Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 2/8 tsamba 21-26
  • Magwero a Makhalidwe Abwino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Magwero a Makhalidwe Abwino
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Nchifukwa Ninji Munthu Ali Wosiyana Motero?
  • Makhalidwe Owongolera Kunyonyotsoka kwa Makhalidwe
  • Kodi Chipembedzo ndi Banja Zingathandize?
  • Mphamvu ya Makhalidwe Abwino Yoikidwa mu Majini Athu
  • Asayansi Awona Zinsinsi Zimene Mulungu Yekha Ndiye Angazimasulire
  • Funani Mulungu, Pindulani, Khalani ndi Moyo Kosatha
  • Mapindu a Makhalidwe Abwino Amene Amabweretsa Chimwemwe
    Galamukani!—1990
  • Muziwaphunzitsa Kufunika Kokhala ndi Makhalidwe Abwino
    Galamukani!—2019
  • Kutsatira Mfundo Zosasinthasintha
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Boma Lodzalimbikitsa Mfundo za Mulungu
    Galamukani!—2003
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 2/8 tsamba 21-26

Magwero a Makhalidwe Abwino

Kuwagwiritsira Ntchito Kudzathetsa Kunyonyotsoka kwa Makhalidwe

MUNTHU akweza maso ake kumwamba kuthambo loŵala ndi nyenyezi, ndipo achita mantha ndi kudabwa kwakukulu. Pamene apenyetsetsa thambolo lodzala ndi nyenyezi lowonekera kutaliko pamwamba pa mutu wake, adzimva kukhala kanthu kopanda pake. Mawu a wamasalmo olankhulidwa kalekale angabweredi kwa iye: ‘Pakuwona ine thambo lakumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mumkumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?’ (Salmo 8:3, 4) Wamasalmo adawona zikwi zingapo za nyenyezi ndipo anadzimva kukhala wochepa; munthu tsopano amadziŵa kuti pali mabiliyoni a milalang’amba uliwonse wokhala ndi mabiliyoni a nyenyezi, ndipo amadzimva kukhala wochepa kopambana. Iye angakhale ndi mafunso ambiri m’maganizo: ‘Kodi ndingasonyeze motani kuti ndimakhudzidwa? Kodi nchifukwa ninji ndiri pano? Ndiiko komwe, kodi ndine yani?’

Koma palibe nyama imene imakhala ndi malingaliro oterowo.

Munthu amayang’ana miyoyo yosiyanasiyana yomzinga ndipo amawona mipangidwe yozizwitsa yokwaniritsira zifuno zothandiza. Amawona mbalame zimene zimasamuka ndi kuuluka mtunda wamakilomita mazana ambirimbiri, nyama zoyamwitsa zimene zimabisala m’nyengo yachisanu, ndi mitundu ina yambiri ya zamoyo zimene zinagwiritsira ntchito sonar (kuyenda ndi namaloŵe), air-conditioning (kuziziritsa kapena kufunditsa mpweya), jet propulsion (kuyenda ndi mphamvu yakutsopa ndi kutulutsa mpweya), desalination (kuchotsa mphamvu ya mchere), antifreeze (kuletsa kuzizira koundanitsa), njira zopumira pamadzi, njira zoundatira mazira, zopimira kuzizira kapena kutentha, kupanga mapepala, magalasi, makoloko, makampasi, magetsi, makina ozungulira, ndi zozizwitsa zina zambiri kalekale munthu asanazilote. Anthu oganiza amazizwa kuti: ‘Kodi ndimotani mmene zozizwitsa zocholoŵanacholoŵana zimenezi zinafikira kukhalako? Kodi ndiluntha lalikulu la mtundu wanji limene linazichititsa?’

Apanso, palibe nyama iriyonse imene imalingalira zimenezi.

Koma munthu amatero. Kodi nchifukwa ninji kuli kwakuti, pazolengedwa zambirimbiri zapadziko lapansi, munthu yekha ndiye amazizwa ndi mantha ndi kudabwa powona zakumwamba ndi zinsinsi za moyo pansi pano padziko lapansi? Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti munthu ali wosiyana.

