Lingaliro la Baibulo
Zopereka Zothandizira Osauka Kodi Ndithayo Lachikristu?
ZOSAFIKA zaka khumi zapitazo, malikulu okhala kummwera koma chakummaŵa kwa United States a Kalabu ya PTL (Praise the Lord [Tamandani Ambuye]), anapemphetsa zopereka zachifundo zoperekedwa kuchipembezo. Mogwiritsira ntchito dongosolo la satellite-TV ndi dongosolo loyendetsera makalata, anasonkhanitsa mamiliyoni mazana ambiri a madola, zimene zinadzadza mabokosi awo andalama—monga ngati kuti zidzagwiritsiridwa ntchito kufalitsira uthenga wabwino.
Talingalirani mmene zikwizikwi za anthu amene anatumiza ndalama ku Kalabu ya PTL anamvera pamene anaŵerenga malipoti a m’nyuzi monga ngati Associated Press yofalitsa nkhani mofulumira imene inanena kuti Jim Bakker, amene kale anali prezidenti wa PTL, limodzi ndi mkazi wake, Tammy, “akusimbidwa kukhala atalipiridwa malipiro ndi ndalama za banyira zokwanira $1.6 miliyoni mu 1986.” Choipa kwambiri nchakuti, lipotilo linanenanso kuti: “Malipiro amenewo anaperekedwa ngakhale kuti gululo liri m’ngongole yofika pafupifupi $50 miliyoni . . . Ndalama zofika pafupifupi $265,000 m’thumba la ndalama la PTL zapatulidwira [Jessica] Hahn kumtseka pakamwa ponena za unansi wake wa [kugonana] ndi Bakker.”
Asanapereke chilango cha kuikidwa m’ndende kwa Bakker chifukwa cha kubera omtsatira, woweruza mlandu pamlandu wake anati: “Ena a ife amene ali ndi chipembedzo akunyansidwa chifukwa cha kupangidwa kukhala zitsiru za alaliki ndi ansembe okonda ndalamawo.”
Chipembedzo sichiri chokha m’kusonkhezera mwachangu malingaliro a osonkha ndalama ndiyeno nkusunga ndalama zochuluka zosonkhedwazo. Nkozoloŵereka kwa magulu enanso osonkhetsa ndalama kusunga 90 peresenti ya zoperekedwa zimene amapemphetsa.
Pamenepo, kodi nkodabwitsa kuti anthu akunyansidwa ndi kupemphetsa koteroko? Komabe, kodi Akristu ayenera kuchitanji? Kodi ali ndi thayo la kupereka ndalama zachithandizo kumagulu opemphetsa? Kodi Baibulo limapereka njira zotani zotsimikizira kugwiritsiridwa ntchito kwanzeru kwa ndalama pothandiza ena? Kodi ndiiti imene ili njira yabwino koposa ndi yothandiza koposa yothandizira ena?
Kupereka ndi Kusapereka
Kunena zowona, uphungu wa Baibulo ngwakuti tikhale okoma mtima ndi owoloŵa manja kwa osoŵa. Kuyambira m’nthaŵi zakale anthu a Mulungu akhala akulimbikitsidwa “kukhala owoloŵa manja, okonzekera kugaŵira ena.” (1 Timoteo 6:18, NW; Deuteronomo 15:7, 10, 11) Kwenikweni, Akristu akuuzidwa pa 1 Yohane 3:17 kuti: “Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosoŵa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?”
Kupatsa, inde; komatu chenjerani! Nthaŵi zonse timakumana ndi magulu opemphetsa ndalama za osoŵa, zipembedzo, ndi mikupiti yochitidwa ndi anthu otumikira m’chitaganya yachaka ndi chaka; ambiri amapemphetsa mokakamiza. Komabe, powapenda nkwabwino kukumbukira mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” (Miyambo 14:15) M’mawu ŵena, chenjerani ndi kuvomereza mawu kapena malonjezo a ndalama za osoŵazo ndi zimene adzachita nazo. Kodi ndalama zosonkhanitsidwazo zimagwiritsiridwa ntchito motani? Kodi magulu amene akuzisonkhanitsawo ali awo amene Mkristu ayenera kuchirikiza? Kodi machitachita awo ngandale za dziko, autundu, kapena ogwirizanitsidwa ndi chipembedzo chonyenga? Kodi cholinga cholumbiriridwacho nchanzeru ndi chosaombana ndi lamulo la mkhalidwe Lamalemba?
