Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 3/8 tsamba 4-6
  • Pamene Muyenera Kuyamba ndi Zimene Muyenera Kunena

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Muyenera Kuyamba ndi Zimene Muyenera Kunena
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kufotokoza Mmene Kubadwa Kumachitikira
  • Muyenera Kuyamba Mwamsanga Chotani?
  • Sizochititsa Kakasi
  • Mmene Mungatetezere Ana Anu
    Galamukani!—2007
  • Phunzitsani Mwana Wanu Kuyambira Paukhanda Wake
    Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja
  • Zimene Mungachite Mwana Akabadwa
    Banja Lanu Likhoza Kukhala Losangalala
  • Zimene Makanda Amafunikira Ndiponso Zimene Amafuna
    Galamukani!—2004
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 3/8 tsamba 4-6

Pamene Muyenera Kuyamba ndi Zimene Muyenera Kunena

MAKOLO ambiri osamala amaganiza kuti kuphunzitsa zakugonana kungachitidwe mwakutenga kaulendo kowongola miyendo m’nkhalango kwa mphindi khumi ndi mwana wazaka 13. Koma kaŵirikaŵiri izi zatsimikizira kukhala osati kokha zosakwanira komanso kuchedwa kwambiri. Sizachilendo kumva kholo likunena kuti: “Zonse zimene ndinayesa kuwauza, zinawonekera kuti anazidziŵa kale.”

Kodi iripo njira yabwinopo yophunzitsira nkhani zofunika kwambiri zimenezi? Ngati iripo, kodi nliti pamene makolo ayenera kuyamba, ndipo ayenera kuchitanji ndi kunenanji?

Kuchita mwanzeru, muyenera kuyamba kuyala maziko ophunzitsira malangizo ofunika ameneŵa pafupifupi kuchokera pakubadwa kwa mwanayo. Ngati muyamba mwanayo adakali wamng’ono, mukhoza kupereka chidziŵitsocho modekha, mwapang’onopang’ono malinga ndi nzeru zake.

Pamene makolo asambitsa ana awo aang’ono, angawaphunzitse ziŵalo za thupi lawo kuti: “Ichi nchifuŵa chako . . . mimba yako . . . bondo lako.” A,a! Nanga bwanji alumpha kuchokera pamimba ndikupita kubondo? Kodi ziri pakatipo nzochititsa manyazi? Kapena kodi sizamtseri basi? Nzowona, sitingagwiritsire ntchito mawu omveka otukwana ogwiritsiridwa ntchito m’khwalala potchula ziŵalo zamtseri zimenezi. Koma bwanji osangoti “mpheto yachimuna” kapena “mpheto yachikazi”? Ziŵirizi ndimbali ya chilengedwe cha Mulungu chonenedwa kuti “zinali zabwino ndithu.”—Genesis 1:31; 1 Akorinto 12:21-24.

Pambuyo pake, mwina pomsintha malaya, mukhoza kumuuza ndi mawu abwino kuti anyamata ali ndi mpheto yachimuna ndipo atsikana ali ndi mpheto yachikazi. Mukhoza kufotokoza bwinobwino kuti zinthu zimenezi nzamtseri. Ziyenera kulankhulidwa m’banja mokha, osati ndi ana ena kapena anthu akunja kwa banja.

Motero, mukhoza kulongosola zinthu zambiri zisanakhale zochititsa manyazi, kuyambira paubwana ndi kumapita patsogolo pamene nzeru ya mwana yakuzindikira zinthu ikukula.

Kufotokoza Mmene Kubadwa Kumachitikira

Mwana akafika zaka zitatu mpaka zisanu,a angayambe kulingalira ponena za kubadwa ndipo angafunse kuti: “Kodi ana amachokera kuti?” Mungangoyankha kuti: “Unakula m’malo ofunda otetezereka, m’mimba mwa amayi ako.” Izi mwina zidzamkhutiritsa pakali pano. Nthaŵi ina mwanayo angadzafunse kuti: “Kodi mwana amatuluka bwanji?” Mungayankhe kuti: “Mulungu anapanga chiboo chapadera chotulukirapo mwana.” Nzeru za mwana zakumva zimakhala zazing’ono, choncho mayankho okhweka ndi olunjika ndiwo abwino koposa. Perekani chidziŵitso chofunikira chaching’ono nthaŵi iriyonse, zowonjezereka mukuzisungira mtsogolo.

Ngati makolo ngatcheru, angapeze mipata yambiri yakuphunzitsa. Ngati wachibale wapafupi akuyembekezera kuwona mwana, amayi akhoza kunena kuti: “Alamu ako a Febi mwina adzakhala ndi mwana posachedwapa—ndinali mmene aliri choncho kutatsala milungu ingapo kuti iweyo ubadwe.” Kubadwa kwa mchimwene kapena mchemwali koyembekezeredwa kungapereke miyezi ya kuphunzitsa kwabwino ndi kosangalatsa.

