Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g93 9/8 tsamba 9-11
  • Pamene Mafuko Onse Adzakhala Pamodzi Pamtendere

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamene Mafuko Onse Adzakhala Pamodzi Pamtendere
  • Galamukani!—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Umboni wa Sayansi
  • Chifukwa Chake Pali Vutolo
  • Kuthetsa Tsankho la Fuko
  • Bwanji Ngati Umatamanda Mtundu Wako?
    Galamukani!—1998
  • Kusankhana Mitundu
    Galamukani!—2014
  • Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yokwatirana ndi Munthu wa Mtundu Wina
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Ubale Wapadziko Lonse Ngwotsimikizirika!
    Galamukani!—1990
Onani Zambiri
Galamukani!—1993
g93 9/8 tsamba 9-11

Pamene Mafuko Onse Adzakhala Pamodzi Pamtendere

“NDI mmodzi [Mulungu] analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:26) Amenewo ndiwo mawu okhweka a Baibulo ponena za chiyambi cha banja la anthu.

Amatanthauza kuti anthu onse, mosasamala kanthu za kumene amakhala kapena mikhalidwe yathupi imene ali nayo, anachokera kwa kholo limodzi. Amatanthauzanso kuti mosasamala kanthu za kusiyanasiyana konse koonedwa, “mitundu yonse ya anthu” ili ndi kuthekera kofanana kwa maluso ndi luntha. Inde, pamaso pa Mulungu, anthu a fuko lililonse kapena mtundu ali ofanana.—Machitidwe 10:34, 35.

Ngati lingaliro la Baibulo lili lolondola, ndiko kuti chiyembekezo chilipo chakuti tsankho lililonse ndi zisalungamo zozikidwa pa kusiyana kwa fuko zikhoza kuchotsedwa. Ndiponso, ngati Baibulo likunena zowona ponena za chiyambi cha banja la anthu, pamenepo buku limodzimodzilo likhoza kutipatsanso chidziŵitso chotiuza mmene fuko la anthu lidzakhalira pamodzi pamtendere.

Eya, kodi zenizeni zimasonyeza chiyani? Kodi cholembedwa cha Baibulo chonena za chiyambi cha anthu chimagwirizana ndi sayansi?

Umboni wa Sayansi

Buku lakuti The Races of Mankind, lolembedwa ndi akatswiri a mitundu ya anthu R. Benedict ndi G. Weltfish limanena kuti: “Nkhani ya m’Baibulo yonena za Adamu ndi Hava, atate ndi amayi a fuko lonse la anthu, inanena kalelo zaka mazana ambiri za chowonadi chimodzimodzi chimene sayansi yasonyeza lerolino: chakuti anthu onse a dziko lapansi ali banja limodzi ndipo ali ndi chiyambi chimodzi.” Alembi ameneŵa akunenanso kuti “mpangidwe wocholoŵana wa thupi la munthu . . . sukanatheka kuti ‘unangochitika wokha’ kukhala wofanana mwa anthu onse ngati iwo analibe chiyambi chimodzi.”

Kabuku kakuti Race and Biology, kolembedwa ndi L. C. Dunn, profesa wa zinyama pa Yunivesite ya Columbia, kakunena kuti: “Mwachionekere anthu onse ali a mtundu umodzi, ofanana m’mikhalidwe yaikulu yonse yathupi. Anthu a mafuko onse akhoza kukwatirana ndipo amaterodi.” Ndiyeno kakupitiriza kufotokoza kuti: “Komabe munthu aliyense ali wosiyana ndipo ngwapadera m’njira zazing’ono ndi munthu wina aliyense. Chifukwa china cha zimenezi ndikaamba ka malo osiyanasiyana amene anthu amakhalamo ndiponso kaamba ka kusiyanasiyana kwa majini amene amabadwa nawo.”

Umboni wa sayansi ngotsimikizirika. Kunena mogwirizana ndi sayansi ya thupi la munthu, palibe chinthu chotchedwa fuko lapamwamba kapena lotsika, fuko losadetsedwa kapena lodetsedwa. Mikhalidwe yonga maonekedwe a khungu, tsitsi, kapena maso—zinthu zimene ena amazilingalira kukhala zonyadira nazo fuko lawo—sizili chisonyezero cha luntha la munthu kapena maluso. M’malomwake, izo zangokhala zochititsidwa ndi majini obadwa nawo.

