Akatswiri Oimba Odziŵa Kulumpha a Dziko la Tizilombo
TIKUVOMEREZA kuti ndife zolengedwa zanjala yaikulu. Indedi, njala yathu ikhozadi kukwiitsa alimi amene amatiyesa tizilombo tosakaza chifukwa timawononga mbewu zawo. Komabe, ziwalafe tili ndi mikhalidwe yokondweretsa—mmene timalumphira, mmene timaulukira, mmene timakwerera, ndi mmene timaimbira “nyimbo.”
Mwachitsanzo, kodi mudziŵa kuti tili ndi maso asanu? Mmalo mwakuvala mandala monga momwe anthu ambiri amachitira, ife tili ndi maso aang’ono atatu kutsogolo kwa mutu wathu owonera pafupi kwambiri. Maso athu ena aŵiri ngaakulu ndipo ali chakumbuyo kwa mutu, otikhozetsa kuwona zimene zikuchitika motizungulira. Ndicho chifukwa chake tikhoza kuthaŵa musanafike. Kodi simungakonde kukhala ndi maso amaluso oterowo?
Kodi luso lathu lakulumpha nlabwino motani? Tikhoza kulumpha msinkhu wathu kuuŵirikiza nthaŵi khumi ndi kukagwera pamtunda wa mamita 0.9. Kuti munthu achite zimenezo, akafunikira kulumpha msinkhu wa nyumba yosanja zipinda zisanu ndi chimodzi. Chinsinsi chathu ndicho minofu yathu yamphamvu kwambiri ya m’miyendo yakumbuyo. Iyo imatipatsa mphamvu ya kukantha yotikhozetsa kulumpha koteroko.
Ngakhale pambuyo pa kulumpha kwathu koyamba kokuchokerani m’njira, tingakuchititse kukhala kovuta kwa inu kuti mutigwire mwakugwiritsira ntchito mapiko athu anayi. Mapiko apamwamba olimba amagwira ntchito imene mapiko andege amachita, pamene mapiko a mkati ofeŵa amatipatsa mphamvu yowonjezereka youlukira. Chotero, mwakuphatikiza pamodzi maluso athu akulumpha ndi kuuluka, kaŵirikaŵiri timakhoza kuulukira kutali kukugwetsani ulesi potithamangitsa.
Kodi mumavutika pokwera mlongoti wokhala ndi mafuta? Kwa ife ndinkhani yapafupi. Ndipotu, tikhoza kukwera chothamanga tsamba la udzu loterera koma osaterereka konse, chifukwa chakuti Mlengi analinganiza mwaluso mapazi athu asanu ndi limodziwo. Kumapazi kwathu tili ndi ubweya umene umatulutsa madzi okangamira, otithandiza kugwira zinthu molimba. Siizo zokha, phazi lililonse lili ndi zida ziŵiri zamphamvu zokoŵera, zimene zimatiletsa kutsetserekera kumbuyo pa materezi aatali. Inde, kalekale anthu asanalingalire za kukwera mapiri, ife tinali okhoza bwino lomwe kuwakwera.
Amuna m’banja lathu la ziwala ndiwo oimba nyimbo. Akazi amakondwera nawo amunawo ndipo amawawona kukhala odalitsidwa. Inde, tikhoza kumva ndi kuyankha mawu osiyanasiyana. Makutu athu ali m’mbali mwa chifuŵa chathu. Motero, atakondwera, mwamuna amanyamula mwendo ndi kumauyendetsa modutsa pamwamba pa mitsempha yokwezeka ya mapiko ake monga momwe woimba mngoli amachitira ndi kandodo kake pa chingwe cha mngoliwo. Kumakhala kwampumulo chotani nanga patsiku lachilimwe kugona pansi pa udzu wokutala ndi kumwerekera m’kumvetsera gulu la oimba la chikwi cha ziwala ndi njenjete. Eya, ndiyo nyimbo ya m’chilimwe!