Magulu ena osonkhetsa ndalama amakhala okhoza kuthandiza bwino kwambiri anthu osoŵa. Atayambukiridwa ndi masoka kapena mliri wa nthenda, Akristu nthaŵi zambiri alandira chithandizo cha magulu amenewo. Komabe, magulu ena othandiza ali ndi kayendetsedwe ka zinthu kodya ndalama zochuluka kapena njira yosonkhanitsira ndalama yokwera mtengo kwambiri, ndi chotulukapo chakuti ndindalama zochepa zokha zosonkhanitsidwa zimene kwenikweni zimagwiritsiridwa ntchito pachifuno chofalitsira kusonkhetsako. Mwachitsanzo, kupenda kwaposachedwapa kwa magulu 117 aakulu osafuna phindu a mu United States, kuphatikizapo magulu osonkhetsa ndalama, kunapezeka kuti oposa 25 peresenti a iwo analipira akuluakulu awo malipiro a ndalama zokwanira $200,000 kapena kuposa pamenepo pachaka. Kaŵirikaŵiri kupenda ndalama kumasonyeza ndalama zowonongedwera kugulira zinthu zaumataya ndi kuchirikizira moyo wachuma. Mosasamala kanthu za dzina la gulu losonkhetsa ndalamalo, kukakhala kokayikitsa ngati kupereka zopereka kumaprogramu otero kukakwaniritsa lamulo la Baibulo la kuthandiza amene ali osoŵa.
Lingaliro Lachikatikati
Ngakhale kuti palibe amene amafuna kuwononga ndalama zake—kapena zoipa kuposa pamenepo, kuwona zikugwiritsiridwa ntchito kulemeretsa anthu odzikhutiritsa—palinso kufunika kwa kukhala maso pakukhala oumira pankhani ya kupatsa. Musagwiritsire ntchito mkhalidwe wa kusakhoza kuchita bwino zinthu kapena kusawona mtima kwa ‘magulu ena osonkhetsa ndalama’ kukhala chodzikhululukira cha kunyalanyazira anthu osoŵa kapena kupondereza malingaliro a kuchitira chifundo. Pa Miyambo 3:27, 28 pamalangiza kuti: “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino. Usanene kwa mnzako, Ukabwerenso, ndipo maŵa ndidzakupatsa; pokhala uli nako kanthu.” (Yerekezerani ndi 1 Yohane 3:18.) Musalingalire kuti magulu onse opemphetsa ndalama amawawanya ndalama kapena amapseterera. Pendani zenizeni, ndiyeno dzisankhireni kaya kupereka kapena ayi.
Ambiri amakonda kuthandiza mwachindunji, kutumizira mphatso munthu wosoŵa kapena mabanja. Motero, opatsawo amakhala otsimikira za kugwiritsiridwa ntchito kothandiza ndi kwachindunji kumene zopereka zawo zikugwira ntchito. Zimenezi zimaperekanso mpata wa kukulitsa ndi kusonyeza kukoma mtima m’mawu ndiponso m’ntchito. Ngakhale ngati mulibe zambiri zoti mupereke mwakuthupi, mungakhalebe ndi chimwemwe m’kupatsa. Nthaŵi ina pamene mudzamva za munthu wosoŵa kwenikweni wofuna chithandizo chotero, mpatseni zimene mungathe kupereka ndi mzimu wa zimene zalembedwa pa 2 Akorinto 8:12 kuti: “Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, simonga chimsoŵa.”
Kumbukiraninso kuti, nthaŵi zina chinthu chimene chingachite zabwino kwambiri ndicho kanthu kena koposa ndalama. Yesu anauza otsatira ake “kupita, kulalikira, kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ . . . Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.” (Mateyu 10:7, 8, NW) Mofananamo lerolino, Akristu amazindikira kuti nthaŵi, nyonga, ndi ndalama zogwiritsidwa ntchito m’kuchirikiza kuchitira umboni za Ufumu—umene umawongolera miyoyo ndi kupereka chiyembekezo—ndizo chithandizo choperekedwa cha mtundu wabwino koposa.
Pamenepo, lingaliro la Baibulo ndilo kukhala okoma mtima, owoloŵa manja, ndi othandiza ena. Limatikumbutsa kuti kaŵirikaŵiri chithandizo chakuthupi nchofunika, ndipo anthu osoŵa sayenera kunyalanyazidwa. Panthaŵi imodzimodziyo musadzimve kukhala omangika ndi thayo la kupatsa munthu aliyense kapena anthu onse amene angakupempheni ndalama. Lingalirani mmene ndalama zimene muli nazo zingagwiritsiridwire ntchito bwino koposa, kotero kuti mukondweretse Mulungu ndi kupereka chithandizo chabwino kwambiri kubanja lanu ndi kwa munthu mnzanu. (1 Timoteo 5:8; Yakobo 2:15, 16) Tsanzirani Yesu m’kukhala wamaso ndi kulabadira zosoŵa za ena—mwauzimu ndi mwakuthupi. Mwamawu a pa Ahebri 13:16: “Musaiŵale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.”