Kugwira Ntchito—Zolimba Pamene Kuli Kwabwino
KU Southeast Asia konse, atsikana achichepere ambiri antchito zapanyumba amayamba alekeza ntchito yawo ya m’khitchini nakhala pansi kuti aonerere mwa dwii pamawailesi akanema pamene seŵero lopangidwa ku Japan la pa TV lotchedwa kuti Oshin liyamba. Limanena za nkhani ya mkazi wina amene anachokera paumphaŵi kumka kuchuma atapirira kwa zaka zambiri za kusauka ndi mavuto. Atalengeza misozi, atsikanawo amadziyerekezera ndi Oshin, ngwazi yachikaziyo. Zochitikazo zimaonekera kukhaladi zimene amafuna kuti ziwathandize kuyang’anizana ndi tsiku linanso la kugwira ntchito zolimba.
Zowonadi, pamene anthu agwira ntchito zolimba tsiku ndi tsiku kufikira pakuika paupandu thanzi lawo ndi moyo, amakhala ali ndi zifukwa zochitira motero. Kodi nchifukwa ninji amatero? Ponena za atsikana antchito zapanyumbawo a ku Asia, ndithudi kufuna kuwongolera mkhalidwe wa moyo ndiko chosonkhezera champhamvu ndi chofala cha kugwirira ntchito zolimba. Komabe, mwachiwonekere, mfupo yakuthupi sindiyo yokha imene imaloŵetsedwamo.
“Kupatsidwa chuma ndiko chisonkhezero chokhumbidwa, komatu zimenezi zimachitika mwakamodzikamodzi,” akulemba motero Stephen D. Cohen ponena za lingaliro la ntchito la nzika za Japan. Nangano, nchiyani chimene chimasonkhezera anthu a ku Japan kugwira ntchito zolimba chotero? “Kukhala opambana pakugulitsa katundu wa kampani mofanana ndi makampani ena ochita nawo mpikisano ndicho magwero a kunyada kwakukulu ndi kudzikhutiritsa. Kugwira ntchito zolimba kumene kumachirikiza cholinga chimenechi nakonso kumafupa mwapadera,” akufotokoza motero Cohen. Kukhulupirika pakampani yawo kumakhala chifukwa champhamvu chimene olembedwa ntchito amagwirira ntchito zolimba, ndipo ntchito imakhala njira yokhayo kwa iwo yosonyezera kufunika kwawo. Chosanyalanyazidwanso ndicho, chisonkhezero cha kukhala ndi malo apamwamba m’kampani. Kuthekera kwakuti tsiku lina adzakwezedwa pantchito kumakhalabe chisonkhezero champhamvu chogwirira ntchito zolimba.
Kodi Nzifukwa Zabwino Zoikira Thanzi Lanu Paupandu?
Kodi zimenezi zili zifukwa zoyenera zoikira thanzi ndi moyo wa munthu paupandu? Kwa munthu amene amagwira ntchito zolimba kuti apeze chuma chakuthupi, Baibulo limati, “diso lake silikhuta chuma.” Potsirizira pake munthu wotero angadabwe kuti: “Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani?” (Mlaliki 4:8) Awo amene amagwira ntchito zolimba kuti alemere amaonekera kukhala osadziŵa kuti ndiliti kapena ndipati pamene ayenera kuimira. Amadzipomboneza mumkhalidwe wovuta wa ntchito, amangogwirabe ntchitoyo. Baibulo limachenjeza momvekera bwino kuti: “Usadzitopetse kuti ulemere.”—Miyambo 23:4.
Bwanji za kukhulupirika pakampani? Pamene kuli kwakuti kungakhale kwabwino, chiyambukiro chothekera cha kugwira ntchito monkitsa chiyenera kulingaliridwa. “Ngati munthu akutopa ndi ntchito sindimfuna pantchito panga pano,” anatero mkulu wina woyang’anira ntchito wa kampani ya ku Amereka. Mkazi wina wa mmodzi wa “antchito omenya nkhondo” analembera nyuzipepala ina mwamuna wake atamwalira chifukwa cha kugwira ntchito monkitsa asanafike pausinkhu wa zaka 40 kuti: “Kodi makampaniwo anganenenso mawu opepesa otani kusiyapo chabe akuti, ‘Tili ndi chisoni kutayikiridwa ndi munthu wofunika chotero’? Anthu ofera makampani amenewo, pamene afa, amaonedwa monga ngati kuti anali ‘zinthu zakutha zotayidwa.’”
Ngakhale ngati munthu apeŵa kutopa ndi ntchito kapena imfa chifukwa cha kugwira ntchito monkitsa, kodi nchiyani chimene chimachitika pamene apumitsidwa ntchitoyo? “Mosasamala kanthu za kugwirira ntchito zolimba makampani awo, iwo amachititsidwa kudziŵa chenicheni chakuti kampaniyo simawafunanso ndi kuti ngakutha ntchito,” akutero Motoyo Yamane, woulutsa mawu wa ku Japan. Ponena za kampani imene munthu amadalira, olembedwa ntchito ogwira ntchito zolimba amangokhala anthu wamba ogwiritsiridwa ntchito, oti aloŵedwe mmalo pamene ali opanda pake. Chifukwa chake mposadabwitsa kuti anthu ambiri a ku Japan akutaya chikhulupiriro m’makampani awo! Akuyamba kuzindikira kuti kukonda kwawo kampani sikudzawapindulitsa.
Kodi nchiyani chimene chinganenedwe ponena za kukwezedwa pantchito? Awo amene akwezedwa pang’ono pantchito amazindikira mofulumira kuti munthu aliyense sadzakwezedwa kwambiri pantchito. Ndiyeno nchiyani chimene chimachitika? Pokhala atalandidwa chiyembekezo cha kukwezedwanso pantchito, iwo amayamba kugwira ntchito kumakampani osiyanasiyana. Chotero kukhulupirika pakampani sikunatsimikizire kukhala ubwino wopindulitsa!
Lingaliro Lachikatikati la Kugwira Ntchito Zolimba
Ngakhale kuti kugwira ntchito zolimba kosonkhezeredwa ndi kukonda ndalama, kukhulupirika pakampani, kapena mzimu wa mpikisano potsirizira pake kumagwiritsa mwala ndi kulefula maganizo, Baibulo silimanyalanyaza phindu la kugwira ntchito zolimba. “Munthu yense adye namwe naone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Baibulo limavomereza kuti tisangalale ndi zipatso za kugwira kwathu ntchito zolimba. Zimenezi zimatithandiza kuwona limene liyenera kukhala lingaliro loyenera la kugwira ntchito zolimba.
Posachedwapa, Unduna wa Zaumoyo ndi Ubwino wa Anthu ku Japan unalangiza ogwira ntchito kuti “aiŵale ntchito ataŵeruka (ndipo) adye chakudya pamodzi ndi mabanja awo.” Atsogoleri ena abizinesi mwachiwonekere amazindikira nzeru ya uphungu umenewu. Mwachitsanzo, prezidenti wa kampani ya sayansi ya za thupi la munthu imene ikukula ananena kuti: “Ndikufuna kuti ogwira ntchito athu onse asamalire bwino mabanja awo choyamba. Kugwira ntchito kwawo m’kampani yathu kwangokhala njira yopezera zofunika za banja.”
Ndithudi, unansi wabwino m’banja ndiwo chonulirapo choyenereradi kugwirira ntchito zolimba. Ngati mkhalidwe wachikondi m’banja uwopsezedwa kapena thanzi lanu liwonongeka chifukwa cha ntchito yanu, simungaone zabwino m’kugwira zolimba ntchito zonse.
Komabe, m’chitaganya cha anthu a ku Japan, mmene dongosolo la kukhala wamkulu pantchito limalamulira, ena akulitsa mkhalidwe wa maganizo wakuti: “Usajombe kuntchito, kapena kukhala wochedwa pochita zinthu, kapena kugwira ntchito.” Amayerekezera kukhala akhama mwa kukhala pantchito mpaka usiku komano akumangoyembekezera kuti kapitao aŵeruke. Kenji, wosatsa malonda wa kampani yoika ziwiya zokongoletsa m’nyumba ku Hiroshima, anali ndi maganizo otero. Ankajomba kuntchito, akumathera nthaŵi m’kantini kapena m’nyumba ya makina yoseŵerera juga.
Kodi mkhalidwe wa maganizo wotero umachititsa chimwemwe? “Wolesi adzakhala ngati kapolo,” umaterotu mwambi wa Baibulo. Lerolino, munthu sangapangidwe kwenikweni kukhala kapolo chifukwa cha ulesi wake. Komabe, ntchito yake ingakhale yothodwetsa, mwamaganizo, ntchito yochitidwa mwaukapolo. Kumbali ina, mwambi umodzimodziwo umasonyeza mapindu a khama kuti: “Dzanja la akhama lidzalamulira.” (Miyambo 12:24) Ngakhale ngati simudzalamulira dziko kapena kampani, inu mudzalemekezedwabe ndi banja lanu ndi kudzilemekeza. Ndiponso mungapeze chidaliro kwa okulembani ntchito, ndi kukhala ndi chikumbumtima choyera.
Kenji anapeza zimenezi kuti zinali chonchodi. Anasankha kuphunzira Baibulo, ndipo moyo wake unasintha kwambiri. “Mwakugwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe a kuwona mtima pantchito, ndinayamba kugwira ntchito ndi mtima wonse pamene bwana analipo kapena palibe. Zimenezo zinamchititsa kundidalira,” iye akutero.
Pamene Kugwira Ntchito Zolimba Kukhala Kwabwino
Chowonadi nchakuti, kuti ntchito ikhale yothandiza, iyenera kukhala yopindulitsa ena. ‘Ntchito yokhutiritsa,’ anafotokoza motero wolemba nkhani wina, ‘ndiyo ntchito imene imadzetsa chiyanjo, kupeza bwino kapena chikondwerero kwa anthu ambiri.’ Ntchito yotero imadzetsa chikhutiro chachikulu kwa wogwira ntchito. Kuli monga momwe Yesu ananenera kuti: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.”—Machitidwe 20:35.
Ngakhale kuli kwakuti kugwirira ntchito ubwino wa ena nkoyamikiridwa, palinso mfundo ina yaikulu yopezera chikhutiro pantchito ndi m’moyo. Mfumu Solomo, atakhala ndi zinthu zonse zaumataya ndi chuma zimene zimaperekedwa ndi moyo, anafikira pakugamula kwakukulu kotere: “Opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndiichi.”—Mlaliki 12:13.
Mwachiwonekere, tiyenera kulingalira chimene chili chifuniro cha Mulungu pantchito iliyonse imene timachita. Kodi tikugwira ntchito mogwirizana ndi chifuniro chake kapena motsutsana nacho? Kodi tikuyesayesa kumkondweretsa kapena kungodzikondweretsa? Ngati tinyalanyaza kuchita chifuniro cha Mulungu, timangokhala okondetsa zinthu zakuthupi kapena wolondola zosangulutsa ndipo potsirizira pake tidzavutika ndi kusukidwa, kupanda pake, ndi kuthedwa nzeru.
Chotero kumbukirani kuti kutumikira Yehova Mulungu—kuchita ntchito imene imakondweretsa Mlengi—sikudzatisiya tili osakhutiritsidwa. Yehova mwiniyo ngwogwira ntchito zolimba, ndipo amatipempa kuti tigwirizane naye ndi kukhala “antchito anzake.” (1 Akorinto 3:9; Yohane 5:17) Koma kodi kugwira ntchito zolimba kotero kumadzetsadi chimwemwe chenicheni?
Mkulu wina woyang’anira kampani yosindikiza, nthaŵi ina anakaona malo osindikizira a Watch Tower ku Japan kuti adziŵe mmene analinganizira. Chidwi chake chinatembenukiranso pakanthu kena kowonjezera pamakina. Iye anaona anyamata okondwa ndi ntchito yawo, ndipo anadabwa kumva kuti onsewo anali ogwira ntchito odzifunira ndi kuti enanso osaŵerengeka apempha ndi mtima wonse kudzagwirizana nawo. Kodi nchifukwa ninji iyeyu anadabwa? Iye anafotokoza kuti, “Tikalemba ntchito anthu khumi pakampani yathu, timauona kukhala mwaŵi ndithu ngati anayi a iwo adakali nafe chaka chimodzi chitatha. Inu a Watchtower muli ndi chuma cha anyamata ogwira ntchito!”
Kodi nchiyani chimene chimapangitsa anyamata ameneŵa kukondwera kwambiri ndi kukhala ogwira ntchito zolimba chotere? Monga antchito odzifunira, mwachiwonekere samagwira ntchito kuti alipidwe ndalama. Nangano, nchiyani chimene chimawasonkhezera? Kudzipatulira kwawo ndi kuyamikira Yehova, Mlengi wawo, ndi chikondi chawo cha pamnansi. Mkhalidwe wawo wa maganizo umasonyeza kuti samagwira ntchito “monga okondweretsa anthu, komatu monga akapolo a Kristu, akuchita chifuniro cha Mulungu chochokera kumtima.”—Aefeso 6:6.
Zonsezi zangokhala chabe chionetsero cha zinthu zilinkudza. Awo amene tsopano akugwira ntchito zolimba kutumikira Yehova angayembekezere nthaŵi pamene adzabwezeretsa Paradaiso ndipo dziko lonse lapansi lidzadzazidwa ndi ntchito zofunika. Yesaya, mneneri wakale wa Mulungu, ananeneratu ponena za moyo wa panthaŵiyo kuti: “Adzamanga nyumba ndi kukhalamo; ndipo iwo adzawoka minda yamphesa, ndi kudya zipatso zake. Iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya; . . . osankhidwa anga adzasangalala nthaŵi zambiri ndi ntchito za manja awo.”—Yesaya 65:21, 22.
Limenelo lidzakhala dalitso lotani nanga! Mwakuphunzira za chifuniro cha Mulungu kwa inu ndi kuchita mogwirizana nacho, mukhaletu pakati pa anthu odalitsidwa ndi Yehova ndi ‘kuona zabwino muntchito zanu zonse’ nthaŵi zonse.—Mlaliki 3:13.
[Bokosi patsamba 24]
Lingaliro Lachikatikati la Ntchito Lipulumutsa Ukwati
Kwa Yasuo, amene amakhala mu Hokkaido, Japan, kuntchito kunali kothera nthaŵi kufikira zaka zingapo zapitazo. Anali ndi malo a manijala wamng’ono, ndipo analemetsedwa maganizo ndi kuwonjezereka kwa malonda. Tsiku ndi tsiku ankagwira ntchito kufikira 11 koloko ya usiku popanda tchuthi. Ndiyeno, iye akukumbukira kuti: “Ndinazindikira kuti mosasamala kanthu ndi mmene ndinagwirira ntchito zolimba, sindinasangalatsidwe ndi ntchito yangayo.” Mkhalidwe wakuthupi wa Yasuo unayamba kuipa. Pokambitsirana ndi mkazi wake, anazindikira kuti panali kanthu kena kofunika kwambiri kuposa ntchito yake—banja lake. Anasintha moyo wake nagwirizana ndi mkazi wake m’kuphunzira Baibulo. Tsopano iye ali mutu wa banja lachimwemwe wokondedwa ndi wolemekezedwa.
[Chithunzi patsamba 24]
Ntchito yanu siyenera kuwopseza unansi wa banja
[Chithunzi patsamba 25]
Onse adzasangalala posachedwa ndi ntchito ya kusanduliza dziko lapansi kukhala paradaiso