Pambuyo pake mwanayo angazizwe nati: “Kodi mwanayo anayambika motani?” Yankho lokhweka nlakuti: “Mbewu yochokera mwa Atate imakumana ndi dzira mkati mwa amayi ndiyeno mwana amayamba kukula, monga momwe mbewu m’nthaka imakulira kukhala duŵa kapena mtengo.” Nthaŵi ina mwanayo angafunsenso kuti: “Kodi mbewu ya atate imaloŵa bwanji mwa amayi?” Mukhoza kulongosola bwinobwino kuti: “Umadziŵa mmene mnyamata aliri. Iye ali ndi mpheto yachimuna. Amayi ali ndi chiboo pathupi pawo pamene mpheto yachimuna imaloŵa, ndipo mbewuyo imadzalidwa. Ndimmene Mulungu anatipangira kotero kuti ana adziyambikira m’malo abwino ofunda, kufikira atakula pamsinkhu wokhoza kukhala paokha. Pamenepo kamwana kabwino kamabadwa!” Mukhoza kulankhula mosonyeza kuzizwa ndi njira imene Mulungu analinganizira zinthuzi.b

Muyenera kukhala wosamala kusapeŵa mafunsowo mwakuchita manyazi ndikunena kuti: “Ndikakuuza utakulako pang’ono.” Izi zidzakulitsa chilakolako cha ana chofuna kudziŵa ndipo zingawasonkhezere kukafunsa kwa anthu osayenera. Mwana wokhoza kufunsa mafunso akhozanso kumva yankho lokhweka laulemu. Kulephera kwanu kuwapatsa yankho kungapangitse ana anu kuleka kudalira pa inu kaamba ka kudziŵa zinthu.

Muyenera Kuyamba Mwamsanga Chotani?

Makolo ambiri amalingalira kuti ana awo ayenera kudziŵa zoyambirira za zinthuzi asanayambe kupita kusukulu, kumene angakamve zosalongosoka kwa ana ena.

Agogo ŵamuna anafotokoza kuti: “Sindinafunsepo mafunso aliwonse, koma pamene ndinafika zaka zisanu ndi chimodzi, atate anaganiza kuti nthaŵi inakwanira yondifotokozera kumene ana amachokera. Iwo ananena kuti kugwirizana kwakugonana kwa mwamuna ndi mkazi kumene kungatulutse mwana kunali kwachibadwa mofanana ndi kudya, koma Mulungu anati izi ziyenera kuchitidwa kokha ndi anthu okwatirana. Motero, nthaŵi zonse pamakhala amayi ndi atate amene amamkonda mwanayo ndi kumsamalira.” Agogo ameneŵa anawonjezera kuti: “Malongosoledwe amene anandipatsa anabwera panthaŵi yake. Ndinali nditawonapo kale ana azaka zisanu ndi chimodzi akuseka zithunzithunzi zachisembwere zomwe anazijambula zimene sindinadziŵe chimene zinatanthauza.”

Ndithudi, malongosoledwe oterowo ayenera kuperekedwa, osati monga chinthu chochititsa manyazi, koma monga chinthu chamtseri. Mukhoza kumachenjeza nthaŵi zonse kuti ndichinsinsi cha m’banja chimene sichiyenera kutchulidwa kwa ana ena kapena anthu akunja kwa banja. Ngati mwana wanu ataya mkamwa pazimenezi, mukhoza kumpapasa ndikuti: “Shhh! Kumbukira, icho ndichinsinsi chathu. Timachilankhulira m’banja mwathu mokha.”

Sizochititsa Kakasi

Ngati chifuno chakukambitsirana zimenezi chichititsa kakasi woŵerenga aliyense, tangolingalirani zakuchuluka kwa makolo achichepere osamala amene akufunafuna njira yaulemu yofotokozera nkhani zimenezi kwa ana awo. Kodi malongosoledwe achindunji m’banja lachikondi sali abwino koposa njira imene makolo ambiri anaphunzirira zimenezi, mwanjira zonyansa kunja kwa banja?

Ngati mumamvetseradi ndipo ngati mumayankha mafunso mwanjira yokhweka ndi yaulemu, mudzakupangitsa kukhala kosavuta kwa ana anu kubwera kwa inu ndi mafunso ena pamene akukula ndi pamene afuna kudziŵa zochulukirapo.

[Mawu a M’munsi]

a Mwana aliyense ali wosiyana. Chotero, misinkhu iriyonse yotchulidwa m’nkhanizi njachisaŵaŵa, kusonyeza kupita patsogolo kwa kaphunzitsidwe kameneka.

b Bukhu la Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe limafotokoza mbali imeneyi ndi zina zambiri zolerera ana m’makhalidwe oyenera ndi moyo wabanja wabwino. Mukhoza kulifunsa kwa anthu amene anakubweretserani magazini ano kapena kwa owafalitsa pamakeyala ali patsamba 5.

[Chithunzi patsamba 6]

Kubadwa kwa mwana koyandikira kumapatsa mwaŵi wakupereka malangizo othandiza

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena