Gawo 6
Sayansi—Kufunafuna Chowonadi kwa Mtundu wa Anthu Komapitirizabe
Kuyang’anizana ndi Zovuta za m’Zaka za Zana la 21
ZISANU ndi zinayi, zisanu ndi zitatu, zisanu ndi ziŵiri, ndi kupitirizabe kuŵerenga mphindi zotsalira! Kodi kumeneku nkuŵerengera mphindi za kuponyedwa kwa chombo cha roketi? Ayi, mmalomwake ndiko kuŵerengera zaka zimene zatsalirabe mtundu wa anthu usanagwere m’mikhalidwe yowopsa ya m’zaka za zana la 21.a
Poona zipambano za sayansi za m’zaka za zana lapita, anthu ambiri mowona mtima angakhulupirire kuti sayansi ikhoza kulimbana ndi zovuta zilizonse zimene zaka za zana la 21 zingadzetse.b Iwo angalingalire monga momwe mlembi wa mabuku wina wa ku Falansa pachiyambi pa zaka za zana la 20 anachitira. Iye analemba kuti: “Lerolino sayansi yalinganizidwira kulamulira dziko. Kuyambira tsopano kumka mtsogolo ulamuliro wa dziko ngwa sayansi osati wa Mulungu, sayansi yakhala yopindulitsa mitundu ya anthu ndi yomasula anthu.”
Kuti sayansi ikwaniritse ziyembekezo zimenezi, iyenera kuchotsa mavuto ambiri amene yapanga.
Kuwonongedwa kwa malo okhala kumene sayansi yakudzetsa nkwakukulu. Buku lakuti 5000 Days to Save the Planet limanena kuti: “Ngati tipitirizabe mchitidwe wathu wa kuwononga malo okhala, funso limene lidzakhalapo silakuti, kodi anthu amakono a m’zaka za zana zotsatirazo adzapulumuka, koma lakuti kodi adzazimiririka mwachiwawa kapena mwakachetechete?”
Zimenezi zikuoneka kukhala zosapeŵeka.
Zolephera za Sayansi
“Asayansi ambiri a m’zaka za zana la 19 . . . kaŵirikaŵiri analingalira kuti tsiku lina iwo adzapeza chowonadi chenicheni ndi kuzindikira kotheratu,” limatero bukulo The Scientist. “Owaloŵa mmalo awo amangonena kokha za kufika pa ‘kuzindikira kwapang’ono’, kwa kuyandikira zenizeni komapitirizabe koma mosafikira pazenizenizo kotheratu,” bukulo limapitirizabe motero. Kusoŵa chidziŵitso kotheratu kumeneku kumalepheretsa kwambiri zimene sayansi ingachite.
Zenizeni za sayansi sizinasinthe m’zaka zambiri zapitazo, pamene kuli kwakuti nthanthi zasayansi zatero—ndipo zimenezi zachitika mobwerezabwereza. Kwenikweni, panthaŵi zina nthanthizo zakhala zikungosinthasintha. Mwachitsanzo, asayansi ya zamankhwala panthaŵi ina analingalira kuti kuchotsa mwazi m’thupi la munthu wodwala kwambiri kunali chinthu chausayansi. Pambuyo pake analingalira kuti kuthira mwazi kunali mankhwala ake. Tsopano ena akuyamba kuzindikira nzeru ya kusachita zonsezo ndi ya kufunafuna njira zina zosakhala ndi upandu waukulu zosamalirira odwala.
Mwachionekere, zimene asayansi amadziŵa nzochepa kwambiri koposa zimene samadziŵa. The World Book Encyclopedia ikunena kuti: “Akatswiri a zomera samadziŵabe bwinobwino mmene mchitidwe wa photosynthesis umagwirira ntchito. Akatswiri odziŵa za thupi ndi akatswiri odziŵa za makemikolo sanapezebe yankho pafunso la mmene moyo unayambira. Akatswiri odziŵa za kuthambo sanapezebe yankho lokhutiritsa la magwero a chilengedwe. Akatswiri a zamankhwala ndi anthenda za maganizo samadziŵa chimene chimayambitsa kansa kapena mankhwala ake ndi mmene angachiritsire nthenda za tizilombo tosiyanasiyana. . . . Akatswiri a zamaganizo samadziŵa chimene chimachititsa nthenda zonse za maganizo.”
