Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 1/8 tsamba 15-17
  • Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri—Kulekeranji?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri—Kulekeranji?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukopa kwa Kudzilamulira
  • ‘Makolo Anga Ngoletsa Kwambiri’
  • Chikhumbo cha Kuvomerezedwa ndi Ena
  • “Mayanjano Oipa”—Kuti?
  • Kupitikitsa Tsoka
  • N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kuulula Zimene Ndimachita Mseri?
    Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri
  • Achichepere Dzichinjirizeni Molimbana ndi Kutsogoza Moyo Wapaŵiri
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Nchifukwa Ninji Ndiyenera Kumvera Makolo Anga?
    Galamukani!—1995
  • Kodi Ndingasiye Motani Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri?
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 1/8 tsamba 15-17

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kukhala ndi Moyo Wapaŵiri—Kulekeranji?

“Ndinali ndi moyo wapaŵiri—wina kwa mabwenzi anga Achikristu ndipo winawo kwa mabwenzi anga akusukulu.”

MKHALIDWE wa mtsikana wogwidwa mawu pamwambapoyo siwachilendo. Koma kodi “kukhala ndi moyo wapaŵiri” kumatanthauzanji? Ruth Bell, wolemba buku lakuti Changing Bodies, Changing Lives, anafotokoza mchitidwewo kukhala “kanthu kalikonse kamene mukuchita kamene simumauza makolo anu.”

Wolemba buku ameneyu anafunsa achichepere ambiri ndipo anasimba kuti: “Achichepere ambiri ananena kuti anali kuchita zinthu m’moyo wawo zimene sakanatha kuuza makolo awo. Mbali zachinsinsi koposa zinali zonena za kugonana ndi mankhwala oledzeretsa ndi kumwa, koma anthu anatchulanso zinthu zonga kufika panyumba usiku, kukayendera limodzi ndi anthu achilendo, kujomba kusukulu, kuchita ndewu, ndi kuyanjana ndi mabwenzi amene makolo awo sanawakonde.”

Nzomvetsa chisoni kuti, ngakhale achichepere ena oleredwa ndi makolo Achikristu amabisira makolo awo ndi anthu ena zimene amachita.a (Yerekezerani ndi Salmo 26:4.) Pamene ali pakati pa makolo ndi okhulupirira anzawo, achichepere ameneŵa amaonekera kukhala achilungamo ndi owopa Mulungu. Koma pamene sakuonedwa, amachita monga ngati kuti ndianthu ena kotheratu.

Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera wachichepere kupitirizabe kukhala ndi moyo wapaŵiri?

Kukopa kwa Kudzilamulira

Baibulo limanena kuti potsirizira pake “mwamuna adzasiya atate wake ndi amake.” (Genesis 2:24) Pamenepo, kuli kokha kwachibadwa kwa inu kufuna kukhala wachikulire, kudziganizira, kudzipangira zosankha. Vuto nlakuti inu mungakhale musanakhwime. Posoŵa chidziŵitso, mufunikirabe chichirikizo cha makolo aumulungu.—Miyambo 1:8.

Achichepere ambiri amaipidwa ndi kuvomereza mfundo imeneyi. Malinga ndi kunena kwa buku lakuti How to Survive Your Child’s Rebellious Teens, achichepere ambiri amafuna “kuyeseza mphamvu zawo, titero kunena kwake, kuyesa nyonga yawo yatsopanoyo, ndi kulengeza kudzilamulira kwawo.” Pamene makolo akana kupereka chilolezo cha kuchita zinthu zimene amalingalira kukhala zosayenera—kapena zolakwa—achichepere ena amapanduka. Ndipo iwo samamva chisoni ndi kupanduka kumeneku. Mtsikana wina wachichepere akuti: “Ndimapeza bwino pochita zinthu zimene [makolo anga] samadziŵa chifukwa chakuti zimandichititsa kukhala wofunika. Ndimakhala ndi moyo wosiyana ndi iwo ndipo sindiganiza kuti amadziŵa zimenezo. . . . Sangakhulupirire zinthu zina zimene ndikuchita.”

‘Makolo Anga Ngoletsa Kwambiri’

Komabe, kodi nchifukwa ninji achichepere ena amene akuleredwa bwino kwambiri mwa Chikristu amaloŵa m’kuchita cholakwa mobisa? Pamene Galamukani! anafunsa funsoli kukagulu ka achichepere, mtsikana wina wachichepere anayankha kuti: “Amakwiyira makolo awo. Iwo amafuna kubwezera chifukwa cha kuwaletsa.” Mosakayikira, Chikristu ndicho njira ya moyo yoletsa. Yesu anati: “Chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo.” (Mateyu 7:14) Ngati mukufuna kulandira mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha, inu simungangochita zina za zinthu zimene zimalingaliridwa kukhala zosangulutsa zimene achichepere ena amachita. Mwachitsanzo, mapwando osalamulirika, timagulu takumwa moŵa, kugonana kosaloleka, kusadzisungira, zonsezo ndizo zinthu zimene zimatsutsidwa m’Baibulo.—Agalatiya 5:19-21.

Ndiyeno pali chenicheni chakuti makolo ena angaonekere kukhala oletsa mopambanitsa. “Sitimaonerera kanema aliyense,” anadandaula motero mtsikana wina wachichepere wotchedwa Kim. “Ndachepetsanso kwambiri nthaŵi yomvetsera nyimbo, ndipo ndayesa kukhala wosankha. Koma atate atiletsa kumvetsera pafupifupi nyimbo iliyonse! Timangomvetsera kokha malekodi a nyimbo za classic ndi jazz.” Atayang’anizana ndi zimene amaona kukhala ngati kuletsa kosayenera, achichepere ena amayamba kusirira ufulu umene anzawo akusangalala nawo.

Chikhumbo cha Kuvomerezedwa ndi Ena

Mtsikana wina wotchedwa Tammy akukumbukira kuti: “Ndinayamba mwa kugwiritsira ntchito mawu otukwana kusukulu. Zinandichititsa kudzimva kuti ndinali wofanana kwambiri ndi ana ena onse. Pambuyo pake ndinayesa kusuta fodya. Ndinkamwa moŵa kufikira nditaledzera. Ndiyeno ndinayamba kukhala ndi mabwenzi achinyamata—mobisa chifukwa chakuti makolo anga anali okaniza ndipo sanandilole kuyenda ndi anyamata.”

Mnyamata wina wachichepere wotchedwa Pete anali ndi chokumana nacho chofanana: “Ndinaleredwa monga mmodzi wa Mboni za Yehova. Koma ndinali kuwopa kwambiri kusekedwa, chotero nthaŵi zonse ndinayesa kukhala m’gulu la anzanga lofunika. Ndinayesa kukhala wotchuka. Ndinkanama ndi kufotokoza zifukwa zodzikhululukira zimene sindinalandirire mphatso iliyonse mkati mwa maholide achipembedzo.”b Pamene Pete anayamba kugonjera pang’onopang’ono, sipanapite nthaŵi kuti aloŵe m’mkhalidwe loipa kwambiri.

“Mayanjano Oipa”—Kuti?

Zokumana nazo zotero zimagogomezera kuwona kwa mawu a mtumwi Wachikristu Paulo akuti: “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Chotero ngati muyanjana ndi achichepere amene samalemekeza miyezo ndi makhalidwe anu ozikidwa pa Baibulo, inu mudzakopeka mosavuta ndi njira yawo ya moyo. Komabe, mokondweretsa, mtumwiyo sanali kunena mwachindunji za kuyanjana ndi osakhulupirira pamene anapereka chenjezo limenelo. Iye anali kuchenjeza za kuyanjana ndi awo amene ali mkati mwa mpingo Wachikristu amene amalephera kuchirikiza chiphunzitso Chachikristu. (1 Akorinto 15:12) Mofananamo lerolino, pangakhale achichepere amene akuyanjana ndi mpingo amene samamamatira kapena samayamikira moyo woyenera Wachikristu. Iwo akhoza kukutsenderezani mwamachenjera kuti mukhale ndi moyo wapaŵiri.

Lingaliraninso za Tammy, amene akuvomereza kuti makolo ake ali “achikondi kwambiri.” Akufotokoza atate wake kukhala “achangu kwambiri, nthaŵi zonse akumalankhula za mmene Yehova amatisamalirira.” Iwo amatumikiranso mumpingo monga mkulu. Nangano, kodi ndimotani mmene iye ananyengedwera? “Mayanjano oipa mkati mwampingo,” iye akutero. “Ena ankandiuza za chisangalalo chimene anali nacho pamapwando osiyanasiyana ndi kumwa moŵa kumene anali kuchita. Kapena ankalankhula za mabwenzi awo achinyamata ndi mmene ankapitira kokavina pambuyo pa misonkhano yampingo.”

