Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingachitenji ndi Homuweki Yochuluka Motero?
“Ntchito yambiri yakusukulu” yanenedwa kukhala chimodzi cha zinthu zochititsa kupsinjika maganizo pakati pa achichepere
“Ngati sunalinganize bwino zinthu, umataya nthaŵi yambiri kulingalira chimene udzachita”
‘TILIBE nthaŵi yokwanira!’ Linadandaula motero gulu la ophunzira akusukulu yasekondale. Kodi nchiyani chinachititsa vutoli? Zofuna za Sukulu ndi homuweki. “Ndimayamba sukulu pa 8:00 a.m. ndi kumaliza pa 5:30,” akutero Véronique wachichepere. “Ndimafika kunyumba ndi 6:30. Nzovuta. Makolo amaganiza kuti kupita kusukulu ndichinthu chosangalatsa. Samamvetsetsa kuti kusukulu kumatopetsa ndi kupsinja maganizo, ndipo tikafika kunyumba, timakhala ndi homuweki.” Sandrine wazaka 17 akuwonjezera kuti: “Ndimathera maola aŵiri kapena atatu usiku uliwonse kulemba homuweki, kuphatikizapo kothera kwa mlungu.”
Véronique ndi Sandrine amakhala ku Falansa, kumene ophunzira ali ndi masiku aatali koposa asukulu mu Ulaya. Ophunzira a m’maiko ena ambiri amadzimva kukhala opsinjika maganizo, olefulidwa, ndi otopetsedwa ndi zonse zofunikira pa nthaŵi yawo. “Ntchito yambiri yakusukulu” yanenedwa kukhala chimodzi cha zinthu zochititsa kupsinjika maganizo pakati pa achichepere.
Popeza kuti nkovuta kwambiri kupeza ntchito masiku ano m’mbali zambiri zadziko, achichepere ambiri amawona kukhala ndi maphunziro abwino monga chinthu chofunika kaamba ka mtsogolo mwawo. Monga momwe Violaine, wophunzira pasukulu yasekondale akunenera kuti: “Mwaŵi wopeza ntchito yabwino ukukhala wovuta kwambiri kotero kuti achichepere lerolino amazindikira kuti pali chinthu chimodzi chokha chomwe angachite—KUPHUNZIRA!”
Kodi Palibe Nthaŵi Yokwanira?
Komabe, amene amachita bwino kusukulu amadziŵa kuti zimafunikira nthaŵi yochuluka ndi nyonga. Ndipo ngati ndinu wachichepere Wachikristu, muli ndi zinthu zambiri zofuna nthaŵi yanu: kufika pamisonkhano Yachikristu, kuphunzira Baibulo, ndi kugaŵana chikhulupiriro chanu ndi ena. (Yohane 17:3; Aroma 10:10; Ahebri 10:24, 25) Baibulo limanenanso kuti pali “mphindi yakuseka” ndi kusanguluka. (Mlaliki 3:1, 4; 11:9) Mofanana ndi achichepere ambiri, mwinamwake mumafuna kukhala ndi kanthaŵi kena kosanguluka ndi kupumula. Koma ntchito yakusukulu ingawoneke kukhala ikukudyerani nthaŵi imene mumafuna kuchita zinthu—ndipo yochepa koposa yochita zinthu zimene mumakonda kuchita.
Komabe, kaŵirikaŵiri vuto silimakhala kusoŵa nthaŵi kokha. Kufufuza kwaposachedwapa kunasonyeza kuti zifukwa ziŵiri zazikulu zimene ophunzira akusekondale amakhalira ndi mavuto akuphunzira zinali “kugwiritsira kwawo molakwa nthaŵi” ndi “kusalinganiza bwino.” Monga momwe wachichepere wotchedwa Olivier anapezera, kulinganiza kwaumwini koipa sikumayambukira magiredi anu okha. Iye akuti: “Ngati sunalinganize bwino zinthu, umataya nthaŵi yambiri kulingalira chimene udzachita.” Pamenepo, kodi mungalinganize motani?
Kawonedwe Kachikatikati ka Ntchito Yakusukulu
Choyamba, muyenera kuiwona bwino ntchito yanu yakusukulu. Baibulo limatiuza “kutsimikizira zinthu zofunika kwambiri.” (Afilipi 1:10, NW) Ndipo pamene mulingalira zimenezo, kodi nchiyani kwenikweni chimene chiyenera kukhala chofunika koposa m’moyo wanu? Kodi sayenera kukhala mathayo anu auzimu? Ndiiko komwe, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Muthange mwafuna ufumu wake ndi chilungamo chake.” (Mateyu 6:33) Zimenezo zimatanthauza kupatsa malo oyamba misonkhano Yachikristu, pemphero, phunziro, ndi ntchito yolalikira kwa ena.
Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ntchito yakusukulu siyofunika? Kutalitali. Koma monga Mkristu, chonulirapo chanu chakupeza maphunziro sichiyenera kukhala kudzikonzekeretsa kaamba ka ntchito ina yakudziko. Mmalomwake, chiyenera kukhala kuphunzira maluso amene adzakuthandizani m’ntchito yanu monga minisitala wa Mulungu. Panthaŵi imodzimodziyo, mukudzikonzekeretsa kukhala wokhoza kupeza ntchito ndi kudzichilikiza nokha, ndipo mwinamwake banja lanu mtsogolo. (1 Atesalonika 4:11, 12; 1 Timoteo 5:8) Kudziŵa zimenezi kuyenera kukuthandizani kukalimira kuchita zimene mungathe kusukulu. Panthaŵi imodzimodziyo, mufunikira kupanga kuyesayesa kwapadera kukhala wolimba mwauzimu.
“Kuipeza nthaŵi” yochita mathayo auzimu, ntchito yapanyumba, kusanguluka, ndi ntchito yakusukulu, kungakhale kovuta kwambiri, koma kungachitidwe.—Aefeso 5:15, 16, NW.
Phindu Lakukhazikitsa Ndandanda
Njira imodzi yopezera nthaŵi ndiyo kuphunzira bwino. Mutu 18 wa buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza umapereka malingaliro ambiri othandiza.a Mwachitsanzo, kodi munayesa kupanga programu kapena ndandanda yochitira ntchito yanu yakusukulu?—Yerekezerani ndi Afilipi 3:16.
Harry Maddox analemba motere m’buku lake lakuti How to Study: “Mosakaikira, vuto lofala kwambiri pophunzira ndilo kulephera kuyamba kusumika maganizo pa ntchitoyo.” Kodi bwanji ponena za inu? Kodi mumanyalanyaza kuchita homuweki yanu kufikira pamene mudzimva kuti mungatero—kapena pamene kuwoneka kukhala koyenerera? Mlaliki 11:4 amachenjeza kuti: “Woyang’ana mphepo sadzafesa; ndi wopenya mitambo sadzakolola.”
Harry Maddox ananenanso kuti: “Nkopepuka kwambiri kutaya nthaŵi yambiri pang’onopang’ono. Ngati simudziikira maola mwinamwake mudzathera nthaŵi kupenyerera T.V., kuŵerenga magazini, . . . kapena kuchita zinthu zambiri zomwe ophunzira opanda luso amakonda kuchita m’malo moyamba ntchito yanu. Ngati muli ndi ndandanda ndipo mufuna kuimamatira, idzakhala ndi mphamvu ya lamulo lomwe siliyenera kuswedwa, ndipo m’kupita kwanthaŵi kuimamatira kudzakhala kosavuta, ndipo mudzayamba kuilingalira monga mbali yachibadwa ya moyo wanu.”
Ngati muchita ntchito yanu yakusukulu molinganizika ndi modziletsa, mudzakhala ndi nthaŵi yambiri. Kukonzekera kwanu kwabwino kungakuthandizeninso kupeŵa kuwombana pakati pa maasainimenti akusukulu ndi kukwaniritsa mathayo anu Achikristu, monga ngati kupezeka pamisonkhano yampingo.
Linganizani Nthaŵi Yanu!
Bwanji nanga za zinthu zina zimene mumafuna kuti zichitidwe, monga ngati ntchito yapanyumba? Panonso, kulinganiza ndiko mfungulo. Yesani kugwiritsira ntchito malingaliro otsatirawa:
Lembani mpambo wa zinthu zoti zichitidwe. Katswiri wolinganiza nthaŵi Stephanie Winston akuvomereza kunyamula kabuku kokhoza kuika m’thumba nthaŵi zonse. Kagwiritsireni ntchito kulembamo “lingaliro lililonse, asainimenti, telephoni, projekiti, ntchito, kapena ulendo—kaya ikule kapena ichepe, isafunike kapena ifunike—panthaŵi imene yabuka.” Poyamba, mpambo wanu ungawoneke waukulu, koma mwakugwiritsira ntchito malingaliro otsatirawa, mungakhoze kuuchepetsa.
Ikani zinthuzo m’dongosolo la kufunika. Zimenezi zingakuthandizeni kusumika maganizo pa zinthu zimene zifunikira kuchitidwa. Panthaŵi imodzimodziyo, mungachotse zinthu zimene zingadikire kapena zimene mulibe nthaŵi yozichita.
Pangani ndandanda. Inde, sinthani mpambo wanu kukhala mmene mungachitire zinthu—ndandanda yolembedwa. Kalenda yaing’ono ya m’thumba, kapena diary ingagwire bwino ntchitoyi. M’malo mochepetsa ufulu wanu, ndandanda yolinganizidwa bwino idzakutheketsani kulamulira bwino nthaŵi yanu.
Linganizani zotheka. Mwakuyesa izi ndi izi, pezani nthaŵi yabwino yochitira zinthu zina. Mwachitsanzo, mungakupeze kukhala kothandiza kuika homuweki yanu panthaŵi yamadzulo kusanade, mukali wogalamuka maganizo.
Komabe, zindikirani kuti simufunikira kulinganiza mphindi iliyonse ya moyo wanu. Pangani ndandanda yanu kukhala yokhoza kusintha, kusiya mpata wa zinthu zosayembekezeredwa ndi zamwadzidzidzi. Sinthani zinthu ngati zikufunikira, koma mamatirani ku ndandanda yanu monga momwe kungathekere. Dziŵani kuti: Kaŵirikaŵiri kumakhala bwino kuchulukitsa nthaŵi imene mukafuna kumaliza ntchito yakutiyakuti. Nthaŵi zonse mukhoza kusintha ngati mwamaliza msanga.
Ikani malire anu. Chimenechi chimakuthandizani kupeŵa chizoloŵezi chakudikira kuchita chinthu pamphindi yomaliza. Ngati muli ndi projekiti yakusukulu, yesani kuika tsiku loimaliza lomwe lingakhale lapatsogolo kuposa tsiku limene mukuyembekezeredwa kuipereka.
Dziletseni nokha kuti mumamatire ku ndandanda yanu. Mungakopeke kupita kunyumba kwa bwenzi lanu pamene mufunikira kukhala pakhomo ndi kuphunzira kukonzekera mayeso omaliza. Koma mutafesa mouma manja m’maphunziro anu, mudzatuta magiredi otsika pambuyo pake. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 9:6.) Ndiponso, mudzasangalala kwambiri ndi nthaŵi yanu yopumula ngati mwamaliza ntchito yanu. Lamulo lamkhalidwe lothandiza nali, Chitani zinthu zofunika choyamba, ndi kumalizira ndi zosangulutsa.
Kupanga ndandanda ndi kulinganiza kumatenga nthaŵi, kuleza mtima, ndi kudziletsa kwakukulu, koma Akristu akuuzidwa kukhala odziletsa m’zinthu zonse. (1 Akorinto 9:25) Kuphunzira kumamatira ku ndandanda ndichizoloŵezi chabwino m’kugwiritsira ntchito lamulo lamkhalidwe limeneli. Zotsatirapo zingakhale chikhutiro cha kukwaniritsa zinthu, kulamulira bwino moyo wanu, ndi nthaŵi yochuluka yochita zinthu zimene mufuna ndi kukhumba kuchita.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Chithunzi patsamba 14]
Pangani ndandanda ya kuphunzira ndi kuimamatira