Ndithudi, zosiyana za fuko zilibe kanthu kwenikweni, monga momwe Hampton L. Carson akulembera m’buku lakuti Heredity and Human Life kuti: “Chodabwitsa chimene tikuyang’anizana nacho nchakuti fuko la anthu lililonse likuoneka kukhala losiyana kunja komabe pansi pa zosiyana zimenezi pali kufanana kwakukulu.”

Ngati anthu onse alidi banja limodzi, bwanji nanga pali mavuto oopsa a fuko?

Chifukwa Chake Pali Vutolo

Chifukwa chachikulu chimene palili tsankho la fuko ndicho chiyambi choipa chimene makolo a anthu anapatsa ana awo. Adamu ndi Hava anapandukira Mulungu mwadala ndipo motero anakhala opanda ungwiro, opunduka. Monga chotulukapo, kupanda ungwiro kwa Adamu—chikhoterero chake pachoipa—chinapitirizidwa kwa mbadwa zake. (Aroma 5:12) Chotero kuyambira pakubadwa mpaka kukula, anthu onse amakhala okhoterera padyera ndi kunyada, zimene zachititsa mkangano wa fuko ndi chipwirikiti.

Pali chifukwa china chimene pakhalira tsankho la fuko. Pamene Adamu ndi Hava anapandukira ulamuliro wa Mulungu, iwo anakhala pansi pa ulamuliro wa cholengedwa chauzimu choipa chimene Baibulo limachitcha Satana, kapena Mdyerekezi. Mosonkhezeredwa ndi ameneyu, amene ‘akunyenga dziko lonse,’ kaŵirikaŵiri pakhala zoyesayesa zakunyenga anthu pankhani ya fuko. (Chivumbulutso 12:9; 2 Akorinto 4:4) Ethnocentrism—lingaliro lakuti anthu a mtundu wako ndiwo apamwamba—lasonkhezeredwa ndi kukhala lingaliro lofala lamphamvu ndipo, modziŵa kapena mosadziŵa, mamiliyoni atengeka nalo, ndi zotsatirapo zatsoka.

Kunena mosabisa kanthu, anthu opanda ungwiro ndi adyera olamuliridwa ndi Satana awanditsa ziphunzitso zonse zonyenga ponena za fuko zimene zapangitsa mavuto a fuko.

Chifukwa chake, kuti fuko la anthu ligwirizane, onse ayenera kukhulupirira kuti tonsefe tilidi anthu a banja limodzi ndi kuti Mulungu anapanga “ndi mmodzi mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi.” (Machitidwe 17:26) Ndiponso, kuti mafuko onse akhale pamodzi pamtendere, chisonkhezero cha Satana chiyenera kuchotsedwa pakati pa zochita za anthu. Kodi zinthu zonsezi zidzachitika konse? Kodi pali maziko alionse okhulupirira kuti zidzachitikadi?

Kuthetsa Tsankho la Fuko

Yesu Kristu anasonyeza mmene tsankho la fuko lingachotsedwere pamene analamula otsatira ake ‘kukondana wina ndi mnzake’ monga momwe iye anawakondera iwo. (Yohane 13:34, 35) Chikondi chimenechi sichinayenera kukhala pakati pa anthu a fuko limodzi kapena pakati pa mafuko ena okha. Kutalitali! “Khalani ndi chikondi cha gulu lonse la abale,” mmodzi wa ophunzira ake analimbikitsa motero.—1 Petro 2:17, NW.

Kodi chikondi Chachikristu chimenechi chimasonyezedwa motani? Baibulo limafotokoza pamene limafulumiza kuti: “Mutsogolerane ndi kuchitira wina mnzake ulemu.” (Aroma 12:10) Talingalirani mmene zingakhalire ngati zimenezi zichitidwa! Aliyense akuchitira ena ulemu weniweni, mosasamala kanthu za fuko kapena mtundu, osawaona kukhala otsika, koma ‘kuwaona kukhala omuposa.’ (Afilipi 2:3) Pamene mzimu wa chikondi chenicheni Chachikristu ukhalapo, vuto la tsankho la fuko lidzatha.

Zowona, anthu amene anaphunzitsidwa tsankho la fuko, amafunikira kumenya nkhondo yaikulu kuti achotse m’maganizo mwawo malingaliro oterowo operekedwa ndi Satana. Koma zikhoza kuchitidwa! M’zaka za zana loyamba, onse amene anabweretsedwa mumpingo Wachikristu anadzasangalala ndi umodzi wosayerekezereka. Mtumwi Paulo analemba ponena za zimenezo kuti: “Muno mulibe Myuda, kapena Mhelene, muno mulibe kapolo, kapena mfulu, muno mulibe mwamuna ndi mkazi; pakuti muli nonse mmodzi mwa Kristu Yesu.” (Agalatiya 3:28) Ndithudi, otsatira enieni a Kristu anadzasangalala ndi ubale weniweni.

Koma ena angatsutse kuti: ‘Zimenezi sizidzachitika lerolino.’ Komabe, zachitika kale pakati pa Mboni za Yehova—gulu la anthu oposa mamiliyoni anayi ndi theka! Zowona, si Mboni zonse zimene zamasuka kotheratu ku tsankho limene zaphunzira m’dongosolo lopanda umulungu lino. Nzika ina ya ku America yachikuda mowona mtima inati ponena za Mboni zinzake zachiyera: “Ndimaona pakati pa ena a iwo maganizo otsalira a kunyada kwaufuko, ndipo nthaŵi zina ndaona ena kukhala osamasuka kwambiri pamene ayanjana ndi anthu a fuko lina.”

Komabe, munthuyu anavomereza kuti: “Mboni za Yehova zataya tsankho la fuko pamlingo wosayerekezereka ndi anthu alionse padziko lapansi. Izo zimalimbikira kukondana wina ndi mnzake mosasamala kanthu za fuko . . . Nthaŵi zina mtima wanga umakondwa moti ndimagwetsa misozi mosaletseka poona chikondi chenicheni cha Mboni zachiyera.”

Kodi umodzi wa mafuko wa anthu oŵerengeka—ngakhale kuti anthuwo amafika m’mamiliyoni—uli kanthu kwenikweni pamene kuli kwakuti mamiliyoni a anthu ena akusonkhezeredwa ndi malingaliro a Satana a kunyada kwaufuko? Ayi, tikuvomereza kuti zimenezo sizimathetsa vuto la fuko. Sizili m’mphamvu ya munthu kuchita zimenezo. Mlengi wathu yekha, Yehova Mulungu, ndiye akhoza kuchita zimenezo.

Mokondweretsa, posachedwapa, Yehova, mwakugwiritsira ntchito Ufumu wake wokhala m’manja mwa Mwana wake, Yesu Kristu, adzachotsera dziko lapansi chisalungamo chonse ndi onse amene mwadyera amachilikiza tsankho ndi chidani, zaufuko ndi zina. (Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10) Pamenepo, pokhala ndi programu yakuphunzitsa yangwiro pansi pa uyang’aniro wa Kristu, mafuko onse adzakhaladi ogwirizana. Pamene maphunzirowo akupita patsogolo, iwo adzakhala m’chigwirizano chenicheni popanda chizindikiro chilichonse cha tsankho la fuko. Potsirizira pake, lonjezo la Mulungu lakuti: “Zoyambazo zapita. . . . Taonani, ndichita zonse zikhale zatsopano,” lidzakwaniritsidwa.—Chivumbulutso 21:4, 5.

Kodi ndinu munthu amene amalakalaka kuona nthaŵiyo pamene ubale weniweni udzakhalapo, pamene mafuko onse adzakhala pamodzi pamtendere? Ngati nditero, tikukuitanirani kufika pa Nyumba Yaufumu yokhala pafupi nanu, kumene Mboni za Yehova zimasonkhana nthaŵi zonse kuphunzira Baibulo. Kadzionereni nokha ngati izo sizimasonyeza chikondi chenicheni Chachikristu—kwa anthu a mafuko onse.

[Chithunzi patsamba 10]

Posachedwapa mafuko onse kulikonse adzakhalira pamodzi pamtendere

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena