Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 4/8 tsamba 12
  • Kodi Pangakhaledi Nkhondo Yolungama?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Pangakhaledi Nkhondo Yolungama?
  • Galamukani!—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Armagedo—Liti?
    Nsanja ya Olonda​—1990
Galamukani!—1992
g92 4/8 tsamba 12

Kodi Pangakhaledi Nkhondo Yolungama?

MKATI mwa zaka mazanawa, Chikristu Chadziko chanena zambiri ponena za lingaliro la “nkhondo yolungama.” Chaka chatha magazini a Time anafalitsa ziyeneretso zazikulu zisanu ndi chimodzi zimene akatswiri a maphunziro azaumulungu amalingalira kuti nkhondo iyenera kuzikwaniritsa kuti ilingaliridwe kukhala “yolungama.” Mbiri yakale imatsimikizira kuti palibe iriyonse ya nkhondo zochilikizidwa ndi Chikristu Chadziko yomwe inakwaniritsadi ziyeneretso zimenezi.

Koma Harmagedo, nkhondo yomwe Mulungu walonjeza kubweretsa pa dongosolo la zinthu loipali, ikukwaniritsa miyezo yonse isanu ndi umodzi ya akatswiri a maphunziro azaumulungu.

“Imakhala ndi ‘cholinga chabwino,’ monga kudzichinjiriza kapena kulaka choipa.” Harmagedo idzachotseratu mbali zonse za dziko loipa lomwe Satana Mdyerekezi ali mulungu wake. Chotero, zinganenedwe kwa Kristu Yesu, Wankhondo wa Mulungu “Wokhulupirika ndi Woona,” pa Harmagedo kuti ‘aweruza, nachita nkhondo molungama.’—Chivumbulutso 19:11; 2 Akorinto 4:4.

“Ikulengezedwa ndi kutsogozedwa ndi ‘munthu wokhoza.’” Harmagedo ikudziŵika mosalakwa kukhala ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse’—nkhondo yake. Kodi ndani angakhale munthu wokhoza kwambiri kuposa Mlengi wa chilengedwe chonse mwiniyo?—Chivumbulutso 16:14; onaninso 11:17, 18; yerekezerani ndi Yesaya 36:10.

“Ndiyo ‘njira yomalizira’ pambuyo pakulephereka kwa njira zamtendere.” Kwa zaka zikwi zambiri tsopano, Mlengi walimbikitsa—ngakhale kuchonderera—anthu ‘kuyanjanitsidwa ndi Mulungu’ ndi ‘kutumikira Yehova ndi mantha.’ Koma mwakusalabadira zoyesayesa zakudzetsa mtendere ndi machenjezo ochokera kwa Mulungu kwa zaka 6,000, munthu sanasiire Mlengi njira ina yoposa nkhondo.—2 Akorinto 5:20; Salmo 2:2, 10-12.

“Ili ndi ‘kuthekera’ kwa chipambano.” Talingalirani mbali zolimbanazo. Kumbali imodzi kuli magulu onse a mitundu yadzikoli, pamodzi ndi nkhokwe zawo zonse za zida zowopsa. Kumbali ina kuli Mlengi wa chilengedwe chonse. Chimodzi cha zolengedwa zake zazing’ono, dzuŵa, nding’anjo yaikulu ya kutentha kochititsidwa ndi kuphulika kwamphamvu kwa zitima za maatomu kotero kuti ngakhale mitundu itaphulitsa panthaŵi imodzi zida zawo zonse za nyukiliya, kuphulika kumeneko kukawoneka ngati macheso okanika kuyaka. Yehova akhoza kugwiritsira ntchito mphamvu zonse zachilengedwe kutsimikizira kuti nkhondo yake idzakhaladi yachipambano.—Yesaya 40:15; 54:17.

“‘Njolinganiza’—zabwino zodzakwaniritsidwa zidzaposa chiwonongeko chomwe chidzachitidwa.” Talingalirani mtsogolo mopanda nkhondo ya Mulungu ya Harmagedo. Anthu ali okhoterera modzifunira kudziwononga. Atasiidwa kuchita zofuna zake, kodi munthu akatenga utali wotani kuti awononge pulaneti lino ndikusoloka mwamanyazi, mofanana ndi mitundu ya zinyama imene iye waisolotsa? Kodi akakhala masana amodzi okha a chipiyoyo cha nyukiliya? kapena zaka makumi angapo a kuipitsa mbulunga? Mulimonse mmene zingakhalire, ngati Mulungu saloŵerera m’zochita za anthu, ndiye kuti anthu ali paupandu. Kumbali ina, talingalirani zabwino zimene Harmagedo ikulonjeza kudzazikwaniritsa—mtsogolo mwamtendere mwa anthu opembedza papulaneti lino, sikudzakhalanso kuipitsa, nkhondo, umphaŵi, matenda ngakhale imfa. Mulungu akulonjeza kuti: ‘Tawonani, ndichita zonse zikhale zatsopano.’—Chivumbulutso 21:3-5.

“‘Njosankha,’ kupeŵa kuvulaza amene sakutengamo mbali pamene kuli kotheka.” Harmagedo idzakhala yosankha. ‘Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.’—Salmo 37:9.

Onse ofuna kudzakhala opulumuka nkhondo yolungama imeneyi ayenera kudziŵa maziko a ‘kuika chiyembekezo mwa Yehova’ mwakukhala ndi phunziro laumwini la Mawu ake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena