Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 2/8 tsamba 23-25
  • Kupenda Zochititsa Mkangano

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupenda Zochititsa Mkangano
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “Usalamulire Moyo Wanga!”
  • “Simundikonda!”
  • “Kodi Chavuta Nchiyani, Wokondedwa?”
  • “Simumandimvetsera Konse!”
  • “Ndinu Wosasamala!”
  • “Mulungu Alibe Tsankhu”
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Amuna Angatani Kuti Akazi Awo Azisangalala?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Zimene Mungachite Kuti Banja Lanu Lizisangalala
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Mungatani Kuti Musamakangane Pokambirana Mavuto Anu?
    Galamukani!—2016
Galamukani!—1994
g94 2/8 tsamba 23-25

Kupenda Zochititsa Mkangano

MKAZI amafuna kusonyeza mmene amamvera. Mwamuna amafuna kupereka zothetsera mavuto. Mikangano mamiliyoni ambiri ya muukwati kuyambira kalekale yakhala yosiyanasiyana, koma kaŵirikaŵiri pakhala zifukwa zake zazikulu zochititsa zosiyanasiyana. Kuzindikira malingaliro kapena njira yolankhulana yosiyana ya mnzanu wa muukwati kungathandize kuchepetsa moto wolirima wotentha nkhalango umenewu kukhala moto wofunditsa m’nyumba yachimwemwe.

“Usalamulire Moyo Wanga!”

Mawu ofananawo onenedwa mosalekeza a mkazi wokonda kulamulira, wovutitsa, angavutitse banja akumapangitsa amuna ambiri kukhala oletsedwa kwambiri ndi uphungu, mapempho, ndi zisulizo. Baibulo limasonyeza malingaliro otero, kuti: “Makangano a mkazi ndiwo kudonthadonthabe.” (Miyambo 19:13) Mkazi angapereke pempho limene mwamuna wake angalitsutse mwakachetechete pazifukwa zosadziŵika kwa mkaziyo. Poganiza kuti sanamve, iye tsono akumuuza zimene ayenera kuchita. Kukana kwake kukukhala kwamphamvu. Kodi ndiwo mkazi wovutitsa ndi mwamuna wouma khosi? Kapena kodi angokhala anthu aŵiri osakhoza kulankhulana bwino?

M’lingaliro la mkaziyo, iye amasonyeza chikondi chake bwino koposa kwa mwamuna wake pamene apereka uphungu wothandiza. M’lingaliro la mwamuna wake, mkaziyo akumlamulira ndipo akupereka lingaliro lakuti iye ngwosakhoza kuchita zinthu. “Musaiŵale chola chanu” ndiwo mawu osonyeza kusamala kwake, otsimikizira kuti wanyamula zonse zomwe afunikira. Mawuwa amakumbutsa mwamunayo za amake akumafuula kwa iye pakhomo kuti, “Kodi watenga juzi yako?”

Mkazi amene watopa anganene mwaulemu kuti, “Kodi mukufuna kukadyera kulesitiranti madzulo ano?” kwenikweni akumatanthauza kuti, “Kodi simumka nane kukadya kulesitiranti lero madzulo? Sindingathe kuphika chifukwa ndatopa.” Koma mwamuna wake wachikondiyo angagwiritsire ntchito mpata umenewu kuyamikira zomwe amaphika ndi kunenetsa kuti amazikonda kuposa zina zilizonse. Kapena angalingalire kuti, ‘Mkaziyu akuyesa kundilamulira mochenjera!’ Zidakali choncho, mkaziyo moipidwa anganene mumtima kuti, ‘Aa, kodi ndimafunsiranji?’

“Simundikonda!”

“Kodi angalingalire zimenezo motani?” akutero mwamuna wogwiritsidwa mwala ndi wovutika maganizo. “Ndimagwira ntchito, kupereka ndalama zolipirira zinthu, ndi kumbweretsera ngakhale maluŵa nthaŵi zina!”

Pamene kuli kwakuti anthu onse amafuna kukondedwa, mkazi amafuna kutsimikiziridwa mwapadera zimenezi ndi mobwerezabwereza. Iye sanganene zimenezi momvedwa, koma mumtima mwake amamva monga chothodwetsa, makamaka pamene nthaŵi yake ya kusamba ikumchititsa kukhala wotsenderezeka maganizo. Panthaŵi zotero mwamuna wake angatalikirane naye, akumaganiza kuti mkaziyo akufuna nthaŵi yoti akhale yekha. Mkaziyo angaone kutalikirana naye kwa mwamunayo monga chitsimikiziro cha nkhaŵa yake yaikuluyo—yakuti samamkondanso. Angamlalatire, akumayesayesa kumuumiriza kumkonda ndi kumchirikiza.

“Kodi Chavuta Nchiyani, Wokondedwa?”

Njira yosamalira vuto lopsinja maganizo ya mwamuna ingakhale ya kupeza malo abata kuti alisinkhesinkhe. Mkazi angazindikire mwachibadwa kuti pali vuto nasonkhezereka kuchitapo kanthu mwa kuyesa kumchititsa kuti alankhulane. Komabe mulimonse mmene zoyesayesa zimenezi zingakhalire zabwino, mwamuna angazione kukhala mkhalidwe wa kududukira ndi womchititsa manyazi. Pamene akudzipatula kuti asinkhesinkhe za vuto lake, akuyang’ana kumbuyo ndi kuona mkazi wake wokhulupirikayo akumlondola mosalekeza. Mwamunayo akumva liwu lachikondi losalekezalo: “Kodi muli bwino wokondedwa? Chavuta nchiyani? Tiyeni tikambitsirane.”

Ngati palibe yankho, mkaziyo angavutike mtima. Pamene ali ndi vuto, mkaziyo amafuna kukambitsirana za ilo ndi mwamunayo. Koma mwamuna amene amakondayo sakufuna kukambitsirana naye malingaliro ake. “Sakundikondanso” iye angagamule motero. Chotero pamene mwamuna wosazindikirayo achoka mumkhalidwe wake wodzipatulawo, wokhutiritsidwa ndi chothetsera vuto chimene wapeza, amapezanso, osati mnzake wa muukwati wachikondi amene anamsiya, koma mkazi wokwiya wokonzekera kumuimba mlandu chifukwa cha kumsiya yekhayekha.

“Simumandimvetsera Konse!”

Chinenezo chimenechi chimaonekera kukhala choseketsa. Kwa mwamunayo kumaonekera monga ngati kuti zomwe ayenera kuchita ndizo kumvetsera basi. Koma pamene mkazi wa mwamunayo akulankhula, mkaziyo amakhala akulingalira mwapadera kuti mawu ake akutengedwa ndi kupendedwa ndi kompyuta yoŵerengera masamu. Zikayikiro zake zimatsimikiziridwa pamene, mkati mwa kulankhula kwake, mwamunayo molanda mawu anena kuti: “Chabwino, bwanji osango . . . ?”

Pamene mkazi adza kwa mwamuna wake ndi vuto, kaŵirikaŵiri samamuimba mlandu kapena kudzafunafuna yankho kwa iye. Chimene amafuna kwambiri ndicho munthu amene adzamumvetsera momvera chisoni, osati pa zenizeni zokha, koma malingaliro a mkaziyo pa izo. Ndiyeno amafuna, osati uphungu, koma kuvomerezedwa kwa malingaliro ake. Nchifukwa chake kaŵirikaŵiri mwamuna wokhala ndi cholinga chabwino amabutsa mkangano kokha pamene anena kuti: “Usalingalire choncho, wokondedwa. Imeneyo sinkhani yaikulu kwambiri.”

Kaŵirikaŵiri, anthu amayembekezera anzawo a muukwati kudziŵa zimene akuganiza. “Takhala muukwati kwa zaka 25,” mwamuna wina anatero. “Ngati sakudziŵa zimene ndimafuna kufikira tsopano lino, ndiye kuti sasamala kapena samvetsera.” Wolemba mabuku wina m’buku lake akunena za maunansi a ukwati kuti: “Pamene anthu a muukwati sauzana zimene akufuna ndi kusulizana mosalekeza chifukwa cha kuphonya mpata wochitira zinthu, nkosadabwitsa kuti mzimu wachikondi ndi kugwirizana zimazimiririka. Mmalo mwake mumadza . . . mpikisano umene wa muukwati aliyense amayesayesa kuumiriza wina kukwaniritsa zofuna zake.”

“Ndinu Wosasamala!”

Mwina mkazi sanganene zimenezo mwachindunji kwa mwamuna wake, koma angapereke lingaliro lake moonekera bwino kwambiri m’kamvekedwe ka liwu lake. Mawu akuti “Kodi mwachedweranji kwambiri chotere?” angaonekere kukhala ofuna mafotokozedwe. Komabe, mwachionekere kwambiri, kayang’anidwe kake koimba mlandu dzanja lili m’chuuno kamanena kwa mwamuna wake kuti: “Kamwana kosasamala iwe, wandivutitsa maganizo. Chifukwa ninji sunandiimbire foni? Ndiwe wosalingalira bwino eti! Taona tsopano wawonongetsa chakudya!”

Zowonadi, iye ngwolondola ponena za chakudya. Koma ngati pabuka mkangano, kodi unansi wawonso ungakhale pachiswe? “Mikangano yambiri imachitika osati chifukwa chakuti anthu aŵiri sakugwirizana, koma chifukwa chakuti mwina mwamuna akulingalira kuti mkazi sakuvomereza lingaliro lake kapena chifukwa chakuti mkazi sakuvomereza mmene akulankhulirana naye,” akutero Dr. John Gray.

Ena ali ndi malingaliro akuti munthu ayenera kukhala womasuka kunena chilichonse chimene akufuna panyumba. Koma munthu wodziŵa bwino kulankhulana amafunafuna mgwirizano ndi kubweretsa mtendere, akumalingalira malingaliro a womvetsera. Tingayerekezere mwawamba kulankhulana kotero ndi kupatsa mnzanu wa muukwati tambula ya madzi ozizira mosiyana ndi kumuwaza nawo kumaso. Tinganene kuti kusiyana kwake kuli m’kaperekedwe.

Kugwiritsira ntchito mawu a pa Akolose 3:12-14 kudzachotsa mikangano ndi kudzetsa moyo wa banja wachimwemwe: “Valani . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso [Yehova, NW] anakhululukira inu, teroni inunso; koma koposa izi zonse khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”

[Chithunzi patsamba 25]

Mwamuna akunena zinthu mochirikiza umboni, mkazi akunena zinthu mochirikiza malingaliro

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena