Mboni za Yehova ‘Ziperekedwa kwa Akulu Amilandu’
CHIKRISTU chakumana ndi chitsutso kuyambira pachiyambi chake. Popereka malangizo kwa ophunzira ake, Yesu anachenjeza kuti: “Koma chenjerani ndi anthu; pakuti adzakuperekani inu kwa akulu a mlandu nadzakukwapulani inu m’masunagoge mwawo; ndiponso adzamuka nanu kwa akazembe ndi mafumu chifukwa cha ine, kukhala mboni ya kwa iwo ndi kwa anthu akunja.” (Mateyu 10:17, 18) M’maiko ambiri lerolino, kutsutsa Ufumuwo kwakhala kwamachenjera kwambiri koposa funde la chizunzo cha kupha mwambanda limene linakhalapo mwamsanga pambuyo pa kuphedwa kwa Yesu. M’dziko locholoŵana limene timakhalamo, nkhani zodzutsidwa ndi otsutsa siziri za kufalitsidwa kwa mbiri yabwino ya Ufumu kokha.
Nkhani za Amene Adzasunga Mwana
Bwalo lamilandu limodzi kumene zina za Mboni za Yehova zaperekedwa mowonjezerekawonjezereka ndilo bwalo lamilandu la nkhani zamabanja. Mu Austria, Belgium, Canada, France, Norway, United States, ndi maiko ena, kagulu kakang’ono ka otsutsa kayesa kupangitsa chipembedzo kukhala nkhani yaikulu pogamula nkhani za amene adzasamalira ana pamene Mboni zokhulupirika za Yehova zisudzulidwa ndi anzawo amuukwati osakhulupirira. Kokha chifukwa chakuti iwo anali Mboni za Yehova, makolo amene ali Mboni anataikiridwa ndi kuyenera kwa kusunga ana awo.
Mboni imodzi inataikiridwa ndi kuyenera kwa kusunga mwana wake wamwamuna wazaka zitatu zakubadwa ndipo Mboniyo inakanizidwa ngakhale kutchula chipembedzo mkati mwa nyengo ya kumchezetsa. Dipatimenti ya Zamalamulo ya Watchtower Society inachita apilo lamulo limeneli m’bwalo lamilandu la maapilo. Mlandu wa apilowo unatengedwera ku Bwalo Lamilandu Lapamwamba la ku Ohio State. Mwachimwemwe, pa April 15, 1992, bwalo lamilandulo linagamula mokomera ufulu wa Mboniyo. Chikalata chamasamba 11 chinakantha wotchedwa kuti katswiri wa mboni, amene kwenikweni ali munthu wochotsedwa wodzinenera kukhala katswiri wa zamaganizo. Bwalo lamilandulo linanena kuti iye “anapereka umboni, pamaziko a mawu ochuluka amene adalemba, wakuti nthenda zamaganizo zinali zofala pakati pa Mboni za Yehova koposa pakati pa anthu ena onse. Umboni umenewu unali kuyesayesa kopanda manyazi kwa kupereka chithunzi cholakwika cha chipembedzo chonse chathunthu. . . . [U]mboni umodzi wa ziŵerengero umenewu ngwopanda tanthauzo.”
Bwalo lamilandulo lapereka chiŵeruzo chatsopano, likumati: “[K]uyenera kwa kusamalira mwana sikudzamanidwa kholo kokha chifukwa chakuti iye sadzalimbikitsa mwana wake kuchitira sawacha mbendela, kuchita mapwando amaholide, kapena kuphatikizidwa m’zochita za pambuyo pa sukulu. Tikusintha ziweruzo za mlandu wa kusamalira ndi kuchezera mwana chifukwa chakuti zosankha zimenezi molakwa zinazikidwa pa zikhulupiriro zachipembedzo [za kholo].” Monga chotulukapo, mayi ameneyu anasangalala kufika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu pa April 17 limodzi ndi mwana wake wamwamuna pambali pake m’Nyumba Yaufumu.
Dipatimenti ya Zamalamulo ya ofesi yanthambi ya ku Canada ya Watch Tower Society iri ndi milandu iŵiri imene tsopano ikuyembekezera kuzengedwa ndi Bwalo Lamilandu Lapamwamba la ku Canada pankhani yofananayi. Nthambi ya ku Austria inali ndi chipambano chachikulu cha mlandu pamaso pa European Commission of Human Rights. Kuwonjezerapo, Belgium, France, ndi Norway asimba za zipambano za Mboni zoukiridwa m’milandu yaposachedwapa ya m’mabwalo amilandu m’nkhani zina za kusunga ana m’zimene chipembedzo chinali chandamale chachikulu cha chiukirocho. M’chochitika chirichonse, monga momwe Yesu adanenera, wakhala umboni osati kokha kumabwalo amilandu ndi maloya komanso kwa akunja mwa kufalitsidwa kochitidwa ndi zoulutsira mawu.
Nkhani ya Mwazi
Nkhani ina imene Mboni zikuyang’anizana nayo ndiyo nkhani ya mwazi. Mosasamala kanthu za zilakiko zaposachedwa ponena za ufulu wachipembedzo ndi kudzisankhira kwa Mboni za Yehova m’Mabwalo Amilandu Apamwamba a Florida, Illinois, Massachusetts, ndi New York ndipo mosasamala kanthu za zoyesayesa zosalekeza za Mautumiki a Chidziŵitso cha Chipatala ndi makomiti ambiri olankhulana ndi chipatala a Mboni za Yehova kuzungulira dziko (la United States) lonselo, nkhani yosakondweretsa imeneyi ikupitirizabe kumakhalapo. Komabe, osamalira zaumoyo akupeza umboni, ndipo zipatala zina zikuyesa kuzindikira mwamsanga ndi mwachiwonekere odwala amene ali Mboni za Yehova.
Mboni Yachijapani ku California inachita kuti kaimidwe kake pankhani ya mwazi kalemekezedwe mwa kukhala ndi makambitsirano olinganizidwa m’San Diego. Mkaziyo anavutika ndi nthenda yotupa mitsempha yamwazi muubongo ndipo anakomoka. Khadi lake losainidwa bwino lotchedwa Medical Directive limodzi ndi umboni woperekedwa ndi katswiri wa nthenda za ana amene anamfunsa mafunso ambiri ponena za nkhani ya mwazi pamene anapeza katswiri wa nthenda za ana ameneyo m’ntchito ya pakhomo ndi khomo zinali zokwanira kukhutiritsa woweruzayo kuti Mboni imene inakomokayo sikanavomereza kuthiriridwa mwazi m’mikhalidwe iriyonse.
Mlandu wa ku Long Island kumene Mboni inamangidwa ndi kuthiriridwa mwazi pamene mwamuna wake anagwidwa wapititsidwa ku Bwalo Lamilandu Lapamwamba la New York ndi Dipatimenti ya Zamalamulo ya Watchtower Society. Chiweruzo choyanja zimene Mboni za Yehova ziri ndi kuyenera kwawo chinaperekedwa, ndipo mlanduwo tsopano ukukonzekeretsedwa usanazengedwe m’bwalo lamilandu lamomwemo. Mlandu wa wazaka 16 zakubadwa limodzi ndi mayi wake m’bwalo lamilandu lalikulu ku Atlanta uli pafupi kuŵeruzidwa. Mnyamata wachichepereyo anamangidwa ndi kuthiriridwa mwazi kwamaola asanu ndi atatu. Mlandu wa kupeza lamulo la bwalo lamilandu lovomereza mchitidwe umenewu unazengedwa m’chipatala ndi kuloledwa popanda kudziŵitsa mnyamatayo kapena amayi ake. Pali milandu ina yambirimbiri imene ikuyembekezera mabwalo amilandu a apilo ndi ina yatsopano yomabuka tsiku lirilonse. Nkhondo zikulakidwa, koma kulimbanira zoyenerera za anthu sikunathe. Mboni za Yehova zikuyang’ana kwa Yehova kuti alemekeze lamulo lake pankhani imeneyi, m’nthaŵi yake yokwanira.
Kuyambira mu 1943 Mboni za Yehova zingapo mu United States zaperekedwa kumabwalo amilandu amomwemo pankhani ya kulalikira. Komabe, mlungu uliwonse Watchtower Society imalandira mafoni ndi makalata makumi ambiri ochokera kumabungwe a akulu akumapempha chithandizo pamene Mboni za Yehova ziyang’anizana ndi mavuto muuminisitala wawo wapoyera. Lipoti lina lochokera kuchigawo cha Washington linali ndi chochitika choseketsa kwambiri. Mwininyumba wokwiya anatsekera galimoto ya kagulu ka Mboni mkati mwa mpanda wa nyumba yake naitana apolisi. Mawu ake aukali ndi kuwopseza kwachiwawa kunaŵapangitsa kuyembekezera ali chete mkati mwa galimoto yawo. Pamene galimoto ya kagulu ka apolisi inafika, mmalo mwa kumanga Mbonizo kaamba ka kuloŵa mumpandawo mosaloledwa, apolisiwo anaziyamikira. Mwawona nanga, apolisiwo ananyumwira kuti mwininyumbayo anali wozembera, koma anali osakhoza kufika panyumbayo kuti akatsimikizire. Tsopano popeza kuti anaŵaitanira panyumba yake, iwo anatsimikizira amene iye anali namponyera m’ndende limodzi ndi mkazi amene anali kukhala naye, pamene Mbonizo zinapitirizabe ndi ntchito yawo yolalikira ndi kuphunzitsa.
Mikhalidwe ikusonyeza kuti padzakhala nkhondo zambiri zomenyera zokomera Ufumu. Watchtower Society imayamikira chikondwerero, nkhaŵa, ndi mapemphero a Mboni zambiri kuzungulira padziko lonse kaamba ka chitsogozo ndi malangizo a Yehova posamalira nkhani zovuta zalamulo zimene zikupezeka pochita ntchito ya Mulungu lerolino. Yehova anauza mtundu wa Israyeli kuti iwo sakagonjetsa Dziko Lolonjezedwa panthaŵi imodzi koma kuti zikachitika “pang’ono pang’ono.” (Deuteronomo 7:22) Kupita patsogolo kwa zoyenera za anthu amakono a Yehova kuli pafupifupi kofanana; mwapang’ono pang’ono amapanga kupita patsogolo. Koma mosasamala kanthu kuti akupambana kapena akulephera, nkotsimikizirika kuti paliponse pamene anthu a Yehova akutengedwera patsogolo pa akalonga, mafumu, mabwalo amilandu, kapena pa wina aliyense, pamakhala chotulukapo cha umboni kwa iwo ndi kumitundu.
Mtsogolo pafupipa Yehova adzadzilemekeza iyemwini kotheratu osati kokha pankhani zophatikizapo mwazi ndi kusunga ana komanso pankhani yalamulo yophatikizapo ulamuliro wake. Pamenepo anthu ake adzakhala omasuka kwa otsutsa onse ndi kusangalala ndi chimwemwe chachikulu pansi pa ulamuliro wa Ufumuwo—chifukwa chakuti Yehova ndiye wokonda chiŵeruzo cholungama.—Salmo 37:28.
[Mawu Otsindika patsamba 21]
Mnyamata wachichepere anamangidwa ndi kuthiriridwa mwazi kwamaola asanu ndi atatu