Kodi Nchifukwa Ninji Munthu Ali Wosiyana Motero?

Chifukwa chakuti iye yekha analengedwa m’chifaniziro ndi chikhalidwe cha Mulungu: ‘Ndipo anati Mulungu, Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.’ (Genesis 1:26) Mawuŵa amasonyeza mpata wosagwirizanitsika pakati pa munthu ndi nyama. Amasonyeza chifukwa chake padziko lapansi palibe cholengedwa chirichonse choyandikana ndi munthu m’kufanana. Amasonyeza chifukwa chake munthu ali cholengedwa cholingalira, wokhala ndi mafunso ponena za dziko lomzinga, ndi kulingalira za makhalidwe abwino.

Kodi ndimotani mmene munthu aliri m’chifaniziro ndi chikhalidwe cha Mulungu? Ndi mwakukhala ndi zikhoterero ndi mikhalidwe ya Mulungu, monga chikondi, chifundo, chiweruzo cholungama, nzeru, mphamvu, kukoma mtima, ubwino, kuleza mtima, kuwona mtima, kunena zowona, kukhulupirika, kuchitachita, ndi luso lakupanga zinthu. Iyi inali mikhalidwe yabwino imene poyamba inaikidwiratu mwa munthu, koma pamene anthu aŵiri oyamba anagwiritsira ntchito molakwa ufulu wakudzisankhira, kumene kunadzetsa chipanduko chawo, mikhalidwe imeneyi inadodometsedwa ndipo motero siinapitirizidwe mwangwiro kwa mbadwa zawo. Mikhalidweyi sinakhalenso yolinganizika, ndipo mwakugwiritsiridwa ntchito molakwa ina inachokeratu m’maganizo a anthu. Komabe, Akolose 3:9, 10 amasonyeza kuti, mwakupeza chidziŵitso cholongosoka chonena za Mulungu ndi kuchigwiritsira ntchito, tikhoza kuvala umunthu watsopano ndi kukhalanso ‘m’chifaniziro ndi chikhalidwe cha Mulungu.’

Pamene Yehova Mulungu anapatsa Aisrayeli Chilamulo cha Mose, chinali ndi makhalidwe enieni, ena a iwo anali Malamulo Khumi ndi chilangizo cha ‘kukonda anansi monga anadzikonda iwo eni.’ (Levitiko 19:18; Eksodo 20:3-17) Mikhalidwe imeneyi inayenera kupitirizidwa monga choloŵa ku mibadwo yamtsogolo. Mose anauza Israyeli kumvera Chilamulo chimenechi, ndipo anatinso: ‘Muuze ana anu asamalire kuwachita mawu onse a chilamulo ichi. Pakuti sichikhala kwa inu chinthu chopanda pake, popeza ndicho moyo wanu.’ (Deuteronomo 32:46, 47) Zaka mazana ambiri pambuyo pake, Miyambo 8:18 inawatcha ‘chuma chosatha.’

Makhalidwe Owongolera Kunyonyotsoka kwa Makhalidwe

Komabe, ambiri amatsutsa kuti, chitaganya tsopano nchachikulu kwakuti palibe mpambo umodzi wa malamulo amakhalidwe umene ungakhale wothandiza kwa munthu aliyense. Kusiyanasiyana kwa makulidwe ndi miyambo kumafunikiritsa malamulo osiyanasiyana a makhalidwe malinga ndi anthuwo. Koma kodi ndivuto lamakono lotani limene silingathetsedwe mwakugwiritsira ntchito lamulo la Yesu lakukonda mnansi wako monga udzikonda iwe mwini? Kapena kuchitira ena zimene mukafuna iwo kukuchitirani? Kapena mwakutsatira makhalidwe abwino opezeka m’Malamulo Khumi? Kapena mwakukalimira kubala zipatso za mzimu wa Mulungu zosonyezedwa pa Agalatiya 5:22, 23: ‘Koma chipatso cha mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.’ Palibe chirichonse cha zimenezi chimene chiri chosatheka; chirichonse cha izo chikachepetsa mokulira masoka a chitaganya chamakono.

‘Koma anthu sadzakhalapo ndi mikhalidwe yoteroyo!’ ndiko kungakhale kudzuma kwanu. Komabe, ngati muganiza kuti njira zimenezi nzovuta kwambiri, musayembekezere kuti mavutowo adzathetsedwa ndi njira zina zokhweka. Nkothekera kwa chitaganya kugwiritsira nchito njira zimenezi, ngakhale kuti mwachiwonekere anthu saali ofunitsitsa kuchita tero. Mbadwo uno sumadziletsa mwanjira iriyonse m’maufulu ake, kuphatikizapo ufulu wakuchita zolakwa ndi kuvutika ndi zotulukapo zake.

Nyuzipepala ya Bottom Line/Personal ikufunsa kuti: “Kodi Nchiyani Chinachitikira Kudziletsa?” Pambuyo pofotokoza kuti “anthu ambiri akuchita mantha ndi zotulukapo za mbadwo wolekerera m’zakugonana,” ikupitiriza kuti: “Komabe anthu akupitirizabe kuchirikiza mkhalidwe wakumwerekera m’zisembwere zokhutiritsa zilakolako zakugonana. . . . Anthu amayembekezeredwa kusamala kadyedwe, kuchita maseŵera olimbitsa thupi, kuleka kusuta, kusamalira bwino moyo wawo kuti akhale ndi thanzi labwino. Kukhutiritsa chilakolako chakugonana ndiko kokha kumene kukuwonekera kupatsidwa ufulu wopanda malire wakumwerekeramo.” Sikuti sangathe kuwagwiritsira ntchito makhalidwe abwinowo; koma chenicheni nchakuti iwo sadzatero. Chotero chitaganya chimafesa ndi kututa.

Lerolino makhalidwe abwino ameneŵa akhala onyansa. Ambiri amatcha zoipa zabwino ndi zabwino zoipa, monga momwe kunanenedweratu kuti akatero: ‘Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m’malo mwa kuyera, ndi kuyera m’malo mwa mdima; amene aika zoŵaŵa m’malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m’malo mwa zoŵaŵa.’ (Yesaya 5:20) Komabe, ena ali ndi nkhaŵa zomakulakula. Akuwona zotulukapo zonyansa zimene zimachitidwa ndi mzimu wa dziŵa zako ndipo amafunadi kuti makhalidwe amakono onyonyotsokawo awongokere.

Kodi Chipembedzo ndi Banja Zingathandize?

Maprogramu ambiri amakhazikitsidwa oyesa kubwezeretsa makhalidwe abwino. Imodzi ya iwo ndiyo chipembedzo. Icho chimawonedwa kukhala chopereka nyonga yauzimu yamakhalidwe. Koma nyonga imeneyo siimapezeka m’zipembedzo zosunga mwambo za Chikristu Chadziko. Zipembedzo zina za Chikristu Chadziko zagwera m’chikunja ndi kubutsanso ziphunzitso zachitonzo monga Utatu, kuzunzika kwamuyaya, ndi moyo wosakhoza kufa. Zina zakana dipo ndi kulengedwa nizigonjera ku chipembedzo chasayansi ya chisinthiko. Zimachirikiza kusuliza kwapamwamba kumene kumatsutsa umphumphu wa Mawu a Mulungu, Baibulo. Zimaphunzitsa “Chikristu” chosukuluka ndi choluluzika chopanda chabwino chirichonse chotsalamo, ndipo mbadwo wachichepere umangowonamo chinyengo ndi kupanda pake. Ayi, sitiyenera konse kucheukira ku zipembedzo zodwala motero kaamba ka nyonga yauzimu koma kulambira kowona kumodzi kokha kozikidwa pa Baibulo kumene kumalengeza Ufumu wa Yehova monga chiyembekezo chokha cha dziko.

Chikhalirechobe, patsala magwero ena amene anthu odera nkhaŵa angapezeko chithandizo, ndiwo banja, makonzedwe m’mene makolo akhoza kukhomereza makhalidwe abwino mwa ana awo. Kugwirizana kumene kunayamba paubwana kuyenera kupitiriza. Ana amene amakonda ndi kudalira makolo awo amafuna kufanana nawo, kutsanzira mmene amalankhulira, kuchita zinthu, kuyeseza kudzisungira kwawo, ndi kutengera makhalidwe awo, ndipo mkupita kwa nthaŵi makhalidwe amakolo amakhalanso makhalidwe a anawo. Kulongosola zinthu mosavuta, osati mauphungu aatali; kulankhulana kwa anthu aŵiri, osati kumangopereka zigamulo, ziri njira zogwira mtima.

Makolo amene samangolankhula komanso amachita makhalidwe abwino adzakhala ndi ana amene adzatengera makhalidwe amenewo. Ana oterowo sadzawonongedwa ndi zitsanzo zoipa za ausinkhu wawo kusukulu kapena kwina kulikonse. Miyambo 22:6 imati: ‘Phunzitsa mwana poyamba njira yake; ndipo ngakhale atakula sadzachokamo.’ Phunzitsani mwakupereka uphungu wopindulitsa. Chofunika kwambiri, phunzitsani mwakupereka chitsanzo chopindulitsa.

Mphamvu ya Makhalidwe Abwino Yoikidwa mu Majini Athu

Yesu anati: “Odala ali awo ozindikira kusoŵa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) Uku ndikusoŵa kwachibadwa koikidwiratu mwa ife, monga momwe akatswiri azamaganizo ena anenera. Nzowonanso kuti nyonga yauzimu yokha ndiyo ingatitheketse kupeŵa makhalidwe ochirikizidwa lerolino.

Mogwirizana ndi chenicheni chakuti tinalengedwa m’chifaniziro ndi chikhalidwe cha Mulungu, okhala ndi mphamvu ya makhalidwe abwino mkati mwathu, Thomas Lickona, profesa wa maphunziro, akunena kuti: “Ndiganiza kuti mphamvu zakukhala munthu wabwino zimakhalapo kuyambira pachiyambi.” Komanso iye akuwonjezera kuti “makolo ayenera kukulitsa mphamvu zachibadwa zimenezo mongadi momwe amathandizira ana awo kukhala aŵerengi abwino kapena ochita maseŵera anyonga kapena oimba.”

Norman Lear, mkonzi wa maprogramu a pa TV anali wokamba nkhani wachilendo pamsonkhano wa dzikolo wa National Education Association. Pambuyo pozindikira “vuto la anthu omveka, amaphunziro apamwamba—awo amene amawona kufunafuna cholinga chirichonse chosakhala chakuthupi kukhala kopanda pake kapena kosayenera,” iye anati: “Sindimavutika konse kupanga chigamulo, mwakupenda mbiri ya anthu, chakuti kulabadira ku umoyo, Umunthu, mphamvu yakukhulupirira chinachake choposa iwe mwini, kuli kwamphamvu kwambiri ndi kosapeŵeka monga momwe sitingasinthire mkhalidwe wa majini athu.”

Lear anapatsa mlandu malonda aakulu ndi kusonyezedwa kwa wailesi yakanema kwa zaka makumi anayi yosonyeza “dongosolo la makhalidwe atsopano” loyambukira mwamphamvu makhalidwe a anthu ndi a munthu payekha limene labala mavuto ambiri m’kakhalidwe ka anthu: sukulu ndi makoleji kumene anthu amamaliza maphunziro koma osadziŵa kuŵerenga ndi kulemba; kuwonjezereka kwa kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa; kukhala ndi ana kwa asungwana osakwatiwa; ndi mabanja osaikiza ndalama oloŵerera m’ngongole. Kenako Lear anawonjezera kuti: “Pamene tilankhula za mavuto ambirimbiri akakhalidwe ka anthu—ndikuwona kuti tikulankhula za mavuto amene apitirizidwa kuchokera ku mbadwo umodzi kumka ku unzake, amene mothandizidwa ndi wailesi yakanema, aluluza mwambo wa anthu onse.” Ndipo ananenanso kuti ‘amakhulupirira kuti, m’majini mwathu muli mphamvu ndi chinsinsi zimene zimaumba umunthu wathu, zimene tiyenera kuperekako chisamaliro.”

Katswiri wa zamaganizo wotchuka C. G. Jung ananena kuti chipembedzo “ndicho kaimidwe kamaganizo kachibadwa ka munthu aliyense payekha, ndipo zizindikiro zake zikhoza kupezeka m’mbiri yonse ya anthu.” Chachibadwanso ndicho chikumbumtima chimene chimazindikira chabwino ndi choipa: ‘Pakuti pamene anthu amitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo awonetsa ntchito ya lamulolo lolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.’ (Aroma 2:14, 15) “Chikumbumtima” ndicho “kudziŵa kwa mkati kwa munthu mwini” kuchita ngati khoti la chiweruzo cholungama lochitidwira mkati mwathu kupereka zigamulo pa mayendedwe athu, kutiimba mlandu kapena kutimasula. Komabe, ngati “tinyoza khoti” la m’chikumbumtima chathu, mphamvu yake idzazilala ndipo chidzaleka kugwira ntchito.

Asayansi Awona Zinsinsi Zimene Mulungu Yekha Ndiye Angazimasulire

Yochititsa chidwi kwambiri ndi mfundo yakuti pamene asayansi akuphunzira zowonjezereka ponena za dziko lapansi ndi kumwamba, asayansi ena amakakamizika kukhulupirira kuti pali luntha linalake limene liyenera kukhala linazilinganiza. Komabe, iwo amamkana Mulungu wa m’Baibulo.

Katswiri wazakuthambo George Greenstein, m’bukhu lake lakuti The Symbiotic Universe, anafotokoza “zimene zingawoneke kukhala tsatanetsatane wozizwitsa ndi ngozi zowonekera kukhala zosakhoza kuchitika zimene zinachititsa kukhalako kwa moyo. Pali ndandanda ya zamalunji, zonsezo zofunika kaamba ka kukhalako kwathu.” Greenstein ananena kuti ndandandayo inatalikirako, zamalunji sizinakhalenso zamwangozi, ndipo panakhala lingaliro lakuti mphamvu inayake yosakhala yachibadwa ndiyo inkazichititsa. “Kodi kuli kotheka,” iye analingaliro tero, “kuti mwadzidzidzi, mosadziŵa, tatulukira umboni wasayansi wosonyeza kukhalako kwa Wamoyo Wamkulukulu? Kodi anali Mulungu amene analoŵererapo ndi kulinganiza zakuthambo kaamba ka ubwino wathu?” Iye anakhala ndi “malingaliro ovutitsa” pazimenezi ndipo anakakamizika kunena kuti: “Mulungu sindiye yankho.” Komabe kuchuluka kwa “zamalunji” kunamkakamiza kufunsa mafunsowo.

Katswiri wina wazakuthambo, Fred Hoyle wopata mphotho ya Nobel, m’bukhu lake lakuti The Intelligent Universe, anafotokoza malunji azinsinsi amenewo amene anavutitsa Greenstein motere: “Mikhalidwe yotereyi ikuwoneka kukhala ikupezeka m’zinthu zachilengedwe monga zochitika mwangozi zosangalatsa. Koma pali zamalunji zambiri kwambiri zochirikiza moyo zosonyeza kuti payenera kukhala wina wozichititsa.” Hoyle akuvomerezanso Greenstein kuti izo sizikanachitika mwangozi. Chotero, Hoyle akunena kuti, ‘chiyambi cha chilengedwe chimafunikira luntha,’ ‘luntha lapamwamba,’ ‘luntha limene linakhalako ife tisanatero ndipo limene linagwiritsiridwa ntchito kulenga zinthu zochirikiza moyo.’

Einstein analankhula za Mulungu koma osati m’lingaliro la chipembedzo chosunga mwambo. Lingaliro lake la Mulungu linasonya kwa “mzimu wa ukulu wopanda malire” umene anawona ukuvumbuluka m’chilengedwe. Timothy Ferris, m’nkhani yake yakuti “Einstein Wina,” anagwira mawu Einstein motere: “Zimene ndikuwona m’chilengedwe ndimpangidwe wodabwitsa umene sitingathe kuumvetsetsa kwenikweni, umene uyenera kupatsa munthu woganiza malingaliro a ‘kudzichepetsa.’ Ili ndilingaliro lenileni la chipembedzo limene liribemo chinsinsi. . . . Malingaliro anga achipembedzo ali akuchita chidwi modzichepetsa ponena za mzimu wa ukulu wopanda malire umene umawonekera wokha, umene timazindikira pang’ono ndi maganizo athu ochepetsetsa ndi opereŵera. . . . Ndifuna kudziŵa mmene Mulungu analengera dziko lino. Ndifuna kudziŵa malingaliro ake, zotsalazo nzovuta kupeza.”

Guy Murchie, pambuyo pofotokoza zina za zinsinsi zosamveka za chilengedwe, akunena m’bukhu lake la The Seven Mysteries of Life kuti: “Nkosavuta kuwona chifukwa chake asayansi ya physics amakono, amene akhala akupita patsogolo m’kudziŵa zachilengedwe zobisika mwinamwake kuposa asayansi ena alionse m’zaka za mazana aposachedwapa, ali patsogolo kwa anzawo onse m’kuvomereza kuti zinsinsi za chilengadwe chonse zinasonya kwa Mulungu.”

Funani Mulungu, Pindulani, Khalani ndi Moyo Kosatha

Munthu akufunafuna. Wofunafunidwayo ndiye Mulungu. Ena anachita zimenezi m’tsiku la Paulo. Iye anati: ‘Kuti afunefune Mulungu, kapena akamfufuze ndi kumpeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife.’ (Machitidwe 17:27) Palibe nyama imene imafunafuna Mulungu. Palibe ngakhale imodzi imene imadziŵa za Mulungu. Munthu amatero, anapangidwa m’chifaniziro cha Mulungu, ndipo pali mpata wosatha kugwirizanitsidwa womsiyanitsa ngakhale ndi nyama zochenjera koposa. Ndipo monga momwe lembalo likutiuzira, Mulungu ‘sakhala patali ndi yense wa ife.’

Timawona umboni wake m’zolengedwa zake zotizinga konsekonse, monga momwe Aroma 1:20 akunenera kuti: ‘Chilengedwere dziko lapansi zawoneka bwino zosawoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mawu akuŵiringula.’ Pamene asayansi akuwona zamalunji ndi zocholoŵanacholoŵana zomwe satha kuzilongosola ndi pamene asinkhasinkha pa zozizwitsa zochititsa mantha za m’chilengedwe, mwinamwake owonjezereka a iwo adzazindikira Luntha Lalikulu lokhala kumbuyo kwa zinthuzo ndi kuzindikiranso Mlengi wake, Yehova Mulungu.

Dziko lapansi ndi zopezekapo zonse nza Yehova. Iye wakhazikitsa miyezo kwa amene adzakhalapo ndi moyo. Wapereka makhalidwe abwino monga njira zopezera chimwemwe ndi moyo. Wapatsanso anthu ufulu wakudzisankhira. Sakakamizidwa kummvera. Iwo angafese zimene akukhumba, koma pambuyo pake adzatuta zimene adafesa. Mulungu sanyozeka. Iye wapereka makhalidwe enieni, sikaamba ka ubwino wake, koma kaamba ka phindu la nzika zake zapadziko lapansi. Yesaya 48:17, 18 akuti: ‘Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde anyanja.’

Anthu onse akamvera kuchonderera kwa Yehova, pamenepo adzayenda m’njira imene ayenera kuyendamo ndipo adzatchera khutu ku malamulo a Mlengi wawo. Onse adzapeza mtendere monga mtsinje ndi chilungamo monga mafunde anyanja. Onse adzagwiritsira ntchito makhalidwe abwino achibadwa ndipo sadzayang’anizananso ndi kunyonyotsoka kwa makhalidwe. Ndipo kodi zonsezi zidzakhalako liti? Posachedwapa, pamene pemphero lidzayankhidwa lakuti: ‘Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’—Mateyu 6:10.

[Zithunzi patsamba 23]

Kuyenda ndi mphamvu yakutsopa ndi kutulutsa mpweya

Kuchotsa mphamvu ya mchere

Kupanga mapepala

Kuyenda ndi namaloŵe

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena