Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 2/8 tsamba 14-15
  • Phwando la ku Sapporo la Chipale ndi Madzi Oundana

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Phwando la ku Sapporo la Chipale ndi Madzi Oundana
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyendayenda m’Malo a Phwandolo
  • Mmene Zifanizo za Chipale Zimapangidwira
  • Zokopa Zochititsa Chidwi
  • Kukhala Bwinobwino M’chipale Chofewa
    Galamukani!—2008
  • Madyerero Osaiŵalika a m’Mbiri ya Israyeli
    Nsanja ya Olonda—1998
Galamukani!—1994
g94 2/8 tsamba 14-15

Phwando la ku Sapporo la Chipale ndi Madzi Oundana

Ndi mtola nkhani wa Galamukani! mu Japan

MKATI mwa miyezi ya nyengo yaitali ya chisanu, Sapporo, mzinda wa kumpoto kwa Japan, umakhala wokutidwa ndi chipale. Kwa miyezi isanu mpaka isanu ndi umodzi m’chaka, panalibe zambiri zomwe anthu ake ankachita m’machitachita a zosangulutsa kufikira pamene akuluakulu a mzindawo anakambitsirana za mkhalidwewo ndipo anapeza mankhwala ake: phwando la chipale loonetsera zifanizo zazikulu zopangidwa ndi chipale.

Mu 1950, ophunzira sukulu yasekondale anathandizidwa kupanga zifanizo zisanu ndi chimodzi, za misinkhu yoyambira pa mamita atatu kufikira anayi. Anthu pafupifupi 50,000 anabwera kudzaona chifanizo chachipale chotchedwa “Venus de Milo” ndi zifanizo zina. Yuki Matsuri, kapena Phwando la Chipale, linali ndi chiyambi chabwino.

Kwa zaka zambiri phwandolo lawonjezereka muukulu ndi kutchuka kwake. Chaka chilichonse tsopano, alendo pafupifupi mamiliyoni aŵiri, kuphatikizapo ambiri ochokera kumaiko akunja, amabwera kudzaona modabwa mazanamazana a zifanizo zopangidwa ndi madzi oundana ndi chipale. Chochitika chochititsa chidwi cha m’chisanu cha masiku asanu ndi aŵiri chosakhala chachipembedzo chimenechi chakhala chachikulu koposa pazochitika za mtundu wake zonse mu Japan yense.

Kuyendayenda m’Malo a Phwandolo

Pakati pa malo atatu aphwandolo, Ōdori Park ndiwo aakulu kwambiri. Malo amenewa omwe kale anali otairako chipale chokokololedwa amatenga gawo lalikulu pakati pa Sapporo. Kunoko ndi ku Makomanai, kamtunda pang’ono, mukhoza kuona zosemedwa zazikulu zochititsa chidwi. Ana amachita mantha ndi zifanizo zazikulu mopambanitsa za anthu amene anawo amakonda kuonerera pa wailesi yakanema ndi m’mabuku a nkhani zopeka. Pali chifanizo cha munthu wopeka wozizwitsa wotchedwa Ultraman amene anyamata achichepere amakonda kutsanzira. Ndipo chapafupi pali chifanizo cha Chibi Maruko-chan ndi mabwenzi ake, ana oonetsedwa m’programu yopeka ya pawailesi yakanema.

Achikulire nawonso amadabwa. Nyumba yochitiramo maseŵero youmbidwa bwino kwambiri yotchedwa Paris Opera House, yopangidwa ndi zipupa zozokotedwa mokongola ndipo ngakhale ndi zifanizo za oimba padenga lake, imachititsa chidwi kwambiri. Palinso nyumba ya malamulo yakale yotchedwa German Diet House, chimango choumbidwa ndi chipale mumpangidwe wokometseredwa koposa. Nsanja yotchedwa Arabian Castle yosonyeza Aladdin ndi ‘nyali yake yamatsenga’ imazindikirika mosavuta.

Zimene zimaoneka monga zazifupi kwambiri chifukwa cha maonekedwe a zifanizo zazitali ndizo zosema za mu Citizens Square, zambiri za izo zokhala ndi mauthenga apadera. Chosema cha chipilala chachikumbutso cha Brandenburg Gate chimakumbutsa kugwirizana kwaposachedwa kwa Germany. Zina za zosemazo zimasonyeza kuderera nkhaŵa dziko lapansi, malo ake, ndi nyama zake.

Kumapeto kwa Ōdori Park tikupeza bwalo lotchedwa International Square kumene matimu ochokera kumaiko osiyanasiyana amapikisanira. Ena a amisiri ali aluso kwambiri amene kaŵirikaŵiri amagwiritsira ntchito miyala ya njereza, miyala wamba, ndi zinthu zina. Aliyense wa iwo anapatsidwa chipale choumitsidwa kale cha mamita atatu monsemonse ndi kupatsidwa masiku atatu akuti atsirize zosema zawo za mpikisano.

Koma kodi zifanizo zazikuluzo zimapangidwa motani ndipo kodi ndimotani mmene amisiriwo amakhozera kusema mwaluso kwambiri mbali zake zosiyanasiyana?

Mmene Zifanizo za Chipale Zimapangidwira

Kupanga chifanizo chachikulu motero sikuli ntchito yofeŵa. Pantchito imodzi yokha, kupanga kwenikweniko kungatenge pafupifupi mwezi umodzi, kukuloŵetsamo ntchito ya munthu mmodzi ya tsiku limodzi kuichulukitsa nthaŵi zoposa 1,500. Chosema china chachikulu cha mpikisano chinali chifanizo cha Flinders Street Station, ku Melbourne, mu Australia. Ukulu wake unali mamita 35 muutali, mamita 35 m’bwambi, ndi mamita 15 muusinkhu. Panafunikira malole okwanira 1,400, iliyonse ikunyamula matani 5 a chipale kututa matani 7,000 a chipale chogwiritsiridwa ntchito kuchiumba. Nchifukwa chake chiyambire mu 1955 ntchito yaikulu ya kupanga zifanizo zazikulu yakhala ikuchitidwa ndi gulu la asilikali aboma, amene pambuyo pake anadzagwirizana ndi gulu la ophunzira kuzimitsa moto. Tiyeni tione mmene amapangira zifanizo zazikulu zaluso zachipale zimenezo.

Choyamba, mutu wankhani uyenera kusankhidwa. Mawu onena za nkhaniyo ndi zithunzithunzi zimasonkhanitsidwa. Mozikidwa pa zimenezi, zifanizo zimaumbidwa ndi dongo, mapepala, kapena zinthu zina. Ndiyeno, pafupifupi mwezi umodzi phwandolo lisanafike, chipale choyera chimasonkhanitsidwa ndi kututidwira kumalo opangira. Kumeneko chimakhuthulidwa, kukanikiziridwa m’babokosi aakulu athabwa ndi kulimbitsidwa ndi madzi. Chotsatira bokosilo limachotsedwako, aimika nsanamira, ndiyeno amayamba kusema mosamalitsa.

Kaŵirikaŵiri akumagwira ntchito usiku wonse pamene kuli kozizira kwambiri, amisiriwo amagwiritsira ntchito titemo ndi mafosholo pantchito yoyambirira ndi zipangizo zazing’ono zozokotera mbali zocholoŵana.

Anthu mmodzi ndi mmodzi ndi timagulu angatengemo mbali m’chotitika chosangalatsacho. Pafupifupi gawo limodzi mwa atatu a mazana ambiri ofunsira kuchokera kumbali zonse za dzikolo osankhidwa mwamwaŵi amapatsidwa malangizo ndi gulu lapadera la akatswiri. Wofunsira aliyense amapatsidwa nchinchi yachipale youmitsidwa ya mamita aŵiri monsemonse ndi kuŵerengeredwa masiku asanu a kutsiriza choumba chakecho.

Zokopa Zochititsa Chidwi

Zosema zopangidwa ndi chipale choyera chokha zimawonjezera kukongola kwina kwa phwandolo. Zimenezi zimapangidwa kwakukulukulu ndi ziŵalo za gulu la Ice Carvers Union. Ochuluka a iwo ali akuluakulu a ophika a ku mahotela otchuka kwambiri amene kaŵirikaŵiri amaonetsera maluso awo a m’zipinda za madyerero. Iwo amakhala olakalaka kubwera ku Sapporo, ndipo zotulukapo zake zimakhala zosangalatsa kwambiri.

Oimba nyimbo ndi zionetsero zina amawonjezera chisangalalo cha phwandolo. Kumakhala mipikisano, magulu oguba, ovina, ochita maseŵera apidigoli m’matherezi amadzi oundana, ndi ena ambiri. Ana amakondwanso ndi zikuku zotsetsereka pamadzi oundana zoperekedwa kuti asangalale nazo, zopangidwira mkati mwa zosemedwazo.

Nthaŵi yausiku imakhaladi nthaŵi yabwino yoonera phwandolo. Miyandamiyanda ya timagulobu tamagetsi tating’ono tounikira m’nthambi za mitengo yopanda masamba m’pakimo, limodzi ndi nyali zamagetsi zambiri zokongola zikumaunikira zifanizo zonyezimirazo, zimapanga kuunika ndi maonekedwe okopa maso m’dziko la zozizwitsalo la m’chisanu. Mutaona phwandolo, mukhoza kukhala wosangalatsidwa ndi zimene maganizo aluso a munthu operekedwa ndi Mulungu ndi manja ake aluso akhoza kuchita.

[Zithunzi patsamba 15]

Zifanizo zachipale zazikulu zonga chili pansipa zingafikire mamita 35 m’bwambi ndi mamita 15 mumsinkhu, zikumafunikira matani 7,000 a chipale chozipangira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena