Dziko Lokopa la Zosangulutsa
HOLLYWOOD! Mosasamala kanthu za kumene mumakhala padziko, dzinalo mwinamwake limakukumbutsani za akanema ndi zosangulutsa zina. Limatchedwa mosiyanasiyana monga malikulu apadziko lonse a zosangulutsa kapena tawuni yonyezimira mopambanitsa, ndipo palibe malo ena aliwonse amene angafanane ndi mzinda umenewu wa Los Angeles, mu California m’malonda akuwonetsa akanema. Umawonekera ndithu kukhala chimake cha padziko lonse cha zosangulutsa ndi zochititsa chidwi. Ziridi monga momwe wolemba nkhani wina ananenera kuti, “chithunzi cha Hollywood monga malo opekera maloto a akanema ochititsa chidwi chafikira dziko lonse.”
Zosangulutsa—Malonda Aakulu
Koma sichithunzi chokha cha Hollywood chimene chafalikira padziko lonse; “Hollywood” ndimalonda aakulu, ogulitsa zinthu kumaiko akunja kuzungulira dziko lonse lapansi. Kwenikweni, malinga ndi kunena kwa magazini a Time, pambuyo pa makina akuthambo, zosangulutsa ndizo zachiŵiri pazinthu zogulitsidwa kwambiri kumaiko akunja zopangidwa ndi United States. Malonda a zosangulutsa amapezera dzikolo madola mabiliyoni mazana ambiri chaka chirichonse, ndipo unyinji wina—pafupifupi 20 peresenti—umachokera ku maiko ena.
United States amapeza ndalama kuyambira pa 35 peresenti m’malonda apadziko lonse akugulitsa mabuku, 50 peresenti ya ndalama zopezedwa m’nyimbo zojambulidwa, 55 peresenti ya ndalama zopezedwa ponse paŵiri pa akanema ndi mavidiyo, ndi kuyambira pa 75 mpaka 85 peresenti ya ndalama zopezedwa pa TV.
Pamene akupeza phindu lalikulu limeneli, Hollywood nayenso amasangulutsa dziko lonse. Sikuti nthaŵi zonse dziko limakondwera naye—maiko oposa limodzi adandaula ponena za kululuza miyambo ya ena kwa Amereka, popeza kuti achichepere awo akusiya miyambo ndi mikhalidwe yawo ndi kutsatira malingaliro ndi makhalidwe opambanitsa ochokera ku Amereka. Komabe, sikuti zosanguluka zimachokera ku United States kokha. Maiko ambiri ali nazo zosangulutsa zawo—akanema, ma TV, nyimbo zojambulidwa, mabukhu, maseŵera, ndi zina zotero.
Zosangulutsa—Zosavuta Kupeza Lerolino
Mosasamala kanthu kuti ndani amene amasangulutsa dziko kapena amene ayenera kutero, chodziŵika kwambiri nchakuti zosangulutsa izo zenizo zimapezeka mosavuta, nzochuluka kwambiri lerolino kwakuti pali mipangidwe yake yachilendo kotheratu. Tifotokoze mwafanizo: Ngati mukadakhalako zaka zana limodzi zapitazo, kodi mukadasangulutsidwa kangati ndi akatswiri amaseŵero? Ngakhale ngati mukadakhala m’maiko olemera koposa, mukadasoŵadi zokusangulutsani malinga ndi kawonedwe ka mbadwo wa lerolino. Mwachitsanzo, mukadakhala ndi vuto lokafika kumene kuli kanema kapena gulu la oimba konsati. Lerolino timangomvetsera pa masteriyo okhoza kunyamulidwa amene amaimba nyimbo iriyonse yokhalapo, kapena timangokhala pampando m’nyumba, kusinika batani, basi nkusangulutsidwa ndi maseŵera aliwonse amene tingalingalire.
M’dziko lotukuka lirilonse, mukhoza kupeza m’nyumba zambiri TV, VCR, ndi CD kapena kasetipuleya, limodzi ndi zipangizo zina zamagetsi. Ana ena amakulira m’nyumba zimene ma TV ali zinthu zofala ngati akalilole. M’maiko otukuka pang’ono, midzi yambiri ndi malo ozungululira ali ndi TV yapamudzipo kumene anthu amasonkhana madzulo kukasangulutsidwa. Mtundu wa anthu wakhala wotengeka maganizo ndi TV. Maola a kupuma amadzazidwa ndi mitundu yowonjezerekawonjezereka ya zosangulutsa.
Kodi pali cholakwika chirichonse ndi zimenezo? Kodi pali maupandu aliwonse m’zosangulutsa zamakono? Kapena kodi kuchulukitsitsa kwa zosangulutsa zamakono kumangotanthauza kupanda pake kwa chuma? Tiyeni tipende dziko lokopa la zosangulutsa ndi lingaliro lachikatikati.