Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g92 12/8 tsamba 4-7
  • Ana Akupanikizidwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ana Akupanikizidwa
  • Galamukani!—1992
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Matenda
  • Kudya Mosakwanira
  • Mavuto a Malo Otizungulira
  • Nkhondo
  • Kuchitira Ana Nkhanza
  • Zinthu Zofunika
  • Zoyesayesa za Kupulumutsa Ana
    Galamukani!—1994
  • Kufunafuna Njira Zothetsera Mavuto a Ana Kukupitirizabe
    Galamukani!—2000
  • Kodi Pagona Vutoli Mpati, Nanga Kuipa Kwake N’kotani?
    Galamukani!—2003
  • Ana Ayenera Kufunidwa Ndiponso Kukondedwa
    Galamukani!—2000
Onani Zambiri
Galamukani!—1992
g92 12/8 tsamba 4-7

Ana Akupanikizidwa

Mnyamata, wazaka 12, akugwira ntchito yakalavulagaga kwamaola 11 patsiku kuphwanya miyala mumgodi wa ku India. Iye amalipiridwa 85 sensi (U.S.) patsiku.

Msungwana, wazaka khumi, akugulitsa thupi lake m’nyumba ya mahule m’Bangkok. Iye sali kumeneko chifukwa chakuti akufuna kutero. Atate wake anamgulitsa kaamba ka $400.

Msilikali wachichepere, wazaka khumi, akugwira ntchito ya kusecha pamsewu m’dziko lina la ku Afirika. Mfuti yachiwaya yakoloŵekedwa paphewa lake; iye akuthera nthaŵiyo kusuta chamba.

MIKHALIDWE yotero yonseyo njofala kwambiri m’maiko osatukuka. Ana opanikizidwa ali mamiliyoni ambiri. Mamiliyoni asanu ndi aŵiri akuvutikira m’misasa ya othaŵa; mamiliyoni 30 akungoderukaderuka m’makwalala ali opanda pokhala; mamiliyoni 80 amausinkhu apakati pa zaka 10 ndi 14 akugwira ntchito zimene zikuvulaza kukula kwawo kwanthaŵi zonse; oposa bwino lomwe mamiliyoni 100 akuyang’anizana ndi imfa m’zaka za khumi lino chifukwa cha kusoŵa chakudya, madzi oyera, ndi chisamaliro chaumoyo.

Talingalirani ochepa chabe a mavuto oyang’anizana ndi ana kuzungulira padziko lonse lapansi.

Matenda

Ana pafupifupi 8,000 amafa tsiku lirilonse chifukwa chakuti sanabaidwe katemera wa chikuku ndi chifuwa. Ena 7,000 amafa tsiku lirilonse chifukwa chakuti makolo awo samadziŵa mmene angachitire ndi kutha madzi m’thupi kumene kumachititsidwa ndi kuphanguka m’mimba. Tsiku lirilonse ana ena 7,000 amafa chifukwa chakuti samapatsidwa mankhwala ogulidwa ndi ndalama zochepa chabe kulimbanira ndi nthenda za zifuwa.

Kwazaka zambiri mankhwala ndi akatemera akhala opezeka kutetezera kapena kuchiritsira ambiri a matenda amene kwanthaŵi yaitali akantha banja laumunthu. Koma sanafikiridwe ndi mamiliyoni ambiri amene akuwafunikira. Monga chotulukapo, mkati mwa zaka makumi aŵiri zapitazo, ana pafupifupi mamiliyoni zana limodzi aphedwa ndi matenda ophanguka m’mimba ndi zifuwa zokha. “Kuli monga ngati kuti potsirizira pake mankhwala ochiritsira kansa anapezedwa koma ochepa chabe ndiwo anagwiritsiridwa ntchito kwazaka 20,” linadandaula motero lipoti lotchedwa UNICEF’s State of the World’s Children 1990.

Mosasamala kanthu za mkhalidwe wowopsawo, kupita patsogolo kwapangidwa. Mwachitsanzo, gulu la UNICEF ndi la WHO (World Health Organization) apitirizabe ndi mkupiti waukulu wa katemera. Mu 1991 kunalengezedwa kuti 80 peresenti ya ana a padziko lonse anali atabaidwa akatemera a nthenda zisanu ndi imodzi zokhoza kupewedwa mwakatemera—chikuku, konye, diphtheria, polio, kholozi, ndi chifuwa chokoka mtima cha ana. Limodzi ndi zoyesayesa zapanthaŵi imodzimodziyo za kuthetsa matenda a kuphanguka m’mimba, zimenezi zapulumutsitsa miyoyo ya achichepere mamiliyoni angapo chaka chirichonse.

Koma m’zaka zaposachedwapa nthenda ina—AIDS—yatulukira niwopseza ndipo mwinamwake ngakhale kubwezera mmbuyo kupita patsogolo konse kopangidwa pankhani ya kupulumuka kwa ana a mu Afirika kopangidwa m’zaka khumi zapitazo. Mkati mwa zaka khumi za ma 90, achichepere ambiri kufikira mamiliyoni 2.7 angaphedwe ndi AIDS mu Afirika mokha. Podzafika m’chaka cha 2000, ana ena mamiliyoni atatu kufikira asanu Pakati ndi Kummaŵa kwa Afirika angadzakhale ana amasiye chifukwa cha kuphedwa ndi AIDS kwa makolo awo.

Kudya Mosakwanira

Tonsefe tazoloŵerana moŵaŵa mtima ndi zithunzithunzi zomvetsa chisoni za ana ofa ndi njala owonda kukhala mafupa okhaokha, otupa mimba, ndi maso otong’oka. Achichepere omvetsa chisoni amenewo akuimira mbali yaing’onong’ono chabe ya vuto la kusadya mokwanira. M’maiko onse osatukuka, ana pafupifupi mamiliyoni 177—1 mwa 3 alionse—amagona ndi njala. Ndipo chiŵerengero chawo chikuwonjezereka.

Kusadya mokwanira kopitirizabe kumapangitsa ana kusafikira mkhalidwe wokwanira wamaganizo ndi wakuthupi. Ana odya mosakwanira ochulukitsitsa ali olobodoka, ogodomala, amaso ololomoka, ndi amphwayi. Iwo amaseŵera pang’ono ndipo amaphunzira mochedwera koposa ana omadya bwino. Iwo amayambukiridwanso mwamsanga ndi matenda, mfundo yaikulu imene imathandizira pafupifupi mbali imodzi mwa zitatu za imfa za ana mamiliyoni 14 m’maiko osatukuka chaka chirichonse.

Monga momwedi sayansi yamakono yapezera mankhwala ogonjetsera nthenda, choteronso yakupangitsa kukhala kotheka kulima ndi kubweretsa chakudya choposa chokwanira kaamba ka aliyense padziko lapansi. Koma palibe zothetsera zamwamsanga za kudya mosakwanira. Sikungathetsedwe ndi kutumizidwa kwa chakudya ndi mibulu yamavitamini. Nakatande wake ndiye umphaŵi wosatha, umbuli wofala, madzi oipa, mikhalidwe yauve, ndi kupanda malo olima m’madera okanthidwa ndi umphaŵi.

Mavuto a Malo Otizungulira

Pamene kupanikizika kwapadziko lonse lapansi kwa malo otizungulira kukulakulabe, ali ana amene amayambukiridwa kopambana. Talingalirani za kuipitsidwa kwa mpweya. Pausinkhu wosafikira zaka zitatu mwana amakoka mpweya woŵirikiza kaŵiri, ndipo limodzi nawo zinyansi zoŵirikiza kaŵiri, koposa wachikulire amene akupuma. Ndipo popeza kuti ana ali ndi impso, chiŵindi ndi maenzyme zosakhwima kwambiri, iwo ali osakhoza kuchita ndi zoipitsazo mogwira mtima kwambiri monga momwe achikulire angachitire.

Chotero ana amavulazidwa kwambiri koposa achikulire ndi msanganizo ya mtovu m’mafuta okhoza kuyaka ndi mpweya wonga wa carbon monoxide, nitric oxides, ndi dioxide ya sulfure. Kufulumira kuyambukiridwa kumeneku kumawonjezera mwachindunji imfa za ana oposa mamiliyoni 4.2 azaka zosafikira zisanu zakubadwa amene amafa ndi nthenda za zifuwa chaka chirichonse m’maiko osatukuka. Opulumuka ambiri amakula ali ndi matenda a kusapuma bwino amene amaŵakantha kwamoyo wawo wonse.

Popeza kuti adakakulabe mwakuthupi, ana alinso osavuta kuyambukiridwa ndi kudya mosayenera koposa achikulire. M’maiko osiyanasiyana, ana ndiwo otaikiridwa kwambiri pamene nkhalango zizimiririka, zipululu zikula, ndipo nthaka ya minda yolimidwa mopambanitsa ikokololedwa, ifikira posukuluka, ndi kutulutsa chakudya chocheperachepera. M’Afirika mokha ana pafupifupi mamiliyoni 39 amapinimbira chifukwa cha kupanda chakudya cholimbitsa thupi.

Kowonjezeredwa pavutolo ndiko kupereŵera kwakukulu kwa madzi abwino. M’maiko onse osatukuka, theka limodzi chabe la ana ndilo limene limapeza madzi akumwa oyera, ndipo ocheperapodi amapeza ziŵiya zotairako zinyalala.

Nkhondo

M’nthaŵi yapita, mikhole yambiri ya nkhondo inali asilikali. Osati tsopano. Chiyambire nkhondo yadziko yachiŵiri, 80 peresenti ya mamiliyoni 20 ophedwa ndi mamiliyoni 60 ovulazidwa m’nkhondo zosiyanasiyana anali anthu wamba—kwakukulukulu akazi ndi ana. Panthaŵi ina mkati mwa ma 1980, ana 25 mu Afirika ankaphedwa ola lirilonse ndi nkhondozo! Ana osaŵerengeka aphedwa, kupundulidwa, kunyanyalidwa, kupangidwa kukhala amasiye, kapena kutumbidwa.

Mamiliyoni ambiri a ana amene tsopano akukulira m’misasa ya othaŵa kaŵirikaŵiri amapangitsidwa kusadzidziŵa kuti ndani ndi kuti kwawo nkuti namanidwa chakudya chokwanira, chisamaliro cha zaumoyo, ndi maphunziro. Ambiri amakupeza kukhala kosatheka kupeza maluso amene adzawapezetsa ntchito m’chitaganya.

Koma ana sali mikhole ya nkhondo chabe; alinso omenya nkhondo. M’zaka zaposachedwapa achichepere 200,000 ausinkhu wosafikira zaka 15 zakubadwa alembetsedwa, kupatsidwa zida, ndi kuphunzitsidwa kupha. Pakati pawo pali awo amene anafa kapena kupunduka pamene anamvera malamulo a kulambula njira yopyola m’malo otcheredwa mabomba.

Kuchitira Ana Nkhanza

M’maiko onse osatukuka, umphaŵi umapangitsa makolo kugulitsa ana awo pamtengo waung’ono kwambiri kotero kuti apeŵe njala kapena kulipilira ngongole zawo. Kodi chimachitikira achichepereŵa nchiyani? Ena amakakamizidwa kukhala mahule kapena akapolo ogwira ntchito yotopetsa yamalipiro ochepa m’mafakitale auve. Ena amagulitsidwanso ndi ndalama zofikira ku US$10,000 ndi anthu olemera mwachikatikati kapena magulu olera a ku Madzulo.

Zisonyezerozo zimasonyeza kuti uhule wa ana ukuwonjezereka ndipo umaphatikizapo ana aang’ono kwambiri, ponse paŵiri anyamata ndi asungwana. M’Brazil mokha, kukulingaliridwa kuti muli mahule azaka 13-19 ambiri ofikira ku 500,000. Zithunzithunzi zosonyeza ana amaliseche nazonso zikuchuluka ndipo zawonjezeredwa ndi ziŵiya zamavidiyo zopezedwa mosavuta.

Zinthu Zofunika

Nkovuta kumvetsetsa ululu ndi kuthedwa nzeru kwa ziŵerengerozo. Mwamwaŵi, sitingathe kuzindikira kuvutika kwa mamiliyoni kapena kwa zikwizo. Komabe, ambiri a ife timadziŵa mmene kuliri kovuta kuwona mazunzo kapena imfa ya mwana mmodzi yekha—munthu wokhala ndi umunthu wakewake, moyo wamtengo wapatali kwa Mulungu, munthu wokhala ndi kuyenera kwa kukhala ndi moyo ndi kukula mofanana ndi wina aliyense.

Popanda kuthera nthaŵi yambiri kulingalira nkhani yosakondweretsa yonena za chifukwa chake mkhalidwe wa ana uli mumkhalidwe wake ulipowu, nthumwi za ku Msonkhano wa Dziko wa Ana zinalankhula mwachidaliro ponena za mtsogolo nizilumbira kusalekereranso konse mkhalidwewo. “Makonzedwe a Kuchitapo Kanthu” awowo anatsimikiza, pakati pa zinthu zina, kufikira zonulirapo zotsatirapozi podzafika m’chaka cha 2000:

◻ Kuchepetsa mlingo wa imfa za ana ausinkhu wosafikira zaka zisanu amene anafa mu 1990 ndi mbali imodzi mwa zitatu.

◻ Kuchepetsa mlingo wa kusadya bwino kwakukulu kapena kwachikatikati kwa ana azaka zosafikira zisanu kukhala theka la milingo ya 1990.

◻ Kupereka madzi akumwa abwino m’dziko lonse ndi njira zaukhondo zotaira chimbudzi.

◻ Kutetezera ana m’mikhalidwe yovuta mwapadera, makamaka m’mikhalidwe ya nkhondo.

Mtengo wowonjezereka wa maprogramu okwaniritsira zonulirapo zimene zikapewetsa imfa za ana mamiliyoni 50 m’ma 1990 wayerekezeredwa kukhala zikwi mamiliyoni US$2.5 pachaka.

Zimenezo siziri ndalama zochuluka kwambiri pamlingo wa dziko lonse. M’chaka chimodzi makampani a ku America amawonongera zikwi mamiliyoni US$2.5 kutsatsira malonda afodya. M’tsiku limodzi dziko limawonongera zikwi mamiliyoni US$2.5 pazankhondo.

Pakali pano, ndalama zowonongedwera pazankhondo—zoyerekezeredwa mosapambanitsa ndi gulu la Mitundu Yogwirizana kukhala zoposa US$1,000,000,000,000 pachaka—zimapambana ndalama zolandiridwa pachaka ndi theka la anthu aumphaŵi kopambana. Kupambutsidwa kwa 5 peresenti yokha ya chiwonkhetso chankhaninkhani chimenechi kukakhala kokwanira kufulumizitsa kupita patsogolo kulinga kukufikira zonulirapo zamsonkhanowo. Mwachitsanzo, mtengo wa ndege yankhondo yajeti imodzi ya F/A-18 (yochita mamiliyoni US$30) ngwolingana ndi mtengo wogulira mankhwala akatemera okwanira kutetezera ana mamiliyoni 400 kumatenda akupha.

Mitundu iri yokhoza kufikira zonulirapo zokhumbidwazo zolinganizidwa pamsonkhanowo. Iri ndi chidziŵitso, luso lazopangapanga, ndi ndalama. Funso liripobe lakuti, Kodi idzatero?

[Bokosi patsamba 6]

Kugonjetsa Kudya Mosakwanira

Mfundo Zisanu ndi Imodzi Zimene Makolo Ayenera Kudziŵa

1. Mkaka wa maere wokha ndiwo chakudya chabwino kopambana kaamba ka moyo wa mwana wamiyezi inayi kufikira isanu ndi umodzi. Umapereka chakudya chokwanira chotetezera mwana kumatenda ofala.

2. Podzafika usinkhu wamiyezi inayi kufikira isanu ndi umodzi, mwanayo afunikira chakudya china. Kufulumira kumpatsa chakudya cholimba kumawonjezera upandu wa kuyambukiridwa ndi matenda; kuchedwa kumpatsa kumatsogolera kumatenda opangitsidwa ndi kudya kosakwanira.

3. Mwana wausinkhu wosafikira zaka zitatu afunikira kupatsidwa chakudya nthaŵi zoŵirikiza kaŵiri koposa wachikulire, ndi m’milingo yochepa ya chakudya chopatsa thanzi.

4. Simuyenera kuleka kumpatsa chakudya ndi zakumwa pamene mwana wadwala kapena akuphanguka.

5. Pambuyo pa kudwala, mwana afunikira chakudya chowonjezereka patsiku kwa mlungu umodzi kuti afikitse kukula kumene anataikiridwa nako.

6. Nthaŵi yosachepera zaka ziŵiri mwana atabadwa ndipo wina asanabadwe njofunika kaamba ka thanzi labwino la onse aŵiri mayi ndi mwanayo.

[Mawu a Chithunzi]

UNICEF/C/91/ Roger Lemoyne

Magwero: United Nations Children Fund

[Chithunzi patsamba 5]

Theka lokha la ana a m’maiko osatukuka ndiwo amene amapeza madzi abwino akumwa

[Mawu a Chithunzi]

UNICEF/3893/89/ Maggie Murray-Lee

[Chithunzi patsamba 7]

Mwana aliyense, limodzi ndi umunthu wake wapadera, ngwamtengo wapatali kwa Mulungu ndipo ali ndi kuyenera kwa kukula mofanana ndi wina aliyense

[Mawu a Chithunzi]

Photo: Cristina Solé/Godo-Foto

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena