Njira Yoletsera Kuloŵedwa ndi Ululu wa Mtovu
MOSASAMALA kanthu za mbiri yoipa ya kuloŵedwa ndi ululu wa mtovu, mkhalidwewu suli wopandiratu chiyembekezo. Mosiyana ndi matenda ambiri amene sititha kulamulira, umenewu uli chiwopsezo cha umoyo chimene akulu a zaumoyo amanena kuti tingathedi kuchitapo kanthu kena.
“Kuloŵedwa ndi ululu wa mtovu kulidi koletseka,” Newsweek inasimba zimene Secretary of Health and Human Services ya United States ananena. Upandu wa kuloŵedwa ndi ululu wa mtovu “ukhoza kuchotsedwa kosatha,” analengeza motero katswiri wina wotchuka wa payunivesiti wopenda za ululu. “Tsopano zambiri zadziŵidwa ponena za magwero ndi njira zimene mtovu umaipitsira ndi za njira zoletsera kuipitsa kumeneku kotero kuti zoyesayesa zingayambe kuchitidwa kuthetsa nthendayi kwachikhalire,” ikutero CDC (Centers for Disease Control ya ku United States). Ndipo potsiriza, Department of Health and Human Services ya United States ikuwonjezera lingaliro lake kuti: “Tidziŵa zochititsa kuloŵedwa ndi ululu wa mtovu kwa paubwana ndipo, chofunika koposa, mmene kungathetsedwere. Kugwirizana kwa anthu pakuchita kuyesayesa kungathetsedi nthendayi m’zaka 20.”
Zimene Mungachite
Kodi zimenezi zingachitidwe motani? Choyamba, akatswiri amavomereza kuti utoto ndi madzi ali chandamale chachikulu. Mwachitsanzo, katswiri wa za ululu wotchulidwa pamwambapa akunena kuti chofunika kwambiri pakuletsa kuloŵedwa ndi ululu wa mtovu nchakuti eninyumba ndi okhalamo ake achite zonse zothekera kuchotsa utoto wakale ndi mapaipi. Chotero, okhala m’nyumba angafune kudziŵa ngati nyumba zawo siziri zoipitsidwa.
“Koma osatekeseka,” akutero magazini a In Health. “Utoto wosakanganuka suli wowopsa, ngakhale kuti utoto wokanganuka ndi fumbi la utotowo nzowopsa. . . . Funafunani utoto wokanganuka mkati ndi kunja kwa nyumba yanu, mukuyang’ana makamaka m’mbali mwa zitseko zamatabwa ndi maferemu a mazenera, m’mene mphepo ndi kukwichisa zimakanganula utoto kukhoma.” Dipatimenti ya zaumoyo ya boma lakwanu ingakhoze kukuthandizani kufufuza ngati nyumba yanu iri pangozi, mwinamwake mwakukuuzani kupita kunyumba zopimira za ophunzitsidwa kufufuza ndi kuchotsa mtovu. Nali chenjezo: Musayese kuuchotsa nokha. Ana angaloŵedwe ndi mtovu pamene makolo awo apala ndi kufufuta utoto wakale kumakoma ndi nsitchi, akumadzaza mpweya ndi fumbi lamtovu.
Madzi, Madzi Ponseponse
M’nyumba zimene madzi ali nakatande, vuto lingachokere m’mapaipi amene amalunzanitsa nyumbayo kupaipi yaikulu ya madzi. Nyumba yakale ingakhale ndi mapaipi amtovu, amene ali magwero odziŵikiratu a kuipitsa. Ngakhale mapaipi a mkuwa ndi chitsulo angakhale olunzanitsidwa ndi mtovu. M’maiko ena kungakhale kothandiza kufufuza malamulo a kumanga pofuna kudziŵa za miyezo yoikira mapaipi m’dera lanu. Ngati muli ndi chifukwa chokhulupirira kuti madzi anu ngoipitsidwa, mungasankhe kuti apimidwe. M’maiko ochuluka muli nyumba zopimira zokonzekera kuchita zimenezi pamtengo wabwino.
Bwanji ngati madzi anu ali ndi mlingo wowopsa wa mtovu? Kodi mungachite nawo chiyani? Ndiiko komwe, sialiyense amene angachitepo kanthu, monga ngati kusinthiratu mapaipi. Akulu a zaumoyo akupereka njira zosavuta zingapo zochepetsera mlingo wa mtovu. Musanatunge madzi kumpope, lolani madzi ozizira kutuluka kwa mphindi imodzi kapena ziŵiri, makamaka ngati mpopewo sunatsegulidwe kwa maola oposa asanu ndi limodzi. Kutereku kudzathandizira kutulutsa madzi oipitsidwa. Ndipo osagwiritsira ntchito mpang’ono pomwe madzi otentha akumpope monga akumwa ndi ophikira. Mothekera mudzakhala mtovu wochuluka m’madzi otentha akumpope kuposa m’madzi ozizira akumpope.
Ngati mumwa madzi apakasupe wamagetsi kusukulu, muofesi kapena m’fakitale, madziwo ayenera kuloledwa kutuluka kwa timphindi tingapo musanawagwiritsire ntchito. Akasupe ena ali ndi mapaipi olunzanitsidwa ndi mtovu.
Mtovu m’Zakudya ndi Zakumwa
Food and Drug Administration (FDA) ya ku Amereka yapereka malingaliro ponena za kugwiritsira ntchito ziŵiya zagalasi zamtovu. Magazini a Good Housekeeping ananena kuti: “Pamene palibe aliyense amene akunena kuti musiiretu kuzigwiritsira ntchito, FDA ikupereka lingaliro la kupeŵa kugwiritsira ntchito ziŵiya zamtovu kusungiramo zakudya ndi zakumwa kwa nyengo yaitali, makamaka posunga zakudya za asidi (sumu; malalanje, matimati, ndi zakumwa zina za zipatso; vinyo; ndi viniga) . . . FDA ikuperekanso lingaliro lakuti makanda ndi ana asamayamwitsidwa kumabotolo amtovu . . . kapena ziŵiya zina zirizonse zamtovu.”
Bwanji za mabotolo a vinyo ovundikiridwa ndi mtovu? Akatswiri ena azaumoyo akupereka lingaliro la kuchotsa mtovu wonse ndipo, pambuyo pakuchotsa chivimbo, nkunyowetsa nsalu ndi madontho ochepera a vinyo ndiyeno kupukuta nayo mlomo wa botolo.
Anakubala ndi akazi apanyumba, kodi muli ndi chizoloŵezi cha kugwiritsiranso ntchito matumba a mkate apulasitiki kusungiramo chakudya? Ofufuza apeza mtovu wochuluka muinki wogwiritsiridwa ntchito kulembera pamatumbawo, umene ungaloŵe m’zakudya. Mtovuwo sumaloŵa m’pulasitiki ndi kukaipitsa mkate umene uli mkati; komabe, pamene wogulayo atembenuza thumbalo, inki wamtovu ungaipitse ziri m’thumbalo. Ngati mugwiritsiranso ntchito thumbalo, tsimikizirani kuti zilembo zake sizikhudza chakudya.
Pomalizira, magazini a Discover akupereka chenjezo ili: “Opita paulendo kumaiko akutali, makamaka m’maiko Osatukuka, ayenera kuchenjera ndi ziŵiya za dothi; utoto wake wamtovu ungakhale wosawotchedwa ndi moto wotentha kwambiri wofunikira kuletsa kugamphuka, kukanganuka, ndi kuloŵa m’chakudya kwa zidutswa zamtovu.”
Khalani Wachikatikati
Chitsogozo chimodzi chofunika kukumbukira polingalira zimenezi kapena pafupifupi mavuto osautsa aliwonse a lerolino a m’malo otizungulira nchakuti: Khalani wachikatikati. Kuli kosavuta kwambiri kuchita mantha, ndipo mantha sathandiza konse. Umboni womvetsa chisoni ngwakuti malo athu otizungulira akuipitsidwa ndi zoipitsa zosaŵerengeka kuwonjezera pa mtovu. Kuti tikhale ndi moyo wosaipitsidwa kwambiri, mwinamwake tikayenera kusamukira kumalo ena akutali kwambiri. Koma kodi ndani amene angafune kukhala yekha kuti apeŵe chabe kuipitsa? Njira yokha yoyenera yochitira ndi mavuto otero ndiyo kumvera machenjezo aliwonse oyenera ofunika kuti tidzitchinjirize ifeyo ndi ana athu kuupandu wowopsawu. Tchinjirizo lokwanira kuziyambukiro zodzetsedwa ndi munthu mwakugwiritsira ntchito molakwa zinthu za m’dziko lapansi lidzadza pambuyo pake.
Ndipo lidzabweradi! Kodi mudziŵa kuti Mlengi wa planetili akulonjeza nthaŵi pamene anthu adzagwiritsira ntchito nyonga zawo kulisanduliza kukhala paradaiso? Munthu sadzatayanso zoipitsa zakupha ndi kuipitsa malo alionse. Yesaya 11:9 amawonjezera lonjezo ili: ‘Iwo [anthu] sadzaipitsa, sadzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.’ Nkosakaikiritsa kuti ‘kudziŵa Yehova’ kudzaphatikizapo chidziŵitso cha mmene zinthu zochuluka za paplaneti lino zidzagwiritsidwira ntchito m’njira yosavulaza ana kapena akulu—kapena munthu aliyense.