Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingachite Motani Ngati Chibwenzi Chatha?
“ANANDICHITITSA kudzimva kukhala wapadera. Ndinali kumva bwino kuposa mmene ndinachitira ndi kalelonse. Komano iye anati anaganiza kuti chibwenzicho sichikatha kupitiriza. Ndinalingalira kuti moyo wanga unali utatha. Ndinalira usana ndi usiku wonse. Sindinadye, sindinagone, ndinataya kulemera kwanga kwa [makilogramu 15] pamiyezi yoŵerengeka, ndipo ndinadwala chifuŵa cha bronchitis. Moyo sunatanthauzenso kanthu kwa ine.”—Renee.
Ngati munayamba mwapwetekedwapo ndi kutha kwa chibwenzi, muyenera kukumvetsetsa bwino kudandaula kumeneku. Mumadziŵa mmene kumakhalira kukonda kwambiri munthu wina kenaka ziyembekezo zanu nkuwonongedwa. Kukanidwa nkopweteka kwambiri, ndipo nkochititsa manyazi. Pamene muyesa mwamphamvu kuthetsa kupwetekako, mungalingalire kuti, ‘Kodi nchifukwa ninji sindingoziiŵala—kuiŵala munthuyo ndi kudziŵa za moyo wanga?’ Sikuli kopepuka motero.
Kodi Nchifukwa Ninji Kuli Kovuta Motero?
Kupenda kwina kunasonyeza kuti chikondi cha m’chibwenzi chingakhale champhamvu. Chayerekezeredwa ndi chikondi chimene chili pakati pa kholo ndi mwana. Ngakhale kuli kwakuti mosakayikira kumatenga nthaŵi yaitali kuti chikondi m’chibwenzicho chikule kukhala champhamvu, kupweteka mtimako kungakhalepo kuyambira pachiyambi. Simungangokuyambitsa ndi kukuletsa. Ndipo ngati muli mumkhalidwe umene Baibulo limatcha kuti “unamwali,” kudzutsidwa kwa chilakolako chakugonana kungakhale pafupifupi kokugonjetsani. (1 Akorinto 7:36) Zimenezo zimapangitsa kutayikiridwa ndi bwenzi lachinyamata kapena lachisungwana kukhala kovuta kwenikweni kupirira.
Chizoloŵezi cha kuyerekezera chingachitenso mbali ina. Kupenda kwina kochitidwa ndi ofufuza kumafotokoza kuti anthu osinkhukirapo ndiwo amene “ali paupandu kwambiri wa kutayikiridwa chifukwa chakuti pamene aloŵa muunansi wa chibwenzi, amakonda kuyerekezera zamtsogolo limodzi ndi mnzawoyo. Kuyerekezera kumeneku kungaphatikizepo kulota zokwatiŵa, kukhala ndi ana, ndi kukhalira limodzi moyo wawo wonse.” Maloto otero angakhale ovuta kwambiri kuwaleka, ngakhale ngati pali maziko osalimba kwenikweni.
Mukali Okondedwa
Motero kupenda kofananako kumanena kuti “kutayikiridwa ndi mnzanu wokondana naye . . . kungatsogolere kumalingaliro a kukhala wolephera kwa munthu mwini ndi kusakhoza.” Jeanette akukumbukira kuti: “Umakhala wopsinjika maganizo, monga ngati kuti palibe aliyense wokuchilikiza. Sumasamalanso. Umadzimva kukhala wokanidwa.” Mofanana naye, ambiri amakhala opsinjika maganizo, aliwongo, kudzimva kukhala osanunkha kanthu, osakhoza kulingalira bwino. Ena adziphadi.
Chotero imeneyi ingakhale nthaŵi yanu yaupandu. Komabe, kumbukirani, chisonkhezero cha Yesu cha ‘kukonda mnansi wako monga iwe mwini.’ (Marko 12:31) Mlingo wa kudzikonda wakutiwakuti umafunika ndipo ngwoyenerera. Chenicheni chakuti munthu wina analephera kukusonyezani chikondi sikumatanthauza kuti muli wosakondedwa, sichoncho kodi? Inu kwenikweni simungalingalire kuti palibe aliyense amene adzakuwonani kukhala wokhumbika kapena wokongola, mungatero kodi? Kodi mulibe ziŵalo zabanja ndi mabwenzi amene amakukondani?
Chinthu chofunika kwambiri nchakuti, kodi Mulungu amakuwonani motani? Leya, mkazi amene anakhala ndi moyo m’nthaŵi za m’Baibulo, ayenera kukhala atamva ululu wa kukanidwa kwambiri. Iye anadziŵa bwino lomwe kuti mwamuna wake, Yakobo, ananyengedwa kuti amkwatire ndi kuti anakonda kwambiri mng’ono wake Rakele. Mposadabwitsa kuti anadziwona kukhala ‘wodedwa,’ titero kunena kwake, ndi wopanda pake. Komabe, Mulungu anawona kanthu kena kabwino mwa Leya. Anamdalitsa ndi ana ambiri, ndipo mzera wa unsembe wa Israyeli ndi wachifumu womwe—umene unatulutsa Mesiya—unadzera mwa iye, osati mwa Rakele.—Genesis 29:30-35.
Palibe kuchuluka kwa kukanidwa kumene kungasinthe kutsimikizirika kwa dalitso la Mulungu ndi chikondi. Kumbukirani, Mlengi wa chilengedwe chonse amakukondani kwambiri kwakuti analola Mwana wake kuvutika ndi kukuferani. (Yohane 3:16) Inu simuli wosakondedwa, ndipo ndithudi simuli wopanda pake.
Pamene Kutha kwa Chibwenzi Kulidi Dalitso
Inu mungawone monga ngati kuti kutha kwa chibwenzi kumeneku ndiko chimodzi cha zinthu zoipitsitsa koposa zimene sizinayambe zakuchitikirani, komatu zimenezo zingakhale zosiyana kwambiri. Chinkana kuti zingawoneke kukhala zovuta kuzikhulupirira, mwinamwake kutha kwa kukondana kwanu kuli dalitso. Zili choncho motani kodi? Maunansi a chibwenzi a achichepere ochuluka alibe lonjezo lenileni lachipambano. Achichepere amakhala akukula ndipo akusintha; ngotengeka maganizo ndi zikhumbo ndi chikondi cholakwika. Mosasamala kanthu za zimenezo, chaka chilichonse achichepere zikwi zambiri amakwatirana, kungopeza kuti kuchita motero kunali kolakwa. Mkulu wina wa nyuzipepala ina ukwati wake utatha anati: “Kunalidi kulakwa kukwatirana tili achichepere. Sindinazindikiredi kuti tinali ndi makhalidwe osiyana ndi ziyambi.”
Maukwati a achichepere ali ndi mlingo waukulu kwambiri wa kulephera. Ngakhale kuti mukupwetekedwa mtima tsopano lino, khalani wotsimikiza za chinthu chimodzi—mukanavutika kwambiri ngati mukanaloŵa muukwati wopanda chimwemwe. Dzifunseni ngati munalidi wokonzekera ukwati wa moyo wonse, limodzi ndi mathayo ake onse, kuphatikizapo kulera ana. Ndipo kodi munthu amene munakondayo analidi wokonzekera ndiponso wokhwima maganizo? Kumbukirani, kutha kwa kupalana chibwenzi nkosapweteka maganizo kwambiri kuposa kutha kwa ukwati.
Kutha kwa chibwenziko kunali dalitso makamaka ngati munapanga cholakwa cha kudziphatikiza ndi munthu wina amene samalemekeza malamulo a makhalidwe abwino aumulungu ndi miyezo yabwino ya chikhalidwe cha mtima. (2 Akorinto 6:14) Shana akukumbukira maupandu akutayikiridwa ndi chikhalidwe cha mtima chifukwa cha kukhala ndi mabwenzi adziko kuti: “Nthaŵi zonse iye ankanena kuti amandikonda. Komano ankandipempha kugona naye. Ndinkanena kuti ayi. Ndinakuzindikira kukhala kolakwa. Pambuyo pakanthaŵi, analeka kundifikira. Ndinalira usiku uliwonse—kulekana naye kunali kovuta!” Komabe, mwachiwonekere, kutha kwa chibwenzi kumeneku kunapulumutsa Shana kugwera m’ngozi yauzimu.
Chotero inu mungakhoze kuwona kutha kwa chibwenzi monga chokumana nacho chophunzirirapo. Monga momwe Miyambo 22:3 imanenera kuti, “wochenjera awona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” Kodi chokumana nacho chimenechi chidzakupangani kukhala wochenjera kwambiri, kotero kuti mupeŵe mavuto mtsogolo?
