Kodi Nchifukwa Ninji Pali Chiyembekezo Chachidwi Choterocho cha Dziko Latsopano?
Mapeto a Dziko—Kodi Ali Pafupi Motani?
KODI kutha kwa dzikoli kumatanthauzanji? Kuwonongedwa kwa dziko lapansi ndi moto, monga mmene zimaphunzitsira zipembedzo zina? Ayi; kodi zimenezo zingachitike motani, pamene Salmo 104:5 limati: “Silidzagwedezeka ku nthaŵi yonse”?
Yankho limapezeka pamene tiyang’ana m’mbuyo zaka mazana ambiri ku dziko limene linaliko lisanakhale lino. Ilo linaipa ndi kupandukira Mulungu, chotero “dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka.” Koma pamene dziko limenelo, lophatikizapo ponse paŵiri miyamba ndi dziko lapansi, linawonongedwa ndi Chigumula cha tsiku la Nowa, miyamba yeniyeni ndi dziko lapansi sizinapite. Moteronso mapeto a dziko lino samatanthauza chiwonongeko cha moto cha miyamba yokhala ndi nyenyezi ndi pulaneti Dziko Lapansi.—2 Petro 3:5, 6; Genesis 6:1-8.
Nthaŵi zina Baibulo limagwiritsira ntchito liwu lakuti “miyamba” ndi “dziko lapansi” mophiphiritsira. “Miyamba” ingagwiritsiridwe ntchito kutanthauza Satana, mulungu wa dziko lino; olamulira okhala pansi pa ulamuliro wake; ndi auzimu a choipa m’zakumwamba—zonse zomwe zimapereka chisonkhezero chauchiwanda pa anthu. (2 Akorinto 4:4; Aefeso 6:12) Kaŵirikaŵiri “dziko lapansi” limagwiritsiridwa ntchito kusonya kwa anthu padziko lapansi. (Genesis 11:1; 1 Mafumu 2:1, 2; 1 Mbiri 16:31; Salmo 96:1) Ndimiyamba yophiphiritsira ndi dziko lapansi la dziko loipa lilipoli limene 2 Petro 3:7 akunena kuti lidzawonongedwa ndi “moto.”—Agalatiya 1:4.
Petro anapereka mbiri yosangalatsa yakuti dziko lakaleli lidzaloŵedwa m’malo ndi latsopano: “Koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.”—2 Petro 3:13.
Dziko Latsopano Lopanda Misozi Kapena Imfa
Chilengezo cha Petro chakuti chilungamo chidzakhalitsa m’dziko latsopano limenelo ndi mbiri yolandiridwa, koma zimene Yohane akuwonjezera ponena za ilo zimapangitsa munthu kukondwera kwakukulu! Iye akunena za ilo pa Chivumbulutso 21:3, 4 kuti: “Ndipo ndinamva mawu aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Tawonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”
M’malo mowononga dziko lapansi ndi moto, Yehova akufuna kuti padzakhale anthu kosatha: “Pakuti atero Yehova amene analenga kumwamba, Iye ndiye Mulungu amene anaumba dziko lapansi, nalipanga; Iye analikhazikitsa, sanalilenga mwachabe; Iye analiumba akhalemo anthu.”—Yesaya 45:18.
Chilungamo chidzakhalitsamo chifukwa chakuti palibe munthu wosalungama amene adzakhalamo: “Pakuti oongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.”—Miyambo 2:21, 22.
Mouziridwa, wamasalmo Davide akutsimikiziranso nkhaniyi kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:10, 11.
Yesu iyemwini akutsimikizira zimenezi, akumanena mu Ulaliki wake wa pa Phiri kuti: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.” Monga boma lawo, ofatsa ameneŵa adzadalitsidwa ndi miyamba yatsopano yolungama imene amapemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 5:5; 6:10.
Mtendere wochuluka umene nzika za dziko latsopano limenelo zidzasangalala nawo udzafutukukira ngakhale kwa zinyama: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. . . . Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga [madzi] adzaza nyanja.”—Yesaya 11:6-9.
Kodi Lili Pafupi Motani?
Ngati mukulingalira zonsezi kukhala madzi amphutsi, kukhala zosakhulupiririka, taimani ndi kusinkhasinkha. Kuwonjezera pa mbali za chizindikiro chachiungwe cha kukhalapo kwa Kristu Yesu, pali kuŵerengera zaka kwa Baibulo kumene kunasonya ku 1914 kukhala kuyamba kwa kukhalapo kwake. M’magazini a Watch Tower a July 1879, Mboni za Yehova zinafalitsa deti la 1914 kukhala chaka chapadera m’zochitika za ulamuliro wa Ufumu wa Yehova padziko lapansi. Olemba mbiri yakale ambiri ndi openyerera zochitika zadziko avomereza kuti chaka cha 1914 chinabweretsa nyengo yosiyana kotheratu ndi yapadera m’mbiri yonse ya anthu, monga momwe bokosilo likusonyezera.
Chochitika china chimene Yesu anapereka chikupezeka pa Mateyu 24:21, 22: “Pakuti pomwepo padzakhala masauko aakulu, monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso. Ndipo akadaleka kufupikitsidwa masiku awo, sakadapulumuka munthu aliyense: koma chifukwa cha osankhidwawo masiku awo adzafupikitsidwa.”
Yesu anasonyezanso kuti chizindikiro chachiungwe chimenechi chikamalizidwa mkati mwa moyo wa mbadwo umene unawona chikuyambika mu 1914. Pa Mateyu 24:32-34, iye anati: “Koma phunzirani ndi mkuyu fanizo lake; pamene tsopano nthambi yake ili yanthete, niphuka masamba ake, muzindikira kuti dzinja liyandikira; chomwechonso inu, pamene mudzawona zimenezo, zindikirani kuti iye ali pafupi, inde pakhomo. Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka, kufikira zinthu zonsezi zidzachitidwa.”
Kuwona dziko lakaleli—limodzi ndi nkhondo zake zonse, njala, matenda, ndi imfa—zitachotsedweratu kudzakhala kosangalatsa. Kuliwona likuloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano lolungama la Yehova Mulungu—kuthetsa kulira, misozi, matenda, ndi imfa—kudzadzetsa chisangalalo chosatha ndi chimwemwe ndi chitamando chamuyaya kwa Yehova Mulungu, Mlengi Wamkulu ndi Mfumu Yachilengedwe.
Pokhala ndi chiyembekezo chimenechi patsogolopa, nkosadabwitsa kuti ambiri akhala ndi chidwi choterocho kuti dziko latsopano lolungama la Yehova lifulumire ndi kuloŵa m’malo lakaleli lodzazidwa ndi chisoni, upandu, matenda, ndi imfa! Nkosadabwitsa kuti chidwi chawo nchachikulu kwakuti amakhoterera kuika madeti apafupi a kufika kwake! Komabe, tsopano sipali zidutswa zokha za chizindikiro cha kufika kwake zimene zingatipangitse kupereka machenjezo abodza. Tsopano tikuwona chizindikiro chachiungwe chonse chikufunyululuka kupereka maziko amphamvu oikapo chiyembekezo chathu cha chidwi cha mapeto a dziko loipali ndi kuloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano la Yehova.
[Bokosi patsamba 26]
1914—Posinthira Zinthu M’mbiri
NGAKHALE Pambuyo Pa Nkhondo Yadziko Yachiŵiri, Ambiri Amaloza Ku 1914 Kukhala Posinthira Zinthu M’mbiri Yamakono:
“Chilidi Chakacho 1914 Osati Cha Hiroshima Chimene Chimazindikiritsa Posinthira Zinthu M’nthaŵi Yathu.”—René Albrecht-carrié, The Scientific Monthly, July 1951.
“Chiyambire 1914, Aliyense Wozindikira Mikhalidwe M’dziko Wavutika Maganizo Kwambiri Ndi Chimene Chawonekera Ngati Ulendo Wolinganizidwiratu Ndi Wotsimikizirika Womka Kutsoka Lokulirapo Mowonjezerekawonjezereka. Anthu Ambiri Olingalira Kwambiri Afika Pa Kulingalira Kuti Palibe Chimene Chingachitike Kupeŵa Kuloŵa M’chiwonongeko.”—Bertrand Russell, The New York Times Magazine, September 27, 1953. “Nyengo Yamakono . . . Inayamba Mu 1914, Ndipo Palibe Amene Amadziŵa Kuti Idzatha Liti Kapena Motani. . . . Ikhoza Kuthera M’kupululutsa Kwakukulu.”—The Seattle Times, January 1, 1959.
“Dziko Lonse Linasweka Pafupifupi Pa Nkhondo Yadziko i Ndipo Sitidziŵabe Chifukwa Chake. . . . Zabwino Zinali Pafupi. Kunali Mtendere Ndi Kukhupuka. Ndiyeno Zonse Zinasweka. Takhala M’malere Kuyambira Panthaŵiyo.”—Dr. Walker Percy, American Medical News, November 21, 1977.
“Mu 1914 Dziko Linataya Kugwirizana Komwe Silinathe Kukupezanso Chiyambire Panthaŵiyo. . . . Imeneyi Yakhala Nthaŵi Ya Kusokonezeka Ndi Chiwawa Chachilendo, Ponse Paŵiri Kudutsa Malire Adziko Ndi Mkati Mwa Maikowo.”—The Economist, London, August 4, 1979.
“Zonse Zinali Kupita Patsogolo. Limeneli Linali Dziko Limene Ndinabadwiramo. . . . Mwadzidzidzi, Mosayembekezereka, M’maŵa Wina Mu 1914 Lingaliro Lonselo Linatha.”—Mkulu Waboma Wa Ku Briteni Harold Macmillan, The New York Times, November 23, 1980.
[Chithunzi patsamba 25]
Mtendere wochuluka kwa onse m’dziko latsopano lolonjezedwa