Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 3/8 tsamba 10-12
  • Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kusamuka?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kusamuka?
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Mabanja Osamuka
  • Kusokonezeka Maganizo
  • Chifukwa Chake Kusamuka Kuli Kopsinja Maganizo
  • Kuyang’anizana ndi Kusamuka
  • Kodi Ndimotani Mmene Ndingasinthire pa Kusamuka Kwathu?
    Galamukani!—1994
  • “Tuluka ku Dziko Lako ndi kwa Abale Ako”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kodi Bwenzi Langa Lapamtima Linasamukiranji?
    Galamukani!—1997
  • Kodi ndingakwanitse kukakhala pandekha?
    Galamukani!—2010
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 3/8 tsamba 10-12

Achichepere Akufunsa Kuti . . .

Kodi Nchifukwa Ninji Tiyenera Kusamuka?

Ukufika panyumba kuchokera kusukulu utalinganiza zambiri zochita pakutha kwa mlungu—tsiku lokasambira kudziŵe, kukaseŵera mpira, ndi usiku wabata woŵerenga zinthu zina. Koma pamene Amayi afika panyumba kuchokera kuntchito, nkhope yawo ikukusonyeza kuti zinthu sizili bwino. ‘Akuntchito lero anena kuti ndisankhe pakati pakusamukira kwina ndi ntchito ndi kuchotsedwa ntchito,’ iwo akutero. ‘Ndiganiza kuti tidzasamuka.’ Mwadzidzidzi m’nkhongono mukuzizira.

NGATI banja lanu lili pafupi kusamuka, simuli nokha. M’maiko ena okhuphuka, kusamuka kwafikira kukhala njira ya moyo kumabanja ambiri. Mwachitsanzo, ku United States gulu la Bureau of the Census likuyerekezera kuti munthu wamba wa ku America adzasamuka nthaŵi zokwanira 12 m’moyo wake. Eya, chaka chilichonse achichepere pafupifupi mamiliyoni 12 a ku America amatsenderezeka maganizo chifukwa cha kusamuka! Komabe, zofufuzidwa zotero zingakhale zosatonthoza pamene banja lanu ndilo limene likusamukira kwina. Inu mungathedwe mphamvu ndi lingalirolo. Mungafunse mowawidwa mtima kuti ‘Kodi nchifukwa ninji tiyenera kusamuka?’

Mabanja Osamuka

Kaŵirikaŵiri banja limakhala lopanda chochita pankhaniyo. M’nthaŵi za Baibulo banja la Elimeleki ndi Naomi linakakamizika kuthaŵira kudziko loyandikana nalo la Moabu pamene njala inakantha Israyeli. (Rute 1:1, 2) Lerolino makolo ambiri amaloŵa mumkhalidwe wovuta wofananawo. M’maiko osatukuka, chilala ndi kulekerera malo okhala zaumiriza mamiliyoni kusamukira m’mizinda ya anthu ambirimbiri ndi kumalo achithandizo—kapena kumaiko ena. Ku maiko Akumadzulo, kutsika kwa chuma kwachititsa mafakitale ndi mabizinesi ambirimbiri kutsekedwa. Malo amene kale anali auchikumbe otukuka akhala osadzetsa phindu. Ntchito zakhala zovuta kupeza. Chifukwa chake makolo anu angasoŵe chochita kusiyapo kungosamukira kumalo abwinopowo.

Komabe, simabanja onse amene amasamuka chifukwa chothaŵa umphaŵi. Kukwezedwa pantchito, kusamutsidwa kwa malo antchito a khololo, kutha kwa ukwati, kudwaladwala, mikhalidwe yoipa yakunja—zonsezi zili zifukwa zofala zimene mabanja ena amasamukira kwina. Katswiri wazachitaganya cha anthu John D. Kasarda akufotokoza chifukwa china chofala kuti: “Kukulingaliridwa kuti mizinda njangozi kwambiri lerolino. Makamaka mankhwala oledzeretsa, achititsa kuwonjezereka kofulumira kwa upandu kwa anthu osiyanasiyana ndi katundu.” Ena amalingalira kuti kukakhala kumilaga yakutali kapena kumatauni aang’ono kuli kotetezerekapo.

