Kodi Uchidakwa Uli Choloŵa?
Malinga ndi kufufuza kolembedwa mu The Journal of the American Medical Association, asayansi akulingalira kuti kwa anthu ena, chikhoterero cha kukhala zidakwa chingalandiridwe kudzera mwa jini inayake. Magaziniwo ananena kuti iwo apeza jini imene imaika anthu paupandu wakukhala zidakwa. Komabe, asayansi akuchenjeza kuti palibe jini imene imachititsa uchidakwa. Mkulu wa gulu lofufuzalo anati: “Ambuye wabwino sanapange jini yauchidakwa, koma imene imawoneka kukhala yoloŵetsedwa m’mikhalidwe yokonda zokondweretsa.”
Lipotilo linapitiriza kuti: “Ofufuza ananena kuti palibe jini iriyonse, kuphatikizapo imeneyo, imene inachititsapo mpangidwe uliwonse wa uchidakwa. Anthu ena okhala ndi jini yofufuzidwayo sanakhale zidakwa, pamene kuli kwakuti ena amene alibe jini imeneyi anakhala zidakwa . . . Zinthu zina za kakhalidwe ndi miyambo zimayambitsa vuto limeneli mwa zidakwa zambiri.”