Sayansi imalepheranso m’lingaliro lakuti singakhale yabwinopo kuposa anthu ake. M’mawu ŵena, kupanda chidziŵitso kwa wasayansi kumakulitsidwa ndi kupanda ungwiro kwake. Alembi a bukulo 5000 Days to Save the Planet anatulukira kuti “kaŵirikaŵiri . . . magulu okhala ncholinga chapadera cha ogwiritsira ntchito molakwa mafufuzidwe, apotoza zopendedwa zopindulitsa ndi kubisa chidziŵitso kuti agulitse zinthu zimene zikhoza kuvulaza anthu kapena kupitirizabe machitachita amene ali aupandu kumalo okhala.”
Ngakhale ngati asayansi ambiri angakhale owona mtima, chimenechi sichili chifukwa chotamandira mopambanitsa ntchito yawo. “Iwo ngofanana ndi munthu aliyense,” ikunena motero nzika ina ya ku Britain, Edward Bowen, amene ali wasayansi. “Iwowa ali ndi zophophonya zawo. Ena ngodzipereka, ena osawona mtima, ena nganzeru kwambiri, ena ndi mbuli. Ndimadziŵa za anthu ena asayansi odziŵika kwambiri, amuna amene achitira dzikoli zabwino. Ndipo pamene kuli kwakuti ndimadziŵanso kuti palibe wasayansi aliyense amene anaikidwa m’ndende, ndikudziŵa za amene ali oyenerera kwambiri kuikidwamo.”
Mwachimvekere, chifukwa cha kupereŵera kwake, sayansi yamakono sidzalimbana mokwanira ndi zovuta za m’zaka za zana la 21. Sayansi yalepheradi kutetezera malo okhala, ndipo mmalo mwa kuthetsa nkhondo, yathandizira kupangidwa kwa zida zankhondo zowonongera anthu.
Kuchitapo Kanthu Mwamsanga Kukufunika
Munthu aliyense akuvomereza kuti kanthu kena kayenera kuchitidwa mwamsanga. Mwezi wa November wapitawo gulu la asayansi 1,575, kuphatikizapo anthu 99 opambana mphoto ya Nobel, anatulutsa chikalata chotchedwa kuti “Chenjezo Kumtundu wa Anthu la Asayansi a Dziko Lonse” mmene analemba kuti: “Pangotsala zaka khumi kapena zaka makumi oŵerengeka, mwaŵi wa kupeŵa tsoka limene tikuyang’anizana nalo usanatayike ndipo ziyembekezo za mtundu wa anthu zisanazimiririke kotheratu.” Iwo ananena kuti: “Anthu ndi dziko lenilenili ali pamkhalidwe wakuti adzawombana.”
Machenjezo ofanana nawo ananenedwapo. Kwenikweni, mu 1952, Bertrand Russell, wanthanthi wa m’zaka za zana la 20 wa ku Britain amenenso anali wochilikiza sayansi, anati: “Ngati moyo wa munthu uti upitirizebe kukhalapo mosasamala kanthu za sayansi, anthu adzafunikira kudziŵa kudzilanga pamalingaliro awo kumene kalelo kunali kosafunika. Anthu afunikira kugonjera ulamuliro, ngakhale pamene aganiza kuti lamulolo silabwino ndi losayenera. . . . Ngati zimenezi sizichitika mtundu wa anthu udzatha, ndipo udzatha chifukwa cha sayansi. Chosankha chodziŵika bwino chiyenera kupangidwa mkati mwa zaka 50, kusankha pakati pa Kulingalira Bwino ndi Imfa. Ndipo mwa kunena kuti ‘Kulingalira Bwino’ ndikutanthauza kufunitsitsa kugonjera lamulo loperekedwa ndi ulamuliro wa mitundu yonse. Ndikuwopa kuti mtundu wa anthu mwina ungasankhe Imfa. Ndikhulupirira kuti mwina ndikuganiza molakwa.”
Chenicheni nchakuti, anthu amene ali ofunitsitsa kugwirizana ndi miyezo yolungama masiku ano ngoŵerengeka. Mtsogoleri womenyera nkhondo zoyenera za chitaganya cha anthu, malemu Martin Luther King molondola anati: “Mphamvu yathu yausayansi yaposa mphamvu yathu ya zinthu zauzimu. Tili ndi zombo zankhondo zotsogozedwa molunjika bwino ndi anthu otsogozedwa molakwika.” Komabe, Russell anatulukira mosadziŵa chothetsera mavuto a dziko pamene ananena kuti mtundu wa anthu udzayenera “kugonjera lamulo loperekedwa ndi ulamuliro wa mitundu yonse.”
Kodi Ndani Amene Angathetse Zovutazo?
Zowona, Bertrand Russell sanali kunena za ulamuliro waumulungu pamene analankhula za lamulo loperekedwa ndi ulamuliro wa mitundu yonse. Komabe, kumvera malamulo a ulamuliro wotero ndiko kumenedi kukufunika. Malamulo a anthu ndi maulamuliro a anthu salidi yankho. Iwo sangathe kusintha dzikoli naletsa tsoka. Mbiri yomvetsa chisoni ya anthu imasonyeza kuti anthu afunikira ulamuliro wa Mulungu.c
Indedi, ndi Mulungu Wamphamvuyonse yekha, amene dzina lake ndilo Yehova, amene angapereke ulamuliro wa mitundu yonse ndi mphamvu ndi kukhoza kuthetsa zovuta za m’zaka za zana la 21. (Salmo 83:18) Ulamuliro umene anthu onse ayenera kugonjera ngati akufuna kulandira moyo ndiwo Ufumu wa Mulungu, umene uli boma lakumwamba ladziko lokhazikitsidwa ndi Mlengi, Yehova Mulungu.
Kalelo Baibulo linaneneratu ponena za boma limeneli kuti: “Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa: ndipo boma lidzakhala papheŵa lake: ndipo adzamutcha dzina lake . . . Kalonga wa Mtendere. Za kuwonjezera boma lake ndi mtendere sizidzatha.” (Yesaya 9:6, 7, King James Version) Namwali Mariya anakhala ndi pakati pa mwana wonenedweratu ameneyu, Yesu Kristu, ndipo anabadwira m’Betelehemu wa Yudeya.—Luka 1:30-33.
Pamene anali padziko lapansi Yesu anaphunzitsa otsatira ake kupempherera boma la Mulungu pamene anati: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: . . . Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ndimzimu woyera wamphamvu wa Yehova Mulungu wokha, kapena mphamvu yogwira ntchito, umene ungathandize anthu ofunitsitsa kupanga masinthidwe ofunika m’miyoyo yawo mogwirizana ndi malamulo olungama a boma lake. Sayansi singathe kutero. Zaka zikwi zambiri za kusagwirizana ndi chisokonezo ndizo umboni wakuti sayansi singathe kutero.
Yehova Mulungu, amene ali ndi nzeru ya sayansi yolongosoka yopanda malire, adzatsimikizira kuti dziko lapansi lili ndi mikhalidwe ya Paradaiso, monga momwedi zinaliri ndi munda wa Edene, pamene analenga anthu aŵiri oyamba. Panthaŵiyo iye anawalangiza kuti: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.” (Genesis 1:28) Ngakhale kuti anthuwo analephera kukhala omvera ndipo sanachite zimene anatumidwa, Yehova Mulungu adzatsimikizira kuti chifuno chake choyambacho kaamba ka dziko lapansi kuti likhale paradaiso chikukwaniritsidwa. “Ndanena, ndidzachionetsa,” iye akutero. (Yesaya 46:11) Koma kodi ndiliti pamene chifuno choyamba chimenechi cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi chidzakwaniritsidwa?
Yesu Kristu ndi atumwi ake anafotokoza mikhalidwe imene ikakhala padziko lapansi mu “masiku otsiriza,” Ufumu wa Mulungu usanachotse maboma a anthu. (2 Timoteo 3:1-5; Mateyu 24:3-14, 37-39; 2 Petro 3:3, 4) Pamene munthu aŵerenga maulosi a Baibulo otchulidwa pano ndi kuwayerekezera ndi zochitika za dziko, zonse zimaonekera bwino kuti tikukhala ndi moyo panthaŵi imene Ufumu wa Mulungu udzachitapo kanthu kofotokozedwa m’Baibulo pa Danieli 2:44 kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja [maboma a anthu amene akulamulira tsopano] Mulungu wakumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka kunthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”
Moyo Umene Uli Pafupi Mtsogolomu
Tangoyerekezerani zimene zidzachitika pafupipa mtsogolomu! Ndizinthu zokondweretsa chotani nanga zimene zasungidwira mtundu wa anthu m’zaka za zana zilinkudzazo, mwinanso ngakhale tisanafike kumeneko! Ziyambukiro zoipa za zaka zikwi zambiri za ulamuliro wa anthu opanda ugwiro, chipembedzo chonyenga, magulu amalonda aumbombo, ndi sayansi ya dzikoli zidzaloŵedwa m’malo ndi ulamuliro wa Mulungu, umene udzadalitsa anthu kuposa mmene anayembekezera.
Umu ndimo mmene Baibulo limafotokozera zochitika zimene zidzachitikadi m’dziko latsopano lolungama la Mulungu: “Tawonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo, Mulungu wawo; ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Chifukwa chake, chinthu chofunika kwambiri kwa inu ndicho kuzindikira za kuŵerengedwa kwa nthaŵi kumene kudzafika pamapeto posachedwapa pachiwonongeko cha dongosolo la dzikoli limene lili muulamuliro wa wolamulira wamphamvu wosaoneka, Satana Mdyerekezi. (Yohane 12:31; 2 Akorinto 4:3, 4) Nkofunika kuti muphunzire za chifuniro cha Mulungu ndi kuchichita, pakuti Baibulo limalonjeza kuti: “Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthaŵi zonse.”—1 Yohane 2:17.
Chotero, pamenepa, malinga ngati nthaŵi ilola, mugwiritsiretu ntchito mwanzeru makonzedwe a chipulumutso a Yehova. Pamenepo mudzakhala ndi mwaŵi wa kulandira moyo mtsogolo, inde, m’zaka za zana la 21 likudzalo—ndiponso la 22, 23, ndi mazana ena osaŵerengeka pambuyo pake. Ngati mungakhale ndi mafunso alionse okhudza Baibulo pambuyo poŵerenga magazini ano, chonde khalani aufulu kufikira Mboni za Yehova pa Nyumba Yaufumu yakwanuko, kapena kulembera ofalitsa magazini ano. (Onani patsamba 5.)
[Mawu a M’munsi]
a Kunena mwadongosolo lake, zaka za zana la 21 zidzayamba pa January 1, 2001. Komabe, kagwiritsiridwe ntchito kotchuka, kamasonyeza zaka za zana la 1 kukhala zinayambira m’chaka cha 1 ndi kuthera mu 99 (panalibe chaka cha 0); zaka za zana la 2, zikumayambira m’chaka cha 100 ndi kukathera mu 199; ndipo moyenerera, zaka za zana la 21, zidzayambira m’chaka cha 2000 ndi kuthera mu 2099.
b Imeneyi ndinkhani yotsiriza mumpambo wa nkhani zisanu ndi imodzi za sayansi m’magazini a Galamukani!
c Kusakhoza kwa maboma a anthu kunafotokozedwa mumpambo wa nkhani khumi za mu Galamukani (August 8, 1990 kufikira January 8, 1991) za mutu wakuti “Ulamuliro wa Anthu Wayesedwa Pamiyeso.”
[Bokosi patsamba 31]
Pakati pa Mbiri Yoipa, Pali Mbiri Yabwino
Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwa sayansi, unyinji wa ana okanthidwa ndi njala ndi anthu achikulire ofooka ndi kuwonda chifukwa chosoŵa chakudya udakapezekabe. Koma posachedwa pansi pa Ufumu Waumesiya, “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.”—Salmo 72:16.
Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwa sayansi, kutsenderezana ndi chiwawa ndiko mikhalidwe ya anthu mamiliyoni ambiri. Koma posachedwa Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Waumesiya ‘idzapulumutsa waumphaŵi wofuulayo; ndi wozunzika amene alibe mthandizi. . . . Idzawombola moyo wawo ku chinyengo ndi chiwawa.’—Salmo 72:12-14.
Mosasamala kanthu za kupita patsogolo kwa sayansi, kuwonjezereka kwa anthu okhala m’makonde a masitolo, kusoŵa nyumba zokhalamo ndi kupereŵedwa chakudya, kukupitirizabe kuwonjezereka padziko lonse. Koma posachedwa, pansi pa Ufumu wa Mulungu Waumesiya, anthu “adzamanga nyumba ndi kukhalamo; . . . sadzamanga, ndi wina kukhalamo; iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.
Mosasamala kanthu za kupita patsogolo m’zamankhwala, nthenda zokhoza kutetezereka zikupitirizabe kupha mamiliyoni ambiri. Koma posachedwa pansi pa Ufumu wa Mulungu Waumesiya, “wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
[Chithunzi patsamba 32]
Moyo padziko lapansi udzakhala wokondweretsa paliponse
[Mawu a Chithunzi]
Courtesy Hartebeespoortdam Snake and Animal Park