Sankhani Moyo m’Dziko Latsopano Limenelo
MWACHIWONEKERE, Mulungu anali ndi chifuno polenga planeti laling’ono lokongolali. Ndipo analinganiza mtundu wa anthu kukhala ndi mbali yaikulu m’chifunocho. (Yesaya 45:18) Mikhalidwe yowopsa imene dziko lathu lapansili lagweramo siimabweretsa chitamando kwa Mulungu. Koma kodi mumakhulupiriradi kuti iye adzalola mkhalidwewu kupitirizabe? Ndithudi ayi!
Kulakalaka kwa munthu dziko latsopano ndithudi nkochititsidwa ndi kukhumba kanthu kena kamene mtundu wa anthu panthaŵi ina unali nako. Kameneko kanali paradaiso wa padziko lapansi, weniweni, wowoneka. Aŵiri aumunthu oyamba anaikidwa m’malo oterowo, ndipo chinali chifuno choyambirira cha Mlengi kuti mtundu wa anthu usangalale ndi Paradaiso ameneyo padziko lapansi kosatha.—Genesis 1:28.
Yehova Mulungu tsopano akukulonjezani mwaŵi wa moyo m’dziko lake latsopano, kumene adzadalitsa anthu okhulupirika kukhutiritsa zikhumbo za mitima yawo. (Salmo 10:17; 27:4) Kodi mudzasankha kukhala m’menemo?
Muli ndi Chosankha
Aisrayeli amene anamva mawu otsazika a Mose anali ndi chosankha chofananacho choti apange. Anafunikira kusankha kaya ulamuliro wa Mulungu kapena wa amitundu a panthaŵiyo. Nawu uphungu wa Mose: “Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, . . . Potero sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbewu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake ndi kummamatira iye.” (Deuteronomo 30:19, 20) Inde, chosankha chanu chirinso nkhani ya moyo ndi imfa.
Chimenechi ndicho chifukwa chake nkhani zino zonena za dziko latsopano la Mulungu zikufalitsidwa—kuti zikhudze mtima wanu kotero kuti mulisankhe mmalo mwa kuika chiyembekezo chanu m’malonjezo achabechabe a anthu a kulenga dziko latsopano. Pali zinthu zodabwitsa zambiri zimene mufunikira kuphunzira ponena za dziko latsopano la Mulungu.
Mwachitsanzo, kodi pali umboni wotani wakuti dziko latsopano limeneli liri pafupi? Kodi ndimotani mmene lidzalowera m’malo mwa maboma onse apadziko lapansi? Kodi ndizochitika zotani zimene zidzatsogolera kuzimenezi? Kodi tingatsimikizire motani kuti zimene Baibulo limalonjeza zidzakwaniritsidwa?
Mayankho a mafunso amenewa ndi ena ambiri ngopezeka. Mboni za Yehova zikasangalala kukusonyezani m’kope lanu la Baibulo mavesi amene amafotokoza osati kokha madalitso a dziko latsopano la Mulungu komanso amasonyeza kuti ndiliti ndipo ndimotani mmene boma la Mulungu likuyambira ulamuliro wake ndipo potsirizira kufutukula ulamuliro umenewo kuti ulamulire dziko lonse lapansi.
Mukulimbikitsidwa kulabadira monga momwe anachitira Abereya a m’zaka za zana loyamba amene anamvetsera mtumwi Paulo. Iwo anathera nthaŵi “nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.” (Machitidwe 17:11) Mwanzeru, muyenera kuchita chimodzimodzi. Tsimikizirani kuti makambitsirano anu Abaibulo ndi Mboni za Yehova adzakubweretserani chikhutiro chauzimu chachikulu pamene mukuphunzira za mtsogolo mokondweretsa mmene Mulungu akutilonjeza.
Mufunikira kupanga chosankha—kaya cha kutumikira Mulungu ndi zabwino za boma lake Laufumu kapena kuika chidaliro chanu ndi chiyembekezo m’zoyesayesa za anthu za kudzilamulira. Tikukulimbikitsani kuphunzira zambiri monga momwe mungathere ponena za malonjezo a Mulungu kotero kuti chosankha chanu chidzakhala chanzeru. Sikokha kuti kupeza chidziŵitso Chabaibulo kudzapangitsa chiyembekezo chanu chamtsogolo kukhala chamoyo komanso kudzathandiza kukusungani muli wamoyo mwauzimu kupulumuka masiku otsiriza a ulamuliro wa anthu.—2 Timoteo 1:13.
Zaka zambiri za munthu za kulakalaka dziko latsopano ziri pafupi kutha. Mboni za Yehova zifuna kuti inu mudzaloŵe m’dziko latsopano limenelo ndi kusangalala ndi moyo kosatha. Ndizo zimenenso Mulungu amafuna. Kukuyembekezereredwa mowona mtima kuti mudzasankha dziko latsopano la Mulungu. Ngati mutero, pamenepo mudzawona kuti chikhumbo cha anthu chimenecho cha dziko latsopano sichinali konse pachabe.