Kulimbana ndi Kupweteka kwa Mtima
Komabe, ngakhale ngati kutha kwa chibwenzi kunali chinthu chabwino koposa kwa inu, zimenezo sizimakupangitsabe kukhala kosapweteka. Kodi mungachite motani ndi kupweteka kwa mtima kumene kuwonekera kukhala kosatha? Eya, kuyerekezera kuti simukumva kalikonse sikudzakuthandizani. Monga momwe magazini a ’Teen posachedwapa ananenera pankhaniyi, “kupweteka kwa mtima sindiko chinthu chimene mungachithaŵe kapena kuchibisalira. Potsirizira pake, kudzakupezani.”
Nkwachibadwa kwa inu kukhala woputidwa, wokwiya kwambiri ndi zimenezi. Komatu musazisunge mumtima, mukumapita kukagona muli wosokonezeka maganizo usiku uliwonse. Tsatirani uphungu wanzeru wa Baibulo wakuti: “Kwiyani koma musachimwe; dzuŵa lisaloŵe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Simbani za kukhosi kwanu kwa bwenzi lodalirika kapena munthu womkhulupirira. “Zolingalira zizimidwa popanda upo,” imatero Miyambo 15:22. Makolo anu kapena akulu Achikristu angakhale othandiza kwambiri m’mikhalidwe imeneyi. Mungapeze kuti iwo onse anapyola zokumana nazo zofananazo pamene anali achichepere.
Chithandizo china polimbana ndi kupwetekedwa kwanu mtima ndicho kukhala otanganitsidwa. Inu mwina mungakonde kukhala du, kudzipatula, kumwerekera m’kuyerekezera zinthu, ndi kutaya chikondwerero m’moyo. Jeanette akukumbukira kuti: “Sumafuna kuchita kanthu kalikonse. Umangogonagona kwambiri.” Koma lemba la Miyambo 18:1 limachenjeza kuti, “ [iye wodzipatula, NW] afunafuna chifuniro chake; nakangana ndi nzeru yonse yeniyeni.” Chotero mmalomwake, khalani wotanganitsidwa. Bwereraninso m’mayanjano a m’kagulu ndi awo amene adzakulimbikitsani kuyenda m’njira yoyenera.
Njira yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito nyonga yanu ndiyo kudziloŵetsa inu mwini muuminisitala Wachikristu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa chake, abale anga okondedwa, khalani okhazikika, osasunthika, akuchuluka muntchito ya Ambuye, nthaŵi zonse, podziŵa kuti kuchititsa kwanu sikuli chabe mwa Ambuye.” (1 Akorinto 15:58) Moyo wanu sufunikira kumva uli wopanda kanthu kapena wopanda tanthauzo. Kunena mbiri yabwino kwa ena kumadzetsa chimwemwe ndi chikhutiro.—Machitidwe 20:35.
Kumbukiraninso kuti, mudzakhala ndi zokumana nazo za masiku abwino ndi masiku oipa kwakanthaŵi. Pamasiku oipa mungawone monga ngati kuti simudzadzithetsa. Koma chowonadi nchakuti, mudzapeza bwino. Chilonda kuti chipole—chilonda chilichonse—chimatenga nthaŵi. Musachedwetse mchitidwewo mwa kungolingalirabe chibwenzicho kapena ndi nyimbo zachikondi ndi kumayerekezera zinthu ponena za chikondi chanu chotaikacho. Dalirani pa nyonga ya Yehova. Iye amadziŵa bwino kwambiri zimene zikukuchitikirani ndi mmene mumamvera. “Yehova ali pafupi ndi iwo amtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.”—Salmo 34:18.
Nthaŵi Zabwino Zili Mtsogolo
Monga wachichepere, limodzi la madalitso anu aakulu koposa ndilo nthaŵi. Pali nthaŵi yochuluka kwambiri patsogolo panu yoti muphunzire ndi kupeza chidziŵitso. Chotero gwiritsirani ntchito chuma chamtengo wapatali chimenechi mwanzeru; kulitsani mikhalidwe imene idzakuthandizani kukhala munthu wachikulire wokhazikika ndi wosungika. Mwanjira imeneyo mudzakhala wokhoza kupanga zosankha zanzeru ponena za kupalana chibwenzi ndi ukwati mtsogolo.
Ngakhale kuti nyengo yopweteka imeneyi ili yovuta motere, idzatha, ndipo mungakhale woichenjerera. Renee, wogwidwa mawu poyambirirapo, akunena kuti: “Ndili wokhoza kulimbana ndi malingaliro anga bwino kwambiri tsopano. Ndaphunzira zambiri. Ndaphunzira kuti kuli kokha mwa kuchita zinthu m’njira ya Yehova pamene zinthu zidzayenda bwino.”