M’nthaŵi za Baibulo, Abrahamu anasamuka kumalo abwino akwawo ku Uri kotero kuti akatumikire zifuno za Mulungu. (Genesis 12:1; Ahebri 11:8) Lerolino mofananamo, mabanja ena pakati pa Mboni za Yehova asamukira kumadera kumene kukufunika alaliki ambiri a uthenga wa Ufumu. (Mateyu 24:14) Ena ayamba kuloŵa misonkhano kumpingo woyandikana nawo kumene kukufunika oyang’anira kapena atumiki otumikira. Pamene kuli kwakuti kusamuka kotero sikungafunikiritse kusintha malo okhala, kumatanthauza kusinthira kwa anthu ena atsopano ndi mikhalidwe.

Chilichonse chimene chili chifukwa cha kusamuka kwa banja lanu, mwinamwake sichinali lingaliro lanu. Momvetsetseka, mwina inu simungakondwe nako kwambiri.

Kusokonezeka Maganizo

Sikuti kusamuka konse nkoipa. Justin wa zaka 12 amachita tsinya pamene amakumbukira za kumene anali kukhala poyamba m’mzinda waukulu. “Anali malo oipa,” iye akutero. “Anali achiwawa kwambiri. Sunkatha kuyenda [mamita] 50 kuchoka panyumba popanda kuopa timagulu tachiwawa. Anthu ankadzitsekera m’nyumba zawo. Ndinadanadi nazo. Pamene ndinamva kuti tikusakumira kumidzi, ndinakondwa.”

Chikhalirechobe, kulingalira za kusiyana ndi mabwenzi anu ndi malo ozoloŵereka kungakuchititseni kusokonezeka maganizo. Anita wachichepere anakhala ndi malingaliro otero pamene anadziŵa kuti banja lake linali kusamukira kwina. “Ndinakulira kwambiri pamsasa wa malo ankhondo wa United States ku England,” iye akukumbukira motero. “Ndinadzilingalira kwambiri kukhala nzika ya Britain koposa nzika ya ku America. Pamene ndinali wazaka khumi, ndinatulukira kuti atate anali kusamutsidwira kwawo ku United States, ku New Mexico—chipululu! Poyamba sindinadziŵe choganiza. Ndinali wokondwera komanso wamantha. Sindinafune kusiyana ndi mabwenzi anga. Imeneyo inali mbali yovuta kwambiri ya kusamukako.”

Chifukwa Chake Kusamuka Kuli Kopsinja Maganizo

Lerolino, achichepere amaonekera kukhala oyambukiridwa mwapadera ndingozi ya chipsinjo cha kusamuka. Reader’s Digest ikunena kuti: “Akatswiri azathanzi la maganizo akutiuza kuti ngakhale kusamukira kwina kopindulitsa kumakhala chokumana nacho chopweteka, chovutitsa mtima.”

Choyamba, mkwiyo ndi chiyembekezo cha kusamukako nzopsinja maganizo. Kuchedwa kwa kayendedwe ka zinthu kosapeŵeka ndi zolepheretsa kungawonjezere mavutowo. Baibulo limati: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” (Miyambo 13:12) Ngakhale pamene aliyense akukuyembekezera mokondwa, “kusamuka kungayambitse mkhalidwe wachisoni ndi nkhaŵa m’ziŵalo za banja,” akutero magazini otchedwa Parents. “Zimenezi zimachitika chifukwa chakuti kutsazikana kumayambitsa malingaliro a kutayikiridwa ndi kusatsimikizirika kwa zamtsogolo.” Chotero sikwachilendo kupyola m’mavuto a malingaliro—mantha, mkwiyo, kugwiritsidwa mwala, ndipo ngakhale kutsenderezeka.

Buku lakuti The Teenager’s Survival Guide to Moving limati: “Kusamuka kumatanthauza zochuluka koposa kungosintha malo anu okhala. Kumatanthauza kusintha mbali zambiri zazikulu za moyo wanu—sukulu yanu, aphunzitsi anu, zochitachita zanu, mabwenzi anu. Ndipo kusintha nthaŵi zonse nkovuta, ngakhale ngati kusinthako kuli kaamba ka kuwongolera mkhalidwe.” Wogwira ntchito yothandiza osauka Myra Herbert akunena kuti kusamuka kwakaŵirikaŵiri kungachititse “kulephera ndi mavuto.” Choyamba, ana amene amasamukasamuka “nthaŵi zonse amasintha maprogramu awo a sukulu ndipo makamaka ngati kuphunzira kuli kovuta kwa iwo, amalekera panjira.” Iye akuti, kusiyana ndi mabwenzi “kuli kovuta kwambiri” kwa achichepere.

Kuyang’anizana ndi Kusamuka

Pamenepo, nkosavuta kuona chifukwa chake chiyembekezo cha kusamuka chingakupangitseni kukhala wa mtima wapachala, wokwiya, kapena wopsa mtima. Ngakhale kuti zili choncho, kukhalabe ndi malingaliro osakondweretsa kudzangopangitsa zinthu kukhala zovuta kwambiri. Kuli bwino kuyesa kukulitsa lingaliro labwino la zinthu. Malingaliro osakondweretsa, onga ngati nkhaŵa kapena chisoni, ngachibadwa m’mikhalidwe imeneyi. Kaŵirikaŵiri malingaliro ameneŵa amazimiririka m’kupita kwa nthaŵi. Pakali pano, yesani kusumika maganizo pamapindu a kusamukako.

Anita, wotchulidwa papitapoyo, tsopano ali ndi zaka 15 ndipo chiyambire pamenepo anasamukiranso kwina. “Pamene ndinasamuka, ndinali wachisoni,” iye akukumbukira motero. “Komano ndinalingalira za mbali yake yabwino—yakuti ndidzadziŵana ndi anthu atsopano ndi kumka kumalo okondweretsa.” Iye ngwachimwemwe ndipo wazoloŵera kwawo kwatsopanoko.

Nthaŵi zina, mosasamala kanthu za zoyesayesa zanu zabwino koposa, malingaliro osakondweretsa amapitirizabe. Ngati ndichoncho, musawanyalanyaze. Ndi iko komwe, “mzimu wosweka” ungakuvulazeni mwakuthupi. (Miyambo 17:22) Mwinamwake mufunikira kusamala pachosoŵa chanu cha kupuma, kulimbitsa thupi, kapena chakudya choyenera. Panthaŵi imodzimodziyo, inu mungafune kulankhula ndi wina za malingaliro anu, makamaka ndi makolo anu. (Miyambo 23:26) Adziŵitseni za mantha anu ndi nkhaŵa.

Mwachitsanzo, kodi mukuvutika mtima ndi kuti muyenera kutaya zinthu zokondedwa chifukwa chakuti ‘chipinda nchaching’ono’? Kapena kodi mukulingalira kuti kusamukako kwayandikirana ndi mayeso asukulu ndi kuti muli pansi pachitsenderezo chachikulu? Lililonse limene lingakhale dandaulo lanu, lemba la Miyambo 13:10 limatikumbutsa kuti: “Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.” Makolo anu angakulolezeni pa zinthu zina. Ngati zimenezi zili zosatheka, mosakayikira, iwo angakuchitireni chisoni, kukuchirikizani, ndi kukulimbikitsani.

Musalole mphekesera ndi mbiri zowopsa zonena za malo anu atsopano kufooketsa zoyesayesa zanu za kukhala ndi mkhalidwe wa maganizo wabwino. Pa Miyambo 14:15 pamati: “Wachibwana akhulupirira mawu onse; koma wochenjera asamalira mayendedwe ake.” Fufuzani zenizeni inu eni. Anita akuti: “Ndinapita ku laibulale ndi kukafufuza za mkhalidwe ndi mwambo wa malo amene tinasamukirako.” Mwinamwake inu mukhoza kukaona malo anu atsopanowo pasadakhale ngati simukusamukira kutali kwambiri. Zimenezi zingachite zambiri pothetsa zikayikiro zanu ndi kukuchititsani kukhala wokonzekera mwamaganizo.

Zowona, kusamuka sikudzakhala kosavuta. “Musanasamuke,” likupereka lingaliro lotero bukulo The Teenager’s Survival Guide to Moving, “kaoneni kotsiriza malo anu okondedwa . . . , ndi kutsazikana nawo.” Inu mungafune kudzaza zithunzithunzi mu alubamu kapena buku losungamo zosiyanasiyana zodzakumbukira. Chofunika kwambiri nchakuti, patulani nthaŵi yotsazikana ndi mabwenzi anu. Atsimikizireni kuti ubwenzi wanu sunathe. Mtumwi Yohane anagwiritsira ntchito “kalata ndi kapezi” kukambitsirana ndi awo amene anakonda, ndipo nanunso mukhoza kutero! (2 Yohane 12) Mwa kutsimikizira ndi kuyesayesa, ngakhale maubwenzi akutali akhoza kukula.

M’kupita kwa nthaŵi misozi yanu ya kutsazikana idzauma, ndipo mudzayang’anizana ndi chitokoso cha kusinthira kumalo anu atsopano—mutu wa nkhani m’nkhani yathu yotsatira.

[Chithunzi patsamba 11]

Bwanji osafufuza pasadakhale ndi kudziŵa za malo anu atsopano?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena