogwira ntchito kwa maola ambiri, ndinamaliza kupanga chifanizo changa. Monga momwe ena anenera kuti chimawoneka chochititsa kaso, chingalaŵa chenichenicho chinali chachitali kuwirikiza nthaŵi zana limodzi m’litali, m’bwambi, ndi msinkhu wake kuposa chifanizo changacho. Kunena m’mawu ŵena, pakafunikira zifanizo zanga zokwanira miliyoni imodzi kuti chilingane ndi ukulu wa chingalaŵa choyambiriracho. Pamenepo, nkosadabwitsa kuti ntchito yangayo inadzutsa chilakolako changa chakufuna kuphunzira zowonjezereka ponena za chingalaŵa chenichenicho. Ndipo ngati ndidzakhala ndi mwaŵi wakukhala ndi moyo kudzawona dziko latsopano la Mulungu ndi kuwona kuukitsidwa kwa akufa, mwinamwake ndidzampempha Nowa kundithandiza kupanga chifanizo chatsopano—chimene chidzakhala cholondola m’tsatanetsatane aliyense.—Yoperekedwa.
[Zithunzi patsamba 16]
Kodi chinthu chanu chapamtima chimasangalatsa ponse paŵiri inuyo ndi ena?
Kusonkhanitsa zithunzi za maiko a Baibulo kungakuthandizeni kuwona ndi diso lanu lamaganizo zochitika Zamalemba