Kupitikitsa Tsoka

Musanyalanyaze kudzisungira koipa kotero kwa achichepere mwa kungolingalira kuti, ‘Yangokhala mbali ya kukula kwa munthu’ kapena, ‘Ana onse amabisira makolo awo zinthu.’ Onani chenjezo limene Mulungu akupereka kwa achichepere pa Mlaliki 11:9, 10: “Kondwera ndi unyamata wako, mnyamata iwe; mtima wako nukasangalale masiku a unyamata wako, nuyende m’njira za mtima wako, ndi monga maso ako aona; koma dziŵitsa kuti Mulungu adzanena nawe mlandu wa zonsezi. Chifukwa chake chotsani zopweteka m’mtima mwako, [nupitikitse tsoka m’thupi, NW] lako.”

Kukhala ndi moyo wapaŵiri kungaonekere kukhala kokondweretsa. Koma potsirizira pake kumakhala msampha wakupha. (Yerekezerani ndi Salmo 9:16.) Machitidwe a kusamvera amatsogolera mosapeŵeka kumachitidwe ena owopsa kwambiri a choipa. Mwachitsanzo, Pete wachichepereyo anali womwerekera kale m’chisembwere pamene anachoka panyumba pausinkhu wa zaka 17. Podzafika zaka 18, Pete anali atamangidwa chifukwa cha kuba ndi mfuti.

Kaŵirikaŵiri achichepere ambiri amaonekera kukhala akuzemba chilango cha kupulupudza kwawo. Mungayambe kulingalira mosavuta monga momwe anachitira wolemba Baibulo Asafu, amene anavomereza kuti: “Ndinachita nsanje . . . Ndinaona kuti anthu oipa zinthu zimawayendera bwino. Samavutika ndi zoŵaŵa; ngamphamvu ndi athanzi. Samasauka monga anthu ena.” Koma mkhalidwe wowonekera kukhala wotetezereka wa oipa unakhaladi chinyengo chachikulu. Potsiriza Asafu anati: “[Mulungu] adzawaika m’malo oterera ndi kuwachititsa kugwera m’chiwonongeko!” (Salmo 73:3-5, 18, Today’s English Version) Pamenepo, ndi chifukwa chabwino Baibulo limachenjeza kuti: “Mtima wako usachitire nsanje akuchimwawo; koma opabe Yehova tsiku lonse.”—Miyambo 23:17.

Bwanji za lingaliro lakuti kusamvera makolo kumathandiza wachichepere kukula ndi kukhala wodzilamulira? Limeneli limaombana ndi uphungu wa Baibulo wa kumvetsera makolo anu. (Miyambo 23:22) Ndithudi, khalidwe lopusa kapena losasamala likangododometsa kukula kwamalingaliro ndi kwauzimu kwa munthu. Mmalomwake, ndimwanjira ya kugwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe Abaibulo pamene wina amakhala “munthu wachikulire” (NW) wokhala ndi “muyeso wa msinkhu wa chidzalo cha Kristu.”—Aefeso 4:13.

Zowonadi, makolo ena angaonekere kukhala oletsa mosayenera. Koma kodi chimenecho sichifukwa cha chikondi chawo chachikulu kwa inu ndi chikhumbo chawo cha kukutetezerani? Chotero ngati mulingalira kuti makolo anu afunikira kukupatsani ufulu pang’ono, bwanji osakambitsirana nawo—mmalo mwa kupanduka mobisa?c Kupandukako kukangodzetsa chisoni chachikulu kwa iwo, kwa inu, ndipo, koposa onse, kwa Yehova Mulungu mwiniyo.—Miyambo 10:1; 27:11.

Komabe, bwanji ngati mwayamba kale kukhala ndi moyo wapaŵiri? Kodi pali njira ya kuwonjokamo? Nkhani zotsatira zidzayankha mafunso ameneŵa.

[Mawu a M’munsi]

a Onani nkhani yakuti “Achichepere—Dzichinjirizeni Molimbana ndi Kutsogoza Moyo Wapaŵiri,” m’kope la Nsanja ya Olonda la August 1, 1988.

b Kuti mupeze nkhani ya kaimidwe ka Mboni za Yehova pamaholide achipembedzo, onani brosha lakuti School and Jehovah’s Witnesses, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

c Onani mutu 3 wa buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Zithunzi patsamba 16]

Kodi mumakhala ndi moyo wapaŵiri?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena