Mmene Dziko Lidzagwirizanitsidwira
ZOYESAYESA za anthu za kudzilamulira iwo eni mwachipambano zalephera kotheratu nthaŵi zonse. Mosakayikira mukuvomereza mawu ouziridwa akuti: “Wina apweteka mnzake pomlamulira.” (Mlaliki 8:9) Kodi nchifukwa ninji anthu alephera momvetsa chisoni kwambiri kudzilamulira?
Baibulo limapereka chifukwa, likumati: “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23) Ayi, munthu alibe mphamvu, kapena kuyenera, kwa kudzilamulira iyemwini kapena anthu anzake. Kumeneko kuli kuyenera kwapadera kwa Yehova Mulungu, Mlengi wathu, amene timauzidwa za iye kuti: “Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu.”—Yesaya 33:22.
Ndikokha pamene anthu onse avomereza Yehova Mulungu monga Wolamulira pamene dziko lidzagwirizana. Koma kodi zimenezo zidzachitikadi? Kalekale mneneri wina wa Mulungu analankhula za “masiku otsiriza,” pamene anthu ambiri akayamba kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka malangizo.
Mtendere Wapadziko Lonse Wonenedweratu
“Ndipo padzakhala masiku otsiriza,” mneneri Yesaya analemba motero, kuti ‘nyumba ya Yehova idzakhazikika pansonga ya mapiri, . . . mitundu yonse idzasonkhana kumeneko. Ndipo anthu ambiri adzamka, nati, Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake.’ Pamene tipitiriza kuŵerenga, timaona chotulukapo cha kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka malangizo. “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape,” ulosiwo ukupitiriza motero. “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:2-4.
Inde, chotulukapo cha kulabadira chiphunzitso chaumulungu chimenechi chikakhala kusamenyananso, kusakhalaponso kwa chiwawa chamafuko ndi nkhondo. Olamulira aumunthu anaganiza kuti angathe kukwaniritsa ulosi Wabaibulo umenewu ndipo analemba ngakhale mbali yake yomalizira pa khoma la United Nations Plaza ku New York City. Komabe, nkhondo ndi chidani pakati pa mitundu ndi mafuko zawonjezereka kufikira kumapeto kwa 1993. Choncho kodi munganene kuti ulosi wa Mulungu walephera?
Ayi, sunalephere—pakuti anthu a mitundu yonse tsopano lino ali kumka kunyumba ya Yehova kukalandira chiphunzitso chaumulungu. Ndithudi, Misonkhano Yachigawo ya “Chiphunzitso Chaumulungu” ya chilimwe chapitachi ya Mboni za Yehova yakhala umboni waukulu chotani nanga wa kukwaniritsidwa kwa ulosi umenewu! Gulu la abale la padziko lonse la Mboni za Yehova silimalola kalikonse—kaya kakhale fuko, mtundu kapena kakhalidwe—kuwachititsa kudana kapena kuphana. Mophiphiritsira iwo asula malupanga awo kukhala zolimira ndi nthungo zawo kukhala anangwape.
‘Komatu,’ wina angatsutse motero, ‘simungayembekezere aliyense kulabadira malangizo a Mulungu a kukondana wina ndi mnzake.’ Ngakhale kuti zimenezi nzowona, Mulungu ali ndi mphamvu ya kuchotsa onse otsutsa chifuniro chake chaumulungu.
Zimene Mulungu Adzachita
Kodi mumapemphera monga momwe Yesu anaphunzitsira otsatira ake, kuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano”? (Mateyu 6:9, 10) Ngati mumatero, mungakhale ndi chidaliro chakuti Atate wathu wachikondi wakumwamba adzayankha pemphero limenelo. Kodi ndimotani mmene adzachitira zimenezo?
Mulungu waika kale Mwana wake, “Kalonga wa Mtendere,” monga wolamulira wosankhidwa wa “boma” lake, Ufumu umene tinaphunzitsidwa kupempherera. (Yesaya 9:6, King James Version) Tifunikira wolamulira wauzimu wosakhala waumunthu wotero, popeza kuti ndiye yekha amene angachotsere anthu chisonkhezero choipa cha Satana ndi ziŵanda zake. Olamulira aumunthu, ngakhale ngati angakhale ndi cholinga chabwino, sakhoza kutero.—1 Yohane 3:8; Chivumbulutso 12:7-12.
Koma, kodi nchiyani chimene chidzachitikira maboma alipowa amene alephera kugonjera ulamuliro waumulungu? Ulosi wina wa Baibulo umene umafotokoza Ufumu umene Yesu anatiphunzitsa kupempherera umati: “Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse. . . . [Ufumu wakumwamba wa Mulungu] udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.” Chotero, kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu udze kumatanthauza kuti tikupempherera boma limodzi la padziko lonse lolamuliridwa ndi “Kalonga wa Mtendere.”—Danieli 2:44; Yesaya 9:6.
Ndiyeno, pamene banja laumunthu ligwirizana mumtendere mu Ufumu wa Mulungu, onse adzakondana wina ndi mnzake mosasamala kanthu za fuko kapena mtundu. Imeneyo idzakhala nthaŵi yosangalatsa chotani nanga! (Chivumbulutso 21:3, 4) Tikukuitanirani kulaŵa mkhalidwe wamtendere umenewo ngakhale tsopano lino pakati pa Mboni za Yehova ndiyeno kuyembekezera mwachidwi limodzi nawo kunthaŵi pamene dziko lonse lidzagwirizana mumtendere.